-
Muziona Kuti Moyo Ndi Mphatso Yamtengo WapataliMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova chifukwa chotipatsa mphatso ya moyo?
Yehova anaona kuti ndinu wamtengo wapatali kungochokera pamene mayi anu anatenga pakati. M’pemphero limene Yehova analola kuti lilembedwe m’Mawu ake, mtumiki wake Davide anauza Yehova kuti: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza.” (Salimo 139:16) Yehova amaona kuti moyo wanu ndi wamtengo wapatali kwambiri. (Werengani Mateyu 10:29-31.) Zimamupweteka kwambiri Yehova akaona munthu wina akuchotsa mwadala moyo wake kapenanso wa munthu wina.a (Ekisodo 20:13) Zimamupwetekanso kwambiri tikamachitira dala zinthu zimene zingaike moyo wathu pa ngozi kapenanso tikamalephera kutsatira malangizo omwe angateteze moyo wathu ndi wa anthu ena. Tikamayesetsa kusamala moyo wathu komanso tikamalemekeza moyo wa anthu ena timasonyeza kuti timayamikira mphatso ya moyo yomwe ndi yamtengo wapatali.
-
-
Muziona Kuti Moyo Ndi Mphatso Yamtengo WapataliMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
5. Muziona kuti moyo wa mwana amene sanabadwe ndi wamtengo wapatali
Davide anafotokoza kuti Yehova amachita chidwi ndi chilichonse chimene chimachitika mwana akamakula m’mimba mwa amayi ake. Werengani Salimo 139:13-17, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Yehova amaona kuti moyo umayamba pa nthawi iti, pamene mayi wangotenga mimba kapena mwana akangobadwa?
Malamulo amene Yehova anapereka kwa Aisiraeli ankateteza moyo wa mayi komanso wa mwana amene sanabadwe. Werengani Ekisodo 21:22, 23, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Yehova ankaona bwanji munthu yemwe wapha mwana wosabadwa mwangozi?
Nanga kodi angaone bwanji munthu yemwe wapha mwana wosabadwa mwadala?b
Kodi inuyo mukuona kuti maganizo a Mulungu pa nkhani imeneyi ndi omveka?
Nthawi zina ngakhale mayi yemwe amaona kuti moyo wa mwana wosabadwa ndi wamtengo wapatali, akhoza kukumana ndi vuto lomwe lingamuchititse kuona kuti sangachitire mwina koma kuchotsa mimba basi. Werengani Yesaya 41:10, kenako mukambirane mafunso awa:
Ngati mayi akukakamizidwa kuti achotse mimba, kodi ayenera kudalira ndani kuti amuthandize? N’chifukwa chiyani mukutero?
-
-
Muziona Kuti Moyo Ndi Mphatso Yamtengo WapataliMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
b Anthu amene anachotsapo mimba sayenera kumadziimba mlandu kwambiri chifukwa Yehova akhoza kuwakhululukira. Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti, “Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yochotsa Mimba?” pagawo lakuti Onani Zinanso m’phunziroli.
-