-
Mafunso Ochokera kwa OwerengaNsanja ya Olonda—2006 | January 1
-
-
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Lemba la Salmo 102:26 limanena kuti dziko lapansi ndi kumwamba “zidzatha.” Kodi mawu amenewa akusonyeza kuti dziko lapansili lidzawonongedwa?
Popemphera kwa Yehova, wamasalmo anati: “Munakhazika dziko lapansi kalelo; ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu. Zidzatha izi, koma Inu mukhala: inde, zidzatha zonse ngati chovala; mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika.” (Salmo 102:25, 26) Nkhani imene ikunenedwa m’salmo limeneli imasonyeza kuti mavesi amenewa sakunena za kuwonongedwa kwa dziko lapansi, koma akunena za umuyaya wa Mulungu. Nkhani ya m’salmoli imasonyezanso chifukwa chake mfundo yoona ndi yofunika imeneyi ili yolimbikitsa kwa atumiki a Mulungu.
-
-
Mafunso Ochokera kwa OwerengaNsanja ya Olonda—2006 | January 1
-
-
Komabe, ngakhale zaka zambiri zomwe dziko lapansi ndi kumwamba zakhalako sizingafanane ndi umuyaya wa Yehova. Wamasalmoyo akuwonjezera kuti: “Zidzatha izi [dziko lapansi ndi kumwamba], koma Inu mukhala.” (Salmo 102:26) Dziko lapansi ndi kumwamba zikhoza kuwonongeka. N’zoona kuti Yehova ananenapo kuti zidzakhala kosatha. (Salmo 119:90; Mlaliki 1:4) Koma zikhoza kuwonongedwa ngati Mulungu atafuna. Mosiyana ndi zimenezi, Mulungu sangafe. Zinthu zolengedwa zimakhala “ku nthawi za nthawi” kokha chifukwa choti Mulungu amaziyang’anira. (Salmo 148:6) Yehova atasiya kusamalira zinthu zolengedwa, “zidzatha zonse ngati chovala.” (Salmo 102:26) Mofanana ndi momwe munthu amakhalira nthawi yaitali kuposa malaya ake, momwemonso zolengedwa za Yehova zikhoza kukhala nthawi yochepa poyerekezera ndi iyeyo, ngati atafuna kutero. Komabe, tikudziwa kuchokera ku malemba ena kuti chimenecho si cholinga chake. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti Yehova wakonza zoti dziko lapansili ndi kumwamba zidzakhale kosatha.—Salmo 104:5.
-