Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kuyambira Ali Akhanda
BAIBULO limanena kuti: “Taonani! Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova. Chipatso cha mimba ndicho mphoto.” (Sal. 127:3) Choncho n’zosadabwitsa kuti makolo achikhristu amasangalala kwambiri mwana akabadwa.
Komabe mwana akabadwa, makolo amakhalanso ndi udindo waukulu kwambiri. Kuti mwanayo akule bwino, ayenera kudya chakudya chopatsa thanzi nthawi zonse. Kuti akhalenso mtumiki wa Yehova wokhulupirika, mwana amafunikira chakudya chauzimu. Choncho makolo ayenera kumuphunzitsa mfundo za m’Baibulo. (Miy. 1:8) Kodi makolo ayenera kumuphunzitsa bwanji ndipo ayenera kuyamba liti?
MAKOLO AMAFUNIKIRA MALANGIZO
Taganizirani za munthu wina wa fuko la Dani, dzina lake Manowa, amene ankakhala m’tauni ya Zoari ku Isiraeli. Mngelo wa Yehova anauza mkazi wa Manowa, yemwe anali wosabereka, kuti adzabereka mwana wamwamuna. (Ower. 13:2, 3) Manowa ndi mkazi wake ayenera kuti anasangalala kwambiri atamva zimenezi koma panali zina zimene zinkawadetsa nkhawa. Manowa anapemphera kuti: “Yehova, lolani kuti munthu wa Mulungu woona amene munam’tuma, abwerenso kuti adzatilangize zoyenera kuchita ndi mwana amene adzabadweyo.” (Ower. 13:8) Manowa ndi mkazi wake ankafunitsitsa kulera bwino mwanayo. Iwo ayenera kuti anaphunzitsa mwana wawo, dzina lake Samisoni, chilamulo cha Mulungu ndipo zotsatira zake zinali zabwino. Baibulo limanena kuti: “Kenako mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa [Samisoni].” Izi zinachititsa kuti Samisoni achite zinthu zambiri zodabwitsa pa nthawi imene anali woweruza wa Aisiraeli.—Ower. 13:25; 14:5, 6; 15:14, 15.
Kodi makolo ayenera kuyamba liti kuphunzitsa ana awo? Timoteyo anaphunzitsidwa ‘Malemba oyera kuyambira pamene anali wakhanda.’ Mayi ake a Yunike ndiponso agogo ake a Loisi ndi amene anamuphunzitsa. (2 Tim. 1:5; 3:15) Izi zikusonyeza kuti Timoteyo anayamba kuphunzitsidwa Malemba ali wamng’ono kwambiri.
Makolo ayenera kukonzekera bwino komanso kupempha Yehova kuti awatsogolere n’cholinga choti ayambe kuphunzitsa mwana wawo ‘kuyambira ali wakhanda.’ Paja lemba la Miyambo 21:5 limati: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.” Choncho makolo ayenera kukonzekera bwino mwana wawo asanabadwe. Mwina angalemberetu zinthu zimene mwana wawo angafunikire. Angachitenso bwino kukonzekera mmene angamuphunzitsire Mawu a Mulungu. Iwo ayenera kukhala ndi cholinga choti ayambe kumuphunzitsa mwanayo ali wakhanda.
Buku lina lopereka malangizo kwa makolo amene ali ndi ana ang’onoang’ono linati: “Kuti ubongo wa mwana amene wangobadwa kumene ukule bwino, amafunika kuti ayambe kuphunzitsidwa m’miyezi yoyambirira. Pa nthawi imeneyi, ubongo wa mwana umakhala wokonzeka kuphunzira zinthu zambiri.” Makolo angachite bwino kwambiri kugwiritsa ntchito nthawi imeneyi kuti ayambe kuphunzitsa mwana wawo Mawu a Mulungu ndiponso makhalidwe abwino.
Ponena za mwana wake wamkazi, mlongo wina amene ndi mpainiya wokhazikika anati: “Ndinayamba kutenga mwana wanga mu utumiki kuyambira ali ndi mwezi umodzi wokha. Ndikudziwa kuti sankazindikira zimene zikuchitika, komabe zinamuthandiza. Atakwanitsa zaka ziwiri, ankapereka timapepala kwa anthu molimba mtima.”
Kuphunzitsa mwana kuyambira ali wakhanda n’kothandiza kwambiri. Koma makolo amaona kuti kuphunzitsa mwana Mawu a Mulungu si kophweka.
“MUZIGWIRITSA NTCHITO BWINO NTHAWI YANU”
Makolo akhoza kuvutika kuphunzitsa mwana chifukwa ana satha kumvetsera kwa nthawi yaitali. Mwana wamng’ono amavutika kuika maganizo pa chinthu chimodzi chifukwa amachita chidwi ndi zinthu zambiri zimene zikuchitika. Kodi n’chiyani chimene makolo angachite kuti mwana wawo azikhala ndi chidwi akamamuphunzitsa?
Taonani zimene Mose ananena pa lemba la Deuteronomo 6:6, 7. Iye anati: “Mawu awa amene ndikukulamula lero azikhala pamtima pako, ndi kuwakhomereza mwa ana ako. Uzilankhula nawo za mawuwo ukakhala pansi m’nyumba mwako, poyenda pamsewu, pogona ndi podzuka.” Mawu akuti ‘kukhomereza’ akusonyeza kuti mwana amafunika kuphunzitsidwa mobwerezabwereza. Mwana wamng’ono ali ngati kamtengo kamene kamafunika kukathirira pafupipafupi. Popeza kuchita zinthu mobwerezabwereza kumathandiza munthu kuti asaiwale, kungathandizenso mwana wanu kuti azikumbukira zinthu.
Makolo amafunika kuti azipeza nthawi yophunzitsa ana awo mfundo za m’Baibulo. Masiku ano, kupeza nthawi yophunzitsa ana n’kovuta. Koma mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti ‘tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu’ kuti tizipeza nthawi yochita zinthu zofunika kwambiri. (Aef. 5:15, 16) Kodi tingachite bwanji zimenezi? M’bale wina amene ndi mkulu ndipo mkazi wake amachita upainiya, poyamba ankavutika kupeza nthawi yophunzitsa mwana wawo, kusamalira maudindo awo mumpingo komanso kugwira ntchito. Kodi iwo amapeza bwanji nthawi yophunzitsa mwana wawo? M’baleyo anati: “M’mawa uliwonse ndisanapite kuntchito, ine ndi mkazi wanga timamuwerengera Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kapena Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Madzulo, timaonetsetsa kuti tamuwerengeranso asanagone, ndipo tikamalowa mu utumiki timamutenga. Tikuyesetsa kumuphunzitsa adakali wamng’ono.”
‘ANA ALI NGATI MIVI’
N’zoona kuti timafuna kuti ana athu akadzakula adzakhale odalirika. Koma cholinga chathu chachikulu tikamawaphunzitsa n’chakuti azikonda kwambiri Mulungu.—Maliko 12:28-30.
Lemba la Salimo 127:4 limanena kuti: “Ana a bambo wachinyamata ali ngati mivi m’dzanja la mwamuna wamphamvu.” Apa ana akuwayerekezera ndi mivi imene munthu amayenera kuiponya molunjika chinthu chimene akufuna kulasa. Munthu akaponya muvi ndi uta n’zosatheka kuti aubweze. Ana amene ali ngati “mivi” amakhala m’manja mwa makolo kwa nthawi yochepa kwambiri. Makolowo ayenera kugwiritsa ntchito nthawi imeneyi pokhomereza mfundo za m’Baibulo m’maganizo ndiponso mumtima mwa ana awo.
Pofotokoza za ana ake auzimu, mtumwi Yohane analemba kuti: “Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.” (3 Yoh. 4) Nawonso makolo achikhristu amasangalala kwambiri ngati ana awo “akuyendabe m’choonadi.”