Banja la Yehova Lili ndi Umodzi Wamtengo Wapatali
“Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi [mu umodzi, NW]!”—SALMO 133:1.
1. Kodi mkhalidwe wa mabanja ambiri lerolino ngwotani?
LERO banja lili pamavuto. M’mabanja ambiri, zomangira zaukwati zili pafupi kuduka. Chisudzulo chikuchitika kwambiri, ndipo ana ambiri a anthu osudzulana ali ndi chisoni chachikulu. Mabanja miyandamiyanda ali osakondwa ndi osagwirizana. Komabe, pali banja limodzi limene lili ndi chimwemwe ndi umodzi weniweni. Ndilo banja la m’chilengedwe chonse la Yehova Mulungu. M’banjalo, angelo miyandamiyanda amachita ntchito zawo mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Salmo 103:20, 21) Koma kodi padziko lapansi pali banja limene lili ndi umodzi umenewo?
2, 3. (a) Kodi ndani amene ali mbali ya banja la Mulungu lapadziko lonse tsopano lino, ndipo Mboni za Yehova zonse tingazifanizire ndi chiyani lerolino? (b) Kodi ndi mafunso otani amene tidzakambitsirana?
2 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndipinda mawondo anga kwa Atate, amene kuchokera kwa iye [banja NW] lonse la m’mwamba ndi la padziko alitcha dzina.” (Aefeso 3:14, 15) Mzera uliwonse wa banja padziko lapansi unapatsidwa dzina ndi Mulungu chifukwa chakuti iyeyo ndiye Mlengi. Ngakhale kuti kumwamba kulibe mabanja aumunthu, mophiphiritsira Mulungu ali wokwatirana ndi gulu lake lakumwamba, ndipo Yesu adzakhala ndi mkwatibwi wauzimu wogwirizana naye kumwamba. (Yesaya 54:5; Luka 20:34, 35; 1 Akorinto 15:50; 2 Akorinto 11:2) Odzozedwa okhulupirika amene ali padziko lapansi tsopano ali mbali ya banja la m’chilengedwe chonse la Mulungu, ndipo “nkhosa zina” za Yesu, zokhala ndi ziyembekezo za padziko lapansi, zili anthu oyembekezeredwa ake. (Yohane 10:16; Aroma 8:14-17; Nsanja ya Olonda, January 15, 1996, tsamba 31) Komabe, Mboni za Yehova zonse lerolino zingafanizidwe ndi banja lapadziko lonse logwirizana.
3 Kodi inu muli mbali ya banja labwino kwambiri lapadziko lonseli la atumiki a Mulungu? Ngati zili choncho, muli ndi limodzi la madalitso aakulu koposa amene munthu angakhale nawo. Ambiri angachitire umboni wakuti banja lapadziko lonse la Yehova—gulu lake looneka—lili malo achonde a mtendere ndi umodzi m’chipululu cha dziko cha nkhondo ndi kusagwirizana. Kodi umodzi wa banja lapadziko lonse la Yehova ungafotokozedwe motani? Ndipo ndi zinthu zotani zimene zimachirikiza umodzi umenewo?
Nkokoma ndi Kokondweretsa Ndithu!
4. Kodi mungafotokoze motani m’mawu anuanu zimene Salmo 133 limanena ponena za umodzi waubale?
4 Wamasalmo Davide anayamikira kwambiri umodzi waubale. Anauziridwadi kuuimba! Muoneni m’maganizo ali ndi zeze wake pamene akuimba kuti: “Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi [mu umodzi, NW]! Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira ku ndevu, inde ku ndevu za Aroni; akutsikira ku mkawo wa zovala zake; ngati mame a ku Hermoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni: Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.”—Salmo 133:1-3.
5. Pamaziko a Salmo 133:1, 2, kodi nkuyerekezera kotani kumene tingachite pakati pa Aisrayeli ndi atumiki a Mulungu amakono?
5 Mawu amenewo anali kunena za umodzi wa ubale umene anthu akale a Mulungu, Aisrayeli, anali nawo. Pamene anali mu Yerusalemu kaamba ka mapwando awo atatu apachaka, anali kukhala pamodzi mu umodzi. Ngakhale kuti anali kuchokera m’mafuko osiyanasiyana, iwowo anali banja limodzi. Kukhalira pamodzi kunali ndi chisonkhezero chabwino pa iwo, monga ngati mafuta odzozera otsitsimula a fungo lokoma. Pamene mafuta amenewo anatsanuliridwa pamutu wa Aroni, anatsikira m’ndevu zake natsikira mu mkawo wa zovala zake. Kwa Aisrayeli, kukhalira pamodzi kunali ndi chiyambukiro chabwino chimene chinawanda mwa anthu onse osonkhanawo. Kusamvana kunathetsedwa, ndipo umodzi unachirikizidwa. Umodzi wofananawo uli pakati pa banja la Yehova lapadziko lonse lerolino. Kuyanjana nthaŵi zonse kumakhala ndi chisonkhezero chabwino chauzimu pa anthu ake. Kusamvana kulikonse kapena zovuta zilizonse zimachotsedwa pamene uphungu wa Mawu a Mulungu ugwiritsiridwa ntchito. (Mateyu 5:23, 24; 18:15-17) Anthu a Yehova amayamikira kwambiri chilimbikitso chachikondi chimene chimakhalapo chifukwa cha umodzi waubale wawo.
6, 7. Kodi umodzi wa Israyeli unafanana motani ndi mame a phiri la Hermoni, ndipo nkuti kumene dalitso la Mulungu lingapezeke lerolino?
6 Kodi Israyeli anakhalanso pamodzi mu umodzi motani monga mame a phiri la Hermoni? Aha, popeza kuti nsonga ya phiri limeneli njokwezeka kuposa mamita 2,800 kuchokera pamwamba panyanja, njokutidwa ndi chipale pafupifupi chaka chonse. Nsonga ya chipale ya Hermoni imachititsa nkhungu usiku ndipo motero zimenezo zimadzetsa mame ambiri amene amakulitsa zomera mkati mwa nyengo yaitali yopanda madzi. Mphepo yozizira yochokera m’phiri la Hermoni imatenga nkhunguyo kumka nayo kutali chakummwera monga kudera la Yerusalemu, kumene imakakhala mame. Chotero wamasalmo ananena molondola za “mame a ku Hermoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni.” Ha, ndi chikumbutso chabwino kwambiri chotani nanga cha chisonkhezero chotsitsimula chimene chimachirikiza umodzi wa banja la Yehova la olambira!
7 Mpingo wachikristu usanakhazikitsidwe, Ziyoni, kapena Yerusalemu, anali phata la kulambira koona. Chifukwa chake, Mulungu analamula kuti dalitso lidzakhala kumeneko. Popeza kuti Magwero a madalitso onse anaimiriridwa kukhala ali m’chihema mu Yerusalemu, madalitsowo anali kudzachokera mmenemo. Komabe, chifukwa chakuti kulambira koona sikuli kozikikanso pa malo ena akutiakuti, dalitso, chikondi, ndi umodzi wa atumiki a Mulungu zingapezeke padziko lonse lapansi lerolino. (Yohane 13:34, 35) Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zimachirikiza umodzi umenewu?
Zinthu Zimene Zimachirikiza Umodzi
8. Kodi timaphunziranji ponena za umodzi pa Yohane 17:20, 21?
8 Umodzi wa olambira a Yehova wazikidwa pa kuchita mogwirizana ndi Mawu a Mulungu omvedwa molondola, kuphatikizapo ziphunzitso za Yesu Kristu. Njira yopangira mpingo wogwirizana wachikristu inatsegulidwa mwa kutumiza kwa Yehova Mwana wake kudziko kudzachitira umboni choonadi ndi kudzafa imfa ya nsembe. (Yohane 3:16; 18:37) Kunena kuti padzakhala umodzi weniweni pakati pa anthu ake kunasonyezedwa bwino pamene Yesu anapemphera kuti: “Sindipempherera iwo okha, komanso iwo akukhulupirira ine chifukwa cha mawu awo; kuti onse akakhale amodzi, monga inu Atate mwa ine, ndi ine mwa inu, kuti iwonso akakhale mwa ife: kuti dziko lapansi likakhulupire kuti inu munandituma ine.” (Yohane 17:20, 21) Otsatira a Yesu anapeza umodzi wofanana ndi umene unali pakati pa Mulungu ndi Mwana wake. Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti anachita mogwirizana ndi Mawu a Mulungu ndi ziphunzitso za Yesu. Mkhalidwe umodzimodziwo ndiwo chochititsa chachikulu cha umodzi wa banja la Yehova lapadziko lonse lerolino.
9. Kodi mzimu woyera umachita mbali yotani mu umodzi wa anthu a Yehova?
9 Chinthu chinanso chimene chimagwirizanitsa anthu a Yehova nchakuti tili ndi mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito. Umatikhozetsa kumvetsa choonadi chovumbulidwa cha Mawu a Yehova ndipo motero kumtumikira mogwirizana. (Yohane 16:12, 13) Mzimuwo umatithandiza kupeŵa ntchito zathupi zonga ndewu, kaduka, kupsa mtima, ndi kukangana. M’malo mwake, mzimu wa Mulungu umatitheketsa kukhala ndi zipatso zochititsa umodzi za chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, chifatso, ndi kudziletsa.—Agalatiya 5:19-23.
10. (a) Kodi nkufanana kotani kumene kungapangidwe pakati pa chikondi chimene chili m’banja laumunthu logwirizana ndi chikondi chimene chimaoneka pakati pa awo odzipereka kwa Yehova? (b) Kodi chiŵalo china cha Bungwe Lolamulira chinafotokoza motani malingaliro ake ponena za kusonkhana ndi abale ake auzimu?
10 A m’banja logwirizana amakondana ndipo ngachimwemwe kukhalira pamodzi. Mofananamo, awo okhala m’banja logwirizana la olambira Yehova amakonda iye, Mwana wake, ndi okhulupirira anzawo. (Marko 12:30; Yohane 21:15-17; 1 Yohane 4:21) Monga momwe banja lachibadwa limasangalalira kudyera chakudya pamodzi, awo amene ali odzipereka kwa Mulungu amasangalala kukhala pa misonkhano ya mpingo yachikristu, misokhano yadera, ndi misonkhano yachigawo kuti apindule ndi mayanjano abwino ndi chakudya chauzimu chabwino kwambiri. (Mateyu 24:45-47; Ahebri 10:24, 25) Chiŵalo china cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova panthaŵi ina chinanena motere: “Kwa ine, kusonkhana ndi abale ndiko chinthu china cha zokondweretsa zazikulu koposa m’moyo ndi magwero a chilimbikitso. Ndimakonda kukhala pakati pa oyamba kufika pa Nyumba ya Ufumu, ndi kukhala pakati pa omaliza kuchoka, ngati kuli kotheka. Ndimakhala ndi chimwemwe mumtima pamene ndikulankhulana ndi anthu a Mulungu. Pamene ndili pakati pawo ndimakhala womasuka kukhala pakati pa banja langali.” Kodi umu ndimo mmene mumamvera?—Salmo 27:4.
11. Kodi Mboni za Yehova zimapeza chimwemwe makamaka mu ntchito yotani, ndipo kodi nchiyani chimene chimachitika chifukwa cha kupanga utumiki wa Mulungu kukhala chinthu chachikulu m’moyo wathu?
11 Banja logwirizana limapeza chimwemwe mwa kuchitira zinthu pamodzi. Mofananamo, awo amene ali m’banja la olambira Yehova amapeza chimwemwe mwa kuchita mogwirizana ntchito yawo ya kulalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kukhala ndi phande mu ntchitoyo kumatikokera pamodzi ndi Mboni zina za Yehova. Kupanga utumiki wa Mulungu kukhala chinthu chachikulu m’moyo wathu ndi kuchirikiza ntchito zonse za anthu ake kumapititsanso patsogolo mzimu wa banja pakati pathu.
Dongosolo la Teokrase Nlofunika
12. Kodi mikhalidwe ya banja lachimwemwe ndi logwirizana njotani, ndipo ndi makonzedwe otani amene anachirikiza umodzi m’mipingo yachikristu ya m’zaka za zana loyamba?
12 Banja limene lili ndi utsogoleri wamphamvu komanso wachikondi ndi limene lili ladongosolo ndiye kuti limakhala logwirizana ndi lachimwemwe. (Aefeso 5:22, 33; Aefeso 6:1) Yehova ndi Mulungu wa dongosolo lamtendere, ndipo awo onse okhala m’banja lake amamuona kukhala “Wam’mwambamwamba.” (Danieli 7:18, 22, 25, 27; 1 Akorinto 14:33) Amazindikiranso kuti iye wasankha Mwana wake, Yesu Kristu, woloŵa malo wa zinthu zonse ndipo wampatsa ulamuliro wonse kumwamba ndi padziko lapansi. (Mateyu 28:18; Ahebri 1:1, 2) Pokhala ndi Kristu monga Mutu, mpingo wachikristu uli gulu ladongosolo, ndi logwirizana. (Aefeso 5:23) Kuti ayang’anire mipingo ya m’zaka za zana loyamba, anapanga bungwe lolamulira la atumwi ndi “akulu” ena aakulu msinkhu mwauzimu. Mpingo uliwonse unali ndi oyang’anira oikidwa, kapena kuti akulu, ndi atumiki otumikira. (Machitidwe 15:6; Afilipi 1:1) Kumvera awo amene anali kutsogolera kunachirikiza umodzi.—Ahebri 13:17.
13. Kodi Yehova amakoka anthu motani, ndipo nchiyani chimachitika pa zimenezi?
13 Koma kodi dongosolo lonseli limapereka lingaliro lakuti umodzi wa olambira Yehova ngwochititsidwa ndi utsogoleri wina wamphamvu ndi wouma mtima? Ndithudi ayi! Palibe mkhalidwe uliwonse wa kuuma mtima kwa Mulungu kapena gulu lake. Yehova amakoka anthu mwa kusonyeza chikondi, ndipo chaka chilichonse zikwi mazana ambiri amakhala mbali ya gulu la Yehova mwaufulu ndiponso mwachimwemwe mwa kubatizidwa posonyeza kudzipatulira kwawo ndi mtima wonse kwa Mulungu. Mzimu wawo uli ngati uja wa Yoswa, amene anafulumiza Aisrayeli anzake kuti: “Mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, . . . koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.”—Yoswa 24:15.
14. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti gulu la Yehova nlateokrase?
14 Monga mbali ya banja la Yehova, ife sitili kokha achimwemwe komanso tili otetezereka. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti gulu lake nlateokrase. Ufumu wa Mulungu uli wateokrase (kuchokera ku the·osʹ wachigiriki, mulungu, ndi kraʹtos, ulamuliro). Ndiwo ulamuliro wochitidwa ndi Mulungu, woikidwa ndi kukhazikitsidwa ndi iye. “Mtundu woyera” wodzozedwa wa Yehova umagonjera ulamuliro wake ndipo chifukwa cha chimenecho nawonso ngwateokrase. (1 Petro 2:9) Pokhala ndi Teokrati Wamkulu, Yehova, monga Woweruza wathu, Wotipatsa Malamulo, ndi Mfumu yathu, tili ndi chifukwa chabwino chokhalira otetezereka. (Yesaya 33:22) Komabe, bwanji ngati pabuka mkangano wina umene ungafune kusokoneza chimwemwe chathu, chisungiko, ndi umodzi?
Bungwe Lolamulira Lichitapo Kanthu
15, 16. Kodi ndi mkangano wotani umene unabuka m’zaka za zana loyamba, ndipo chifukwa ninji?
15 Panthaŵi ndi nthaŵi mikangano imathetsedwa kuti umodzi wa banja usungidwe. Pamenepa, tinene kuti vuto lina lauzimu limene linabuka linafunikira kuthetsedwa kusungitsa umodzi wa banja la olambira Mulungu m’zaka za zana loyamba C.E. Kodi nchiyani chinafunikira kuchitidwa? Bungwe lolamulira linachitapo kanthu, likumapanga zosankha pa nkhani zauzimu. Tili ndi mbiri ya Malemba yolembedwa ya mchitidwe umenewo.
16 Cha ku ma 49 C.E., bungwe lolamulira linasonkhana mu Yerusalemu kudzathetsa vuto lina lalikulu ndipo mwa kutero kusungitsa umodzi wa “banja la Mulungu.” (Aefeso 2:19) Patapita zaka ngati 13 poyambirira pake, mtumwi Petro anali atalalikira kwa Korneliyo, ndipo Akunja oyamba, kapena anthu amitundu, anakhala okhulupirira obatizidwa. (Machitidwe, chaputala 10) Mkati mwa ulendo waumishonale woyamba wa Paulo, Akunja ambiri analandira Chikristu. (Machitidwe 13:1–14:28) Kwenikweni, mpingo wa Akristu Akunja unali utakhazikitsidwa mu Antiokeya, wa Suriya. Akristu ena achiyuda analingalira kuti Akunja otembenukawo ayenera kudulidwa ndi kusunga Chilamulo cha Mose, koma ena anatsutsa. (Machitidwe 15:1-5) Kutsutsana kumeneku kukanachititsa kusagwirizana kwakukulu, ngakhale kupangitsa mipingo yolekana ya Ayuda ndi Akunja. Motero bungwe lolamulira linachitapo kanthu mwamsanga kuti lisungitse umodzi wachikristu.
17. Kodi ndi njira yogwirizana yateokrase yotani imene ikufotokozedwa m’Machitidwe chaputala 15?
17 Malinga ndi kunena kwa Machitidwe 15:6-22, “anasonkhana atumwi ndi akulu kuti anene za mlanduwo.” Ndipo panalinso ena kuphatikizapo nthumwi za ku Antiokeya. Choyamba Petro anafotokoza kuti ‘kupyolera m’kamwa mwake amitundu anamva mawu a uthenga wabwino, nakhulupira.’ Ndiyeno “khamu lonse” linamvetsera pamene Barnaba ndi Paulo anasimba “zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anachita nawo pa amitundu,” kapena Akunja. Kenako Yakobo anapereka malingaliro a mmene nkhaniyo ingathetsedwere. Bungwe lolamulira litapanga chosankha, timauzidwa kuti: “Chinakomera atumwi ndi akulu ndi Eklesia yense kusankha anthu a m’gulu lawo, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnaba.” ‘Anthu osankhidwa’ amenewo—Yudase ndi Sila—anatengera kalata yolimbikitsa kwa okhulupirira anzawo.
18. Kodi bungwe lolamulira linapanga chosankha chotani choloŵetsamo Chilamulo cha Mose, ndipo zimenezi zinayambukira motani Akristu achiyuda ndi Akunja?
18 Kalata imeneyo imene inalengeza chosankha cha bungwe lolamulira inayamba ndi mawu akuti: “Atumwi ndi abale akulu kwa abale a mwa amitundu a m’Antiokeya, ndi Suriya, ndi Kilikiya, tikulankhulani!” Ena anafika pa msonkhano wa mumbiri umenewu, koma mwachionekere bungwe lolamuliralo linali lopangidwa ndi “atumwi ndi abale akulu.” Mzimu wa Mulungu unawatsogolera, pakuti kalatayo ikufotokoza kuti: ‘Chinakomera mzimu woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi; kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.’ (Machitidwe 15:23-29) Akristu sanafunikire kudulidwa ndi kusunga Chilamulo cha Mose. Chosankha chimenechi chinathandiza Akristu achiyuda ndi Akunja kuchita ndi kulankhula mu umodzi. Mipingo inakondwera, ndipo umodzi wamtengo wapataliwo unapitiriza, monga momwe zikuchitikira m’banja la Mulungu lapadziko lonseli lerolino pansi pa chitsogozo chauzimu cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.—Machitidwe 15:30-35.
Kutumikira mu Umodzi wa Teokrase
19. Kodi nchifukwa ninji umodzi wakula m’banja la olambira Yehova?
19 Umodzi umakula pamene a m’banja achita mogwirizana wina ndi mnzake. Zili chimodzimodzinso ndi banja la olambira Yehova. Pokhala ateokrase, akulu ndi ena mumpingo wa m’zaka za zana loyamba anatumikira Mulungu mogwirizana kotheratu ndi bungwe lolamulira ndi kulandira zosankha zake. Ndi thandizo la bungwe lolamulira, akulu ‘analalikira mawu’ ndipo a mumpingo onse ‘ananena chimodzimodzi.’ (2 Timoteo 4:1, 2; 1 Akorinto 1:10) Chotero choonadi chimodzimodzicho cha Malemba chinaperekedwa mu utumiki ndi pamisonkhano yachikristu, kaya munali mu Yerusalemu, Antiokeya, Roma, Korinto, kapena kwina kulikonse. Umodzi wateokrase wotero ulipo lerolino.
20. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tisunge umodzi wathu wachikristu?
20 Kuti tisunge umodzi wathu, tonsefe amene tili mbali ya banja la Yehova lapadziko lonse tiyenera kuyesayesa kusonyeza chikondi chateokrase. (1 Yohane 4:16) Tifunikira kugonjera chifuniro cha Mulungu ndi kusonyeza ulemu waukulu kwa “kapolo wokhulupirika” ndi Bungwe Lolamulira. Monga momwe kudzipatulira kwathu kwa Mulungu kulili, ndimo mmenenso kulili kumvera kwathu, kwaufulu ndi kwachimwemwe. (1 Yohane 5:3) Mmene wamasalmo anagwirizanitsira bwino nanga chimwemwe ndi kumvera! Iye anaimba kuti: “Haleluya. [Wachimwemwe, NW] munthu wakuwopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.”—Salmo 112:1.
21. Kodi tingadzisonyeze motani kuti ndife ateokrase?
21 Yesu, Mutu wa mpingo, ngwateokrase kotheratu ndipo nthaŵi zonse amachita chifuniro cha Atate wake. (Yohane 5:30) Chotero, tiyeni titsatire Wotipatsa Chitsanzo wathu mwa kuchita chifuniro cha Yehova mwateokrase ndi mu umodzi mogwirizana kotheratu ndi gulu Lake. Pamenepo ndi chimwemwe chachikulu ndi kuthokoza, nafenso tingavomerezane ndi nyimbo ya wamasalmo kuti: “Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi [mu umodzi, NW]!”
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi umodzi wathu wachikristu ungagwirizanitsidwe motani ndi Salmo 133?
◻ Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zimachirikiza umodzi?
◻ Kodi nchifukwa ninji dongosolo lateokrase lili lofunika pa umodzi wa anthu a Mulungu?
◻ Kodi bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba linachitapo kanthu motani posungitsa umodzi?
◻ Kodi kutumikira mu umodzi wateokrase kumatanthauzanji kwa inu?
[Chithunzi patsamba 13]
Bungwe lolamulira linachitapo kanthu kusungitsa umodzi