Phunziro pa Kusamalira Mavuto
NDI anthu oŵerengeka amene alimbanapo ndi mavuto onse amene Yobu anali nawo. M’nyengo yaifupi chabe ya nthaŵi, anakanthidwa ndi kuwonongeka kwa chuma chake ndi zomchirikiza, imfa yatsoka ya ana ake onse, ndipo potsirizira pake nthenda yopweteka kwambiri. Atanyanyalidwa ndi mabwenzi ndi achibale, anaumirizidwa ndi mkazi wake ‘kuchitira Mulungu mwano kuti afe!’—Yobu 2:9; 19:13, 14.
Komabe, Yobu ali magwero achilimbikitso apadera kwa aliyense amene akukumana ndi mayesero ofananawo. Chotulukapo chabwino cha chiyeso chimenechi chimasonyeza kuti chipiriro poyang’anizana ndi nsautso chimakondweretsa mtima wa Yehova, pamene tisonkhezeredwa ndi kudzipereka kwaumulungu koona m’malo mwa phindu laumwini.—Yobu, machaputala 1, 2; 42:10-17; Miyambo 27:11.
Nkhani ya Baibulo imeneyi ilinso ndi maphunziro ofunika ponena za mmene tingasamalilire mavuto. Imapereka zitsanzo zabwino kwambiri za mmene munthu wina amene akuyang’anizana ndi mayesero ayenera—ndi mmene sayenera—kupatsidwira uphungu. Ndiponso, chokumana nacho cha Yobu mwiniyo chingatithandize kuchita zinthu m’njira yoyenera pamene timakanthidwa ndi mavuto aakulu.
Phunziro pa Kupereka Uphungu Moipa
Mawuwo “wotonthoza Yobu” amagwiritsiridwa ntchito ponena za munthu amene, mmalo mwa kumvera chisoni panthaŵi ya tsoka, amapaka mchere pachilonda. Koma mosasamala kanthu za mbiri imene mabwenzi atatu a Yobu anadzipangira okha, sitiyenera kulingalira kuti zolinga zawo zonse zinali zoipa. Iwo anafuna kuthandiza Yobu kumlingo wina wake, molingana ndi malingaliro awo olakwawo. Kodi nchifukwa ninji analephera? Kodi ndimotani mmene anakhalira zida za Satana, amene anali wofunitsitsa kuswa umphumphu wa Yobu?
Chabwino, iwo kwakukulukulu anapereka uphungu wawo pa maziko a kungoganizira: kuti kuvutika kumadza kwa awo okha amene amachimwa. M’kulankhula kwake koyamba Elifazi anati: “Watayika ndani wosapalamula konse? Kapena oongoka mtima alikhidwa kuti? Monga umo ndaonera, olimira mphulupulu, nabzala vuto, akololapo zomwezo.” (Yobu 4:7, 8) Elifazi anakhulupirira molakwa kuti osapalamula samagweredwa ndi tsoka. Analingalira kuti popeza kuti Yobu anali m’mavuto aakulu, ayenera kukhala atachimwira Mulungu.a Onsewo Bilidadi ndi Zofari mofananamo anaumiriza Yobu kulapa machimo ake.—Yobu 8:5, 6; 11:13-15.
Mabwenzi ake atatuwo anadetsanso mtima wa Yobu mwa kunena za malingaliro a iwo eni m’malo mwa nzeru yaumulungu. Elifazi anafikiradi pakunena kuti ‘Mulungu sakhulupirira atumiki ake’ ndi kuti zinalibe kanthu kwa Yehova kuti kaya Yobu anali wolungama kapena ayi. (Yobu 4:18; 22:2, 3) Nkovuta kulingalira za mawu ena olefula maganizo kwambiri—kapena onama kwambiri—kuposa amenewo! Mosadabwitsa, Yehova pambuyo pake anadzudzula Elifazi ndi mabwenzi ake kaamba ka mwano umenewu. “Simunandinenera choyenera,” iye anatero. (Yobu 42:7) Koma chinenezo china chovulaza koposa chinalinkudza.
Potsirizira pake Elifazi anachita mopambanitsa mwa kupereka zinenezo zachindunji. Popeza kuti anali wosakhoza kuumiriza Yobu kuti avomereze liwongo, anatembenukira pa machimo ongoganizira amene analingalira kuti Yobu ayenera kukhala atachita. “Zoipa zako sizichuluka kodi? Ndi mphulupulu zako sizikhala zosaŵerengeka kodi?” Elifazi anafunsa motero. “Pakuti wamtenga chikole kwa mbale wako wopanda chifukwa, ndi kuvula ausiwa zovala zawo. Sunampatsa wolema madzi amwe, ndi wanjala unammana chakudya.” (Yobu 22:5-7) Zinenezo zimenezi zinali zopanda maziko nkomwe. Yehova mwiniyo anali atafotokoza Yobu kukhala munthu amene anali “wangwiro ndi woongoka.”—Yobu 1:8.
Kodi ndimotani mmene Yobu anachitira pa ziukiro zimenezi pa umphumphu wake? Zoonadi, zinampangitsa kukhala wopwetekedwa mtima ndi wopsinjidwa komano wotsimikiza mtima mokulirapo kusasintha kuposa ndi kale lonse kuti asonyeze kuti zinenezo zimenezi zinali zonama. Kwenikweni, iye anatengeka maganizo ndi kudzitetezera, kwakuti m’njira ina, anayamba kuimba mlandu Yehova kaamba ka tsoka lakelo. (Yobu 6:4; 9:16-18; 16:11, 12) Nkhani zenizeni zimene zinaloŵetsedwamo zinanyalanyazidwa, ndipo kukambitsiranako kunakhala mkangano wopanda pake wonena zakuti kaya Yobu anali munthu wolungama kapena ayi. Kodi ndi maphunziro otani amene Akristu angatengepo pa kachitidwe kopereka uphungu koipa kameneka?
1. Mkristu wachikondi samangolingalira kuti mavuto a mbale ali odziputira. Kusuliza mwamphamvu zophophonya zakale—kaya zikhale zenizeni kapena zongoyerekezera—kumangofooketseratu munthu amene akuyesayesa kupitirizabe molimbika. Moyo wopsinjika umafunikira ‘kulimbikitsidwa’ m’malo mwa kuimbidwa mlandu. (1 Atesalonika 5:14) Yehova akufuna kuti oyang’anira akhale “pobisalira mphepo,” osati ‘otonthoza mtima olemetsa’ monga Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari.—Yesaya 32:2; Yobu 16:2.
2. Sitiyenera konse kuimba mlandu munthu popanda umboni wooneka bwino. Mphekesera kapena kuganizira—konga kuja kwa Elifazi—sizili maziko oyenera operekera chidzudzulo. Mwachitsanzo, ngati mkulu aimba munthu mlandu molakwa, iye angataye kudaliridwa kwake ndi kudzetsa kupsinjika mtima. Kodi Yobu anamva motani pomvetsera uphungu wolakwa umenewo? Anasonyeza kuvutika mtima kwake ndi mawu owaseka akuti: “Wamthandiza bwanji wopanda mphamvu!” (Yobu 26:2) Woyang’anira wodera nkhaŵa ‘adzalimbitsa manja ogooka,’ osati kukulitsiratu vutolo.—Ahebri 12:12.
3. Uphungu uyenera kuzikidwa pa Mawu a Mulungu, osati pa malingaliro a munthu mwini. Zigomeko za mabwenzi a Yobu zinali ponse paŵiri zolakwa ndi zowononga. M’malo mwa kuyandikiza Yobu kwa Yehova, anamchititsa kuganiza kuti panali chopinga cholekanitsa iye ndi Atate wake wakumwamba. (Yobu 19:2, 6, 8) Komabe, kugwiritsira ntchito Baibulo mwaluso, kungalungamitse zinthu, kupatsa nyonga ena, ndi kupereka chitonthozo chenicheni.—Luka 24:32; Aroma 15:4; 2 Timoteo 3:16; 4:2.
Pamene kuli kwakuti buku la Yobu limathandiza Akristu kudziŵa mbuna zina, limaperekanso phunziro lothandiza pa kupereka uphungu wogwira mtima.
Mmene Tingaperekere Uphungu
Uphungu wa Elihu unali wosiyanadi ndi wa mabwenzi atatu a Yobu, ponse paŵiri m’mawu ake ndi mmene Elihu anachitira ndi Yobu. Iye anatchula Yobu ndi dzina lake nalankhula naye monga bwenzi, osati monga woweruza wa Yobu. “Komatu, Yobu, mumvere maneno anga, mutcherere khutu mawu anga. Taonani, ndikhala kwa Mulungu ngati inu; inenso ndinaumbidwa ndi dothi.” (Yobu 33:1, 6) Elihu analinso wofulumira kuyamikira Yobu kaamba ka njira yake yoongoka. “Ndifuna kukulungamitsani,” anatsimikiziritsa Yobu motero. (Yobu 33:32) Kuwonjezera pa mkhalidwe wokoma mtima umenewu wa kupereka uphungu, Elihu anali wachipambano kaamba ka zifukwa zinanso.
Pokhala atayembekezera mofatsa kufikira enawo atatsiriza kulankhula, Elihu anali wokhoza bwinopo kudziŵa nkhanizo asanapereke uphungu. Popeza kuti Yobu anali munthu wolungama, kodi Yehova akanamlangiranji? “Nkutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama!” Elihu ananena motero. “Sawachotsera wolungama maso ake.”—Yobu 34:10; 36:7.
Kodi kulungama kwa Yobu nkumenedi kunali nkhani yaikulu ya mkanganowo? Elihu anasonyeza Yobu lingaliro lake lolakwika. “Umo mukuti, Chilungamo changa chiposa cha Mulungu,” iye anafotokoza motero. “Yang’anani kumwamba, nimuone, tapenyani mitambo yokwera yakuposa inu.” (Yobu 35:2, 5) Monga momwe mitambo ilili yokwera kuposa mmene tilili, moteronso njira za Yehova zili zokwera kuposa zathu. Tili osakhoza kuweruza njira imene amachitira zinthu. “M’mwemo anthu amuwopa, iye sasamalira aliyense wanzeru mumtima,” Elihu anamaliza motero.—Yobu 37:24; Yesaya 55:9.
Uphungu wanzeru wa Elihu unakonzekeretsa Yobu kulandira malangizo owonjezereka ochokera kwa Yehova mwiniyo. Kwenikweni, pali kufanana kwakukulu pakati pa kufotokoza kwa Elihu “zodabwiza za Mulungu,” m’chaputala 37, ndi mawu a Yehova mwiniyo kwa Yobu, olembedwa m’machaputala 38 mpaka 41. Mwachionekere, Elihu anaona nkhaniyo m’lingaliro la Yehova. (Yobu 37:14) Kodi ndimotani mmene Akristu angatsanzirire chitsanzo chabwino cha Elihu?
Monga Elihu, makamaka oyang’anira afunikira kukhala achifundo ndi okoma mtima, akumakumbukira kuti nawonso ali opanda ungwiro. Kungakhale bwino kuti amvetsere mosamalitsa kotero kuti adziŵe zenizeni ndi kumvetsetsa nkhaniyo asanapereke uphungu. (Miyambo 18:13) Ndiponso, mwa kugwiritsira ntchito Baibulo ndi zofalitsidwa za Malemba, angatsimikizire kuti lingaliro la Yehova ndilo limene likulamulira.—Aroma 3:4.
Kuwonjezera pa kupereka maphunziro othandiza ameneŵa kwa akulu, buku la Yobu limatiphunzitsa mmene tingalimbanirane ndi mavuto m’njira yoyenera.
Mmene Tingapeŵere Kuchita Mosayenera Poyang’anizana ndi Mikhalidwe Yoipa
Pokhala wosweka mtima ndi kuvutika kwake ndi kugwiritsidwa mwala ndi otonthoza ake onyengawo, Yobu anaŵaŵidwa mtima ndi kupsinjika maganizo. “Litayike tsiku lobadwa ine . . . Mtima wanga ulema nawo moyo wanga,” iye anabuula motero. (Yobu 3:3; 10:1) Posadziŵa kuti Satana ndiye anali wosonkhezera, iye analingalira kuti Mulungu ndiye amene anali kumbweretsera masoka akewo. Kunaonekera kukhala kosayenera konse kuti iyeyo—munthu wolungama—azivutika. (Yobu 23:10, 11; 27:2; 30:20, 21) Mkhalidwe umenewu unaphimba maganizo a Yobu pa kulingalira zinthu zina ndi kumchititsa kuimba mlandu Mulungu pa zochita ndi mtundu wa anthu. Yehova anafunsa kuti: “Chingakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi? Udzanditsutsa kuti ndili woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?”—Yobu 40:8.
Mwina mwake chimene chimafika msanga m’maganizo pamene tiyang’anizana ndi nsautso ndicho kulingalira kukhala wochitiridwa nkhanza, monga momwe Yobu mwachionekere anachitira. Mchitidwe wofala ndiwo wa kufunsa kuti, ‘Ine ndiye ndatani? Nanga bwanji ena—amene ali oipitsitsa kuposa ine—akusangalala ndi moyo wopanda mavuto?’ Ameneŵa ali malingaliro osakondweretsa amene tingalimbane nawo mwa kusinkhasinkha Mawu a Mulungu.
Mosiyana ndi Yobu, ife tili okhoza kuzindikira nkhani zazikulu zimene zikuloŵetsedwamo. Timadziŵa kuti Satana “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.” (1 Petro 5:8) Monga momwe buku la Yobu likusonyezera, Mdyerekezi akakondwera kuswa umphumphu wathu mwa kutidzetsera mavuto. Iye ali wofunitsitsa kusonyeza chinenezo chake kukhala choona chakuti ife tili kokha Mboni za Yehova zotsata phindu chabe. (Yobu 1:9-11; 2:3-5) Kodi tidzakhala olimba mtima kuchirikiza uchifumu wa Yehova ndipo motero tikumasonyeza Mdyerekezi kukhala wonama?
Chitsanzo cha Yesu, ndi atumiki ena a Yehova okhulupirika osaŵerengeka, chimasonyeza kuti mitundu ina ya kuvutika ili yosapeŵeka m’dongosolo lino la zinthu. Yesu anati ophunzira ake ayenera kukhala ofunitsitsa ‘kunyamula [mtengo wawo wozunzirapo, NW]’ ngati akufuna kumtsata. (Luka 9:23) ‘Mtengo wathu wozunzirapo’ ungakhale nsautso imodzi kapena nsautso zambiri zimene Yobu anapirira—kudwala, imfa ya okondedwa, kupsinjika maganizo, mavuto a ndalama, kapena chitsutso cha osakhulupirira. Uliwonse umene ungakhale mtundu wa mavuto amene timakumana nawo, umakhala ndi mbali ina yabwino. Tingaone mkhalidwe wathuwo kukhala mwaŵi wosonyezera chipiriro chathu ndi kukhulupirika kwathu kosagwedezeka kwa Yehova.—Yakobo 1:2, 3.
Imeneyo ndiyo njira imene atumwi a Yesu anachitira. Posapita nthaŵi pambuyo pa Pentekoste iwo anakwapulidwa chifukwa cha kulalikira za Yesu. M’malo mwa kulefulidwa, anamka ‘mokondwera.’ Anali okondwera, osati chifukwa cha kuvutikako, koma chifukwa chakuti “anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo [la Kristu].”—Machitidwe 5:40, 41.
Zoonadi, si mavuto onse amene amatigwera chifukwa cha kutumikira Yehova. Mavuto athu mwina angakhale odzibweretsera tokha—kumlingo wina wake. Kapena mwina, osati chifukwa cha ife eni, vuto lingayambukire kukhazikika kwathu kwauzimu. Muli monse mmene zingakhalire, mkhalidwe wodzichepetsa wonga uja wa Yobu udzatikhozetsa kuzindikira pamene palakwika. Yobu anavomereza kwa Yehova kuti: “Ndinafotokozera zimene sindinazizindikira.” (Yobu 42:3) Munthu amene amazindikira zolakwa zake mwanjira imeneyi ali wothekera kwambiri kupeŵa mavuto ofananawo mtsogolo. Monga momwe mwambiwo umanenera kuti, “wochenjera aona zoipa, nabisala.”—Miyambo 22:3.
Chofunika koposa nchakuti, buku la Yobu limatikumbutsa kuti mavuto athu sadzakhalako kosatha. Baibulo limati: “Tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Tingakhale otsimikizira kuti Yehova mofananamo adzafupa kukhulupirika kwa atumiki ake lerolino.
Timayembekezeranso nthaŵi pamene mavuto amtundu uliwonse—“zoyambazo”—adzakhala atapita. (Chivumbulutso 21:4) Kufikira pamene tsikulo lifika, buku la Yobu likupitirizabe kukhala chitsogozo chamtengo wosayerekezeka chimene chingatithandize kusamalira mavuto mwanzeru ndi molimbika.
[Mawu a M’munsi]
a Pamene kuli kwakuti Baibulo limanena kuti “chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta,” zimenezi sizimatanthauza kuti kuvutika kwa munthu kuli chilango cha Mulungu. (Agalatiya 6:7) M’dziko lolamulidwa ndi Satanali, kaŵirikaŵiri olungama amavutika kwambiri kuposa mmene amachitira oipa. (1 Yohane 5:19) “Adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa,” Yesu anauza motero ophunzira ake. (Mateyu 10:22) Matenda ndi mitundu ina ya tsoka zingagwere atumiki a Mulungu okhulupirika alionse.—Salmo 41:3; 73:3-5; Afilipi 2:25-27.
[Chithunzi patsamba 28]
“Tapenyani mitambo yokwera yakuposa inu.” Elihu anathandiza Yobu motero kuzindikira kuti njira za Mulungu zili zokwera kuposa njira za munthu