Yehova Amakusamalirani
‘Tayani pa [Mulungu] nkhaŵa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.’—1 PETRO 5:7.
1. Kodi ndi mbali yaikulu iti imene Yehova ndi Satana ndi osiyana kwambiri?
YEHOVA ndi Satana ndi osiyana kwambiri. Munthu aliyense amene amayandikira kwa Yehova amadedwa ndi Mdyerekezi. Buku lina lamaumboni lodziŵika bwino linafotokoza kusiyana kumeneku. Pankhani ya zimene Satana amachita malinga ndi mmene buku la m’Baibulo la Yobu limafotokozera, buku lakuti Encyclopædia Britannica (la 1970) limati: ‘Ntchito ya Satana ndiyo kuyendayenda m’dziko lapansi kufunafuna zochitika kapena anthu oti awaneneze. Motero, zimene iye amachita n’zosiyana kwambiri ndi zimene “maso a Ambuye” amachita, amene amayang’ana uku ndi uku padziko lapansi kulimbikitsa onse amene akuchita zabwino (2 Mbiri 16:9). Satana amakayikira kuti anthu amachita zabwino mopanda dyera ndipo Mulungu amam’lola kuyesa anthuwo koma mosapitirira malire amene Iye waika.’ Ee, palitu kusiyana kwakukulu!—Yobu 1:6-12; 2:1-7.
2, 3. (a) Kodi tanthauzo la liwu lachigiriki la “Mdyerekezi” likuonekera bwino bwanji pa zimene zinachitikira Yobu? (b) Kodi Baibulo likusonyeza bwanji kuti Satana akupitiriza kuneneza atumiki a Yehova padziko lapansi?
2 Liwu lachigiriki la “Mdyerekezi” limatanthauza “woneneza.” Buku la Yobu limavumbula kuti Satana ananeneza Yobu, mtumiki wokhulupirika wa Yehova, kuti anali kum’tumikira chifukwa cha phindu limene ankapezapo. Anati: “Kodi Yobu aopa Mulungu pachabe?” (Yobu 1:9) Nkhani ya m’buku la Yobu imasonyeza kuti ngakhale kuti Yobu anayesedwa kwambiri, iye anayandikirabe kwambiri kwa Yehova. (Yobu 10:9, 12; 12:9, 10; 19:25; 27:5; 28:28) Atatha mayesero ake, iye anauza Mulungu kuti: “Kumva ndidamva mbiri yanu, koma tsopano ndikupenyani maso.”—Yobu 42:5.
3 Kodi Satana anasiya kuneneza atumiki okhulupirika a Mulungu kuyambira nthaŵi ya Yobu? Ayi. Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti m’nthaŵi ya mapeto ino, Satana akupitiriza kuneneza abale a Kristu odzozedwa ndiponso mosakayika, anzawo okhulupirika. (2 Timoteo 3:12; Chivumbulutso 12:10, 17) Motero, tonsefe monga Akristu oona tifunika kungonjera kwa Mulungu wathu, Yehova, amene amatisamalira, kumutumikira chifukwa cha kumukonda kwambiri ndipo motero kutsimikizira kuti kuneneza kwa Satana n’kwabodza. Tikachita zimenezi, tidzasangalatsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11.
Yehova Amafuna Kutithandiza
4, 5. (a) Mosiyana ndi Satana, kodi Yehova amayang’ana chiyani padziko lapansi? (b) Ngati tikufuna kuti Yehova atiyanje, kodi tifunika kuchita chiyani?
4 Mdyerekezi amayendayenda padziko lapansi, kufunafuna winawake woti amuneneze ndi kumulikwira. (Yobu 1:7, 9; 1 Petro 5:8) Mosiyana ndi iye, Yehova amafuna kuthandiza anthu amene akufuna kuti iye awalimbikitse. Mneneri Hanani anauza Mfumu Asa kuti: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.” (2 Mbiri 16:9) Palitu kusiyana kwambiri pakati pa kutifufuza kwanjiru kwa Satana ndi kutisamala kwachikondi kwa Yehova!
5 Yehova satifufuza mwamseri kuti aone cholakwika chilichonse chimene tingachite. Wamasalmo analemba kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?” (Salmo 130:3) Yankho lake ndilakuti: palibe. (Mlaliki 7:20) Ngati tiyandikira kwa Yehova ndi mtima wonse, maso ake adzakhala pa ife, osati n’cholinga choti atiimbe mlandu, koma kuona khama lathu ndi kuyankha mapemphero athu oti atithandize komanso kutikhululukira. Mtumwi Petro analemba kuti: “Maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.”—1 Petro 3:12.
6. Kodi nkhani ya Davide ndi yolimbikitsa komanso yochenjeza motani?
6 Davide anali wopanda ungwiro ndipo anachita machimo aakulu. (2 Samueli 12:7-9) Koma anatsanulira mtima wake kwa Yehova ndipo anayandikira kwa iye mwa kupemphera kuchokera pansi pa mtima. (Salmo 51:1-12, timawu tating’onoting’ono timene tatsogolera salmoli) Yehova anamva pemphero la Davide ndipo anamukhululukira, ngakhale kuti anaona zopweteka chifukwa cha tchimo lakeli. (2 Samueli 12:10-14) Zimenezi ziyenera kutilimbikitsa komanso kutichenjeza. N’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova ndi wokonzeka kutikhululukira machimo athu ngati tilapa moona mtima, komanso n’zochenjeza kudziŵa kuti nthaŵi zambiri tchimo limabweretsa mavuto aakulu. (Agalatiya 6:7-9) Ngati tikufuna kuyandikira kwa Yehova, tifunika kutalikira kwambiri chilichonse chimene sichimusangalatsa.—Salmo 97:10.
Yehova Amadzikokera Anthu Ake
7. Kodi Yehova amayang’ana anthu otani, ndipo amadzikokera bwanji anthu oterowo?
7 Davide analemba m’salmo lake lina kuti: “Angakhale Yehova n’ngokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza am’dziŵira kutali.” (Salmo 138:6) Mofanana ndi zimenezi, salmo lina limati: “Akunga Yehova Mulungu wathu ndani? Amene akhala pamwamba patali, nadzichepetsa apenye zam’mwamba ndi za pa dziko lapansi. Amene autsa wosauka kumchotsa kupfumbi.” (Salmo 113:5-7) Inde, Mlengi wamphamvuyonse amene analenga zonse amadzichepetsa n’kuyang’ana padziko lapansi, ndipo maso ake amaona “wopepukayo,” “wosauka,” anthu amene “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zi[ku]chitidwa.” (Ezekieli 9:4) Amadzikokera anthu oterowo kudzera mwa Mwana wake. Yesu ali padziko lapansi anati: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye; . . . palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate.”—Yohane 6:44, 65.
8, 9. (a) N’chifukwa chiyani tonsefe tifunika kupita kwa Yesu? (b) Kodi chochititsa chidwi kwambiri n’chiyani pa makonzedwe a dipo?
8 Anthu onse afunika kupita kwa Yesu ndi kukhulupirira nsembe yake ya dipo chifukwa iwo anabadwa ali ochimwa, osiyanitsidwa ndi Mulungu. (Yohane 3:36) Afunika kuyanjanitsidwa ndi Mulungu. (2 Akorinto 5:20) Mulungu sanayembekezere kuti anthu ochimwa am’pemphe kuti apereke makonzedwe oti akhale pa mtendere ndi iye. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife. Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.”—Aroma 5:8, 10.
9 Mtumwi Yohane anatsimikizira choonadi chapamwamba chakuti Mulungu akudziyanjanitsa ndi anthu. Analemba kuti: “Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, alowe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye. Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.” (1 Yohane 4:9, 10) Anayamba ndi Mulungu osati anthu. Kodi sizikukulimbikitsani kuyandikira kwa Mulungu amene anasonyeza chikondi chachikulu choterechi kwa ife amene tinali “ochimwa” komanso “adani”?—Yohane 3:16.
Tifunika Kufunafuna Yehova
10, 11. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tifunefune Yehova? (b) Kodi dongosolo la zinthu la Satana tiyenera kuliona bwanji?
10 Monga tikudziŵa, Yehova satiumiriza kuti tiyandikire kwa iye. Tiyenera kumufunafuna, ‘kumufufuza ndi kum’peza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife.’ (Machitidwe 17:27) Tiyenera kuzindikira kuti Yehova ali ndi ufulu wotilamula kuti timugonjere. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Mverani Mulungu; koma kanizani mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu. Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m’manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iŵiri inu.” (Yakobo 4:7, 8) Tisazengereze kum’tsutsa zolimba Mdyerekezi ndi kukhala kumbali ya Yehova.
11 Zimenezi zimafuna kuti tidzipatule ku dongosolo loipa la Satana. Yakobo analembanso kuti: “Kodi simudziŵa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4) N’chimodzimodzinso kuti ngati tikufuna kukhala mabwenzi a Yehova, tiyenera kuyembekezera kuti dziko la Satana lidzadana nafe.—Yohane 15:19; 1 Yohane 3:13.
12. (a) Kodi Davide analemba mawu olimbikitsa otani? (b) Kodi ndi chenjezo lotani limene Yehova anapereka kudzera mwa mneneri Azariya?
12 Dziko la Satana likatitsutsa m’njira inayake, tifunika kwambiri kupemphera kwa Yehova, kum’pempha kuti atithandize. Davide amene anapulumutsidwa ndi Yehova nthaŵi zambiri, analemba mawu otilimbikitsa, akuti: “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m’choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kupfuula kwao, nadzawapulumutsa. Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawawononga.” (Salmo 145:18-20) Salmo limeneli likusonyeza kuti Yehova angatipulumutse pamene tikuyesedwa patokha ndiponso kuti adzapulumutsa anthu ake onse pamodzi panthaŵi ya “chisautso chachikulu.” (Chivumbulutso 7:14) Yehova adzatiyandikira kwambiri ngati ife tiyandikira kwambiri kwa iye. Motsogozedwa ndi “mzimu wa Mulungu,” mneneri Azariya ananena mawu amene tinganene kuti ndi mfundo yogwira ntchito m’mbali zambiri, akuti: “Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukam’funa Iye, mudzam’peza; koma mukam’siya adzakusiyani.”—2 Mbiri 15:1, 2.
Yehova Ayenera Kukhala Weniweni kwa Ife
13. Kodi tingasonyeze bwanji kuti Yehova ndi weniweni kwa ife?
13 Mtumwi Paulo analemba za Mose kuti “anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:27) Kunena zoona, Mose sanamuone Yehova maso ndi maso. (Eksodo 33:20) Koma Yehova anali weniwenidi kwa iye moti anali ngati akumuona. Mofananamo, mayesero a Yobu atatha, iye anamuona Yehova bwinobwino ndi maso ake achikhulupiriro. Anamuona monga Mulungu amene amalola atumiki ake okhulupirika kukumana ndi ziyeso koma yemwe sawasiya. (Yobu 42:5) Enoke ndi Nowa anawanena kuti ‘anayenda ndi Mulungu.’ Anachita zimenezi mwa kuyesetsa kukondweretsa Mulungu ndi kumumvera. (Genesis 5:22-24; 6:9, 22; Ahebri 11:5, 7) Ngati Yehova ndi weniweni kwa ife monga mmene analili kwa Enoke, Nowa, Yobu, ndi Mose, ‘tidzamulemekeza’ m’njira zathu zonse, ndipo iye “adzawongola mayendedwe [athu].”—Miyambo 3:5, 6.
14. Kodi “kum’mamatira” Yehova kumatanthauza chiyani?
14 Aisrayeli atatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawalangiza kuti: “Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mawu ake, ndi kumtumikira iye, ndi kummamatira.” (Deuteronomo 13:4) Anafunika kutsata Yehova, kumuopa, kumumvera, ndi kum’mamatira. Ponenapo za liwu limene pano analitembenuza kuti “kum’mamatira,” munthu wina wa maphunziro apamwamba a Baibulo ananena kuti “liwulo likusonyeza ubwenzi weniweni ndiponso wapamtima.” Wamasalmo ananena kuti: “Ubwenzi ndi Yehova ngwa iwo akuopa iye.” (Salmo 25:14, NW) Tidzakhala pa ubwenzi wapadera ndi wapamtima ngati umenewu ndi Yehova ngati iye ndi weniweni kwa ife ndiponso ngati timamukonda kwambiri moti timaopa kusamukondweretsa mwa njira iliyonse.—Salmo 19:9-14.
Kodi Mumadziŵa Kuti Yehova Amakusamalirani?
15, 16. (a) Kodi Salmo 34 limasonyeza bwanji kuti Yehova amatisamalira? (b) Kodi tiyenera kutani ngati tikulephera kukumbukira zinthu zabwino zimene Yehova watichitira?
15 Machenjera ena amene Satana amagwiritsa ntchito ndiwo kutiiŵalitsa mfundo yakuti Mulungu wathu, Yehova, amasamalira nthaŵi zonse atumiki ake okhulupirika. Mfumu Davide ya Israyeli inazindikira kuti Yehova amateteza ngakhale pamene inakumana ndi zinthu zoopsa kwambiri. Pamene inakakamizika kunamizira kuti inali yamisala pamaso pa Mfumu Akisi ya ku Gati, iyo inalemba nyimbo, salmo labwino kwambiri, imene ili ndi mawu osonyeza chikhulupiriro akuti: “Bukitsani pamodzi ndine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi. Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m’mantha anga onse. Mngelo wa Yehova azinga kuwachinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo. Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino; wodala munthuyo wakukhulupirira Iye. Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi. Masautso a wolungama mtima achuluka: koma Yehova am’landitsa mwa onseŵa.”—Salmo 34:3, 4, 7, 8, 18, 19; 1 Samueli 21:10-15.
16 Kodi mukukhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu yopulumutsa? Kodi mukuzindikira kuti amateteza pogwiritsa ntchito angelo ake? Kodi inu panokha mwalaŵa ndi kuona kuti Yehova ndi wabwino? Kodi ndi nthaŵi iti posachedwapa pamene munaona kuti Yehova anakhaladi wabwino kwa inu? Tayesani kukumbukira. Kodi panali panyumba yomaliza imene munafikapo muli muutumiki, panthaŵi imene munaganiza kuti simukanatha kupitiriza? Mwina pamenepo munakambirana bwino ndi mwininyumba. Kodi munakumbukira kuthokoza Yehova chifukwa chokupatsani mphamvu zina zimene munafunikira ndiponso pokudalitsani? (2 Akorinto 4:7) Mwina mukulephera kukumbukira chinachake chabwino chimene Yehova anakuchitirani. Mwina mungafunike kuganiza zimene zinachitika mlungu watha, mwezi watha, chaka chatha, kapena zaka zapitazo. Ngati ndi choncho, bwanji osachita khama kuyandikira kwa Yehova ndi kuona mmene akukutsogolererani? Mtumwi Petro analangiza Akristu kuti: “Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu . . . ndi kutaya pa Iye nkhaŵa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.” (1 Petro 5:6, 7) Inde, mudzadabwa kuona mmene amakusamalirani!—Salmo 73:28.
Pitirizani Kufunafuna Yehova
17. Kodi n’chiyani chikufunika kuti tipitirize kufunafuna Yehova?
17 Tiyenera kupitiriza kukhalabe paubwenzi ndi Yehova. Yesu ananena m’pemphero kwa Atate wake kuti: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Kudziŵa za Yehova ndi Mwana wake kumafuna kuchita khama nthaŵi zonse. Timafunikira pemphero ndi mzimu woyera kuti zitithandize kumvetsa “zakuya za Mulungu.” (1 Akorinto 2:10; Luka 11:13) Timafunikanso kutsogoleredwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti adyetse maganizo athu ndi chakudya chauzimu chimene amapereka “panthaŵi yake.” (Mateyu 24:45) Kudzera m’njira imeneyi, Yehova watilangiza kuŵerenga Mawu ake tsiku ndi tsiku, kupezeka pamisonkhano yathu yachikristu nthaŵi zonse ndi kulalikira nawo ndi mtima wonse ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Mateyu 24:14) Ngati tichita zimenezi, tidzapitiriza kufunafuna Mulungu wathu, Yehova, amene amatisamalira.
18, 19. (a) Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani? (b) Ngati titsimikiza mtima kutsutsa Mdyerekezi ndi kupitiriza kufunafuna Yehova, kodi adzatidalitsa bwanji?
18 Satana akuchita zonse zimene angathe kuti azunze, atsutse, ndi kuvutitsa m’njira zosiyanasiyana anthu a Yehova. Amayesetsa kusokoneza mtendere wathu ndi kuwononga ubwenzi wathu wabwino ndi Mulungu. Safuna kuti tipitirize ntchito yathu yopeza anthu oona mtima ndi kuwathandiza kuti akhale kumbali ya Yehova pankhani ya ulamuliro wachilengedwe chonse. Koma tiyenera kutsimikiza mtima kukhulupirikabe kwa Yehova, kumukhulupirira kuti adzatipulumutsa kwa woipayo. Ngati tilola kuti Mawu a Mulungu atitsogolere ndi kukhalabe achangu pamodzi ndi gulu lake looneka, tingatsimikize kuti iye adzakhala wokonzeka kutithandiza nthaŵi zonse.—Yesaya 41:8-13.
19 Ndiyetu tiyeni tonse titsimikize mtima kukaniza Mdyerekezi ndi machenjera ake, nthaŵi zonse tizifunafuna Mulungu wathu wokondeka, Yehova, amene sadzalephera ‘kutikhazikitsa, kutilimbitsa.’ (1 Petro 5:8-11) Motero, ‘tidzadzisunga tokha m’chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Kristu, kufikira moyo wosatha.’—Yuda 21.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi liwu lachigiriki la “Mdyerekezi” limatanthauza chiyani, ndipo zochita za Mdyerekezi zimagwirizana bwanji ndi tanthauzo limenelo?
• Kodi Yehova amasiyana bwanji ndi Mdyerekezi pankhani ya mmene Iye amaonera anthu padziko lapansi?
• N’chifukwa chiyani munthu afunika kukhulupirira dipo polankhula kwa Yehova?
• Kodi “kum’mamatira” Yehova kumatanthauza chiyani, ndipo tingatani kuti tipitirizebe kum’funafuna?
[Chithunzi patsamba 15]
Ngakhale kuti Yobu anayesedwa, iye anazindikira kuti Yehova anali kumusamalira
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, kupezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse ndi kugwira nawo mwachangu ntchito yolalikira kumatikumbutsa kuti Yehova amatisamalira