-
Yobu Afupidwa Chifukwa ChokhulupirikaNsanja ya Olonda—1998 | May 1
-
-
Koma Yobu sanafunikire kusangalala chifukwa cha kuchita manyazi kwawo. Ndithudi, Yehova anamuuza kuti apempherere omdzudzulawo. Yobu anachitadi zimene anauzidwazo, ndipo anadalitsidwa chifukwa cha zimenezo. Choyamba, Yehova anachiritsa matenda ake oopsawo. Kenaka, abale, alongo, ndi mabwenzi akale a Yobu anafika kudzamtonthoza, “nampatsanso yense ndalama ndi mphete.”a Ndiponso, Yobu “anali nazo nkhosa zikwi khumi ndi zinayi, ndi ngamila zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi ng’ombe zamagoli chikwi chimodzi, ndi abulu aakazi chikwi chimodzi.”b Ndipo mwachionekere mkazi wa Yobu anasintha maganizo nayanjana nayenso. M’kupita kwa nthaŵi, Yobu anadalitsidwa ndi ana aamuna asanu ndi aŵiri ndi ana aakazi atatu, ndipo anakhala ndi moyo mpaka mbadwo wachinayi wa mbadwa zake.—Yobu 42:10-17.
-
-
Yobu Afupidwa Chifukwa ChokhulupirikaNsanja ya Olonda—1998 | May 1
-
-
b Mwachionekere, anatchula kuti panali abulu aakazi pofuna kusonyeza phindu lawo la kuswana.
-