Kodi Mudzapindula Kuchokera ku Mapangano a Mulungu?
“‘Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.’ Kotero kuti iwo achikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo.”—AGALATIYA 3:8, 9.
1. Nchiyani chomwe mbiri yakale imasonyeza ponena za chiyambukiro cha maulamuliro ambiri?
“NDUNA zaubwino [kapena, zowunikiridwa]” ndi mmene olamulira ena a ku Europe a mu zana la 18 amatchedwera. Iwo ‘analingalira bwino kulamulira anthu awo ndi kukoma mtima kwa utate, koma makonzedwe awo analakwika ndipo masinthidwe awo analephera kotheratu.’a (The Encyclopedia Americana) Ichi chinali chochititsa chotsogolera cha masinthidwe omwe posachedwapa anakuta Europe.
2, 3. Ndimotani mmene Yehova amasiyanirana ndi mafumu a anthu?
2 Ndi mosiyana chotani nanga mmene Yehova aliri kwa olamulira a umunthu osadziwikiratu. Tingakhoze kuwona mopepuka chifuno chowawa cha mtundu wa anthu kaamba ka kusintha komwe potsirizira pake kudzatulutsa zothetsera zenizeni kaamba ka kupanda chilungamo ndi kuvutika. Koma sitifunikira kudera nkhaŵa kuti kachitidwe ka Mulungu kobweretsera chimenechi kamadalira pa zina zake. M’bukhu lofalitsidwa koposa m’dziko, iye walongosola lonjezo lake la kubweretsa madalitso osatha kwa mtundu wa anthu okhulupirira. Ichi chidzakhala mosasamala kanthu za utundu wakale wa anthu, fuko, maphunziro, kapena kaimidwe ka mayanjano. (Agalatiya 3:28) Koma kodi inu mungadalire pa ichi?
3 Mtumwi Paulo anagwira mawu mbali ya chitsimikiziro chimene Mulungu anapereka kwa Abrahamu kuti: “[Motsimikizirika, NW] kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe.” Paulo anawonjezera kuti popeza kuti “Mulungu sakhoza kunama,” ife “tikakhale nacho chotichenjeza cholimba ife amene tidathaŵira kugwira chiyembekezo choikika pamaso pathu.” (Ahebri 6:13-18) Chidaliro chathu m’madalitso amenewo chingalimbikitsidwe mowonjezereka mwa kudziŵa njira ya dongosolo mu imene Mulungu anakhazikitsira maziko kaamba ka kukwaniritsa chimenechi.
4. Ndimotani mmene Mulungu amagwiritsira ntchito mapangano osiyanasiyana kukwaniritsa chifuno chake?
4 Tawona kale kuti Mulungu anapanga pangano ndi Abrahamu lophatikiza mbewu yomwe ikakhala chiwiya m’kudalitsa “mitundu yonse ya dziko lapansi.” (Genesis 22:17, 18) Aisrayeli anakhala mbewu yeniyeni yakuthupi, koma m’lingaliro lauzimu lofunika kwambiri, Yesu Kristu anatsimikizira kukhala mbali yokulira ya mbewu ya Abrahamu. Yesu analinso Mwana, kapena Mbewu, ya Abrahamu Wamkulu, Yehova. Akristu omwe “ali a Kristu” amapanga mbali yachiŵiri ya mbewu ya Abrahamu. (Agalatiya 3:16, 29) Pambuyo pa kupanga pangano la Abrahamu, Mulungu anawonjezera mosakhalitsa pangano la Chilamulo ndi mtundu wa Israyeli. Ilo linatsimikizira kuti Aisrayeli anali ochimwa omwe anafunikira wansembe wa nthaŵi zonse ndi nsembe yangwiro. Chinachinjiriza mzere wa Mbewu ndi kuthandiza kumuzindikira iye. Pangano la Chilamulo linasonyezanso kuti, mwa njira inayake, Mulungu akabweretsa mtundu wa mafumu-ansembe. Pamene Chilamulo chinkagwirabe ntchito, Mulungu anapanga pangano ndi Davide kukhala ndi ulamuliro wa ufumu mu Israyeli. Pangano la Ufumu wa Davide linaloza kwa winawake wokhala ndi ulamuliro wosatha pa dziko lapansi.
5. Ndi mafunso otani kapena mavuto omwe afunikirabe kuthetsedwa?
5 Komabe, panali mbali kapena zolinga za mapangano amenewa zomwe zinawonekera kukhala zosakwanira kapena zofunikira kumveketsedwa. Mwachitsanzo, ngati Mbewu yomadzayo inafunikira kukhala mfumu mu mzere wa Davide, ndimotani mmene iye akakhalira wansembe wosatha yemwe akachita zochulukira kuposa ansembe apapitapo? (Ahebri 5:1; 7:13, 14) Kodi Mfumu imeneyi ikalamulira kuposa ufumu wa pa dziko lapansi wokhala ndi polekezera? Ndimotani mmene mbali yachiŵiri ya mbewuyo ikayenerera kukhala banja la Abrahamu Wamkulu? Ndipo ngakhale ngati iwo akatero, ndi ufumu wotani womwe iwo akakhala nawo, popeza kuti ziwalo zambiri sizinachokere kwa Davide? Tiyeni tiwone mmene Mulungu anatengera masitepi a lamulo mu mtundu wa mapangano owonjezereka omwe akathetsa mafunso amenewo, akumatsegula njira kaamba ka dalitso lathu losatha.
Pangano kaamba ka Wamsembe Wakumwamba
6, 7. (a) Mogwirizana ndi Salmo 110:4, ndi pangano lowonjezereka lotani limene Mulungu anakhazikitsa? (b) Ndi mbali ya kumbuyo yotani imene ingatithandize ife kumvetsetsa pangano lowonjezereka limeneli?
6 Monga momwe tawonera, mkati mwa kawonedwe ka pangano la Chilamulo, Mulungu anapangana ndi Davide kaamba ka mbadwa (mbewu) yomwe ikalamulira kosatha pa ufumu wa pa dziko lapansi. Koma Yehova anavumbulanso kwa Davide kuti wansembe wosatha akadza. Davide analemba kuti: “Yehova walumbira (ndipo sadzadzimva moipa) kuti: ‘Inu ndinu wansembe wosatha monga mwa chilongosoko cha Melikizedeke!’” (Salmo 110:4) Kodi nchiyani chomwe chinali kumbuyo kwa mawu a lumbiro amenewa a Mulungu omwe anafikira ku pangano laumwini pakati pa Yehova ndi Wansembe wakudzayo?
7 Melikizedeke anali mfumu ya Salemu wakale, amene mwachiwonekere anali pa malo pamene pambuyo pake mzinda wa Yerusalemu (dzina lophatikiza “Salemu”) unamangidwa. Cholembedwa cha zochita za Abrahamu ndi iye chimawunikira kuti iye anali mfumu yemwe analambira “Mulungu Wam’mwambamwamba.” (Genesis 14:17-20) Komabe, ndemanga ya Mulungu pa Salmo 110:4 imasonyeza kuti Melikizedeke analinso wansembe, kumpangitsa iye kukhala munthu wapadera. Iye anali ponse paŵiri mfumu ndi wansembe, ndipo anatumikira kumene mafumu a Davide ndi ansembe a Alevi pambuyo pake anachita machitidwe awo okonzedwa mwaumulungu.
8. Pangano limeneli la wansembe wofanana ndi Melikizedeke linapangidwa ndi ndani, ndipo ndi chotulukapo chotani?
8 Paulo akutipatsa ife tsatanetsatane wowonjezereka ponena za pangano limeneli kaamba ka wansembe wofanana ndi Melikizedeke. Mwachitsanzo, iye akunena kuti anali Yesu Kristu yemwe “anaitanidwa ndi Mulungu wansembe monga mwa dongosolo la Melikizedeke.” (Ahebri 5:4-10; 6:20; 7:17, 21, 22) Ngakhale kuti Melikizedeke mwachidziŵikire anali ndi makolo aumunthu, palibe cholembera cha makolo ake. Chotero m’malo mwakuti Yesu alowe m’malo ake a unsembe mogwirizana ndi mzere wolembedwa kuchokera kwa Melikizedeke, kusankhidwa kwake kunadza mwachindunji kuchokera kwa Mulungu. Unsembe wa Yesu sudzapatsiridwa kwa wolowa m’malo, popeza kuti “iye akhala wansembe kosatha.” Ichi chiri tero, popeza kuti mapindu a utumiki wake wa unsembe adzakhala osatha. Ife tingakhale odalitsidwa mowonadi m’kukhala ndi wansembe yemwe “akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa iye” ndi kulangiza ndi kutsogoza okhulupirika kosatha.—Ahebri 7:1-3, 15-17, 23-25.
9, 10. Ndimotani mmene chidziŵitso cha pangano lachisanu limeneli chimakulitsira kumvetsetsa kwathu kwa mmene chifuno cha Mulungu chidzakwaniritsidwira?
9 Nsonga ina yapadera iri yakuti thayo la Yesu monga Mfumu-Wansembe imapyola kayang’anidwe ka pa dziko lapansi. M’mawu ozungulira ofananawo kumene iye anatchula pangano limeneli kaamba ka wansembe wofanana ndi Melikizedeke, Davide analemba kuti: “Yehova anena kwa Ambuye wanga: ‘Khalani pa dzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.’” Chotero tingawone kuti Yesu—Ambuye wa Davide—anafunikira kukhala ndi malo m’mwamba ndi Yehova, chomwe chinachitika pa kukwera kwake kumwamba. Kuchokera kumwamba, Kristu angatsanulire ulamuliro ndi Atate wake kuti agonjetse adani ndi kupereka ziŵeruzo.—Salmo 110:1, 2; Machitidwe 2:33-36; Ahebri 1:3; 8:1; 12:2.
10 Mofananamo, mwa kudziŵa ponena za pangano lachisanu limeneli, tiri ndi kawonedwe kofutukulidwa ka njira yolongosoka, yosamalitsa mu imene Yehova adzakwaniritsira chifuno chake. Iyo imakhazikitsa kuti mbali yoyambirira ya mbewuyo idzakhalanso wansembe m’mwamba ndi kuti ulamuliro wake monga Mfumu-Wansembe udzakhala ndi mlingo wa chilengedwe chonse.—1 Petro 3:22.
Pangano Latsopano ndi Mbali Yachiŵiri ya Mbewu
11. Ndi kucholowanacholowana kotani komwe kulipo ponena za mbali yachiŵiri ya mbewu?
11 Pamene poyambirirapo talingalira pangano la Abrahamu, tawona kuti Yesu anakhala mbali yoyambirira ya mbewuyo mwa kuyenera kwakuthupi. Iye mwachindunji anachokera kwa kholo Abrahamu, ndipo monga munthu wangwiro, iye anali Mwana wolandirika wa Abrahamu Wamkulu. Bwanji, ngakhale ndi tero, ponena za anthu omwe ali ndi mwaŵi wa kukhala mbali yachiŵiri ya mbewu ya Abrahamu, “olowa m’malo a lonjezano”? (Agalatiya 3:29) Pokhala opanda ungwiro, mbali ya banja la Adamu wochimwa, iwo akakhala osayeneretsedwa kukhala m’banja la Yehova, Abrahamu Wamkulu. Ndimotani mmene chikhoterero cha kupanda ungwiro chikagonjetsedwera? Chimenecho chikakhala chosatheka kwa anthu, koma sichiri chosatheka kwa Mulungu.—Mateyu 19:25, 26.
12, 13. (a) Ndimotani mmene Mulungu ananeneratu pangano lina? (b) Ndi mbali yapadera yotani ya pangano limeneli imene imafunikira chisamaliro chathu?
12 Pamene Chilamulo chinkagwirabe ntchito, Mulungu ananeneratu kupyolera mwa mneneri wake kuti: “Ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda; si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo awo . . . ‘pangano langa limenelo analiswa’ . . . ndidzaika chilamulo changa mkati mwawo, ndipo mu mtima mwawo ndidzachilemba. Ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, nadzakhala iwo anthu anga. Ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake . . . ‘Mudziŵe Yehova!’ pakuti iwo onse adzandidziŵa . . . Ndidzakhululukira mphulupulu yawo, ndipo sindidzakumbukira chimo lawo.”—Yeremiya 31:31-34.
13 Onani kuti mbali ya pangano latsopano limeneli inali kukhululukidwa kwa machimo, mwachiwonekere m’njira imene inali ‘yosafanana’ ndi makonzedwe a nsembe za nyama pansi pa Chilamulo. Yesu anawunikira pa ichi pa tsiku lomwe iye anafa. Pambuyo pa kugwirizana ndi ophunzira ake m’kukumbukira M’gonero monga momwe kunafunidwira ndi Chilamulo, Kristu anakhazikitsa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Kukumbukira kwa chaka ndi chaka kumeneku kukaphatikizapo chikho chogawanamo cha vinyo, ponena za chimene Yesu ananena kuti: “Chikho ichi ndi pangano latsopano mwazi wanga, wothiridwa chifukwa cha inu.”—Luka 22:14-20.
14. Nchifukwa ninji pangano latsopano liri lofunika m’kutulutsa mbali yachiŵiri ya mbewu?
14 Chotero, pangano latsopano likapangidwa kugwira ntchito ndi mwazi wa Yesu. Pa maziko a nsembe yangwiro yoteroyo, Mulungu akakhoza ‘kukhululukira zophophonya ndi chimo’ kamodzi ndi kosatha. Tangolingalirani chimene icho chikatanthauza! Pokhala wokhoza kukhululukira machimo a anthu odzipereka kotheratu m’banja la Adamu, Mulungu akawawona iwo monga opanda uchimo, kuwabala iwo monga ana auzimu a Abrahamu Wamkulu, ndipo kenaka kuwadzoza iwo ndi mzimu woyera. (Aroma 8:14-17) Chotero, pangano latsopano lolimbitsidwa ndi nsembe ya Yesu limatheketsa ophunzira ake kukhala mbali yachiŵiri ya mbewu ya Abrahamu. Paulo analemba kuti: “Mwa imfa [Yesu akakhoza] kumuwononga iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye, Mdyerekezi; [nakakhoza] kumasula iwo onse amene chifukwa cha kuwopa imfa m’moyo wawo wonse adamangidwa ukapolo. Pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbewu ya Abrahamu.”—Ahebri 2:14-16; 9:14.
15. Ndani omwe ali mbali ku pangano latsopanolo?
15 Pamene kuli kwakuti Yesu akakhoza kukhala Nkhoswe ndi nsembe yochirikiza ya pangano latsopano, ndani omwe anali mbali ya panganolo? Yeremiya ananeneratu kuti Mulungu akapanga pangano limeneli ndi “nyumba ya Israyeli.” Israyeli uti? Osati Israyeli wakuthupi wodulidwa pansi pa Chilamulo, popeza kuti pangano latsopano linapangitsa pangano lakale limenelo kukhala losagwira ntchito. (Ahebri 8:7, 13; onani tsamba 31.) Tsopano Mulungu akachita ndi Ayuda ndi Akunja omwe mwachikhulupiriro anali ‘odulidwa mu mtima mwa mzimu’ mophiphiritsira. Ichi chimagwirizana ndi kunena kwake kwakuti awo a m’pangano latsopano akakhala ndi ‘malamulo ake olembedwa m’nzeru zawo ndi mitima yawo.’ (Aroma 2:28, 29; Ahebri 8:10) Paulo anatcha Ayuda auzimu amenewo “Israyeli wa Mulungu.”—Agalatiya 6:16; Yakobo 1:1.
16. Ndimotani mmene pangano latsopano limathandizira m’kukwaniritsa chimene Eksodo 19:6 inalozerako?
16 Popeza kuti Mulungu tsopano anali kuchita ndi Israyeli wauzimu, chitseko cha mwaŵi chinatseguka. Pamene Mulungu anakhazikitsa Chilamulo, iye anali atalankhula za ana amuna a Israyeli kukhala kwa iye “ufumu wa ansembe ndi mtundu woyera.” (Eksodo 19:6) M’chenicheni, Israyeli wakuthupi sakakhoza nkomwe ndipo sanakhalepo mtundu mu umene onse a iwo anali mafumu-ansembe. Koma Ayuda ndi Akunja omwe analandiridwa monga mbali yachiŵiri ya mbewu ya Abrahamu akakhoza kukhala mafumu-ansembe.b Mtumwi Petro anatsimikizira chimenechi, akumauza oterowo kuti: “Inu ndinu ‘mbadwa yosankhika ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwiniwake, kotero kuti mukalalikire zoposapo’ za iye amene anakuitanani mutuluke mu mdima.” Iye analembanso kuti ‘cholowa chosafota koma chosungikira m’mwamba kwa inu.’—1 Petro 1:4; 2:9, 10.
17. Nchifukwa ninji pangano latsopano liri “labwinopo” kuposa pangano la Chilamulo?
17 Mofananamo, pangano latsopano limagwira ntchito ndi kukhalapo kwa pasadakhale kwa pangano la Abrahamu kutulutsa mbali yachiŵiri ya mbewuyo. Pangano latsopano limeneli pakati pa Yehova ndi Akristu obadwa ndi mzimu limalola kaamba ka kupangidwa kwa mtundu wa kumwamba wa mafumu-ansembe m’banja lachifumu la Abrahamu Wamkulu. Tingawone, kenaka, chifukwa chimene Paulo ananenera kuti iri ndi “pangano labwino koposa, [lomwe lakhazikitsidwa mwa lamulo pa, NW] malonjezano oposa.” (Ahebri 8:6) Malonjezano amenewo amaphatikizapo madalitso a kukhala ndi lamulo la Mulungu litalembedwa m’mitima ya odzipereka amene machimo awo sakukumbukiridwa, ndi kukhala ndi onse ‘odziŵa Yehova, kuchokera kwa wam’ng’ono kufika kwa wamkulu.’—Ahebri 8:11.
Pangano la Yesu kaamba ka Ufumu
18. Ndi mwa lingaliro lotani mmene mapangano omwe talingalira pakali pano sanakwaniritse kotheratu chifuno cha Mulungu?
18 Kuwunikira pa mapangano asanu ndi limodzi omwe takambitsirana, chingawoneke kuti Yehova wakonzekera mwalamulo zonse zomwe zikufunikira kukwaniritsa chifuno chake. Komabe, Baibulo limabweretsa pangano lina lomwe limagwirizana ndi chomwe talingalira, pangano lomwe limakuta mbali zowonjezereka za nkhani yofunika imeneyi. Akristu obadwa ndi mzimu amayembekezera molondola kuti ‘Ambuye adzawalanditsa iwo ku ntchito yonse yoipa nadzawapulumutsa kulowa ufumu wake wa kumwamba.’ (2 Timoteo 4:18) M’mwamba, iwo adzakhala mtundu wa mafumu-ansembe, koma kodi nchiyani chomwe chidzakhala ufumu wawo? Pamene aukitsidwa kupita kumwamba, Kristu ali kale kumeneko monga wansembe wamkulu wangwiro. Iye adzakhalanso ataima kale ndi mphamvu ya ufumu kaamba ka kulamulira kwa chilengedwe chonse. (Salmo 2:6-9; Chibvumbulutso 11:15) Kodi nchiyani chomwe chiri kumeneko kaamba ka mafumu-ansembe kuchichita?
19. Ndi liti ndipo ndimotani mmene pangano lachisanu ndi chiŵiri linapangidwira?
19 Pa Nisani 14, 33 C.E., madzulo amene Yesu anakhazikitsa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ndi kutchula “pangano latsopano mwazi [wake] wothiridwa,” iye analankhula za pangano lina, lachisanu ndi chiŵiri kaamba ka kukambitsirana. Iye anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “Inu ndinu amene munakhala ndi ine chikhalire m’mayeso anga; ndipo ine [ndipanga pangano ndi inu, NW], monganso Atate wanga [apangira pangano ndi ine, NW], anandiikira ine, kuti mukadye ndi kumwa ku gome kwanga mu ufumu wanga, ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu, ndi kuŵeruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.” (Luka 22:20, 28-30) Monga mmene Atate anapangira pangano ndi Yesu kukhala wansembe monga Melikizedeke, chotero Kristu anapanga pangano laumwini ndi atsatiri ake okhulupirika.
20. Pangano la Ufumu linapangidwa ndi yani, ndipo nchifukwa ninji? (Danieli 7:18; 2 Timoteo 2:11-13)
20 Atumwi 11 amenewo motsimikizirika anali anamamatira ndi Yesu m’mayeso ake, ndipo panganolo linasonyeza kuti iwo akakhala pa mipando yachifumu. Mowonjezereka, Chibvumbulutso 3:21 chimatsimikizira kuti Akristu obadwa ndi mzimu onse omwe atsimikizira kukhala okhulupirika adzakhala pa mipando yachifumu ya kumwamba. Chotero, pangano limeneli liri ndi a 144,000 onse omwe agulidwa ndi mwazi wa Yesu kutengedwa kupita kumwamba monga ansembe ndi “kulamulira monga mafumu pa dziko lapansi.” (Chibvumbulutso 1:4-6; 5:9, 10; 20:6) Pangano limene Yesu akupanga ndi iwo limagwirizanitsa iwo kwa iye kugawana m’kulamulira kwake. M’lingaliro lina, chiri monga ngati kuti mkwatibwi kuchokera ku banja lotchuka anagwirizanitsidwa ndi chikwati kwa mfumu yolamulira. Mkaziyo chotero amabwera m’malo a kugawana kulamulira kwa ufumu wa mwamunayo.—Yohane 3:29; 2 Akorinto 11:2; Chibvumbulutso 19:7, 8.
21, 22. Ndi dalitso lotani lomwe lingayembekezeredwe chifukwa cha chimene mapangano amenewa akukwaniritsa?
21 Ndi mapindu otani amene ichi chidzatsegula kaamba ka mtundu wa anthu omvera? Osati Yesu ngakhalenso a 144,000 omwe adzakhoza kufanana ndi nduna zaubwino zomwe “sizikanakhoza kupereka zothetsera zenizeni.” M’malomwake, tiri otsimikiziridwa kuti Yesu ali wansembe wamkulu “yemwe wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.” Ife chotero tingamvetsetse chifukwa chimene iye ‘angamverere chifundo’ ndi anthu okhala ndi zofooka ndi chifukwa chimene “nkhosa zina,” monga momwe zakhalira zowona ndi Akristu odzozedwa, zingakhozenso, kupyolera mwa Kristu, kufikira mpando wachifumu wa Mulungu “ndi ufulu wa kulankhula.” (NW) Chotero, iwo kachiŵirinso “angalandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi yakusowa.”—Ahebri 4:14-16; Yohane 10:16.
22 Awo ochita pangano kugawana ndi Yesu monga mafumu-ansembe amagawanamonso mu dalitso la mtundu wa anthu. Monga mmene ansembe a Chilevi akale anapindulitsira mtundu wonse wa Israyeli, chotero awo otumikira m’mipando yachifumu ya kumwamba ndi Yesu adzaŵeruza m’chilungamo awo onse okhala pa dziko lapansi. (Luka 22:30) Mafumu-ansembe amenewo poyamba anali anthu, chotero iwo adzakhala achifundo ku zosowa za mtundu wa anthu. Mbali yachiŵiri ya mbewu imeneyi idzagwirizana ndi Yesu m’kuwona kuti “mitundu yonse idzadalitsidwa.”—Agalatiya 3:8.
23. Ndimotani mmene aliyense payekha ayenera kuchitira mogwirizana ndi mapangano amenewa?
23 Onse omwe amakhumba kugawana mu dalitso limenelo pa mtundu wa anthu, mwakutero kupindula kuchokera ku mapangano a Mulungu, akuitanidwa tsopano kuchita tero. (Chibvumbulutso 22:17) Sitepi limodzi labwino kwambiri liri kukhalapo kwa kukondwerera kwa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, chomwe chidzachitidwa pambuyo pa kuloŵa kwa dzuŵa pa Lachitatu, March 22, 1989. Chonde pangani makonzedwe tsopano akukapezekako ndi umodzi wa mipingo ya Mboni za Yehova. Kumeneko mudzaphunzira zochulukira ponena za mapangano aumulungu ndipo mudzawona mowonjezereka mmene mungapindulire kuchokera ku iwo.
[Mawu a M’munsi]
a “Ngakhale masinthidwe opambana koposa anasiya nzika zosauka, okhala ndi mwaŵi mopambanitsa, otchuka olipiritsidwa msonkho wochepera, gulu lapakati linalowerera mosakwanira m’boma ndiponso m’chitaganya . . . Chiyenera kunenedwa kuti pamene kuli kwakuti malo a unduna owunikiridwa anayamba kuyang’anizana ndi mafunso omwe sakanakhoza kunyalanyazidwanso, iwo sakanakhoza kupereka chothetsera chenicheni mkati mwa zenizeni za ndale zadziko ndi chuma cha nyengoyo.”—Western Civilization—Its Genesis and Destiny: The Modern Heritage.
b Yesu sali mbali ya pangano latsopano. Iye ali Nkhoswe yake ndipo alibe machimo ofunikira kukhululukidwa. Kuwonjezerapo, sichiri choyenerera kaamba ka iye kukhala mfumu-wansembe ndi ilo, popeza kuti iye ali mfumu mogwirizana ndi pangano la Davide ndiponso wansembe mofanana ndi Melikizedeke.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Nchifukwa ninji pangano lotchulidwa pa Salmo 110:4 linapangidwa, ndipo nchiyani chomwe linakwaniritsa?
◻ Ndani omwe ali m’pangano latsopano, ndipo ndimotani mmene ilo linathandizira kutulutsa mtundu wa mafumu-ansembe?
◻ Nchifukwa ninji Yesu anapanga pangano laumwini ndi otsatira ake?
◻ Ndi ati omwe ali mapangano asanu ndi aŵiri omwe talingalira?
[Chithunzi patsamba 17]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Pangano la mu Edeni Genesis 3:15
Pangano la Abrahamu
Pangano la chilamulo
Pangano la Ufumu wa Davide
Pangano la kukhala wansembe wofanana ndi Melikizedeke
Mbewu yoyamba
Mbewu yachiŵiri
Madalitso osatha
[Chithunzi patsamba 19]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Pangano la mu Edeni Genesis 3:15
Pangano la Abrahamu
Pangano la Chilamulo
Pangano latsopano
Pangano la Ufumu wa Davide
Pangano la kukhala wansembe wofanana ndi Melikizedeke
Mbewu yoyamba
Pangano la Ufumu wa kumwamba
Mbewu yachiŵiri
Madalitso osatha