Musamaone Zinthu Zachabe
“Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.”—SAL. 119:37.
1. Kodi maso athu ndi ofunika motani?
MASO athu ndi ofunika kwambiri. Timatha kuwagwiritsa ntchito kuona bwinobwino mtundu wa zinthu zosiyanasiyana zimene zatizungulira. Amatithandiza kuona mabwenzi athu okondedwa ndiponso zinthu zoopsa. Timatha kuona kukongola kwa zinthu, zolengedwa zodabwitsa ndiponso kuzindikira ulemelero wa Mulungu komanso umboni wakuti aliko. (Sal. 8:3, 4; 19:1, 2; 104:24; Aroma 1:20) Popeza timagwiritsa ntchito maso kupereka uthenga ku maganizo athu, maso athu ndi ofunika kuti tidziwe bwino Yehova ndiponso kuti tizimukhulupirira.—Yos. 1:8; Sal. 1:2, 3.
2. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ndi zimene timaona, ndipo kodi tikuphunzira chiyani pa zimene wamasalmo anapempha?
2 Komabe, zimene timaona zikhozanso kutiwononga. Pali kugwirizana kwambiri pakati pa zimene timaona ndi zimene timaganiza, moti zimene timaona zingatipangitse kuti tizilakalaka zinazake. Ndipo popeza tikukhala m’dziko loipa ndiponso la anthu odzikonda, lomwe wolamulira wake ndi Satana Mdyerekezi, timaona ndi kumva zinthu zimene zingatisocheretse mosavuta ngakhale titangoziyang’ana kanthawi kochepa. (1 Yoh. 5:19) Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti wamasalmo anapempha Mulungu kuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.”—Sal. 119:37.
Mmene Maso Athu Angatisocheretsere
3-5. Kodi ndi nkhani za m’Baibulo ziti zimene zikusonyeza kuopsa kwa kulola maso athu kutinyenga?
3 Taganizirani zimene zinachitikira mkazi woyamba, Hava. Satana anamuuza kuti akadya chipatso cha “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa,” maso ake “adzatseguka.” Hava ayenera kuti anachita chidwi ndi mfundo yakuti maso ake “adzatseguka.” Chidwi chake chofuna kudya chipatso choletsedwa chinakula pamene ‘anaona kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m’maso, mtengo wolakalakika.’ Kuyang’ana mtengo moulakalaka kunachititsa kuti Hava asamvere Mulungu. Nayenso mwamuna wake Adamu sanamvere, ndipo zimenezi zinabweretsa mavuto kwa anthu onse.—Gen. 2:17; 3:2-6; Aroma 5:12; Yak. 1:14, 15.
4 M’nthawi ya Nowa, angelo ena nawonso anakopeka ndi zimene anaona. Ponena za angelo amenewa, lemba la Genesis 6:2 limati: “Ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.” Kuyang’anitsitsa ana a anthu mowakhumbira, kunachititsa kuti angelo opanduka amenewa akhale ndi chilakolako chosakhala chachibadwa chofuna kugonana ndi anthu. Angelowa anakhala ndi ana omwe anali a chiwawa kwambiri. Kuipa kwa anthu a m’nthawi imeneyi kunachititsa kuti anthu onse awonongedwe kupatulapo Nowa ndi banja lake.—Gen. 6:4-7, 11, 12.
5 Patapita zaka mazana ambiri, Mwisiraeli wina dzina lake Akani, ‘anaona’ zinthu zina mumzinda wa Yeriko, womwe unali utawonongedwa, ndipo anaziba. Mulungu anali atalamula kuti zinthu zonse mumzindawo ziwonongedwe kupatulapo zinthu zina zimene zinayenera kuperekedwa mosungira chuma cha Yehova. Aisiraeli anachenjezedwa kuti ‘asakhudze choperekedwacho’ kuopera kuti angakhumbire n’kutengako zinthu zina. Chifukwa cha kusamvera kwa Akani, Aisiraeli anagonjetsedwa ndi anthu a mumzinda wa Ai ndipo ambiri anaphedwa. Akani sanaulule tchimo lake mpaka pamene anaonekera poyera. Akani anati: “Pamene ndinaona” zinthuzo “ndinazikhumbira ndi kuzitenga.” Chilakolako cha maso ake chinachititsa kuti iye awonongedwe limodzi “ndi zake zonse.” (Yos. 6:18, 19; 7:1-26) Akani analakalaka zinthu zimene analetsedwa.
Tifunika Kukhala Odziletsa
6, 7. Kodi ndi “machenjera” ati a Satana amene nthawi zambiri amagwiritsidwa ntchito kutikopa, ndipo otsatsa malonda akuwagwiritsa ntchito bwanji?
6 Masiku anonso anthu angayesedwe mofanana ndi Hava, angelo opanduka ndiponso Akani. Pa “machenjera” onse amene Satana akugwiritsa ntchito pofuna kusocheretsa anthu, “chilakolako cha maso” n’chimene chimagwira ntchito kwambiri. (2 Akor. 2:11; 1 Yoh. 2:16) Akatswiri amakono otsatsa malonda amadziwa bwino kuti chilakolako cha maso chakhala champhamvu kuyambira kalekale. Katswiri wina wamalonda ku Ulaya anati: “Maso ndi osocheretsa kwambiri kuposa chiwalo chilichonse. Nthawi zambiri ndi amene amalamulira ziwalo zina, ndipo angapangitse munthu kuchita zinthu mosiyana ndi zimene akudziwa kuti ndi zolondola.”
7 N’chifukwa chake otsatsa malonda amationetsa zinthu zokonzedwa mwaluso kwambiri n’cholinga chakuti tikopeke kenako n’kukagula katundu wawo. Katswiri wina wofufuza zinthu wa ku America amene anaphunzira mmene anthu otsatsa malonda amakopera anthu anati: “Cholinga cha anthu otsatsa malonda sikungopereka uthenga basi, koma amafunanso kuti woonayo atengeke mtima ndi kukagula katunduyo.” Zinthu zolaula ndi zimene zimagwiritsidwa ntchito kwambiri. Ndiyetu tifunika kukhala odziletsa pa nkhani ya zinthu zimene timaonera ndiponso zimene timalowetsa m’maganizo ndi mumtima mwathu.
8. Kodi Baibulo limatsindika bwanji mfundo yakuti tiyenera kuteteza maso athu?
8 Akhristu oona nawonso amakhala ndi chilakolako cha maso ndi cha thupi. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kukhala odziletsa pa nkhani ya zinthu zimene timaona ndi zimene timakhumbira. (1 Akor. 9:25, 27; werengani 1 Yohane 2:15-17.) Munthu wolungama Yobu anazindikira kuti pali kugwirizana pakati pa kuona ndi kukhumbira. Iye anati: “Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?” (Yobu 31:1) Yobu anakana kukhudza mkazi m’njira yachiwerewere komanso sanalole kumaganiza zinthu zoterozo m’pang’ono pomwe. Yesu anatsindika mfundo yakuti sitiyenera kuganizira zachiwerewere. Iye anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.”—Mat. 5:28.
Zinthu Zachabe Zimene Tiyenera Kupewa
9. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala kwambiri makamaka pogwiritsa ntchito Intaneti? (b) Kodi chingachitike n’chiyani ngakhale titangoona pang’ono zinthu zolaula?
9 Masiku ano, anthu ochuluka amakonda ‘kuyang’anitsitsa’ zinthu zolaula makamaka pa Intaneti. Kodi tingaone bwanji mwangozi zinthu zimenezi ngakhale ngati sitinazifufuze? Chithunzi chotsatsa malonda koma chokopa chingaonekere mwadzidzidzi pa kompyuta yanu. Kapena mungatsegule imelo imene mwadzidzidzi ingabweretse zithunzi zolaula zimene zinakonzedwa mwanjira yoti zimakhala zovuta kuzitseka. Ndipo ngakhale mutangoona pang’ono musanazichotse, zithunzizi zimakhala kuti zakhazikika kale m’maganizo mwanu. Ngakhale kungoona pang’ono zinthu zolaula kumakhala ndi zotsatirapo zoipa. Kumachititsa munthu kukhala ndi chikumbumtima choipa ndipo amavutika kuti zimenezi zichoke m’maganizo mwake. Komanso munthu amene mwadala ‘amayang’anitsitsa’ zinthu zoterezi, ndiye kuti sanafetse zilakolako zoipa zimene zili mumtima mwake.—Werengani Aefeso 5:3, 4, 12; Akolose 3:5, 6.
10. N’chifukwa chiyani ana ndi amene makamaka angakopeke mosavuta ndi zinthu zolaula, ndipo zotsatira zake zimakhala zotani akamaonera zinthu zimenezi?
10 Ana angaonere zinthu zolaula chifukwa mwachibadwa amakhala ndi chidwi chofuna kudziwa zinthu. Ngati zimenezi zitachitika, zingakhudze mmene angamaonere nkhani ya kugonana. Katswiri wina anati, zimenezi zingawachititse kukhala ndi maganizo olakwika ofuna kuchita chilichonse chowakomera pa nkhani ya kugonana, “angamavutike kukondana ndi ena; angamaone akazi molakwika ndiponso angamakonde kuonera zinthu zolaula. Zimenezi zingasokoneze maphunziro awo a kusukulu, mmene amakhalira ndi anthu ena ndiponso achibale awo.” Komanso vuto lalikulu limakhala mmene zimenezi zimadzakhudzira ukwati wawo.
11. Perekani chitsanzo chosonyeza kuopsa koona zinthu zolaula.
11 M’bale wina analemba kuti: “Pa zinthu zonse zimene ndinkazikonda kwambiri, ndisanakhale Mboni, kuonera zinthu zolaula n’kumene kunandivuta kwambiri kuti ndisiye. Nthawi zina ndikangomva fungo linalake, nyimbo inayake, kuona chinachake kapena ndikayamba kuganiza zolakwika, ndimaonabe zinthu zimenezi m’maganizo mwanga. Zimenezi zimandivutitsa tsiku ndi tsiku.” M’bale wina ali mwana ankaonera zithunzi zolaula za bambo ake omwe si Mboni. Iye ankachita zimenezi makolo ake akachokapo. Iye analemba kuti: “Zithunzi zimenezi zinawononga kwambiri maganizo anga. Ngakhale kuti tsopano patha zaka 25, ndimalephera kuiwala zinthu zimenezi. Ngakhale ndiyesetse bwanji kuziiwala ndimaziganizirabe. Zimenezi zimandipangitsa kuvutika maganizo ngakhale pa nthawi imene sindikuziganizira.” Ndiyetu ndi nzeru kupewa kuvutitsidwa ndi chikumbumtima mwa kusaonera zinthu zolaula. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Muyenera kuyesetsa ‘kutenga lingaliro lililonse ukapolo kuti likhale lomvera Khristu.’—2 Akor. 10:5.
12, 13. Kodi ndi zinthu zachabe ziti zimene Akhristu sayenera kuonera ndipo n’chifukwa chiyani?
12 ‘Chinthu china choipa’ kapena kuti chachabe chimene tiyenera kupewa, ndi zosangalatsa zimene zimalimbikitsa kukonda chuma ndiponso zamizimu, zimene zimaonetsa zachiwawa, kukhetsa magazi, komanso kuphana. (Werengani Salmo 101:3.) Yehova wapatsa makolo achikhristu udindo wosankha bwino zinthu zimene akuonera m’nyumba zawo. Koma n’zodziwikiratu kuti palibe Mkhristu weniweni amene angamaonere mwadala zinthu zamizimu. Ngakhale ndi choncho makolo ayenera kudziwa kuti pali mafilimu, masewero a pa TV, masewera apakompyuta, mabuku ndi timabuku ta zinthuzi ndiponso nkhani zoseketsa za ana zimene zimasonyeza chiwawa ndi zinthu zina zauchiwanda.—Miy. 22:5.
13 Kaya ndife wachinyamata kapena wachikulire, maso athu asamakonde masewera apakompyuta achiwawa ndiponso oonetsa anthu akuphana. (Werengani Salmo 11:5.) Tiyenera kuyesetsa kuti tisamaganize zinthu zilizonse zimene Yehova amadana nazo. Musaiwale kuti Satana akufuna kwambiri kusokoneza maganizo athu. (2 Akor. 11:3) Ngakhale zosangalatsa zimene tingaone kuti n’zoyenera, zingasokoneze kulambira kwathu kwa pabanja, kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndiponso kukonzekera misonkhano ngati timathera nthawi yochuluka tikuzionerera.—Afil. 1:9, 10.
Tsatirani Chitsanzo cha Yesu
14, 15. Kodi chochititsa chidwi n’chiyani pa zimene Satana anachita poyesa Khristu kachitatu, ndipo n’chiyani chinathandiza Yesu kusagonja?
14 N’zomvetsa chisoni kuti popeza tikukhala m’dziko loipali, sitingapeweretu kuona zinthu zachabe. Ngakhale Yesu anaonetsedwa zinthu ngati zimenezi. Pamene Satana ankayesa Yesu kachitatu pofuna kumulepheretsa kuchita zofuna za Mulungu, “anamutenganso ndi kupita naye pa phiri lalitali kwambiri, ndipo anamuonetsa maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo.” (Mat. 4:8) N’chifukwa chiyani Satana anachita zimenezi? Mosakayikira iye ankafuna kugwiritsa ntchito mphamvu imene maso ali nayo. Kuona ulemerero wa mafumu onse a dziko lapansi, kukanachititsa Yesu kukhala ndi mtima wofuna kutchuka umene anthu amakhala nawo. Kodi Yesu anatani?
15 Yesu sanayang’anitsitse zinthu zokopa zimenezi. Iye sanalole zilakolako zoipa kukhala mumtima mwake. Sanafunikire kuganizira kaye zimene Mdyerekezi anamusonyeza kuti athe kuzikana. Yesu anakana nthawi yomweyo. Ananena kuti: “Choka Satana!” (Mat. 4:10) Yesu ankaganizira kwambiri ubwenzi wake ndi Yehova ndipo anayankha mogwirizana ndi cholinga chake chomwe ndi kuchita zimene Mulungu amafuna. (Aheb. 10:7) Zimenezi zinachititsa kuti Yesu athe kukana machenjera a Satana.
16. Kodi chitsanzo cha Yesu chimatiphunzitsa chiyani pa nkhani yokana mayesero a Satana?
16 Tingaphunzire zambiri pa chitsanzo cha Yesu chimenechi. Choyamba, palibe amene sangayesedwe ndi Satana. (Mat. 24:24) Chachiwiri, zinthu zimene timaona zingachititse kuti mtima wathu uzilakalaka zinthu zabwino kapena zoipa. Chachitatu, Satana amagwiritsa ntchito “chilakolako cha maso” mmene angathere n’cholinga chakuti atisocheretse. (1 Pet. 5:8) Ndipo chachinayi, ifenso tingatsutse Satana makamaka ngati tichita zinthu mosazengereza.—Yak. 4:7; 1 Pet. 2:21.
Khalani ndi Diso “Lolunjika Chimodzi”
17. N’chifukwa chiyani si chinthu cha nzeru kuyembekeza kuti tione kaye zinthu zachabe kenako n’kumaganiza bwino zochita?
17 Pamene tinadzipereka kwa Yehova, mwa zina, tinalonjeza kuti tidzapewa zachabe. Popeza tinalumbira kuti tidzachita zimene Mulungu amafuna, nafenso timanena ngati wamasalmo kuti: “Ndinaletsa mapazi anga njira ili yonse yoipa, kuti ndisamalire mawu anu.” (Sal. 119:101) Si chinthu cha nzeru kuyembekeza kuti tione kaye zinthu zachabe kenako n’kumaganiza bwino zochita. Zinthu zimene Malemba amatsutsa zafotokozedwa bwino ndipo tikuzidziwa. Ndipo tikudziwa machenjera onse a Satana. Kodi ndi liti pamene Satana anayesa Yesu kuti asinthe miyala kukhala mikate? N’kuti Yesu atasala kudya masiku 40, usana ndi usiku ndipo anali ndi “njala.” (Mat. 4:1-4) Satana amatha kudziwa nthawi imene tafooka moti tingathe kugonja mosavuta titayesedwa. Choncho, inoyo ndiyo nthawi yoganizira mosamala nkhani zimenezi. Musazengereze. Tsiku ndi tsiku tikamakumbukira lonjezo lathu la kudzipereka kwa Yehova, tidzatsimikiza mtima kupewa kuona zinthu zachabe.—Miy. 1:5; 19:20.
18, 19. (a) Kodi munthu wa diso “lolunjika chimodzi” amasiyana bwanji ndi munthu wa diso “loipa”? (b) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira zinthu zopindulitsa, ndipo lemba la Afilipi 4:8 lili ndi malangizo otani pa nkhani imeneyi?
18 Tsiku lililonse timaona zinthu zambiri zimene zingatisokoneze ndipo zinthu zoterezi zikuchulukirachulukira. Choncho, kuposa ndi kale lonse, tifunika kutsatira malangizo a Yesu akuti tiyenera kukhala ndi diso “lolunjika chimodzi.” (Mat. 6:22, 23) Munthu wa diso “lolunjika chimodzi” nthawi zonse amakhala ndi cholinga chimodzi chomwe ndi kuchita zimene Mulungu amafuna.Koma munthu wa diso “loipa” amakhala wa chinyengo, wosirira mwa nsanje ndipo amakonda kuona zinthu zachabe.
19 Musaiwale kuti zimene timaona, n’zimene timaganizira ndipo zimene timaganizira, n’zimene zimakhazikika mumtima mwathu. Choncho, nthawi zonse tifunika kuganizira zinthu zopindulitsa. (Werengani Afilipi 4:8.) Ndithudi, tiyeni tipitirize kunena mawu apemphero la wamasalmo akuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe.” Choncho tikamayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu amenewa, tidzakhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova ‘adzatipatsa moyo mu njira yake.’—Sal. 119:37; Aheb. 10:36.
Tibwereze
• Kodi maso, maganizo ndiponso mtima zimagwirizana motani?
• Kodi kuonera zinthu zolaula n’koopsa motani?
• N’chifukwa chiyani tifunika kukhalabe ndi diso “lolunjika chimodzi”?
[Zithunzi patsamba 23]
Kodi ndi zinthu zachabe ziti zimene Akhristu sayenera kuonera?