“Akunga Yehova Mulungu Wathu Ndani?”
“Akunga Yehova Mulungu wathu ndani, amene akhala pamwamba patali?”—SALMO 113:5.
1, 2. (a) Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zimawonera Mulungu ndi Baibulo? (b) Kodi ndimafunso otani ofunikira kuwalingalira?
OTAMANDA Yehova ali odalitsidwa kwenikweni. Ndimwaŵi waukulu chotani nanga kukhala m’gulu lalikulu lachimwemwe limeneli! Monga Mboni zake, timalandira uphungu, malamulo, ziphunzitso, malonjezo, ndi maulosi a Mawu a Mulungu, Baibulo. Tiri osangalala kuphunzira za m’Malemba ndi kukhala “ophunzitsidwa ndi Yehova.”—Yohane 6:45, NW.
2 Chifukwa cha ulemu wawo waukulu kwa Mulungu, Mboni za Yehova zikhoza kufunsa kuti: “Akunga Yehova Mulungu wathu ndani?” (Salmo 113:5) Mawu a wamasalmo amenewo amasonyeza chikhulupiriro. Koma kodi nchifukwa ninji Mbonizo ziri ndi chikhulupiriro chotero mwa Mulungu? Ndipo ziri ndizifukwa zotani zimene zimatamandira Yehova?
Chikhulupiriro ndi Chitamando Nzoyenera
3. Kodi Masalmo a Haleli nchiyani, ndipo kodi nchifukwa ninji amatchedwa motero?
3 Chikhulupiriro mwa Yehova nchoyenera chifukwa chakuti iye ali Mulungu wapadera. Izi zikugogomezeredwa m’Masalmo 113, 114, ndi 115, amene ali mbali ya otchedwa Masalmo a Haleli asanu ndi limodzi. Malinga ndi Sukulu Yachirabi ya Hillel, Masalmo 113 ndi 114 anaimbidwa pachakudya cha Paskha Wachiyuda pambuyo pakuthiridwa kwa chikho chachiŵiri cha vinyo ndi kufotokozedwa kwa tanthauzo la phwandolo. Masalmo 115 mpaka 118 anaimbidwa pambuyo pa chikho chavinyo chachinayi. (Yerekezerani ndi Mateyu 26:30.) Iwo amatchedwa “Masalmo a Haleli” chifukwa chakuti amatchula mobwerezabwereza mfuu yakuti Haleluya!—“Tamandani Ya!”
4. Kodi liwu lakuti “Haleluya” limatanthauzanji, ndipo kodi limapezeka kangati m’Baibulo?
4 “Haleluya!” ndikalembedwe ka liwu Lachihebri lopezeka nthaŵi 24 m’Masalmo. M’malo ena m’Baibulo, mpangidwe wake Wachigiriki umapezeka kanayi kusonya ku chisangalalo chokhalapo pakuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, ndi chisangalalo chophatikizidwapo cha kuyamba kwa Yehova Mulungu kulamulira monga Mfumu. (Chivumbulutso 19:1-6) Pamene tsopano tikupenda atatu a Masalmo a Haleli, tikhoza kudziyerekezera ife eni kukhala tikuimba nyimbo zimenezi kutamanda Yehova.
Tamandani Ya!
5. Kodi Salmo 113 limayankha funso liti, ndipo kodi lamulo la pa Salmo 113:1, 2 limagwira ntchito makamaka kwa ayani lerolino?
5 Salmo 113 limayankha funso lakuti, Nkutamandiranji Yehova? Limayamba ndi lamulo lakuti: “Haleluya; Lemekezani, inu atumiki a Yehova; Lemekeza dzina la Yehova. Lodala dzina la Yehova. Kuyambira tsopano kufikira kosatha.” (Salmo 113:1, 2) “Haleluya!” Inde, “Tamandani Ya!” Lamulo limenelo limagwira ntchito makamaka kwa anthu a Mulungu mu “nthaŵi yachimaliziro” ino. (Danieli 12:4) Kuyambira tsopano kumkabe mtsogolo ku umuyaya wonse, Dzina la Yehova lidzakwezedwa padziko lonse lapansi. Mboni zake tsopano zikulengeza kuti Yehova ndi Mulungu, Kristu ndi Mfumu, ndipo Ufumuwo wakhazikitsidwa kumwamba. Satana Mdyerekezi ndi gulu lake sangaletse kutamandidwa kwa Yehova kumeneku.
6. Kodi Yehova akutamandidwa motani ‘chitulukire dzuŵa kufikira kuloŵa kwake’?
6 Nyimbo yachitamando idzaimbidwabe kufikira Yehova aichititsa kudzaza dziko lonse lapansi. “Chitulukire dzuŵa kufikira kuloŵa kwake. Lilemekezedwe dzina la Yehova.” (Salmo 113:3) Zimenezi zimatanthauza zoposa kulambira kwa tsiku ndi tsiku kochitidwa ndi zolengedwa zake zina za padziko lapansi. Dzuŵa limatuluka kummaŵa ndi kuloŵa kumadzulo, kuzungulira dziko lonse lapansi. Kulikonse dzuŵa limaŵala, dzina la Yehova posachedwapa lidzatamandidwa ndi anthu onse omasulidwa muukapolo wa chipembedzo chonyenga ndi gulu la Satana. Kwenikweni, nyimbo imeneyi imene sidzatha konse, tsopano ikuimbidwa ndi Mboni za Yehova zodzozedwa ndi awo amene adzakhala ana apadziko lapansi a Mfumu yake, Yesu Kristu. Ndimwaŵi wotani nanga umene ali nawo monga oimbira Yehova zitamando!
Yehova Ali Wosayerekezereka
7. Kodi ndimbali ziŵiri ziti za ukulu wa Yehova zimene zasonyezedwa pa Salmo 113:4?
7 Wamasalmo akuwonjezera kuti: “Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse, ulemerero wake pamwambamwamba.” (Salmo 113:4) Izi zimasonya ku mbali ziŵiri za ukulu wa Mulungu: (1) Kwa Yehova, Wamkulukulu, “pamwamba pa amitundu onse,” iwo ali ngati dontho lochokera mum’tsuko wamadzi ndi monga fumbi chabe pa miyeso; (Yesaya 40:15; Danieli 7:18) (2) ulemerero wake ngwaukulu kwambiri koposa uja wa miyamba yakuthupi, popeza kuti angelo amachita chifuno chake cholemekezeka.—Salmo 19:1, 2; 103:20, 21.
8. Kodi nchifukwa ninji ndipo ndimotani mmene Yehova amadzichepetsera kuti awone zinthu kumwamba ndi padziko lapansi?
8 Atasonkhezeredwa ndi kukwezeka kwa Mulungu, wamasalmo anati: “Akunga Yehova Mulungu wathu ndani? Amene akhala pamwamba patali. Nadzichepetsa apenye zam’mwamba ndi za padziko lapansi.” (Salmo 113:5, 6) Mulungu ali wokwezeka kwambiri kotero kuti amadzichepetsa kuti awone zinthu za kumwamba ndi padziko lapansi. Ngakhale kuti Yehova sali wochepa kwa aliyense kapena samagonjera kwa ena, amasonyeza kudzichepetsa posonyeza chifundo ndi chisoni kwa ochimwa odzichepetsa. Kupereka Mwana wake, Yesu Kristu, monga “chiwombolo cha machimo” kaamba ka Akristu odzozedwa ndi dziko la mtundu wa anthu ndichisonyezero cha kudzichepetsa kwa Yehova.—1 Yohane 2:1, 2.
Yehova Ali Wachifundo
9, 10. Kodi ndimotani mmene Mulungu ‘amakwezera waumphaŵi, kumkhalitsa pakati pa zinduna’?
9 Akumagogomezera chifundo cha Mulungu, wamasalmo akuwonjezera kuti Yehova “akweza waumphaŵi kumchotsa kudzala; kuti amkhalitse pamodzi ndi zinduna, pamodzi ndi akulu a anthu ake. Asungitsa nyumba mkazi wosawona mwana, akhale mayi wokondwera ndi ana. Haleluya!” (Salmo 113:7-9) Anthu a Yehova ali ndi chikhulupiriro chakuti iye akhoza kupulumutsa amphaŵi owongoka mtima, kusintha mkhalidwe wawo, ndi kukhutiritsa zosoŵa zawo ndi zikhumbo zoyenera. ‘Wapamwamba ndi Wokwezeka atsitsimula mzimu wa odzichepetsa ndi amtima wa osweka.’—Yesaya 57:15.
10 Kodi ndimotani mmene Yehova ‘amakwezera waumphaŵi, kumkhalitsa pakati pa zinduna’? Pamene chiri chifuniro cha Mulungu, iye amaika atumiki ake m’malo aulemerero ofanana ndi a zinduna. Anatero m’chochitika cha Yosefe, yemwe anakhala woyang’anira chakudya mu Igupto. (Genesis 41:37-49) Mu Israyeli, kukhala pakati pa zinduna, kapena amuna olamulira pakati pa anthu a Yehova, kunali mwaŵi woyamikirika. Mofanana ndi akulu Achikristu lerolino, amuna oterowo anali ndi chithandizo ndi dalitso la Yehova.
11. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti Salmo 113:7-9 limagwira ntchito makamaka kwa anthu a Yehova alerolino?
11 Bwanji za ‘kuchititsa mkazi wosabala kukhala nakubala wachisangalalo’? Mulungu anapatsa Hana wowumayo mwana wamwamuna—Samueli, amene anampereka kuutumiki Wake. (1 Samueli 1:20-28) Chofunika koposa, kuyambira pa Yesu ndi pakutsanuliridwa kwa mzimu woyera pa ophunzira ake pa Pentekoste wa 33 C.E., mkazi wophiphiritsira wa Mulungu, Ziyoni wakumwamba, anayamba kubala ana auzimu. (Yesaya 54:1-10, 13; Machitidwe 2:1-4) Ndipo monga momwe Mulungu anabwezeretsera Ayuda kudziko lawo pambuyo paukapolo m’Babulo, mu 1919 anamasula otsalira odzozedwa a “Israyeli wa Mulungu” ku ukapolo wa ku Babulo ndipo wawadalitsa kwambiri mwauzimu kwakuti mawu a Salmo 113:7-9 amagwira ntchito kwa iwo. (Agalatiya 6:16) Monga Mboni za Yehova zokhulupirika, otsalira a Israyeli wauzimu ndi atsamwali awo okhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi akulabadira mwachisangalalo mawu omalizira a Salmo 113 akuti: “Tamandani Ya, anthu inu!”
Umboni wa Kukhala Wapadera kwa Yehova
12. Kodi ndimotani mmene Salmo 114 limasonyezera kukhala wapadera kwa Yehova?
12 Salmo 114 limasonyeza kukhala wapadera kwa Yehova mwakutchula zochitika zapadera zophatikizapo Aisrayeli. Wamasalmo anaimba kuti: “M’mene Israyeli anatuluka ku Aigupto, Nyumba ya Yakobo kwa anthu a chinenedwe chachilendo; Yuda anakhala malo ake oyera, Israyeli ufumu wake.” (Salmo 114:1, 2) Mulungu anamasula Israyeli kuukapolo kwa Aigupto, amene chinenero chawo chinali chachilendo kumakutu awo. Kumasulidwa kwa anthu a Yehova, otchedwa Yuda ndi Israyeli m’ndakatuloyo, kumasonyeza kuti Mulungu akhoza kumasula atumiki ake onse lerolino.
13. Kodi ndimotani mmene Salmo 114:3-6 limasonyezera ukulu wa Yehova ndipo limagwira ntchito motani ku zokumana nazo za Israyeli wakale?
13 Kukwezeka kwa Yehova pamwamba pa chilengedwe chonse kukuwoneka m’mawu akuti: “Nyanjayo inawona, nithaŵa; Yordano anabwerera m’mbuyo. Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo, timapiri ngati ana a nkhosa. Unathawanji nawe, nyanja iwe? Unabwerereranji m’mbuyo, Yordano iwe? Munatumpha-tumphiranji ngati nkhosa zamphongo, mapiri inu? Ngati ana ankhosa, zitunda inu?” (Salmo 114:3-6) Nyanja Yofiira “inathaŵa” pamene Mulungu anatsegula njira kuti anthu ake apite. Ndiyeno Israyeli anawona dzanja lamphamvu la Yehova likuchitapo kanthu motsutsana ndi Aigupto amene anafa m’madzi obwererawo. (Eksodo 14:21-31) M’chochitika chofanana chosonyeza mphamvu yaumulungu, Mtsinje wa Yordano unayamba “kubwerera,” kumalola Aisrayeli kuwolokera m’Kanani. (Yoswa 3:14-16) ‘Mapiri analumphalumpha ngati ana ankhosa’ pamene Phiri la Sinayi linkatulutsa utsi ndi kunjenjemera pamene pangano la Chilamulo linaperekedwa. (Eksodo 19:7-18) Pomafika kumapeto kwa nyimbo yake, wamasalmoyo anaika zochitikazo mwanjira yamafunso, mwinamwake akupereka lingaliro lakuti zinthu zopanda moyozo, nyanja, mtsinje, mapiri, ndi zitunda zinachita mantha ndi ziwonetsero zimenezi za mphamvu ya Yehova.
14. Kodi nchiyani chinachitidwa ndi mphamvu ya Yehova ku Meriba ndi Kadesi, ndipo zimenezi ziyenera kuyambukira motani atumiki ake alerolino?
14 Akusonyabe ku mphamvu ya Yehova, wamasalmoyo anaimba kuti: “Unjenjemere, dziko lapansi iwe, pamaso pa Ambuye, pamaso pa Mulungu wa Yakobo; Amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi, Nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi.” (Salmo 114:7, 8) Motero, m’njira yophiphiritsira, wamasalmo akusonyeza kuti mtundu wa anthu uyenera kuwopa Yehova, Ambuye ndi Wolamulira Wamkulu wa dziko lonse lapansi. Iye anali “Mulungu wa Yakobo,” kapena Israyeli, monga momwe alirinso wa Aisrayeli auzimu ndi atsamwali awo apadziko lapansi. Ku Meriba ndi Kadesi m’chipululu, Yehova anasonyeza mphamvu yake mwakupatsa madzi Israyeli mwanjira yozizwitsa, “Kusanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi, Nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi.” (Eksodo 17:1-7; Numeri 20:1-11) Zikumbutso zoterozo za mphamvu ya Yehova yochititsa mantha ndi chisamaliro chake chachikondi zimapatsa Mboni zake zifukwa zabwino zokhalira ndi chikhulupiriro chosakaikitsa mwa iye.
Mosiyana ndi Milungu ya Mafano
15. Kodi Salmo 115 lingakhale linaimbidwa bwanji?
15 Salmo 115 limatichichiza kutamanda ndi kukhulupirira Yehova. Limasonyeza kuti dalitso ndi chithandizo zimachokera kwa iye ndi kutsimikizira kuti mafano ali opanda pake. Salmo limeneli lingakhale linaimbidwa mopokereza. Ndiko kuti, liwu limodzi mwina linaimba kuti: “Inu akuwopa Yehova, Khulupirirani Yehova.” Ndiyeno mpingo wonse nkupokereza kuti: “Ndiye mthandizi wawo ndi chikopa chawo.”—Salmo 115:11.
16. Kodi ndikusiyana kotani kumene kungasonyezedwe pakati pa Yehova ndi mafano a mitundu?
16 Ulemerero suyenera kudza kwa ife koma kudzina la Yehova, Mulungu wakukoma mtima kwachikondi, kapena chikondi chokhulupirika, ndi chowonadi. (Salmo 115:1) Adani angafunse monyodola kuti: “Ali kuti Mulungu wawo?” Koma anthu a Yehova angayankhe kuti: ‘Mulungu wathu ali kumwamba ndipo amachita chirichonse chomkondweretsa.’ (Mavesi 2, 3) Komabe, mafano a mitundu satha kuchita kalikonse, popeza kuti ali zifanizo zopangidwa ndi munthu za siliva ndi golidi. Ngakhale kuti ali ndi pakamwa, maso, ndi makutu, iwo salankhula, ngakhungu, ndi ogontha. Mphuno ali nazo koma sanunkhiza, miyendo ali nayo koma sayenda, ndipo mmero ali nawo koma satha kunena kanthu. Awo opanga mafano opanda mphamvuwo limodzi ndi awo owakhulupirira nawonso adzakhala opanda moyo.—Mavesi 4-8.
17. Popeza kuti akufa sangatamande Yehova, kodi tiyenera kuchitanji, ndipo tikumakhala ndi ziyembekezo zotani?
17 Ndiyeno chisonkhezero chikuperekedwa cha kukhulupirira Yehova monga Mthandizi ndi Chikopa chotetezera cha Israyeli, cha nyumba ya ansembe ya Aroni, ndi cha onse akuwopa Mulungu. (Salmo 115:9-11) Monga akuwopa Yehova, tiri ndi ulemu waukulu kwa Mulungu ndi mantha oyenera akuwopa kusamkondweretsa iye. Tirinso ndi chikhulupiriro chakuti “Wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi” amadalitsa olambira ake okhulupirika. (Mavesi 12-15) Kumwamba ndiko malo a mpando wake wachifumu, koma Mulungu anapanga dziko lapansi kukhala mudzi wamuyaya wa anthu okhulupirika ndi omvera. Akufa pokhala ali kumalo achete ndipo sadziŵa kanthu bi, sangatamande Yehova, ife, amoyofe, tiyenera kutero mwakudzipereka ndi kumvera kotheratu. (Mlaliki 9:5) Awo okha amene amatamanda Yehova adzasangalala ndi moyo wosatha ndi kukhoza ‘kulemekeza Yehova’ kosatha, akumamthokoza “kufikira nthaŵi yonse.” Chotero tigwirizanetu mokhulupirika ndi awo olabadira chilangizo chakuti: “Tamandani Ya, anthu inu!”—Salmo 115:16-18.
Mikhalidwe Yabwino Koposa ya Yehova
18, 19. Kodi mikhalidwe ya Yehova imamsiyanitsa m’njira ziti ndi milungu yonama?
18 Mosiyana ndi mafano opanda moyo, Yehova ali Mulungu wamoyo, amene amasonyeza mikhalidwe yabwino koposa. Iye ndiye chikondi chenichenicho ndipo ali “wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka.” (Eksodo 34:6; 1 Yohane 4:8) Iye amasiyana chotani nanga ndi Moleki mulungu wankhalwe wa Akanani, kwa amene ana anaperekedwa nsembe! Kumalingaliridwa kuti fano la mulungu ameneyu linali ndi mpangidwe wa munthu ndi mutu wa ng’ombe. Kukusimbidwa kuti fanolo linatenthetsedwa piriŵiri, ndipo ana anaponyedwa m’mikono yake yotambasuka, akumagwera m’ng’anjo yolipuka moto munsi mwake. Koma Yehova ngwachikondi kwambiri ndi wachifundo kotero kuti lingaliro la nsembe za anthu zoterozo “silinaloŵa mumtima” mwake ndi kalelonse.—Yeremiya 7:31.
19 Mikhalidwe yaikulu ya Yehova imaphatikizaponso chiweruzo cholungama, nzeru yopanda malire, ndi mphamvuyonse, yonseyo yangwiro. (Deuteronomo 32:4; Yobu 12:13; Yesaya 40:26) Bwanji za milungu ya m’nthanthi? Mmalo mwakusonyeza chiweruzo cholungama, milungu yachimuna ndi yachikazi ya Babulo inali yolipsira. Milungu ya Igupto sinali zitsanzo za nzeru koma inasonyezedwa kukhala ndi zifooko zaumunthu. Sizodabwitsa zimenezo, popeza kuti milungu yonama yachimuna ndi yachikazi imeneyo inapangidwa ndi anthu “opanda pake m’maganizo awo” odzinenera kukhala anzeru. (Aroma 1:21-23) Kumanenedwa kuti milungu ya Girisi inachitirana chiŵembu. Mwachitsanzo, m’nthanthi, Zeus anagwiritsira ntchito mphamvu zake molakwa kuchotsa pampando wachifumu atate wake, Cronus, amenenso anachotsa atate wake, Uranus, paufumu. Ndidalitso lotani nanga kutumikira ndi kutamanda Yehova, Mulungu wamoyo ndi wowona, amene amasonyeza chikondi changwiro, chiweruzo cholungama, nzeru, ndi mphamvu!
Yehova Ali Woyenerera Chitamando Chosatha
20. Kodi Mfumu Davide anapereka zifukwa zotani zimene anatamandira dzina la Yehova?
20 Monga momwe Masalmo a Haleli akusonyezera, Yehova amayenera chitamando chosatha. Mofananamo, pamene Davide ndi Aisrayeli anzake anapatsa zopereka za kumangidwa kwa kachisi, anati pamaso pampingo: “Wolemekezedwa inu, Yehova Mulungu wa Israyeli, Atate wanthu kunthaŵi zomka muyaya. Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; Pakuti zonse za m’mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse. Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m’dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m’dzanja lanu. Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.”—1 Mbiri 29:10-13.
21. Kodi Chivumbulutso 19:1-6 chimapereka umboni wotani wakulambiridwa kwa Yehova ndi makamu akumwamba?
21 Yehova adzalemekezedwanso ndi kutamandidwa kwamuyaya kumwamba. Mtumwi Yohane anamva “khamu lalikulu m’mwamba” likunena: “Tamandani Ya, anthu inu! Chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu; pakuti maweruzo ake ali owona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu [Babulo Wamkulu], amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake pa dzanja lake la mkaziyo.” Ndipo linatinso: “Tamandani Ya, anthu inu!” Anateronso “akulu makumi aŵiri mphambu anayi ndi zamoyo zinayi.” Liwu lochokera kumpando wachifumu linati: “Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse, akumuwopa iye, ang’ono ndi akulu.” Ndiyeno Yohane anawonjezera kuti: “Ndinamva ngati mawu a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mawu amabingu olimba, nizinena, Tamandani Ya, anthu inu; Pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.”—Chivumbulutso 19:1-6.
22. Kodi Yehova adzatamandidwa motani m’dziko lake latsopano lolonjezedwalo?
22 Nkoyenerera chotani nanga kuti makamu akumwamba akutamanda Yehova! M’dziko lake latsopano limene tsopano layandikira, oukitsidwa okhulupirika adzagwirizana ndi opulumuka mapeto a dongosolo lino m’kutamanda Ya. Mapiri aatali adzatukula mitu yawo kuimba nyimbo zotamanda Mulungu. Zitunda zobiriŵira ndi mitengo yobala zipatso idzaimba zitamando zake. Eya, cholengedwa chirichonse chokhala ndi moyo ndi chopuma chidzatamanda dzina la Yehova m’mang’ombe aakulu a Haleluya! (Salmo 148) Kodi liwu lanu lidzamveka m’gulu lalikulu lachisangalalo limenelo? Lidzatero ngati mokhulupirika mutumikira Ya limodzi ndi anthu ake. Chimenecho chiyenera kukhala chonulirapo chanu m’moyo, popeza kuti akunga Yehova Mulungu wathu ndani?
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nkumtamandiranji Yehova Mulungu?
◻ Kodi ndim’njira zotani zimene Yehova ali wosayerekezereka?
◻ Kodi pali umboni wotani wakuti Yehova ali wachifundo?
◻ Kodi Yehova amasiyana motani ndi mafano opanda moyo ndi milungu yonama?
◻ Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Yehova adzalandira chitamando chamuyaya kumwamba ndi padziko lapansi?
[Chithunzi patsamba 9]
Masalmo a Haleli anaimbidwa pachakudya cha Paskha