Lingaliro la Baibulo
Kodi Akristu Ayenera Kuda Ochita Mathanyula?
MU 1969 anapeka liwu m’chinenero cha Chingelezi lonena za mantha onyanyira kapena kuda ochita mathanyula koopsa. Liwulo ndi “homophobia.” M’zilankhulo zambiri mulibe liwu lachindunji ngati limeneli, komabe kwazaka zikwi zambiri, anthu m’maiko ambiri, ndipo azilankhulo zosiyanasiyana asonyeza chidani kwa ochita mathanyula.
Komabe posachedwapa, anthu ambiri alimbikitsa mathanyula monga njira ina yogonanirana. Posachedwapa, wolemba mbiri yakale Jerry Z. Muller analemba kuti “ambiri akufuna kuti avomerezedwe ndi kulemekezedwa.” Ananena kuti ochita mathanyula “nthaŵi zambiri agwirizana pamodzi kulengeza kuti khalidwe lawolo lili bwino, ndi kuti ena nawonso alione chimodzimodzi.” Izi zimachitika makamaka m’maiko a Kumadzulo. Komabe, m’malo ambiri a dziko lapansi, ngakhale m’maiko otchedwa kuti ngaufulu, ambiri amatsutsa mathanyula ndi kunyansidwa nawo.
Kaŵirikaŵiri ochita mathanyula ndi omwe amawaganizira kuchita mathanyula amawanyoza, kuwavuta, ndi kuwachita chiwawa. Ngakhale atsogoleri azipembedzo asonyeza chidani chotero. Ena ayamba kuchita chomwe chingaoneke kukhala nkhondo yapaokha yolimbana ndi ochita mathanyula. Mwachitsanzo, lingalirani za ndemanga zoperekedwa ndi bishopu wa Greek Orthodox Church zomwe zinalengezedwa posachedwapa pa wailesi ya dziko la Greece. Iye anati: “Mulungu adzatentha ochita mathanyula kwamuyaya m’ng’anjo ya helo. Kulira kwa pakamwa pawo ponyansa kudzamveka kwamuyaya. Matupi awo ochimwa adzazunzidwa koopsa.” Kodi izi nzoonadi? Kodi Mulungu amawaona motani ochita mathanyula?
Malingaliro a Mulungu
Baibulo silinena mwapadera kuti ochita mathanyula ndi gulu loyenera kupatulidwa kapena lodedwa ndi Akristu. Ndiponso, siliphunzitsa kuti Mulungu adzalanga amathanyula—kapena zolengedwa zake zina—mwa kuzitentha kwamuyaya m’ng’anjo ya helo.—Yerekezerani ndi Aroma 6:23.
Komabe, Malemba amalongosola malamulo a Mlengi wathu a khalidwe labwino, amene kaŵirikaŵiri amatsutsana ndi kakhalidwe kamakono. Kuchita mathanyula, kugonana mwamuna ndi mkazi osakwatirana, ndi kugona ndi nyama, zonsezi zimatsutsidwa m’Baibulo. (Eksodo 22:19; Aefeso 5:3-5) Mulungu anawononga Sodomu ndi Gomora chifukwa cha kugonana kwa mtundu umenewo.—Genesis 13:13; 18:20; 19:4, 5, 24, 25.
Ponena za kuchita mathanyula, Mawu a Mulungu amanena mwachindunji kuti: “Chonyansa ichi.” (Levitiko 18:22) Lamulo la Mulungu kwa Israyeli linati: “Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse aŵiri; awaphe ndithu.” (Levitiko 20:13) Chilango chomwecho chinakhazikitsidwanso kwa ogona ndi nyama, ogonana pachibale, ndi ochita chigololo.—Levitiko 20:10-12, 14-17.
Mtumwi Paulo anauziridwa kunena kuti mathanyula ndiwo kutsata “zilakolako zamanyazi” ndi “machitidwe osalingana ndi chibadwidwe.” Iye akulemba kuti: “Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako zamanyazi: pakuti angakhale akazi awo anasandutsa machitidwe awo a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chawo wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwawo. Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m’chidziŵitso chawo, anawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera.”—Aroma 1:26-28.
Malemba sasintha, saluluza zinthu, samapita m’mbali—kuchita mathanyula, chigololo, dama, zonsezi nzonyansa pamaso pa Mulungu. Motero Akristu oona saluluza zomwe Baibulo linanena za “zilakolako zamanyazi” chabe kungoti atchuke kapena kuti ayendere limodzi ndi chimakono. Komanso sagwirizana ndi kagulu kalikonse kamene cholinga chake nkulimbikitsa mathanyula ngati moyo wabwino.
“Danani Nacho Choipa”
Baibulo limalangiza kuti: “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa.” (Salmo 97:10) Motero Akristu amayembekezeredwa kudana ndi machitidwe alionse amene amaphwanya malamulo a Yehova. Anthu ena nthaŵi zina akhoza kusonyeza kuzonda kapena kuipidwa ndi mathanyula kusiyana ndi mitundu ina ya chiwerewere, akumaona mathanyula monga machitidwe oipa osakhala achibadwa pa zakugonana. Komabe, kodi Akristu ayenera kuda munthu wochita zimenezo?
Wamasalmo akutiunikira pankhani imeneyi pa Salmo 139:21, 22 kuti: “Kodi sindidana nawo iwo akudana ndi Inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nawo chisoni iwo akuukira Inu? Ndidana nawo ndi udani weniweni: ndiwayesa adani.” Kukhulupirika kwathu kwa Yehova ndi pa malamulo ake kuyenera kutipangitsa kuda kwambiri awo amene mwadala amapandukira Yehova ndi amene amakhala adani a Mulungu. Satana ndi ziŵanda ali pakati pa adani odziŵika a Mulungu. Anthu ena mwachionekere nawonso ali m’gulu limeneli. Komabe, nkovuta kwambiri kwa m’Kristu kuti azindikire anthu amenewo mwa kungowaona chabe. Sitingathe kudziŵa mitima. (Yeremiya 17:9, 10) Kukhoza kukhala kulakwa kulingalira kuti uje ndi mdani wa Mulungu wosati nkusintha chifukwa chakuti akuchita zoipa. Nthaŵi zambiri ochita zoipa amangokhala chabe kuti sadziŵa malamulo a Mulungu.
Motero, Akristu kaŵirikaŵiri sathamangira kuda anthu anzawo. Ngakhale atakhala kuti amada kwambiri kakhalidwe kamtundu wina, safuna kuvulaza ena, kapenanso kuŵasungira chakukhosi kapena chizondi. M’malo mwake, Baibulo limalangiza Akristu kuti “khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”—Aroma 12:9, 17-19.
“Mulungu Alibe Tsankhu”
Yehova adzakhululukira munthu amene angalapedi mosasamala kanthu za mtundu wa chiwerewere umene amachita. Palibe umboni wakuti Yehova amaona mtundu wina wa chiwerewere monga woipitsitsa kuposa unzake. “Mulungu alibe tsankhu.” (Machitidwe 10:34, 35) Mwachitsanzo, lingalirani zochitika mumpingo wa ku Korinto m’zaka za zana loyamba. Mtumwi Paulo anawalembera kuti: ‘Adama kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna [“amuna ogona ndi amuna,” NW] kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.’ Kenaka Paulo anavomereza kuti ena omwe kale anali adama, achigololo, amathanyula, ndi akuba anali atalandiridwa mumpingo wachikristu m’Korinto. Iye anati: “Ndipo ena a inu munali otere. Koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.”—1 Akorinto 6:9-11.
Ndithudi, Yehova salekerera kupitiriza ndi kuumirira kuswa malamulo ake a makhalidwe abwino. Iye amadana ndi kuumirira kuswa malamulo ake. Komabe amasiya mpata woti nkuyanjananso naye. (Salmo 86:5; Yesaya 55:7) Mogwirizana ndi zimenezi, Akristu sada amathanyula kaya wina aliyense kapena kukhala ndi malingaliro audani, kunyoza kapena kuwanyodola. Akristu oona amaona anthu anzawo monga omwe akhoza kukhala ophunzira a Kristu, kumawachitira ulemu. Baibulo limati: “Pakuti ichi nchokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu; amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.”—1 Timoteo 2:3, 4.
Akristu Amalandira Olapa
Baibulo limanena mobwerezabwereza kuti Mulungu ndi wokhululukira. Limamlongosola monga “Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo.” (Nehemiya 9:17; Ezekieli 33:11; 2 Petro 3:9) Baibulo limapitiriza kumuyerekezera ndi tate m’fanizo la Yesu lonena za mwana woloŵerera, amene anamwaza chuma chake pochita makhalidwe osayenera kudziko lakutali. Atateyo anayembekezera mofunitsitsa kuti alandirenso mwana wakeyo pamene mwanayo anazindikira kulakwa kwake, nalapa, ndi kubwerera kunyumba kwawo.—Luka 15:11-24.
Ndithudi, nkotheka kuti olakwa asinthe. Malemba amasonyeza izi mwa kulimbikitsa anthu kuvula maumunthu awo akale ndi kuvala atsopano ndi kuti ‘akonzeke, nakhale atsopano mu mzimu wa mtima wawo.’ (Aefeso 4:22-24) Amene amachita zoipa, kuphatikizapo ochita mathanyula, akhoza kusintha kwambiri pa kaganizidwe kawo ndi khalidwe lawo, ndipo ambiri akwanitsadi kusintha kumeneku.a Yesu mwiniyo ankalalikira kwa oterowo; ndipo akalapa, anali kuwalandira.—Mateyu 21:31, 32.
Akristu amalandira anthu olapa osiyanasiyana. Atasiya khalidwe loipa, mulimonse mmene analiri, onse akhoza kusangalala mokwana ndi chikhululuko cha Mulungu chifukwa “Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.”—Salmo 145:9.
Akristu ndi ofunitsitsa kupereka chithandizo chauzimu chofunika, ngakhale kwa amene mpaka tsopano akulimbana ndi kuthetsa chilakolako cha kuchita mathanyula. Izi zimasonyeza momwe Mulungu amasonyezera chikondi, chifukwa Baibulo limati: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.”—Aroma 5:8.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Kodi Ndingaletse Motani Zilakolako Zimenezi?,” mu Galamukani! wa April 8, 1995.
[Mawu Otsindika patsamba 14]
Akristu sasintha zomwe Baibulo limanena za mathanyula
[Mawu a Chithunzi patsamba 13]
Punch