-
“Onetsetsani Mbalame”Galamukani!—2014 | August
-
-
Baibulo limatchula mbalame kambirimbiri pofuna kutiphunzitsa mfundo zofunika. Mwachitsanzo, ponena za nthiwatiwa komanso mmene imathamangira, Mulungu anauza Yobu kuti: “Ikatambasula mapiko ake ndi kuwakupiza, imaseka hatchi ndi wokwerapo wake.”a (Yobu 39:13, 18) Mulungu anafunsa Yobu kuti: “Kodi kuzindikira kwako n’kumene kumachititsa kabawi kuuluka pamwamba, . . . kapena kodi lamulo lako n’limene limachititsa chiwombankhanga kuulukira m’mwamba?” (Yobu 39:26, 27) Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Tikuphunzira kuti mbalame zimachita zinthu zogometsa kwambiri popanda kuthandizidwa ndi anthufe. Zimene mbalame zimachitazi zimasonyeza kuti Mulungu ndi wanzeru kwambiri.
-
-
“Onetsetsani Mbalame”Galamukani!—2014 | August
-
-
a Nthiwatiwa ndi mbalame yaikulu kwambiri kuposa mbalame zonse ndipo imathamanga mofulumira kwambiri. Mbalameyi imatha kuthamanga mtunda wa makilomita 72 pa ola limodzi osaima.
-