-
Tikufunika KupulumutsidwaNsanja ya Olonda—2008 | March 1
-
-
Sikuti ambirife tingatsekerezedwe mu mgodi ngati mmene anachitira anthu 9 aja, ndipo mwina sitingafe pa ngozi. Komabe, m’pofunika kuti tipulumutsidwe ku mavuto osapeweka monga matenda, ukalamba ndi imfa. Ndipotu Yobu ananena kuti: “Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto. Atuluka ngati duwa, nafota; athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.” (Yobu 14:1, 2) Mawu amenewa adakali oona masiku ngakhale kuti tsopano papita zaka pafupifupi 3,500 kuchokera pamene ananenedwa. Izi zili choncho chifukwa palibe amene angazembe imfa. Motero, kaya tikukhala kuti kapena tikusamalira bwanji moyo wathu, tifunikira kupulumutsidwa ku mavuto monga ukalamba ndi imfa.
-
-
Tikufunika KupulumutsidwaNsanja ya Olonda—2008 | March 1
-
-
Kaya mukugwirizana ndi maganizo a Yobu pankhani ya moyo ndi imfa kapena ayi, simungapewe mfundo yakuti pamene zaka zikutha inunso ‘mudzathawa ngati mthunzi’ kapena kuti mudzafa. Mudzasiya anzanu, banja lanu, nyumba yanu ndiponso zinthu zanu zonse. Ndipotu Solomo, mfumu yanzeru ya Isiraeli wakale, inalemba kuti: “Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.”—Mlaliki 9:5.
-