“Lemekeza Yehova, Moyo Wanga”
NANCY anati: “Pamiyezi yaposachedwapa, utumiki wanga wakhala wotopetsa ndi wosasangalatsa.”a Kwa zaka khumi, iyeyo wakhala ali mpainiya, wolengeza uthenga wabwino nthaŵi zonse. Komanso anati: “Zimene zikundichitikirazi sizikundisangalatsa iyayi. Uthenga wa Ufumuwu ndikungoupereka mopanda chimwemwe ndipo zosachokera mumtima. Kaya ndingatani kaya?”
Taganizaninso za Keith, mkulu wina mumpingo wa Mboni za Yehova. Anadabwa kwambiri kumva mkazi wake akumuuza kuti: “Inutu mukuganiza zambiri. M’pemphero limene mwangonenali, mwatchulamonso zoti tikuyamikira chakudya, pomwe inoyi si nthaŵi ya chakudya!” Keith naye anavomereza kuti: “Nanenso ndikuona choncho kuti mapemphero anga ndimangowanena mosaganizira.”
Mosakayikira, simufuna kuti mawu anu otamanda Yehova Mulungu akhale ngati ongolota, osachokera mumtima. Koma mukufuna kuti akhale mawu ochokera mumtima, osonyeza kuti mukuyamikiradi. Komabe, munthu sangavale malingaliro a mumtima kapena kuwavula ngati malaya. Malingalirowo ayenera kuchokera mumtima mwa munthuwe. Kodi munthu angayamikire bwanji kuchokera mumtima? Salmo la 103 limatiuza mmene tingachitire pankhani imeneyi.
Mfumu Davide wa Aisrayeli akale ndiye analemba Salmo la 103. Analiyamba ndi mawu akuti: “Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi zonse za mkati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.” (Salmo 103:1) Buku lina linati: “Liwu lakuti lemekeza, ponena za Mulungu, limatanthauza kutamanda, nthaŵi zonse kutamanda kwake kom’sonyeza chikondi chachikulu, ndiponso kom’yamikira kwambiri.” Davide, pofuna kutamanda Yehova ndi mtima wachikondi ndi woyamikira, anauza moyo wake—kudziuza yekha—‘kulemekeza Yehova.’ Koma kodi n’chiyani chinam’pangitsa Davide kukhala ndi mtima woterewu woyamikira Mulungu amene ankam’lambira?
Davide anapitiriza kuti: ‘Usaiŵale zokoma za [Yehova] zonse atichitirazi.’ (Salmo 103:2) Kuthokoza Yehova kumachitika mwa kusinkhasinkha moyamikira zimene “atichitirazi.” Kodi Davide ankanena makamaka ziti zimene Yehova anachita? Munthu akamayang’ana zimene Yehova Mulungu analenga, monga nyenyezi zongoti mbuu kumwamba kopanda mitambo usiku, ndithudi mtima wake umayamikira Mlengi. Davide ataona thambo lodzaza nyenyezi anatsala wopanda mawu. (Salmo 8:3, 4; 19:1) Komabe, m’Salmo la 103, Davide anakumbukira ntchito ya Yehova ya mtundu wina.
Yehova “Akhululukira Mphulupulu Zako Zonse”
M’salmo lino, Davide akusimba zochita za Mulungu zokoma mtima. Potchula chinthu choyamba ndipo chachikulu pazonsezi, anaimba kuti: ‘Yehova akhululukira mphulupulu zako zonse.’ (Salmo 103:3) Davide ankadziŵadi kuti anali wochimwa. Mneneri Natani atamuimba mlandu wakuchita chigololo ndi Bateseba, Davide anavomereza kuti: “Pa inu, inu nokha [Yehova], ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu.” (Salmo 51:4) Anachonderera ndi mtima wachisoni, kuti: “Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga. Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.” (Salmo 51:1, 2) Taganizani mmene Davide anayamikirira pamene anakhululukidwa! Poti anali munthu wopanda ungwiro, anachita machimo ena m’moyo wake, komabe nthaŵi zonse ankalapa, kulandira chidzudzulo, ndi kuwongolera njira zake. Chimene chinam’pangitsa Davide kulemekeza Yehova chinali chifukwa chakuti ankakumbukira zimene Mulungu anam’chitira mwachifundo.
Nanga ifeyo sindife ochimwa? (Aroma 5:12) Ngakhale mtumwi Paulo anadandaula kuti: “Pakuti monga mwa munthu wa mkati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga. Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?” (Aroma 7:22-24) Tiyenera kuyamikira zedi chifukwa chakuti Yehova sasunga chakukhosi! Amaiŵaliratu ngati talapa ndi kum’pempha kutikhululukira.
Davide anadzikumbutsanso yekha kuti: ‘[Yehova] achiritsa nthenda zako zonse.’ (Salmo 103:3) Popeza kuti kuchiritsa ndiko kubwezeretsa munthu mumkhalidwe wake wakale, kumatanthauza kukhululukira tchimo kophatikizaponso zina zambiri. Kumaphatikizapo kuchiritsa “nthenda”—zotsatirapo zoipa za njira zathu zolakwika. Yehova, m’dziko lake latsopano adzachotseratu zinthu zimene zinayambitsidwa ndi uchimo, monga matenda ndi imfa. (Yesaya 25:8; Chivumbulutso 21:1-4) Komabe, ngakhale lero, Mulungu akutichiritsa matenda athu auzimu. Kwa ena, matendawo ndiwo chikumbumtima chawo choipa ndi kusakhala kwawo pamtendere ndi Mulungu. ‘Tisaiŵale’ zimene Yehova watichitira kale tonsefe payekhapayekha pankhani imeneyi.
“Awombola Moyo Wako”
“[Yehova] awombola moyo wako m’dzenje,” anaimba motero Davide. (Salmo 103:4, NW) “Dzenje” ndilo manda a anthu onse—Sheoli, kapena Hade. Ngakhale pamene Davide anali asanalongedwe kuti akhale mfumu ya Israyeli, analoŵa m’kamwa mwa mkango. Mwachitsanzo, Sauli Mfumu ya Israyeli, ankafunafuna Davide ndi maso ofiira namayesayesa kumupha nthaŵi zambiri. (1 Samueli 18:9-29; 19:10; 23:6-29) Afilisti nawonso ankafuna kuti Davide afe. (1 Samueli 21:10-15) Koma nthaŵi zonse Yehova anali kumuwombola “m’dzenje.” Davide ayenera kuti anayamikira kwambiri pamene ankakumbukira zonsezi zimene Yehova anam’chitira!
Nanga inuyo? Kodi Yehova anakuchirikizani panyengo zovuta kapena panthaŵi imene munali wachisoni? Kapena kodi mwaonapo zochitika zina pamene anawombola moyo wa Mboni zake zokhulupirika m’dzenje la Sheoli masiku athu omwe ano? Mwina mwakhudzidwa mtima poŵerenga nkhani zina m’magazini ino za mmene Yehova wapulumutsira anthu ena. Bwanji kumakumbukira moyamikira zinthu zimenezi zimene Mulungu woona wachita? Ndiponso, kunena zoona, tonsefe tili ndi chifukwa chabwino choyamikirira Yehova chifukwa watipatsa chiyembekezo cha chiukiriro.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
Yehova amatipatsa moyo ndi zina zonse zimene zimatipangitsa kukondwera nawo moyowo. Wamasalmo anati Mulungu ‘amakuvekani korona wa chifundo ndi nsoni zokoma.’ (Salmo 103:4) Panthaŵi imene tikufuna chithandizo, Yehova satisiya tokha koma amatithandiza mwa gulu lake looneka ndi akulu oikidwa, kapena abusa, mumpingo. Mwa chithandizo chimenecho, timakhoza kupirira chiyeso china popanda kutaya ulemu wathu. Abusa achikristu amasamala kwambiri nkhosa. Amalimbikitsa odwala ndi okhumudwa ndiponso amayesetsa kudzutsa onse amene agwa. (Yesaya 32:1, 2; 1 Petro 5:2, 3; Yuda 22, 23) Mzimu wa Yehova umawasonkhezera abusawo kukhala ndi mtima wachifundo ndi wokonda gulu lankhosa. ‘Chifundo ndi nsoni zake zokoma’ zilidi ngati korona wotikongoletsa ndiponso wotipatsa ulemu. Tisamaiŵale zinthu zimene Yehova amatichitira, tiyeni tizim’lemekezabe iyeyo ndi dzina lake loyera.
Davide anapitiriza kudzipatsa uphungu yekha kuti: “[Yehova] akhutiritsa m’kamwa mwako ndi zabwino; nabweza ubwana wako unge mphungu.” (Salmo 103:5) Moyo umene Yehova amapatsa n’ngwokhutiritsa ndiponso wosangalatsa. Muonetu, kungodziŵa choonadi kokhako n’chinthu chopambana kwambiri ndiponso chokondweretsa mtima zedi! Ndipo tangoganizani mmene ntchito imene Yehova watipatsa imakhutiritsira, yolalikira ndi kupanga ophunzira. Kupeza munthu wina wofuna kudziŵa za Mulungu woona, ndiyeno kum’thandiza ameneyo kudziŵa Yehova ndi kum’lemekeza, si zosangalatsa zimenezo? Komabe, kaya anthu a m’dera lathu azimvetsera kaya kukana, ndi mwayi waukulu kutengamo mbali m’ntchito yokhudza kuyeretsa dzina la Yehova ndi kuchirikiza uchifumu wake.
Pamene tikulimbikira kugwira ntchito yolengeza Ufumu wa Mulungu, kodi ndani amene salema kapena kulefuka? Koma nthaŵi zonse Yehova amapatsa atumiki ake mphamvu, kuwachititsa kukhala ngati “ziwombankhanga” zokhala ndi mapiko amphamvu zouluka m’mwamba kwambiri mumlengalenga. Poti Yehova Atate wathu wachikondi wakumwamba amatipatsa “mphamvu” imeneyo kuti tizichita utumiki wathu mokhulupirika tsiku ndi tsiku, kodi si choyenera kuyamikira chimenecho?—Yesaya 40:29-31.
Mwachitsanzo: Clara amagwira ntchito yolembedwa ndipo mwezi uliwonse amawonongera maola ngati 50 mu utumiki wakumunda. Anati: “Nthaŵi zina ndimakhala wotopa kwambiri, moti ndimachita kudzikakamiza kupita ku utumiki wakumunda chabe chifukwa chakuti ndimakhala nditapangana ndi wina kukagwira naye ntchito. Koma ndimati ndikapita kumundako, ndimaona kuti ndapezanso mphamvu.” Mwina inunso zinakuchitikiranipo kuona kuti mwapeza mphamvu yopatsidwa ndi Mulungu mu utumiki wachikristu. Mungachite bwinotu nanunso mutanena ngati Davide m’mawu oyamba a Salmo limeneli, kuti: “Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za mkati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.”
Yehova Amalanditsa Anthu Ake
Wamasalmoyo anaimbanso kuti: “Yehova achitira onse osautsidwa chilungamo ndi chiweruzo. Analangiza Mose njira zake, ndi ana a Israyeli machitidwe ake.” (Salmo 103:6, 7) Mwina Davide akutanthauza pamene Aigupto ankhanza anali ‘kusautsa’ Aisrayeli m’masiku a Mose. Kukumbukira mmene Yehova anafotokozera Mose njira zake zowalanditsira kunapangitsa mtima wa Davide kuyamikira zimenezo.
Ifenso tingayamikire mofananamo tikamalingalira mmene Mulungu ankachitira ndi Aisrayeli. Komanso tisamaiŵale zinthu zimene zinachitikira Mboni za Yehova zamakono, monga zija zosimbidwa m’mutu 29 ndi mutu 30 m’buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom. Mwa kuŵerenga nkhani zimene zasimbidwa mmenemo ndi m’zofalitsa zina za Watch Tower Society timaona mmene Yehova wathandizira anthu ake amakono kupirira m’ndende, pochitidwa nkhanza ndi anthu, kupirira pamene ntchito yawo yaletsedwa, ndi kupirira m’misasa yachibalo. Anthu okhala m’mayiko osakazidwa ndi nkhondo, monga ku Burundi, ku Liberia, ku Rwanda, ndi dziko limene kale linali Yugoslavia, akumana ndi ziyeso. Nthaŵi zonse atumiki okhulupirika a Yehova akayamba kuzunzidwa, dzanja lake limawathandiza. Tikamakumbukira zimene Mulungu wathu wamkulu, Yehova wachita, tidzam’yamikira monga mmene Davide anam’yamikirira pamene ankakumbukira zochitika zakulanditsidwa kwa Aisrayeli ku Igupto.
Taganizaninso mmene Yehova amatipepuzira mtolo wa tchimo. Anatipatsa “mwazi wa Kristu” kuti ‘uyeretse chikumbumtima chathu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa.’ (Ahebri 9:14) Ngati talapa machimo athu ndi kupempha Mulungu kutikhululukira mwa mwazi umene Kristu anakhetsa, Mulungu amaika zolakwa zathu kutali—“monga kummaŵa kutanimpha ndi kumadzulo”—ndipo amayamba kutiyanjanso. Ndiyeno taganizaninso zimene Yehova amatigaŵira kudzera m’misonkhano yachikristu, mayanjano olimbikitsa, abusa mumpingo, ndi zofalitsa zina zankhani za m’Baibulo zimene timalandira kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Kodi zonsezi zimene Yehova amatichitira sizitithandiza kulimbitsa unansi wathu ndi iye? Davide anati: “Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wachifundo chochuluka. . . . Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.” (Salmo 103:8-14) Tikamakumbukira mmene Yehova amatisamalira mwachikondi ndithudi tidzam’tamanda ndi kumveketsa dzina lake loyera.
“Lemekezani Yehova, Inu, Ntchito Zake Zonse”
Tikayerekezera ndi Yehova wosakhoza kufayo, “Mulungu wa nthaŵi zonse,” “masiku” a “munthu” n’ngafupi kwambiri—“monga duŵa la kuthengo.” Koma Davide anakumbukira moyamikira zoti: “Chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.” (Genesis 21:33; Salmo 103:15-18) Yehova saiŵala anthu amene amamuopa. Nthaŵi ikakwana adzawapatsa moyo wosatha.—Yohane 16:3; 17:3.
Davide, posonyeza kuti ankayamikira kuti Yehova ndiye mfumu, anati: “Yehova anakhazika mpando wachifumu wake kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo.” (Salmo 103:19) Ngakhale kuti nthaŵi ina Yehova ankalamulira kudzera mu ufumu wa Israyeli, kwenikweni mpando wake wachifumu uli kumwamba. Chifukwa chakuti Yehova ndi Mlengi, iye ndiye Mfumu Yaikulu m’chilengedwe chonsechi ndipo amachita chifuniro chake kumwamba ndi padziko lapansi monga mmene amafunira.
Davide analimbikitsa ngakhale angelo akumwamba. Anaimba kuti: “Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mawu ake, akumvera liwu la mawu ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chom’kondweretsa iye. Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.” (Salmo 103:20-22) Ifenso tikamakumbukira zimene Yehova amatichitira mwachifundo, kodi sizikutisonkhezera kum’yamikira? Ziyeneradi kutisonkhezera! Ndipo ngakhale kuti tili pakati pa anthu aunyinji otamanda Mulungu mofuula, kuphatikizapo angelo olungama, munthu aliyense payekha mawu ake otamanda Mulungu azimvekabe basi. Tiyenitu tizitamanda Atate wathu wakumwamba ndi mtima wonse, tikumam’thokoza nthaŵi zonse. Tiyenitu tingowalabadira mawu a Davide akuti: “Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.”
[Mawu a M’munsi]
a Mayina ena tawasintha.
[Chithunzi patsamba 23]
Davide ankalingalira zimene Yehova anachitira anthu mwachifundo. Nanga inu?