Kwezani Manja Okhulupirika m’Pemphero
“Ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera [“okhulupirika,” NW], opanda mkwiyo ndi makani.”—1 TIMOTEO 2:8.
1, 2. (a) Kodi 1 Timoteo 2:8 amagwira ntchito motani pamapemphero a anthu a Yehova? (b) Kodi tidzapenda chiyani tsopano?
YEHOVA amafuna anthu ake kukhala okhulupirika kwa iye ndi kwa wina ndi mnzake. Mtumwi Paulo anagwirizanitsa kukhulupirika ndi pemphero pamene analemba kuti: “Ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera [okhulupirika], opanda mkwiyo ndi makani.” (1 Timoteo 2:8) Mwachionekere, Paulo anali kunena za pemphero lapoyera “pamalo ponse” pamene Akristu anasonkhana. Kodi ndani anayenera kuimira anthu a Mulungu m’pemphero pamisonkhano ya mpingo? Ndi amuna oyera, olungama, ndi aulemu okha amene anasamala bwino mangawa onse a m’Malemba a kwa Mulungu. (Mlaliki 12:13, 14) Anayenera kukhala oyera mwauzimu ndi mwakhalidwe ndiponso odzipereka kotheratu kwa Yehova Mulungu.
2 Makamaka akulu a mpingo ayenera ‘kukweza manja okhulupirika popemphera.’ Mapemphero awo ochokera pansi pa mtima kudzera mwa Yesu Kristu amaonetsa kukhulupirika kwawo kwa Mulungu ndipo amawathandiza kupewa makani ndi mkwiyo. Ndipotu, mwamuna aliyense wopatsidwa mwayi woimira mpingo wachikristu papemphero lapoyera ayenera kukhala wopanda mkwiyo ndi chidani. Asakhale wosakhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake. (Yakobo 1:19, 20) Kodi pali zitsogozo zinanso zotani m’Baibulo kwa aja opatsidwa mwayi woimira ena pamapemphero apoyera? Ndipo ndi mapulinsipulo ati a m’Malemba amene tiyenera kugwiritsa ntchito m’mapemphero athu patokha ndiponso ndi banja?
Ganizanipo pa Pempherolo Musanalipereke
3, 4. (a) N’chifukwa chiyani kuli kopindulitsa kuliganizapo pemphero pasadakhale? (b) Kodi Malemba amasonyezanji ponena za utali wa mapemphero?
3 Tikapemphedwa kupemphera poyera, mosalephera tidzaliganizapo pempherolo tisanakalipereke. Kuteroko kudzathandiza kutchula mfundo zofunika popanda kupereka pemphero lalitali longozungulira. Inde, popereka mapemphero athu patokha tingamamveketse mawu. Mapempherowo angatalike mmene tifunira. Yesu anapemphera usiku wonse asanasankhe atumwi ake 12. Komabe, pamene anayambitsa Chikumbutso cha imfa yake, mapemphero ake pa mkate ndi vinyo mwachionekere anali aafupipo. (Marko 14:22-24; Luka 6:12-16) Ndipo tikudziŵa kuti ngakhale mapemphero aafupi a Yesu anali olandirika kwa Mulungu.
4 Tinene kuti tapatsidwa mwayi woimira banja m’pemphero tisanayambe kudya. Pemphero limenelo liyenera kukhala lalifupi bwino—komanso zilizonse zomwe zingatchulidwemo ziyenera kuphatikizapo mawu othokoza kaamba ka chakudyacho. Ngati tikupemphera poyera poyamba msonkhano wachikristu kapena pomaliza, sitifunikira kupereka pemphero lalitali lofotokoza mfundo zambirimbiri. Yesu anatsutsa alembi amene ‘monyenga anachita mapemphero aatali.’ (Luka 20:46, 47) Munthu woopa Mulungu sangakonde kuchita zimenezo. Komabe, nthaŵi zina pemphero lalitalipo lapoyera lingakhale loyenera. Mwachitsanzo, mkulu wosankhidwa kupereka pemphero lomaliza pamsonkhano waukulu ayenera kuliganizapo pasadakhale ndipo angafune kutchula mfundo zambiri. Komano, ngakhale pemphero lotero siliyenera kukhala lalitali mopambanitsa.
Fikani kwa Mulungu Mwaulemu
5. (a) Kodi tiyenera kukumbukira chiyani popemphera poyera? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera mosamala komanso mwaulemu?
5 Popemphera poyera tiyenera kukumbukira kuti sitikulankhula ndi anthu anzathu. Koma ndife zolengedwa zochimwa amene tikupemphera kwa Ambuye Mfumu Yehova. (Salmo 8:3-5, 9; 73:28) Ndiye chifukwa chake mwa zimene tinena ndi mmene tineneramo, tiyenera kuonetsa mantha aulemu oopa kusam’kondweretsa. (Miyambo 1:7) Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzaloŵa m’nyumba yanu: ndidzagwada kuyang’ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.” (Salmo 5:7) Ngati tili ndi mtima womwewo, kodi tidzalankhula motani tikapemphedwa kupemphera poyera pamsonkhano wa Mboni za Yehova? Chabwino, ngati tinali kulankhula kwa mfumu yaumunthu, tikanatero mwaulemu komanso mosamala. Choncho kodi mapemphero athu sayenera kuperekedwa mosamala koposa komanso mwaulemu popeza tikupemphera kwa Yehova, ‘Mfumu ya nthaŵi zosatha’? (Chivumbulutso 15:3) Chotero, popemphera tidzapewa mawu onga akuti, “Mwadzuka bwanji, Yehova,” “Landirani moni wathu,” kapena akuti, “Tsalani bwino.” Malemba amasonyeza kuti Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, Yesu Kristu, sanalankhulepo ndi Atate wake wakumwamba mwanjira imeneyo.
6. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ‘poyandikira mpando wachifumu wachisomo’?
6 Paulo anati: “Tilimbike mtima [“tikhale ndi ufulu wa kulankhula,” NW] poyandikira mpando wachifumu wachisomo.” (Ahebri 4:16) Chifukwa cha kukhulupirira kwathu nsembe ya dipo la Yesu Kristu, tingafike kwa Yehova ndi “ufulu wa kulankhula” ngakhale kuti ndife ochimwa. (Machitidwe 10:42, 43; 20:20, 21) Komano, “ufulu wa kulankhula” umenewo sutanthauza kuti tikucheza ndi Mulungu; ndipo sitiyenera kulankhula zinthu zopanda ulemu kwa iye. Kuti mapemphero athu apoyera akondweretse Yehova, ayenera kuperekedwa ndi ulemu wake komanso mosamala, ndipo n’kulakwa kuwagwiritsa ntchito kulengezera zinthu, kupatsira ena uphungu, kapena kukalipira omvetsera.
Pempherani ndi Mzimu Wodzichepetsa
7. Kodi Solomo anaonetsa motani kudzichepetsa popemphera pakupatulira kachisi wa Yehova?
7 Kaya tikupemphera poyera kapena patokha, mfundo yofunika ya m’Malemba imene tiyenera kukumbukira ndi yakuti tiyenera kuonetsa mtima wodzichepetsa m’mapemphero athu. (2 Mbiri 7:13, 14) Mfumu Solomo inaonetsa kudzichepetsa papemphero lake lapoyera popatulira kachisi wa Yehova m’Yerusalemu. Solomo anali atangomaliza imodzi ya nyumba zaulemerero koposa zomangidwa padziko lapansi. Komabe, anapemphera modzichepetsa kuti: “Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi m’Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.”—1 Mafumu 8:27.
8. Kodi kudzichepetsa kumaonekera mwa njira zina zotani popemphera poyera?
8 Monga Solomo, tiyenera kukhala odzichepetsa poimira ena m’pemphero lapoyera. Ngakhale kuti tiyenera kupewa kumveka ngati wopatulika kwambiri, tingaonetse kudzichepetsa mwa kamvekedwe ka mawu athu. Mapemphero odzichepetsa sakhala okometsera mopambanitsa kapena oyerekeza kukhudzidwa mtima. Amapangitsa anthu kuganiza, osati za amene akupempherayo, koma amene akupempherakoyo. (Mateyu 6:5) Kudzichepetsa kumaonekeranso mwa zimene tinena popemphera. Ngati tipemphera modzichepetsa, sitidzamveka monga ngati tikum’lamulira Mulungu kuchita zimene tikufuna. M’malo mwake, tidzapempha Yehova kuchita zimene zikugwirizana ndi chifuniro chake chopatulika. Wamasalmo anaonetsa mzimu woyenera pamene anachonderera kuti: “Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano; tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.”—Salmo 118:25; Luka 18:9-14.
Pempherani Kuchokera mu Mtima
9. Kodi uphungu wabwino woperekedwa ndi Yesu ndi wotani umene ukupezeka pa Mateyu 6:7, ndipo ungagwiritsidwe ntchito motani?
9 Kuti mapemphero athu apoyera kapena apatokha akondweretse Yehova, ayenera kuchokera mu mtima. Chotero, sitidzakhala tikumangobwerezabwereza mawu amodzimodzi m’pemphero lililonse popanda kuganiza za zimene tikunenazo. Pa Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu analangiza kuti: “Popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa [molakwika] kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwawo.” Kunena kwina, Yesu anati: “Osabwebweta; osalankhula mawu opanda tanthauzo mobwerezabwereza.”—Mateyu 6:7, NW; mawu amtsinde.
10. N’chifukwa chiyani kungakhale koyenera kupempherera chinthu chimodzimodzi kangapo?
10 Zoonadi tingafunikire kupempherera chinthu chimodzimodzicho mobwerezabwereza. Kuteroko sikulakwa chifukwa Yesu analimbikitsa kuti: “Pemphani [“Pitirizani kupempha,” NW], ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani [“pitirizani kufunafuna,” NW], ndipo mudzapeza; gogodani [“pitirizani kugogoda,” NW], ndipo chidzatsegulidwa kwa inu.” (Mateyu 7:7) Mwinamwake pafunika Nyumba ya Ufumu yatsopano chifukwa chakuti Yehova akudalitsa ntchito yolalikira kwanuko. (Yesaya 60:22) Ndi koyenera kumatchulabe zimenezi popemphera patokha kapena poyera pamisonkhano ya anthu a Yehova. Kuteroko sikudzatanthauza kuti ‘tikulankhula mawu opanda tanthauzo mobwerezabwereza.’
Kumbukirani Kuthokoza ndi Kutamanda
11. Kodi Afilipi 4:6, 7 amagwira ntchito motani pa pemphero lapatokha ndi lapoyera?
11 Anthu ambiri amangopemphera akamafuna chinachake, koma kukonda kwathu Yehova Mulungu kuyenera kutisonkhezera kum’yamika ndi kum’tamanda m’mapemphero athu patokha ndi poyera. “Musadere nkhaŵa konse,” analemba Paulo, “komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Inde, kuwonjezera pa pembedzero ndi kupempha, tiyenera kuyamikira Yehova kaamba ka madalitso auzimu ndi akuthupi. (Miyambo 10:22) Wamasalmo anaimba kuti: “Pereka kwa Mulungu nsembe yachiyamiko; num’chitire Wam’mwambamwamba chowinda chako.” (Salmo 50:14) Ndipo nyimbo ya Davide ya pemphero inaphatikizapo mawu awa okhudza mtima: “Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliimbira, ndipo ndidzam’bukitsa ndi kum’yamika.” (Salmo 69:30) Kodi sitiyenera kuchita zomwezi m’mapemphero athu poyera ndi patokha?
12. Kodi Salmo 100:4, 5 likukwaniritsidwa motani lero, ndipo tingam’yamikire ndi kum’tamanda Mulungu pachifukwa chotani?
12 Ponena za Mulungu, wamasalmo anaimba kuti: “Loŵani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: m’yamikeni; lilemekezeni dzina lake. Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimamka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.” (Salmo 100:4, 5) Lero, anthu a m’mitundu yonse akuloŵa m’mabwalo a kachisi wa Yehova, ndipo pachifukwa chimenechi tingam’tamande ndi kum’yamika. Kodi mumam’thokoza Mulungu chifukwa cha Nyumba yanu ya Ufumu ndi kusonyeza chiyamikiro chanu mwa kusonkhana komweko nthaŵi zonse ndi awo amene am’konda iye? Pamene muli komweko, kodi mumakweza liwu lanu ndi mtima wonse poimba nyimbo zachitamando ndi chiyamiko kwa Atate wathu wakumwamba wachikondi?
Musachite Manyazi Kupemphera
13. Kodi ndi chitsanzo chiti cha m’Malemba chimene chisonyeza kuti tiyenera kupembedzera Yehova ngakhale ngati tikudzimva kukhala wosayenerera chifukwa chopalamula?
13 Ngakhale ngati tikudzimva kukhala wosayenerera chifukwa chopalamula, tiyenera kutembenukira kwa Mulungu kum’pembedza ndi mtima wonse. Pamene Ayuda anachimwa mwa kutenga akazi akunja, Ezara anagwada, kutambasula manja ake okhulupirika kwa Mulungu, napemphera modzichepetsa kuti: “Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuŵeramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zachuluka pamtu pathu, ndi kupalamula kwathu kwakula kufikira m’Mwamba. Chiyambire masiku a makolo athu tapalamula kwakukulu mpaka lerolino . . . Ndipo zitatigwera zonsezi chifukwa cha ntchito zathu zoipa ndi kupalamula kwathu kwakukulu; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga motichepsera mphulupulu zathu, ndi kutipatsa chipulumutso chotere; kodi tidzabwereza kuphwanya malamulo anu, ndi kukwatana nayo mitundu ya anthu ochita zonyansa izi? Simudzakwiya nafe kodi mpaka mwatitha, ndi kuti pasakhale otsala kapena akupulumuka? Yehova Mulungu wa Israyeli, Inu ndinu wolungama, popeza tinatsala opulumuka monga lerolino; taonani, tili pamaso panu m’kupalamula kwathu; pakuti palibe wakuima pamaso panu chifukwa cha ichi.”—Ezara 9:1-15; Deuteronomo 7:3, 4.
14. Malinga ndi zimene zinachitika m’tsiku la Ezara, kodi chofunika n’chiyani kuti Mulungu atikhululukire?
14 Kuti Mulungu atikhululukire, poulula kwa iye tiyenera kukhalanso achisoni ndi “zipatso zakuyenera kulapa.” (Luka 3:8; Yobu 42:1-6; Yesaya 66:2) M’tsiku la Ezara, kuwonjezera pa mtima wolapa anayesetsanso kukonza cholakwacho mwa kupitikitsa akazi akunja. (Ezara 10:44, NW; yerekezerani ndi 2 Akorinto 7:8-13.) Ngati tikufuna kuti Mulungu atikhululukire tchimo lalikulu, tiulule m’pemphero lodzichepetsa ndi kubala zipatso zoyenera kulapa. Mzimu wolapa ndi kufunitsitsa kukonza cholakwacho zidzatisonkhezeranso kupempha thandizo kwa akulu achikristu.—Yakobo 5:13-15.
Pezani Chitonthozo m’Pemphero
15. Kodi zimene zinachitikira Hana zikusonyeza motani kuti tingapeze chitonthozo m’pemphero?
15 Pamene mtima wathu uli ndi chisoni chifukwa cha zinthu zina, tingapeze chitonthozo m’pemphero. (Salmo 51:17; Miyambo 15:13) Hana wokhulupirikayo anatero. Anali ndi moyo panthaŵi imene mabanja aakulu anali ambiri m’Israyeli, koma iye analibe mwana. Mwamuna wake, Elikana, anali ndi ana aamuna ndi aakazi mwa mkazi wake wina, Penina, amene ankanyodola Hana chifukwa chokhala wosabala. Hana anapemphera ndi mtima wonse nalonjeza kuti akadalitsidwa ndi mwana wamwamuna, ‘akam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake.’ Potonthozedwa ndi pemphero lake ndi mawu a Mkulu wa Ansembe Eli, Hana ‘sanakhalanso wachisoni.’ Anabala mwana wamwamuna namutcha dzina lake Samueli. Pambuyo pake, anam’pereka kukachisi kukatumikira Yehova. (1 Samueli 1:9-28) Pothokoza Mulungu kaamba ka kum’komera mtima, anapereka pemphero lachiyamiko—limene linatamanda Yehova kuti alibe wina wofanana naye. (1 Samueli 2:1-10) Monga Hana, tingapeze chitonthozo m’pemphero, pokhala ndi chidaliro chakuti Mulungu amayankha mapempho onse ogwirizana ndi chifuniro chake. Titatsanulira mtima wathu kwa iye, ‘tisakhalenso achisoni,’ pakuti adzachotsa mtolo wathu kapena adzatithandiza kuusenza.—Salmo 55:22.
16. Malinga ndi mmene nkhani ya Yakobo ikusonyezera, nchifukwa chiyani tiyenera kupemphera pamene tili amantha kapena ankhaŵa?
16 Ngati zinthu zikutiopsa, kutipweteka mtima, kapena kutipatsa nkhaŵa, tisalephere kutembenukira kwa Mulungu m’pemphero kuti atitonthoze. (Salmo 55:1-4) Yakobo anachita mantha pamene anali pafupi kukumana ndi mbale wake Esau amene anali mdani wake. Koma Yakobo anapemphera kuti: “Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isake, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira iwe bwino: sindiyenera zazing’ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndi ndodo yanga ndinaoloka pa Yordano uyu; ndipo tsopano ndili makamu aŵiri. Mundipulumutsetu ine m’dzanja la mkulu wanga, m’dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amayi pamodzi ndi ana. Ndipo Inu munati, Ndidzakuchitira iwe bwino ndithu, ndidzakuyesa mbewu yako monga mchenga wa panyanja yaikulu, umene sungathe kuŵerengeka chifukwa cha unyinji wake.” (Genesis 32:9-12) Esau sanakanthe Yakobo ndi anthu ake. Chotero Yehova ‘anamchitiradi bwino’ Yakobo panthaŵiyo.
17. Mogwirizana ndi Salmo 119:52, kodi pemphero lingatitonthoze motani pamene tikuyesedwa kwambiri?
17 Pamene tikupemphera, tingatonthozedwe mwa kukumbukira zinthu zonenedwa m’Mawu a Mulungu. M’salmo lalitali koposa—pemphero lokongola loimbidwa m’nyimbo—ayenera kuti anali Kalonga Hezekiya amene anaimba kuti: “Ndinakumbukira maweruzo anu kuyambira kale, Yehova, ndipo ndinadzitonthoza.” (Salmo 119:52) Popereka pemphero modzichepetsa pamene tikuyesedwa kwambiri, tingakumbukire pulinsipulo la m’Baibulo kapena lamulo limene lingatithandize kutsata njira imene motonthoza imatitsimikiza kuti tikukondweretsa Atate wathu wakumwamba.
Okhulupirika Amalimbika Kupemphera
18. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ‘okhulupirika onse amapemphera kwa Mulungu’?
18 Onse okhulupirika kwa Yehova Mulungu ‘amalimbika chilimbikire m’kupemphera.’ (Aroma 12:12) M’Salmo la 32, limene liyenera kuti linalembedwa ndi Davide atachimwa ndi Batiseba, anafotokozamo nsautso yake chifukwa cholephera kupempha chikhululukiro ndiponso chitonthozo chimene anapeza mwa kulapa kwake ndi kuuza Mulungu tchimo lake. Ndiyeno Davide anaimba kuti: “Chifukwa chake [chifukwa chakuti Yehova amakhululukira aliyense wolapadi] oyera mtima [“okhulupirika,” NW] onse apemphere kwa Inu, panthaŵi ya kupeza Inu.”—Salmo 32:6.
19. N’chifukwa chiyani tiyenera kukweza manja okhulupirika m’pemphero?
19 Ngati timayamikira unansi wathu ndi Yehova Mulungu, tidzam’pempha kuti atichitire chifundo pamaziko a nsembe ya dipo la Yesu. Ndi chikhulupiriro, tingayandikire kumpando wachisomo ndi ufulu wa kulankhula kuti tilandire chifundo ndi thandizo panthaŵi yake. (Ahebri 4:16) Koma pali zifukwa zambiri zopempherera! Chotero tiyeni ‘tizipemphera kosaleka’—nthaŵi zambiri ndi mawu achitamando ndi kuthokoza Mulungu. (1 Atesalonika 5:17) Usana ndi usiku, tikweze manja okhulupirika popemphera.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi kuliganizapo pasadakhale pemphero lapoyera kuli ndi phindu lanji?
◻ N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera mwaulemu komanso mosamala?
◻ Kodi tiyenera kuonetsa mzimu wotani popemphera?
◻ Popemphera, n’chifukwa chiyani tiyenera kukumbukira chiyamiko ndi chitamando?
◻ Kodi Baibulo limasonyeza motani kuti tingapeze chitonthozo m’pemphero?
[Chithunzi patsamba 17]
Mfumu Solomo inaonetsa kudzichepetsa m’pemphero lake lapoyera popatulira kachisi wa Yehova
[Zithunzi patsamba 18]
Monga Hana, mungapeze chitonthozo m’pemphero