PHUNZIRO 30
Achibale Anu Ndi Anzanu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo
Wachibale kapena mnzathu akamwalira, zimakhala zopweteka kwambiri. N’chifukwa chake Baibulo limati imfa ndi mdani. (1 Akorinto 15:26) M’phunziro 27 munaphunzira kuti Yehova adzagonjetsa mdani ameneyu. Nanga n’chiyani chidzachitikire anthu amene anamwalira? M’phunziroli tiona chinthu chinanso chosangalatsa kwambiri chimene Yehova analonjeza chokhudza anthu amene anamwalira. Iye analonjeza kuti adzaukitsa anthu ambirimbiri amene anamwalira kuti adzakhale ndi moyo mpaka kalekale. Kodi inuyo mukuona kuti zimenezi zidzachitikadi? Kodi anthu amene adzaukitsidwe azidzakhala kuti, kumwamba kapena padzikoli?
1. Kodi Yehova amafuna kudzawachitira chiyani achibale ndi anzathu amene anamwalira?
Yehova amalakalaka kudzaukitsa anthu amene anamwalira. Yobu, yemwe anali munthu wachikhulupiriro sankakayikira kuti akadzamwalira Mulungu adzamuukitsa. Iye anauza Mulungu kuti: “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha [kuchokera kumanda].”—Werengani Yobu 14:13-15.
2. Kodi timadziwa bwanji kuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa?
Yesu ali padzikoli, Mulungu anamupatsa mphamvu zoukitsira anthu. Mwachitsanzo, Yesu anaukitsa kamtsikana kazaka 12 komanso mwana wamwamuna wa mkazi wina wamasiye. (Maliko 5:41, 42; Luka 7:12-15) Pa nthawi inanso Lazaro, yemwe anali mnzake wa Yesu, anamwalira. Yesu anaukitsa Lazaro ngakhale kuti anali atakhala m’manda masiku 4. Yesu atapemphera kwa Mulungu anafuula kuti: “Lazaro, tuluka!” Ndipo “amene anali wakufa uja anatuluka.” (Yohane 11:43, 44) Apatu achibale ndi anzake a Lazaro anasangalala kwambiri.
3. Kodi achibale ndi anzanu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo?
Baibulo limatilonjeza kuti: “Kudzakhala kuuka.” (Machitidwe 24:15) Anthu onse amene Yesu anawaukitsa ali padziko lapansili, sanapite kumwamba. (Yohane 3:13) Iwo anasangalala kwambiri kuukitsidwa kuti akhalenso ndi moyo padziko pompano. Mofanana ndi zimenezi, Yesu adzaukitsa anthu ambirimbiri kuti akhale ndi moyo m’Paradaiso padzikoli mpaka kalekale. Iye ananena kuti anthu ‘onse amene ali m’manda a chikumbutso’ adzaukitsidwa. Anthu amene Mulungu akuwakumbukira akuphatikizapo onse amene tinawaiwala komanso amene sitikuwadziwa n’komwe.—Yohane 5:28, 29.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake Baibulo limanena kuti Yesu ali ndi mphamvu zotha kuukitsa anthu amene anamwalira komanso kuti adzachita zimenezi m’tsogolo. Onani mmene kudziwa kuti akufa adzauka kungakutonthozereni komanso kukupatsani chiyembekezo.
4. Zimene Yesu anachita ndi umboni wakuti akhoza kuukitsa anthu amene anamwalira
Dziwani zambiri zokhudza zimene Yesu anachita poukitsa Lazaro. Werengani Yohane 11:14, 38-44, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi timadziwa bwanji kuti Lazaro anali atamwaliradi?—Onani vesi 39.
Zikanakhala kuti Lazaro wapita kumwamba, kodi zikanakhala zomveka kuti Yesu amuukitse kuchokera kumwambako n’kumubweretsa padziko lapansi pano?
5. Anthu ambiri adzaukitsidwa
Werengani Salimo 37:29, kenako mukambirane funso ili:
Kodi anthu ambirimbiri omwe adzaukitsidwe adzakhala kuti?
Yesu adzaukitsa anthu ambiri, kuphatikizapo amene sankalambira Yehova. Werengani Machitidwe 24:15, kenako mukambirane funso ili:
Ndi ndani amene mungakonde kudzamuona ataukitsidwa?
Taganizirani izi: Yesu sangavutike kuukitsa munthu yemwe anamwalira mofanana ndi mmene bambo angadzutsire mwana wake akagona
6. Kudziwa kuti akufa adzauka kungakutonthozeni komanso kukupatsani chiyembekezo
Nkhani ya m’Baibulo ya mwana wamkazi wa Yairo yalimbikitsa ndi kutonthoza anthu ambiri omwe aferedwa. Werengani nkhaniyi yomwe inachitikadi pa Luka 8:40-42, 49-56.
Yesu asanaukitse mwana wamkazi wa Yairo anauza bambo a mwanayo kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi.” (Onani vesi 50.) Kodi chiyembekezo chakuti akufa adzauka chingakuthandizeni bwanji . . .
wachibale kapena mnzanu akamwalira?
moyo wanu ukakhala pa ngozi?
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Kodi chiyembekezo chakuti akufa adzauka chinathandiza bwanji makolo a Phelicity?
ZIMENE ENA AMANENA: “Anthu amene anamwalira adzakhala ndi moyo kumwamba osati padziko lapansi.”
Inuyo mukuganiza bwanji?
Kodi mungawerenge lemba liti pofuna kuwathandiza kudziwa kuti anthu ambiri amene adzaukitsidwe adzakhala padzikoli?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Baibulo limanena kuti anthu ambirimbiri amene anamwalira adzaukitsidwa. Yehova akufuna kuti anthu amenewa adzakhalenso ndi moyo ndipo anapatsa Yesu mphamvu zoti adzawaukitse.
Kubwereza
Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova ndi Yesu amafunitsitsa kuukitsa anthu amene anamwalira?
Kodi anthu ambiri omwe adzaukitsidwe adzakhala kuti, kumwamba kapena padziko lapansi? N’chifukwa chiyani mukutero?
N’chiyani chikukuchititsani kukhulupirira kuti achibale ndi anzanu amene anamwalira adzaukitsidwa?
ONANI ZINANSO
Onani mfundo zimene zingakuthandizeni mukaferedwa.
Kodi mfundo za m’Baibulo zingathandizedi munthu amene waferedwa?
Kodi ana angatani kuti apirire imfa ya mnzawo kapena wachibale wawo?
Kodi pali anthu ena amene akamwalira amapita kumwamba? Kodi ndi anthu ati amene sadzaukitsidwa?
“Kodi Mawu Akuti Kuuka kwa Akufa Amatanthauza Chiyani?” (Nkhani yapawebusaiti)