Chaputala 15
Edomu Wamakono Wophiphiritsiridwa, Adzachotsedwa
1, 2. Kodi ndimotani mmene Mlengi amawonera mitundu yonyamula zida zankhondo zowopsa, ndipo kodi nchiyani chimene chiri chitsimikizo cha Yehova, mogwirizana ndi kunena kwa ulosi wa Yesaya?
LEROLINO dziko liri ndi zida zankhondo zamphamvu kuposa nthaŵi ina iriyonse kalero. Zida zankhondo zanyukliya za amitundu ziridi chiwopsezo kukukhalako kwenikweniko kwa anthu. Pamenepa, kodi ndimotani, mmene Mlengi wa banja laumunthu, Yehova Mulungu, amawonera mkhalidwewo? Zimenezi zalongosoledwa momvekera bwino m’chaputala 34 cha ulosi wa Yesaya, umene umayamba mwa mawu aŵa:
2 “Idzani pafupi, amitundu inu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko limve, ndi za mommo; dziko ndi zinthu zonse zotulukamo. Pakuti Yehova akwiyira amitundu onse, nachitira ukali khamu lawo lonse; iye wawawononga psiti, wawapereka kukaphedwa. Ophedwa awonso adzatayidwa kunja, ndipo kununkha kwa mitembo yawo kudzamveka, ndipo mapiri adzasungunuka ndi mwazi wawo. Ndipo makamu onse akumwamba adzasungunuka, ndi miyamba [maboma aumunthu olepherawo] idzapindika pamodzi ngati mpukutu; makamu awo onse adzafota monga tsamba limafota pampesa ndi kugwa, ndi monga tsamba lifota pamkuyu.” (Yesaya 34:1-4) Ha ndiulosi wochititsadi nthumanzi chotani nanga!
3. (a) Kodi mitundu ikuitanidwa kumvetsera chiyani, ndipo motero nchifukwa ninji Yehova moyenerera angawalamule? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti mitundu sinamvetsere?
3 Mlengi wa chilengedwe chonse ali ndi mlandu ndi mitundu lerolino. Ndicho chifukwa chake mitundu ikuitanidwa kuti idzamvetsere uthenga wochokera m’Baibulo umene wauchititsa kulengezedwa padziko lonse lapansi chiyambire 1919. Iwo ayenera kumvetsera zimene iye akunena kupyolera mwa Mboni zake. Koma mkhalidwe wa zochitika za dziko ukutsimikizira kuti iwo sanatero, ndipo Mboni zake sizinawonedwe mwamphamvu ndi mitundu, imene inasankha Mitundu Yogwirizana ndipo osati Ufumu wakumwamba kupyolera mwa Mwana wake woikidwa pa mpando wachifumu, “Kalonga wa Mtendere.”
Ulosi wa Yesaya Wotsutsa Edomu
4, 5. (a) Kodi Aedomu anali ayani, ndipo ndimkhalidwe wotani umene anali nawo kulinga kwa mtundu wa mbale wawo wamapasa, Israyeli? (b) Chifukwa chake kodi nchiyani chimene Yehova analengeza ponena za Edomu?
4 Pakati pa timagulu ta amitundu lerolino pali kagulu kena kokhala ndi liwongo lapadera. Kagulu kameneko kanaphiphiritsiridwa ndi Mtundu wa Edomu, umene watchulidwa mwachindunji mu ulosi umenewu. Aedomu anali mbadwa za Esau, amene anagulitsa kuyenera kwake kwa kukhala woyamba kubadwa kwa mbale wake wamapasa, Yakobo, ndi “mphodza.” Panali pa chochitika chimenecho pamene Esau anadzatchedwa Edomu, kutanthauza “Chofiira.” (Genesis 25:24-34) Chifukwa chakuti Yakobo anamtengera kuyenera kwake kwa kukhala woyamba kubadwa kofunikako, Esau anadzazidwa ndi mkwiyo kulinga kwa mbale wake wamapasa. Edomu anafikira kukhala mdani wankhalwe wa mtundu wa Israyeli wakale, kapena Yakobo, ngakhale kuli kwakuti iwo anali mitundu yochokera kwa abale a mapasa. Chifukwa cha chidani chimenechi chotsutsana ndi anthu a Mulungu, Edomu anadzibweretsera mkwiyo woyenerera wa Yehova, Mulungu wa Israyeli, ndipo Iye analengeza chiwonongeko chosatha cha Edomu. Chitsimikizo chaumulungu chimenechi chanenedwa m’mawu a mneneri Yesaya:
5 “Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; tawonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe. Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa ana a nkhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a impso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe m’Bozira [mzinda wotchuka koposa wa Edomu], ndi ophedwa ambiri m’dziko la Edomu.”—Yesaya 34:5, 6.
6. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova akalankhula za kugwedeza “lupanga” lake motsutsana ndi Edomu “m’miyamba”? (b) Pamene ufumu wa Yuda unaukiridwa ndi Babulo, kodi ndimkhalidwe wankhalwe wotani umene Aedomu anasonyeza kulinga kwa anthu a Yehova?
6 Dziko la mtundu wochita mbanda la Edomu liyenera kukhathamira ndi mwazi wa iwo eni kupyolera mwa “lupanga” la Yehova. Edomu anali pachigawo chapamwamba, chamapiri. (Yeremiya 49:16) Chotero pochititsa kuphedwa m’dziko limenelo, Yehova akadanena mophiphiritsira kuti anali kugwedeza lupanga lake lachiweruzo “m’miyamba.” Edomu anali wamphamvu m’zankhondo, ndipo magulu ake ankhondo onyamula zida anali kuyenda piringupiringu m’mapiri okwezeka kwambiri kutetezera dzikolo kwa oukira. Chotero gulu lankhondo la Edomu likanatchedwa moyenerera kuti ‘gulu lankhondo lakumiyamba.’ Koma Edomu wamphamvuyo sanapereke chithandizo kumtundu wochokera kwa mbale wake wamapasa, Israyeli, pamene unaukiridwa ndi magulu ankhondo a Babulo. Mmalo mwake, Edomu anasangalala kuwona kugubuduzidwa kwa ufumu wa Yuda ndipo anasonkhezeradi oukira ake. (Salmo 137:7) Chiŵembu cha Edomu chinafikira pamfundo ya kusaka anthu alionse pa okha othaŵitsa miyoyo yawo ndi kuwabwezera kwa mdani. (Obadiya 10-14) Aedomu anachita makonzedwe a kutenga dziko losiyidwa la Aisrayeli, akumalankhula monyang’wa motsutsana ndi Yehova.—Ezekieli 35:10-15.
7. Kodi ndimotani mmene Mulungu wa Israyeli anawonera khalidwe la chiŵembu la mtundu wa Edomu?
7 Kodi Yehova, Mulungu wa Israyeli wakale, ananyalanyaza khalidwe la udani limeneli lochitidwa ndi Aedomu kulinga kwa anthu ake osankhidwa? Ayi. Ndicho chifukwa chake mtima wa Mulungu unalinganiza “tsiku la kulipsira” ndi ‘chaka cha kubwezera’ kulipsira zimene zidachitidwa mwanjiru kugulu lake lapadziko lapansi, lotchedwa Ziyoni. Ulosiwo unati: “Pakuti liri tsiku la kubwezera la Yehova, chaka cha kubwezera chilango, mlandu [pamaso pa Bwalo la Chilengedwe chonse] wa Ziyoni.”—Yesaya 34:8; Ezekieli 25:12-14.
8. (a) Kodi ndani amene Yehova anaŵagwiritsira ntchito kubweretsa chilango pa Edomu? (b) Kodi nchiyani chimene mneneri Obadiya adaneneratu ponena za Edomu?
8 Mwamsanga pambuyo pa kuwonongedwa kwa Yerusalemu, Yehova anayamba kusonyeza chilipsiro chake cholungama pa Aedomu kupyolera mwa mfumu ya Babulo, Nebukadinezara. (Yeremiya 25:8, 15, 17, 21) Pamene magulu ankhondo a Babulo anaukira Edomu, palibe zimene zikanapulumutsa Aedomu! Magulu ankhondo a Ababulo anakhaulitsa Aedomu mmalo awo apamwambawo amathanthwe. Chinali “chaka cha kubwezera” pa Edomu. Monga momwe Yehova adaneneratu kupyolera mwa mneneri wina kuti: “Chifukwa cha chiwawa unamchitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzawonongeka kunthaŵi yonse. . . . Monga unachita iwe, momwemo adzakuchitira; chochita iwe chidzakubwerera pamutu pako.”—Obadiya 10, 15.
9. Kodi ndani amene ali Edomu wamakono wophiphiritsiridwa, ndipo chifukwa ninji?
9 Zimenezi zikusonyezanso mkhalidwe wa Yehova kulinga ku Edomu wamakono wophiphiritsiridwa. Kodi ameneyo ndani? Eya, m’zaka za zana la 20, kodi ndani amene watsogolera m’kulalatira ndi kuzunza atumiki a Yehova? Kodi silinali Dziko Lachikristu lampatuko kupyolera mwa kagulu kake konyada ka atsogoleri achipembedzo? Inde! Dziko Lachikristu, gawo la Chikristu chonyenga, ladzikweza ngati mapiri m’zochitika za dziko lino. Iro liri mbali yokwezeka ya gulu la dongosolo la zinthu la anthu, ndipo mpangidwe wa zipembedzo zake umapanga mbali yayikulu ya Babulo Wamkulu. Koma Yehova walengeza “chaka cha kubwezera” motsutsana ndi Edomu wophiphiritsiridwa, wamakono chifukwa cha kuchitira nkhalwe anthu ake, Mboni zake.
Mtsogolo Mofanana ndi mwa Edomu
10. Kodi ndimotani mmene Yesaya 34:9, 10 amalongosolera mtsogolo mwa Edomu, koma kodi ndikwayani kumene ulosiwo umagwirako ntchito lerolino?
10 Pamene tipenda mbali yotsatira ya ulosi umenewu wa Yesaya, tingathe kukumbukira Dziko Lachikristu lamakono: “Mitsinjeyo idzasanduka matope akuda, ndi fumbilo lidzasanduka sulfure, ndi dziko lakelo lidzasanduka matope oyaka moto. Sadzazimikai usiku, ngakhale usana; utsi wake udzakwera nthaŵi zonse.” (Yesaya 34:9, 10) Motero dziko la Edomu likulongosoledwa kukhala labwinja kwambiri kotero kuti linali ngati kuti zigwa zake za madzi zinasanduka matope akuda ndipo fumbilo linasanduka sulfure, ndiyeno zinthu zokolera zimenezi zinakolezedwa moto.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 17:16.
11, 12. Kuchokera kumalongosoledwe olosera operekedwa pa Yesaya 34:10-15, kodi dziko la Edomu likakhala chiyani, ndipo mkhalidwe wa dziko umenewo ukapitirizabe kwautali wotani?
11 Ulosi wa Yesaya ukupitirizabe: “M’mibadwomibadwo lidzakhala labwinja, palibe amene adzapitapo nthaŵi za nthaŵi. Koma vuwo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khungubwi adzakhala mmenemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo chingwe chowongolera cha chisokonezo, ndi chingwe cholungamitsa chiriri chosatha kuchita kanthu. Iwo adzaitana mfulu zake ziloŵe mu ufumu, koma sizidzawonekako; ndi akalonga ake onse adzakhala chabe. Ndipo minga idzamera m’nyumba zake zazikulu, khwisa ndi mitungwi m’malinga mwake; ndipo adzakhala malo a ankhandwe, ndi bwalo la nthiŵatiŵa. Ndipo zirombo za m’chipululu zidzakomana ndi mimbulu, tonde adzaitana mnzake; inde mantchichi adzatera kumeneko, nadzapeza popumira. Kumeneko njoka yotumpha idzapanga chisanja chake, niikira [madzira].”—Yesaya 34:10-15.
12 Malinga ndi kunena kwa anthu Edomu akakhala dziko “labwinja.” Anali kudzakhala wapululu wokhala zirombo zokha, mbalame, ndi njoka. Mkhalidwe wadziko umenewu unali kudzapitirizabe, monga momwe vesi 10 limanenera, ku “nthaŵi za nthaŵi.” Sipakakhala kubwezeretsedwa kwa nzika zake zoyamba.—Obadiya 18.
13. Kodi nchiyani chimene chanenedweratu ponena za Dziko Lachikristu “m’bukhu la Yehova,” ndipo kodi nchiyani, molunjika, chimene chiri bukhu limeneli?
13 Ha ndimkhalidwe womvetsa chisoni chotani nanga umene zimenezi zinaphiphiritsira kaamba ka mnzake wamakono wa Edomu—Dziko Lachikristu! Ladzitsimikizira kukhala mdani wamkulu wa Yehova Mulungu, amene Mboni zake lazunza mwauchinyama. Motero chiwonongeko chake choyandikira chimenechi Armagedo isanafike chanenedweratu “m’bukhu la Yehova.” (Yesaya 34:16) Mwachindunji, “bukhu la Yehova” limeneli ndilo bukhu lake la zochitika, lolongosola tsatanetsatane wa zochitika zimene adzafunikira kutherana ndi awo amene ali adani ake ndi opsinja anthu ake. Zimene zinalembedwa “m’bukhu la Yehova” ponena za Edomu wakale zinakwaniritsidwa, ndipo zimenezi zikutsimikizira kuti ulosi monga momwe ukugwirira ntchito ku Dziko Lachikristu, Edomu wamakono, mofananamo udzakwaniritsidwa.
14. Kodi Aedomu ophiphiritsiridwa amakono sanavomereze chiyani, ndipo ndichitsanzo chotani cha anthu a Yehova chimene iwo alephera kutsatira?
14 Aedomu ophiphiritsiridwa amakono sanavomereze Yehova Mulungu kukhala Mfumu mkati mwa ‘mapeto a dongosolo limeneli la zinthu.’ Kwenikweni, popeza kuti Dziko Lachikristu liri mbali yapadera ya Babulo Wamkulu, iro laweruziridwa ku kugaŵanamo m’miliri yake. Iro silinachite mogwirizana ndi lamulo la Yehova la “kutuluka” m’Babulo Wamkulu. (Chivumbulutso 18:4) Iro silinatsatire chitsanzo cha otsalira a Israyeli auzimu kapena cha “khamu lalikulu” la “nkhosa zina.”
15, 16. Kodi nchiyani chimene chiripo pafupi mtsogolo mwa Dziko Lachikristu, monga momwe kwanenedweratu m’Chivumbulutso 17 ndi 18 ndi Yesaya 34?
15 Mtsogolo moyandikira mwa Dziko Lachikristu mulidi mwamdima. Iro likuchita zothekera kukondweretsa mabwenzi ake a ndale zadziko ndi kuwalepheretsa kusonkhana pamodzi kuchitapo kanthu mwankhalwe motsutsana nalo, kuti liwonongedwe kotheratu, koma mosaphula kanthu!
16 Mogwirizana ndi kunena kwa Chivumbulutso chaputala 17 ndi 18, Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova, adzaika m’mitima yawo kuti mphamvu zawo zandale zadziko ndi ankhondo zigwiritsiridwe ntchito mwankhalwe motsutsana ndi Babulo Wamkulu kumbali zake zonse za chipembedzo, kuphatikizapo Dziko Lachikristu. Zimenezi zidzachotsa Akristu m’dzina lokha padziko lonse lapansi. Mkhalidwe wa Dziko Lachikristu udzakhala wofanana ndi mkhalidwe wopanda chiyembekezo wolongosoledwa m’Yesaya 34. Iro silidzakhalapo kuti liwone ‘nkhondo yomaliza nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ yotsutsana ndi mitundu, imene idzakhala itawononga Babulo Wamkulu. Edomu, wophiphiritsiridwa, Dziko Lachikristu, adzachotsedwa kotheratu pankhope ya dziko lapansi, “kunthaŵi za nthaŵi.”
[Chithunzi patsamba 122]
Dziko Lachikristu lidzalandira chiweruzo chofanana ndi cha Aedomu, mbadwa za Esau, amene anagulitsa kuyenera kwa kukhala woyamba kubadwa ndi chakudya chimodzi