Mutu 16
Boma la Mulungu Liyamba Ulamuliro Wake
1. (a) Kodi nkuchiyani kumene anthu a chikhulupiriro ayembekezera nthawi yaitali? (b) Kodi nchifukwa ninji ufumu wa Mulungu ukutchedwa “mudzi”?
KWA ZAKA ZIKWI zambiri anthu okhala ndi chikhulupiriro m’boma la Mulungu ayembekezera nthawi pamene likayamba ulamuliro wake. Mwa chitsanzo, Baibulo limanena kuti Abrahamu wokhulupirika “analindirira mudzi wokhala nawo maziko [enieni], mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.” (Ahebri 11:10) “Mudzi” umenewo ndiwo ufumu wa Mulungu. Koma kodi panopa nchifukwa ninji ukutchedwa “mudzi”? Izi ziri chifukwa chakuti m’nthawi zakale kunali kofala kwa mfumu kulamulira mudzi. Motero anthu kawirikawiri anaganizira za mudzi kukhala ufumu.
2. (a) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Ufumuwo unali weniweni kwa ophunizira oyambirira a Kristu? (b) Kodi iwo anafuna kudziwanji ponena za uwo?
2 Ufumu wa Mulungu unali weniweni kwa atsatiri oyambirira a Kristu. Zimenezi zikusonyezedwa ndi chikondwerero chawo chachikulu mu ulamuliro wake. (Mateyu 20:20-23) Funso m’maganizo mwawo linali: Kodi ndiliti pamene Kristu ndi ophunzira ake akayamba kulamulira? Pa nthawi ina pamene Yesu anawonekera kwa ophunzira ake pambuyo pa chiukiriro chake, iwo anafunsa kuti: “Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” (Machitidwe 1:6) Motero, kodi muli wofunitsitsa kudziwa pamene Kristu ayamba kulamulira monga Mfumu ya boma la Mulungu, monga momwedi ophunzira a Kristu analiri?
BOMA LIMENE AKRISTU AMAPEMPHA
3, 4. (a) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Mulungu nthawi zonse walamulira monga Mfumu? (b) Motero kodi nchifukwa ninji Kristu anaphunzitsa omtsatira kupempha ufumu wa Mulungu kuti udze?
3 Kristu anaphunzitsa omtsatira kupemphera kwa Mulungu: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Koma wina anagfunse kuti: ‘Kodi Yehova Mulungu sanalamulire nthawi zonse monga mfumu? Ndipo ngati watero, nkupempheranji kuti ufumu wake udze?’
4 Zowona, Baibulo limatcha Yehova “Mfumu ya muyaya.” (1 Timoteo 1:17, NW) Ndipo limati: “Yehova anakhazika mpando wachifumu wake kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo.” (Salmo 103:19) Motero Yehova nthawi zonse wakhala Wolamulira Wamkulu pa zolengedwa zake zonse. (Yeremiya 10:10) Komabe, chifukwa cha kupandukira ulamuliro wake m’munda wa Edene, Mulungu analinganiza boma lapadera. Limeneli ndilo boma limene Yesu Kristu pambuyo pake anaphunzitsa omtsatira kupempha. Chifuno chake ndicho kuthetsa mavuto ochititsidwa pamene Satana Mdyerekezi ndi ena anabwevuka ku ulamuliro wa Mulungu.
5. Ngati uli ufumu wa Mulungu, kodi nchifukwa ninji ukutchedwanso ufumu wa Kristu ndi ufumu wa a144,000?
5 Boma Laufumu latsopano limeneli limalandira mphamvu yake ndi kuyenera kwa kulamulira kuchokera kwa Mfumu Yaikuluyo, Yehova Mulungu. Ndilo ufumu wake. Mobwerezabwereza, Baibulo limalitcha “ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:2, 11, 60, 62; 1 Akorinto 6:9, 10; 15:50) Komabe, popeza kuti Yehova waika Mwana wake kukhala Wolamulira wake Wamkulu, limatchedwanso ufumu wa Kristu. (2 Petro 1:11) Monga momwe tinaphunzirira m’mutu wina wapitawo, anthu 144,000 ochokera pakati pa anthu adzalamulira ndi Kristu muufumu umenewu. (Chivumbulutso 14:1-4; 20:6) Motero Baibulo limautchanso kukhala “ufumu wawo.”—Danieli 7:27.
6. Malinga ndi kunena kwa anthu ena, kodi ndiliti pamene ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira?
6 Anthu ena amanena kuti Ufumuwo unayamba ulamuliro wake m’chaka chimene Yesu anabwerera kumwamba. Iwo amanena kuti Kristu anayamba kulamulira pamene anatsanulira mzimu woyera pa atsatiri ake pa tsiku la phwando Lachiyuda la Pentekoste m’chaka cha 33 C.E (Machitidwe 2:1-4) Koma boma Laufumu limene Yehova analinganiza kuti lithetse mavuto onse olengedwa ndi chipanduko cha Satana silinayambe ulamuliro wake nthawi imeneyo. Palibe chirichonse chosonyeza kuti ‘mwana wamwamuna,’ amene ali boma la Mulungu lokhala ndi Kristu monga wolamulira, anabadwa pa nthawi imeneyo ndi kuyamba ulamuliro wake. (Chivumbulutso 12:1-10) Eya, kodi Yesu m’njira iriyonse anali ndi ufumu m’chaka cha 33 C.E.?
7. Kodi Kristu wakhala akulamulira yani chiyambire 33 C.E?
7 Inde, Yesu pa nthawi imeneyo anayamba kulamulira pa mpingo wake wa atsatiri amene, m’kupita kwa nthawi, anayenera kugwirizana naye kumwamba. Motero Baibulo limalankhula za iwo, pamene iwo ali padziko lapansi, kukhala akulowetsedwa mu “ufumu wa Mwana wa chikondi [cha Mulungu].” (Akolose 1:13) Koma ulamuliro umenewu, kapena “ufumu,” pa Akristu okhala ndi chiyembekezo cha moyo wakumwamba suli boma Laufumu limene Yesu anaphunzitsa omtsatira kupempha. Ndiwo ufumu pa anthu 144,000 okha amene adzalamulira naye kumwamba. Mkati monse mwa zaka mazana ambiri iwo akhala nzika zake zokha. Motero ulamuliro umenewu, kapena ‘ufumu wa Mwana wa chikondi cha Mulungu,’ udzatha pamene wotsirizira wa nzika zokhala ndi chiyembekezo cha kumwamba zimenezi afa ndi kugwirizana ndi Kristu kumwamba. Iwo sadzakhalanso nzika za Kristu, koma iwo pa nthawi imeneyo adzakhala mafumu limodzi naye m’boma Laufumu la Mulungu lolonjezedwa kalekale.
CHIYAMBI CHA ULAMULIRO PAKATI PA ADANI
8. (a) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti pambuyo pa kuuka kwa Kristu pakakhala nthawi ya kuyembekezera asanayambe kulamulira? (b) Kodi Mulungu ananenanji kwa Kristu pamene inali nthawi yakuti iye alamulire?
8 Pamene Kristu anabwerera kumwamba pambuyo pa chiukiriro chake, iye sanayambe kulamulira pa nthawi imeneyo monga Mfumu ya boma la Mulungu. M’malo mwake, panayenera kukhala nthawi ya kuyembekezera, monga momwe mtumwi Paulo akufotokozera: “Munthu uyu [Yesu Kristu] anapereka nsembe imodzi ya machimo kosatha nakhala pansi pa padzanja la Mulungu, kuyambira pa nthawi imeneyo kumkabe mtsogolo akuyembekezera kufikira adani ake ataikidwa kukhala chopondapo mapazi ake.” (Aheb. 10:12, 13, NW) Pamene nthawi inafika yakuti Kristu ayambe kulamulira, Yehova anamuuza kuti: “Chitani ufumu [kapena, gonjetsani] pakati pa adani anu.”—Salmo110:1, 2, 5, 6.
9. (a) Kodi nchifukwa ninji sialiyense amene akufuna ufumu wa Mulungu? (b) Pamene boma la Mulungu liyamba ulamuliro wake, kodi mitundu ikuchitanji?
9 Kodi zikumveka zachilendo kuti aliyense akakhala mdani wa boma la Mulungu? Komabe sialiyense amafuna kukhala pansi pa boma limene limafuna nzika zake kuchita chimene chiri chabwino. Motero litasimba mmene Yehova ndi Mwana wake akatengera ulamuliro wadziko, Baibulo limati, “amitundu anakwiya.” (Chivumbulutso 11:15, 17, 18) Mitundu sikulandira ufumu wa Mulungu chifukwa chakuti Satana akuilowetsa m’kuutsutsa.
10, 11. (a) Pamene boma la Mulungu liyamba ulamuliro wake, kodi nchiyani chimene chikuchitika kumwamba? (b) Kodi chiyani chimene chikuchitika padziko lapansi? (c) Motero kodi ndimfundo yofunika yotani imene tikufuna kukumbikira?
10 Pamene boma la Mulungu liyamba ulamuliro wake, Satana ndi angelo ake ali chikhalirebe kumwamba. Popeza kuti iwo akutsutsa ulamuliro Waufumu, nthawi yomweyo nkhondo ikuulika. Monga chotulukapo chake, Satana ndi angelo ake akuchotsedwa kumwamba. Zitatero, mawu opfuula akuti: “Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake.” Inde, ulamuliro wa boma la Mulungu ukuyamba! Ndipo Satana ndi angelo ake pokhala atachotsedwa kumwamba, kumeneko kuli kukondwera. “Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo!” Baibulo limatero.—Chivumbulutso 12:7-12.
11 Kodi inonso ndinthawi yokondweretsa ya dziko lapansi? Ayi! M’malo mwake, pali nthawi ya vuto yaikulu koposa imene dziko lapansi silinakhale nayo. Baibulo limatiuza kuti: “Tsoka mtundu ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.” (Chivumbulutso 12:12) Motero imeneyi ndiyo mfundo yaikulu yokumbukira: Chiyambi cha ulamuliro wa ufumu wa Mulungu sichimatanthauza mtendere wamwamsanga ndi chisungiko padziko lapansi. Mtendere weniweni udzadza pambuyo pake pamene ufumu wa Mulungu utenga ulamuliro wotheratu wa dziko lapansi. Zimenezi zikuchitika pa mapeto a “kanthawi,” pamene Satana ndi angelo ake adzachotsedwa kotero kuli iwo sangachititsire vuto aliyense.
12. Kodi nchifukwa ninji tingayembekezere kuti Baibulo likatiuza nthawi pamene ufumu wa Mulungu uyamba ulamuliro wake?
12 Koma kodi ndiliti pamene Satana akuchotsedwa kumwamba, motero akumachititsa vuto padziko lapansi kwa “kanthawi”? Kodi ndiliti pamene boma la Mulungu likuyamba ulamuliro wake? Kodi Baibulo limapereka yankho? Tiyenera kuyembekezera kuti likatero? Chifukwa ninji? Eya, chifukwa chakuti kalekale pasadakhale Baibulo linaneneratu nthawi pamene Mwana wa Mulungu akawonekera choyamba monga munthu padziko lapansi kuti akhele Mesiya. Kunena zowona, linasonyeza chaka chenicheni chimene iye anakhala Mesiya. Pamenepa, bwanji ponena za kudza kwa Mesiya, kapena Kristu, kofunika kwambiridi, kuti ayambe ulamuliro wake Waufumu? Ndithudi tikayembekezera kuti Baibulo likatiuzanso nthawi pamene zimenezi zikachitika!
13. Kodi ndimotani mmene Baibulo limaneneratu chaka chenicheni chimene Mesiya anawonekera padziko lapansi?
13 Koma munthu angafunse kuti: ‘Kodi mpati pamene Baibulo limaneneratu chaka chenicheni chimene Mesiya anawonekera padziko lapansi?’ Bukhu Labaibulo la Danieli limati: “Kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira Wodzozedwayo ndiye Karonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri,” kapena onse pamodzi masabata 69. (Danieli 9:25) Komabe, amenewa, sali masabata enieni 69, amene akukwanira masiku 483 okha, kapena opitirira pang’ono chaka chimodzi. Iwo ndiwo masabata 69 a zaka, kapena zaka 483. (Yerekezerani ndi Numeri 14:34.) Lamulo la kokonza ndi kumanganso linga la Yerusalemu linaperekedwa mu 455 B.C.E.a (Nehemiya 2:1-8) Motero masabata 69 a zaka amenewa anatha zaka 483 pambuyo pake, mu 29 C.E. Ndipo chimenecho ndicho chaka chenichenicho chimene Yesu anadza kwa Yohane kuti abatizidwe! Pa nthawi imeneyo iye anadzozedwa ndi mzimu woyera ndipo anakhala Mesiya, kapena Kristu.—Luka 3:1, 2, 21-23.
PAMENE BOMA LA MULUNGU LIYAMBA ULAMULIRO WAKE
14. Kodi “mtengowo” m’Danieli chaputala chachinai umaphiphiritsira chiyani?
14 Chabwino, pamenepa, kodi mpati pamene Baibulo limaneneratu chaka chimene Kristu akuyamba kulamulira monga ufumu ya boma la Mulungu? Ndimo m’bukhu Labaibulo limodzimodzili la Danieli. (Danieli 4:10-37) M’menemo, mtengo wautali kufikira kumwamba ukugwiritsiridwa ntchito kuphiphiritsira Mfumu Nebukadinezala ya Baibulo. Iye anali wolamulira waumunthu wapamwamba kwambiri pa nthawi imeneyo. Komabe, Mfumu Nebukadinezala anakakamizidwa kudziwa kuti wina wokulirapo anali kulamulira. Ameneyu ndiye “Wam’mwambamwamba,” kapena “Mfumu ya kumwamba,” Yehova Mulungu. (Danieli 4:34, 37) Motero, m’njira yofunika kwambiri, mtengo wofika kumwamba umenewu, ukudzaphiphiritsira ulamuliro waukulu wa Mulungu, makamaka m’kugwirizana kwake ndi dziko lathu lapansi. Ulamuliro wa Yehova unasonyezedwa kwa kanthawi mwa ufumu umene iye anakhazikitsa pa mtundu wa Israyeli. Motero mafumu a fuko la Yuda amene analamulira pa Aisrayeli ananenedwa kukhala ‘akukhala pa mpando wachifumu wa Yehova.’—1 Mbiri 29:23.
15. Pamene “mtengowo” unalikhidwa, kodi nchifukwa ninji mikombero inaikidwa pa uwo?
15 Malinga ndi kunena kwa cholembedwa Chabaibulo m’Danieli chaputala chachinai, mtengo wofika kumwambawo unalikhidwa. Komabe, chitsa chinasiyidwa, ndipo mkombero wa chitsulo ndi wa mkuwa unaikidwa pa icho. Zimenezi zikachititsa chitsacho kusaphukira kufikira itakhala nthawi ya Mulungu ya kuchotsa mikombero ndi kuchilola kuyamba kuphukiranso. Koma kodi ndimotani ndipo ndiliti pamene ulamuliro wa Mulungu unalikhidwa?
16. (a) Kodi ndimotani ndipo ndiliti pamene ulamuliro wa Mulungu unalikhidwa? (b) Kodi nchiyani chimene mfumu yotsiriza ya Yuda kukhala pa “mpando wachifumu wa Yehova” inauzidwa?
16 M’kupita kwa nthawi, ufumu wa Yuda umene Yehova adakhazikitsa unakhala woipa kwambiri chakuti analola Mfumu Nebukadinezala kuuchotsa, kuulikha. Zimenezi zinachitika m’chakacho 607 B.C.E. Pa nthawi imeneyo Zedekiya, mfumu yotsiriza ya Yuda kukhala mpando wachifumu wa Yehova, anauzidwa kuti: “Chotsa chilemba . . . ndithudi sichidzakhala cha aliyense kufikira iye atadza amene ali ndi kuyenera kwalamulo, ndipo ndiyenera kuchipereka kwa iye.”—Ezekieli 21:25-27, NW.
17. Kodi ndinyengo yanthawi yotani imene inayamba mu 607 B.C.E.?
17 Motero ulamuliro wa Mulungu, monga momwe unaphiphiritsiridwira ndi “mtengo,” unalikhidwa mu 607 B.C.E. Panalibenso boma loimira ulamuliro wa Mulungu m’dziko lapansi. Chifukwa cha chimenecho, mu 607 B.C.E. nyengo ya nthawi inayamba imene Yesu Kristu pambuyo pake anaitchula kukhala “nthawi zoikidwiratu za mitundu,” kapena, “nthawi za Akunja.” (Luka 21:24; King James Version) Mkati mwa “nthawi zoikidwiratu” zimenezi Mulungu analibe boma loimira ulamuliro wake m’dziko lapansi.
18. Kodi nchiyani chimene chinayenera kuchitika pa mapeto a “nthawi zoikidwiratu za mitundu”?
18 Kodi nchiyani chimene chinayenera kuchitika pa mapeto a “nthawi zoikidwiratu za mitundu” zimenezi? Yehova anayenera kupereka mphamvu ya kulamulira kwa Iye ‘amene ali ndi kuyenera kwalamulo.” Ameneyu ndiye Yesu Kristu. Motero ngati tingapeze nthawi pamene “nthawi zoikidwiratu za mitundu” zitha, tidzadziwa nthawi pamene Kristu akuyamba kulamulira monga mfumu.
19. Kodi ulamuliro wa Mulungu padziko lapansi ukadodometsedwa kwa “nthawi zingati?
19 Malinga ndi kunena kwa Danieli chaputala chachinai, “nthawi zoikidwiratu” zimenezi zikakhala “nthawi zisanu ndi ziwiri.” Danieli akusonyeza kuti kudzakhala “nthawi zisanu ndi ziwiri” mkati mwa zimene ulamuliro wa Mulungu, monga momwe unaphiphiritsiridwira ndi “mtengo,” sukakhala ukugwira ntchito padziko lapansi. (Danieli 4:16, 23) Kodi “nthawi zisanu ndi ziwiri” zimenezi nzazitali motani?
20. (a) Kodi “nthawi” imodzi njautali wotani? (b) Kodi “nthawi zisanu ndi ziwiri” nzazitali motani? (c) Kodi nchifukwa ninji tikuwerenga tsiku kukhala chaka?
20 M’Chivumbulutso chaputala 12, vesi 6 ndi 14, tikuphunzira kuti masiku 1,260 ngolingana ndi “nthawi [ndiko kuti, nthawi 1], ndi zinthawi [ndiko kuti nthawi 2], ndi nusu la nthawi.” Ndicho chiwonkhetso cha nthawi 3 1⁄2. Motero “nthawi” ikakhala yolingana ndi masiku 360. Chifukwa cha chimenecho, “nthawi zisanu ndi ziwiri” zikakhala 7 kuchulukitsa ndi 360, kapena masiku 2,520. Tsopano ngati tiwerenga tsiku limodzi kukhala chaka, malinga ndi njira Yabaibulo, “nthawi zisanu ndi ziwiri” zikukwanira zaka 2,520.—Numeri 14:34; Ezekieli 4:6.
21. (a) Kodi ndiliti pamene “nthawi zoikidwiratu za mitundu” zikuyamba ndi kutha? (b) Kodi ndiliti pamene boma la Mulungu likuyamba ulamuliro wake? (c) Kodi nchifukwa ninji kuli koyenerabe kupempha ufumu wa Mulungu kuti udze?
21 Taphunzira kale kuti “nthawi zoikidwiratu za mitundu” zinayamba m’chaka cha 607 B.C.E. Motero mwa kuwerenga zaka 2,520 kuchokera pa deti limenelo, tikufika ku 1914 C.E. Chimenecho ndicho chaka chimene “nthawi zoikidwiratu” zimenezi zinatha. Mamiliyoni ambiri a anthu okhalabe ndi moyo akukumbukira zinthu zimene zinachitika mu 1914. M’chaka chimenecho, Nkhondo Yoyamba ya Dziko inayamba nyengo ya vuto lowopsa imene yapitirizabe kufikira ku nthawi yathu. Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu Kristu anayamba kulamulira monga mfumu ya boma lakumwamba la Mulungu mu 1914. Ndipo chifukwa chakuti Ufumuwo wayamba kale ulamuliro wake, nkwapanthawi yake motani mmene kuliri kuti tikuupempha kuti “udze” ndi kuchotsa padziko lapansi dongosolo la zinthu loipa la Satana!—Mateyu 6:10; Danieli 2:44.
22 Komabe munthu angafunse kuti: ‘Ngati Kristu wabwera kale kudzalamulira muufumu wa Atate wake, Kodi nchifukwa ninji sitikumuwona?’
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka umboni wa mu mbiri wakuti lamulo limeneli linaperekedwa mu 455 B.C.E., wonani nkhaniyo “Artaxerxes” m’bukhulo Aid to Bible Understanding, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
22. Kodi ndifunso lotani limene ena angafunse?
[Tchati pamasamba 140, 141]
Mu 607 B.C.E. ufumu wa Mulungu wa Yuda unagwa.
Mu 1914 C.E. Yesu Kristu anayamba kulamulira monga mfumu ya boma lakumwamba la Mulungu
607 B.C.E.—1914 C.E.
October, 607 B.C.E.—October, 1 B.C.E. = Zaka 606
October, 1 B.C.E.—October, 1914 C.E. = Zaka 1,914
NTHAWI ZISANU NDI ZIWIRI ZA AMITUNDU = Zaka 2,520
[Chithunzi patsamba 134]
“Kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Aisrayeli?”
[Chithunzi patsamba 139]
Mtengo wautali m’Danieli chaputala 4 umaphiphiritsira ulamuliro wa Mulungu. Kwa kanthawi umenewu unasonyezedwa mwa ufumu wa Yuda
[Chithunzi pamasamba 140, 141]
Mtengowo unalikhidwa pamene ufumu wa Yuda unagwetsedwa