-
Olungama Adzatamanda Mulungu KosathaNsanja ya Olonda—2009 | March 15
-
-
11, 12. Kodi anthu a Mulungu amagwiritsa ntchito chuma chawo chakuthupi m’njira monga ziti?
11 Anthu a Mulungu, kaya odzozedwa a gulu la kapolo kapena a “khamu lalikulu,” asonyeza kuti ndi oolowa manja pankhani ya zinthu zakuthupi. Lemba la Salmo 112:9 limati: “Anagawagawa, anapatsa aumphawi.” Masiku ano, Akhristu oona nthawi zambiri amapatsa Akhristu anzawo zinthu zakuthupi ndiponso amapatsa ngakhale anthu oyandikana nawo amene akufunikira thandizo. Iwo amaperekanso chuma chawo chakuthupi pofuna kuthandiza anthu amene agweredwa tsoka. Monga mmene Yesu anasonyezera, Akhristuwa akamachita zimenezi amakhala osangalala.—Werengani Machitidwe 20:35; 2 Akorinto 9:7.
12 Ndiponso taganizirani kuchuluka kwa ndalama zimene zimafunika kuti magazini ino ifalitsidwe m’zinenero 172. Anthu amene amalankhula zambiri mwa zinenerozi ndi osauka. Taganiziraninso kuti magazini ino imapezeka m’zilembo za akhungu, komanso m’zinenero zamanja zimene anthu osamva ndiponso osalankhula amagwiritsa ntchito.
-
-
Olungama Adzatamanda Mulungu KosathaNsanja ya Olonda—2009 | March 15
-
-
‘Adzakwezeka ndi Ulemu’
17. Kodi wolungama ‘adzakwezeka ndi ulemu’ motani?
17 Zidzakhalatu zosangalatsa anthu onse akamadzatamanda Yehova, popanda kutsutsidwa ndi Mdyerekezi komanso dziko lake. Chisangalalo chimenechi chidzakhala mphoto yosatha ya anthu onse amene akuyesetsabe kukhala olungama pamaso pa Mulungu. Iwo sadzagonjetsedwa, chifukwa Yehova analonjezanso kuti, “nyanga” ya olungama “idzakwezeka ndi ulemu.” (Sal. 112:9) Munthu wolungama wa Yehova adzasangalala kwambiri kuona adani onse a Yehova, amene savomereza kuti iye ndiye woyenera kulamulira, akugonjetsedwa.
-