“Mundisanthule, Mulungu”
“Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; . . . nimunditsogolere panjira yosatha.”—SALMO 139:23, 24.
1. Kodi ndimotani mmene Yehova amachitira zinthu ndi atumiki ake?
TONSEFE timafuna kuchita zinthu ndi munthu amene amamvetsetsa, munthu amene amalingalira za mikhalidwe yathu, munthu amene amathandiza pamene tilakwa, munthu amene samatiuza kuchita zimene sitikwanitsa. Yehova Mulungu amachita zinthu ndi atumiki ake mwanjira imeneyo. Lemba la Salmo 103:14 limati: “Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” Ndipo Yesu Kristu, amene ali chitsanzo changwiro cha Atate wake, akupereka chiitano chachifundo chakuti: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa [kapena kuti, “Loŵani m’goli langa ndi ine,” mawu amtsinde, NW] ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: Ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”—Mateyu 11:28-30.
2. Siyanitsani kaonedwe ka Yehova ndi ka anthu ponena za (a) Yesu Kristu, ndi (b) otsatira a Kristu.
2 Yehova amaona atumiki ake mosiyana ndi mmene anthu amawaonera. Iye amaona zinthu ndi lingaliro losiyana ndipo amapenda zinthu zimene anthu ena sangazidziŵe konse. Pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi, “ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu.” Awo amene sanakhulupirire mwa iye monga Mesiya ‘sanamlemekeze.’ (Yesaya 53:3; Luka 23:18-21) Komabe, pamaso pa Mulungu, iye anali “Mwana [wa Mulungu] wokondedwa,” kwa amene Atateyo anati: “Mwa iwe ndikondwera.” (Luka 3:22; 1 Petro 2:4) Pakati pa otsatira a Yesu Kristu pali anthu amene amanyozedwa chifukwa chakuti ali osauka m’chuma chakuthupi ndipo amapirira masautso ambiri. Komabe, m’maso mwa Yehova ndi Mwana wake, anthu oterowo ali olemera. (Aroma 8:35-39; Chivumbulutso 2:9) Kodi nchifukwa ninji pali kuona mwanjira zosiyana?
3. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova amaona anthu mosiyana ndi mmene anthu amaonera? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kwa ife kupenda mtundu wa munthu amene tili mkati mwathu?
3 Lemba la Yeremiya 11:20 limayankha kuti: “Yehova . . . ayesa impso ndi mtima.” Iye amaona zimene tili mkati mwathu, amaona ngakhale mikhalidwe ya umunthu wathu yobisika kwa ena. M’kusanthula kwake, amayang’anitsitsa kwambiri mikhalidwe ndi zinthu zimene zili zofunika kwambiri muunansi wathu ndi iye, imenenso ili yotipindulitsa kwanthaŵi yaitali. Kudziŵa kwathu zimenezo kumatilimbikitsa; kumatitonthozanso. Popeza kuti Yehova amayang’ana zimene tili mkati mwathu, kuli kofunika kwambiri kuti tidzipende zimene tili mkati mwathu ngati tifuna kukhala anthu amene iye amawafuna m’dziko lake latsopano. Mawu ake amatithandiza m’kudzipenda koteroko.—Ahebri 4:12, 13.
Malingaliro a Mulungu Ngamtengo Wapatali Chotani Nanga!
4. (a) Kodi nchiyani chinasonkhezera wamasalmo kunena kuti malingaliro a Mulungu anali amtengo wapatali kwa iye? (b) Kodi nchifukwa ninji ayeneranso kukhala amtengo wapatali kwa ife?
4 Atasinkhasinkha ponena za ukulu ndi kuzama kwa chidziŵitso cha Mulungu cha atumiki ake, ndi ponenanso za mphamvu yapadera ya Mulungu ya kugaŵira chithandizo chilichonse chimene iwo angafunikire, wamasalmo Davide analemba kuti: “Ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu!” (Salmo 139:17a) Malingaliro amenewo, ovumbulidwa m’Mawu ake olembedwa, ali amtengo wapatali kwambiri kuposa alionse ochokera kwa anthu, mosasamala kanthu kuti maganizo awo angaoneke aluntha motani. (Yesaya 55:8, 9) Malingaliro a Mulungu amatithandiza kusumika maganizo athu pazinthu zofunika kwenikweni m’moyo ndi kukhala achangu muutumiki wake. (Afilipi 1:9-11) Iwo amatithandiza kuona zinthu mmene Mulungu amazionera. Amatithandiza kukhala owona mtima kwa ife eni, tikumavomereza mowona mtima mtundu wa munthu amene tili mumtima mwathu. Kodi muli wofunitsitsa kuchita zimenezo?
5. (a) Kodi Mawu a Mulungu amatisonkhezera kuchinjiriza chiyani “koposa zonse”? (b) Kodi cholembedwa cha Baibulo chonena za Kaini chingatipindulitse motani? (c) Ngakhale kuti sitili pansi pa Chilamulo cha Mose, kodi icho chimatithandiza motani kuzindikira zimene zimakondweretsa Yehova?
5 Anthu ali okhoterera kuyang’ana maonekedwe akunja, koma Malemba amatilangiza kuti: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga.” (Miyambo 4:23) Baibulo limatithandiza kuchita zimenezo, ponse paŵiri mwa malamulo ndi zitsanzo. Limatiuza kuti Kaini anali kupereka nsembe zachiphamaso kwa Mulungu pamene mkwiyo unali kutukusira mumtima mwake, kenako anakhala ndi chidani pa mbale wake Abele. Ndipo limatichenjeza kusafanana naye. (Genesis 4:3-5; 1 Yohane 3:11, 12) Limasimba za kumvera kofunidwa ndi Chilamulo cha Mose. Komanso limagogomezera kuti chofunika chachikulu koposa cha Chilamulocho chinali chakuti awo amene analambira Yehova anayenera kumkonda iye ndi mtima wawo wonse, maganizo awo onse, ndi mphamvu zawo zonse; ndipo limanena kuti chofunika chachiŵiri chinali lamulo la kukonda mnansi wawo monga iwo eni.—Deuteronomo 5:32, 33; Marko 12:28-31.
6. Pogwiritsira ntchito Miyambo 3:1, kodi ndimafunso otani amene tiyenera kudzifunsa?
6 Pa Miyambo 3:1, timafulumizidwa osati kungosunga malamulo a Mulungu komanso kutsimikizira kuti kumvera kwathu kuli chisonyezero cha zimene zilidi mumtima mwathu. Monga munthu aliyense payekha, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimenezo nzowona ponena za kumvera kwanga zofuna za Mulungu?’ Ngati tizindikira kuti m’zinthu zina zolinga zathu kapena malingaliro athu ali osayenera—ndipo palibe aliyense wa ife anganene kuti samalakwa—pamenepo tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikuchitanji kuti ndiwongolere mkhalidwewo?’—Miyambo 20:9; 1 Yohane 1:8.
7. (a) Kodi ndimotani mmene chidzudzulo cha Yesu kwa Afarisi cha pa Mateyu 15:3-9 chingatithandizire kutchinjiriza mtima wathu? (b) Kodi ndimikhalidwe yotani imene ingatifunikiritse kuchita zamphamvu kuti tilange maganizo ndi mtima wathu?
7 Pamene Afarisi Achiyuda anasonyeza chiphamaso cha kulemekeza Mulungu pamene mwamachenjera anali kuchilikiza mchitidwe wosonkhezeredwa ndi dyera, Yesu anawadzudzula monga onyenga nasonyeza kuti kulambira kwawo kunali kopanda pake. (Mateyu 15:3-9) Yesu anachenjezanso kuti pofuna kukondweretsa Mulungu, amene amaona mtima, sikumakhala kokwanira kukhala chabe ndi khalidwe labwino lakunja kwinaku, pofuna kusangulutsa maganizo, tikumamwerekera mosalekeza m’malingaliro oipa. Tifunikira kuchita zamphamvu kuti tilange maganizo athu ndi mtima. (Miyambo 23:12; Mateyu 5:27-29) Chilango choterocho chimafunikanso ngati chifukwa cha ntchito yathu, zonulirapo zathu za maphunziro, kapena zosangulutsa zimene timasankha, tikukhala otsanzira dziko, tikumalilola kutiumba mogwirizana ndi miyezo yake. Tisaiŵale konse kuti wophunzira Yakobo akuwatcha “akazi achigololo” awo amene amadzinenera kukhala a Mulungu koma namafuna kukhala mabwenzi a dziko. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”—Yakobo 4:4; 1 Yohane 2:15-17; 5:19.
8. Kuti tipindule mokwanira ndi malingaliro a Mulungu amtengo wapatali, kodi tiyenera kuchitanji?
8 Kuti tipindule mokwanira ndi malingaliro a Mulungu pankhanizi ndi zina, tiyenera kupatula nthaŵi ya kuwaŵerenga kapena kuwamvetsera. Zoposa zimenezo, tifunikira kuwaphunzira, kulankhula ponena za iwo, ndi kuwasinkhasinkha. Oŵerenga ambiri a Nsanja ya Olonda amapezeka mokhazikika pamisonkhano yampingo ya Mboni za Yehova, kumene Baibulo limaphunziridwa. Iwo amawombola nthaŵi ku zochita zina kotero kuti achite zimenezo. (Aefeso 5:15-17) Ndipo zimene amapindulapo zimakhala za mtengo wapatali kuposa chuma chakuthupi. Kodi mmenemo sindimo mmene mumamvera?
9. Kodi nchifukwa ninji ena amene amapezeka pamisonkhano Yachikristu amapita patsogolo mwamsanga kuposa ena?
9 Komabe, ena amene amapezeka pamisonkhano imeneyi amapita patsogolo mofulumira kwambiri kuposa ena. Iwo amagwiritsira ntchito kwambiri chowonadi m’miyoyo yawo. Kodi nchiyani chimachititsa zimenezi? Kaŵirikaŵiri, chochititsa chachikulu chimakhala khama lawo m’phunziro laumwini. Iwo amazindikira kuti sitimakhala ndi moyo ndi mkate wokha; chakudya chauzimu cha tsiku ndi tsiku chimakhala chofunika monga momwe timadyera chakudya chakuthupi nthaŵi zonse. (Mateyu 4:4; Ahebri 5:14) Motero iwo amayesayesa kuthera nthaŵi inayake tsiku lililonse akuŵerenga Baibulo kapena zofalitsidwa zimene zimalifotokoza. Iwo amakonzekera misonkhano yampingo, kukonzekera nkhani zophunziridwa pasadakhale ndi kuŵerenga malemba operekedwa. Amachita zoposa kungoŵerenga nkhanizo; amasinkhasinkha pazimenezo. Kaphunziridwe kawo kamaphatikizapo kulingalira mwamphamvu ponena za chiyambukiro chimene zimene amaziphunzira ziyenera kukhala nacho pa miyoyo yawo. Pamene akukula mwauzimu, amafikira pakumva mmene anachitira wamasalmo amene analemba kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; . . . Mboni zanu nzodabwitsa.”—Salmo 1:1-3; 119:97, 129.
10. (a) Kodi munthu ayenera kupitirizabe kuphunzira Mawu a Mulungu kwa utali wotani kuti apindule? (b) Kodi Malemba amasonyeza motani zimenezi?
10 Kaya taphunzira Mawu a Mulungu kwa chaka chimodzi, zaka 5, kapena zaka 50, samangokhala zobwerezabwereza—samakhala otero ngati malingaliro a Mulungu ali amtengo wapatali kwa ife. Mosasamala kanthu kuti aliyense wa ife waphunzira zochuluka motani m’Malemba, pali zambiri zimene sitikudziŵa. “Maŵerengedwe ake ndi ambirimbiri!” anatero Davide. “Ndikaziŵerenga zichuluka koposa mchenga.” Sitingathe kuŵerenga malingaliro a Mulungu. Ngati tinati tiŵerenge malingaliro a Mulungu kwa tsiku lonse lathunthu mpaka kugona tikuŵerengabe, pamene tidzuka mmaŵa, pakakhalabe ochuluka owalingalira. Motero, Davide analemba kuti: “Ndikauka ndikhalanso nanu.” (Salmo 139:17, 18) Ku umuyaya wonse padzakhalabe zochuluka zoti tiphunzire ponena za Yehova ndi njira zake. Sitidzafika konse pamlingo umene tidzadziŵa zonse.—Aroma 11:33.
Kudana ndi Zimene Yehova Amadana Nazo
11. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kudziŵa osati malingaliro a Mulungu okha komanso kukhala ndi malingaliro ake?
11 Kuphunzira kwathu Mawu a Mulungu sikuli ndi cholinga chongodzaza mutu wathu ndi maumboni. Pamene tiwalola kuloŵa mumtima wathu, timayambanso kukhala ndi malingaliro a Mulungu. Zimenezo nzofunika chotani nanga! Ngati sitikulitsa malingaliro oterowo, kodi chingachitike nchiyani? Ngakhale kuti tingathe kunena zimene Baibulo limanena, tingaonenso zoletsedwa kukhala zokhumbika, kapena tingaone zimene zili zofunika kukhala zotopetsa. Nzowona kuti ngakhale ngati tidana ndi choipa, tingakhalebe pankhondo chifukwa cha kupanda ungwiro kwaumunthu. (Aroma 7:15) Koma ngati sitiyesayesa mowona mtima kuwongolera umunthu wathu wamkati kugwirizana ndi chimene chili choyenera, kodi tingayembekezere kukondweretsa Yehova, amene “ayesa mitima”?—Miyambo 17:3.
12. Kodi kukonda chinthu chimene Mulungu amakonda ndi kuda chinthu chimene Mulungu amada nkofunika motani?
12 Kuda chinthu chimene Mulungu amada kuli chitetezo champhamvu pakuchita choipa, monga momwe kukonda chinthu chimene Mulungu amakonda kumachititsa kuchita chabwino kukhala kosangalatsa. (1 Yohane 5:3) Mobwerezabwereza Malemba amatifulumiza kukulitsa zonse ziŵiri kukonda ndi kuda chinthu. “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa.” (Salmo 97:10) “Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.” (Aroma 12:9) Kodi tikuchita zimenezo?
13. (a) Kodi ndipemphero la Davide liti limene tikuvomereza kotheratu ponena za kuwonongedwa kwa oipa? (b) Malinga ndi pemphero la Davide, kodi ndioipa otani amene iye anawapempherera kuti Mulungu awawononge?
13 Yehova wanena momvekera bwino za chifuno chake cha kuchotsa anthu oipa padziko lapansi ndi kubweretsa dziko lapansi latsopano mmene mudzakhala chilungamo. (Salmo 37:10, 11; 2 Petro 3:13) Okonda chilungamo akulakalaka kuti nthaŵiyo ifike. Iwo akuvomerezana kotheratu ndi wamasalmo Davide, yemwe anapemphera kuti: “Indedi, [mudzapha, NW] woipa, Mulungu: Ndipo amuna [aliŵongo la mwazi adzachokadi, NW] kwa ine. Popeza anena za inu moipa, ndi adani anu atchula dzina lanu mwachabe.” (Salmo 139:19, 20) Davide sanakhumbe kuti iyemwini aphe anthu oipa oterowo. Iye anapemphera kuti kubwezera kukachokera kudzanja la Yehova. (Deuteronomo 32:35; Ahebri 10:30) Iwoŵa sanali anthu amene anangolakwira Davide chabe. Iwo anaiimira Mulungu monama, akumatchula dzina lake mwanjira yachabe. (Eksodo 20:7) Monyenga, iwo anadzinenera kukhala akutumikira iye, koma anali kugwiritsira ntchito dzina lake kuchilikizira zolinga zawozawo. Davide analibe chikondi kwa awo amene anasankha kukhala adani a Mulungu.
14. Kodi alipo anthu oipa amene angathandizidwe? Ngati nditero, motani?
14 Pali mamiliyoni zikwi zambiri amene samadziŵa Yehova. Ambiri a iwo amachita mwaumbuli zinthu zimene Mawu a Mulungu amazinena kukhala zoipa. Ngati iwo apitiriza panjira imeneyo, adzakhala pakati pa awo amene adzawonongedwa m’chisautso chachikulu. Komabe, Yehova samakondwera ndi imfa ya woipa, ndipo nafenso sitiyenera kutero. (Ezekieli 33:11) Malinga ngati nthaŵi ilola, tidzayesayesa kuthandiza anthu oterowo kuphunzira ndi kugwiritsira ntchito njira za Yehova. Koma bwanji ngati anthu ena amasonyeza chidani chachikulu kwa Yehova?
15. (a) Kodi ndani amene wamasalmo anawaona kukhala ‘adani enieni’? (b) Kodi ndimotani mmene ife lerolino tingasonyezere kuti ‘timadana’ ndi awo opandukira Yehova?
15 Ponena za iwo, wamasalmo anati: “Kodi sindidana nawo iwo akudana ndi inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nawo chisoni iwo akuukira inu? Ndidana nawo ndi udani weniweni: Ndiwayesa adani.” (Salmo 139:21, 22) Davide ananyansidwa ndi anthuwo chifukwa chakuti iwo anamuda kwambiri Yehova. Ampatuko amaphatikizidwa mwa awo amene amasonyeza udani wawo kwa Yehova mwakumpandukira. Mpatuko, kwenikweni, ndiwo kupandukira Yehova. Ampatuko ena amadzinenera kuti amadziŵa Mulungu ndi kuti amamtumikira, koma iwo amakana ziphunzitso kapena zofunika zolembedwa m’Mawu ake. Ena amadzinenera kuti amakhulupirira Baibulo, koma amakana gulu la Yehova namayesayesa mwamphamvu kudodometsa ntchito ya gululo. Pamene iwo asankha mwadala machitidwe oipa oterowo atadziŵa kale chimene chili cholondola, pamene zoipazo zikhomerezeka kwambiri nizikhala mbali ya iwo, pamenepo Mkristu ayenera kudana nawo (m’lingaliro la Baibulo la liwulo) awo amene amaumirira mosalekanitsika pazoipa zoterozo. Akristu owona amakhala ndi malingaliro a Yehova kulinga kwa ampatuko oterowo; iwo samalakalaka kudziŵa ponena za malingaliro ampatuko. Mosiyana ndi zimenezo, ‘amanyansidwa’ ndi awo amene adzipanga okha kukhala adani a Mulungu, koma kubwezera amakusiya m’manja mwa Yehova.—Yobu 13:16; Aroma 12:19; 2 Yohane 9, 10.
Pamene Mulungu Akutisanthula
16. (a) Kodi nchifukwa ninji Davide anafuna kuti Yehova amsanthule? (b) Kodi tiyenera kupempha Mulungu kutithandiza kuzindikira chiyani ponena za mtima wathu?
16 Davide sanafune kufanana ndi anthu oipa mwanjira iliyonse. Anthu ambiri amayesa kubisa zimene ali mkati mwawo, koma Davide modzichepetsa anapemphera kuti: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; mundiyese nimudziŵe zolingalira zanga [zosautsa, NW]. Ndipo mupenye ngati ndili nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.” (Salmo 139:23, 24) Potchula mtima wake, Davide sanatanthauze mtima wake weniweniwo. Mogwirizana ndi tanthauzo lophiphiritsira la liwu limenelo, anatanthauza chimene iye anali mkati mwake, munthu wamkati. Ifenso tiyenera kufuna kuti Mulungu asanthule mtima wathu ndi kuona ngati tili ndi zikhumbo, zokonda, maganizo, zonulirapo, zifuno, malingaliro kapena zolinga zilizonse zosayenera. (Salmo 26:2) Yehova akutipempha kuti: “Mwananga, undipatse mtima wako, maso ako akondwere ndi njira zanga.”—Miyambo 23:26.
17. (a) M’malo mwakubisa malingaliro osautsa, kodi tiyenera kuchitanji? (b) Kodi tiyenera kudabwa ngati tipeza zikhoterero zolakwa mumtima mwathu, ndipo tiyenera kuchitanji ponena za izo?
17 Ngati mkati mwathu muli malingaliro obisika alionse opweteka, osautsa chifukwa cha zikhumbo zolakwa kapena zolinga zoipa kapena chifukwa cha mkhalidwe wathu woipa, pamenepotu tidzafuna kuti Yehova atithandize kuwongolera mkhalidwewo. M’malo mwa mawu akutiwo “mayendedwe oipa,” matembenuzidwe a Moffatt amagwiritsira ntchito mawu akuti “njira yolakwa”; The New English Bible imati: “Njira iliyonse imene imakumvetsani chisoni inu [kunena Mulungu].” Ife enife nthaŵi zina sitingamvetsetse bwino lomwe malingaliro athu osautsa, motero sitingadziŵe mmene tinganenere vuto lathu kwa Mulungu, komabe iye amamvetsetsa mkhalidwe wathu. (Aroma 8:26, 27) Siziyenera kutidabwitsa ngati tili ndi zikhoterero zoipa mumtima mwathu; komabe, sitiyenera kuzilungamitsa. (Genesis 8:21) Tiyenera kufunafuna chithandizo cha Mulungu kuti tizichotse kotheratu. Ngati timakondadi Yehova ndi njira zake, tikhoza kumfikira kaamba ka chithandizo tili ndi chidaliro chakuti “Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.”—1 Yohane 3:19-21.
18. (a) Kodi Yehova amatitsogolera motani panjira yosatha? (b) Ngati tipitirizabe kutsatira chitsogozo cha Yehova, kodi ndichiyanjo chotani chimene tingalandire?
18 Mogwirizana ndi pemphero la wamasalmo lakuti Yehova akamtsogolera panjira yosatha, ndithudi, Yehova amatsogoleradi atumiki ake odzichepetsa ndi omvera. Iye amawatsogolera iwo osati kokha panjira yowapatsa moyo wautali chifukwa cha kusachita zoipa komanso panjira ya kumoyo wamuyaya. Iye amagogomezera kwa ife kufunika kwa mtengo wotetezera machimo wa nsembe ya Yesu. Kupyolera m’Mawu ake ndi gulu lake, iye amatipatsa malangizo ofunika kwambiri kotero kuti tikhale okhoza kuchita chifuniro chake. Iye amagogomezera kwa ife kufunika kwa kulabadira chithandizo chake kotero kuti mkati mwathu tikhale munthu amene timamsonyeza kunja. (Salmo 86:11) Ndipo iye amatisonkhezera ndi chiyembekezo cha thanzi langwiro m’dziko latsopano lachilungamo limodzinso ndi moyo wamuyaya zogwiritsira ntchito pomtumikira iye, Mulungu yekha wowona. Ngati tipitiriza kulabadira chitsogozo chake mokhulupirika, iye adzanenadi kwa ife, mmene ananenera kwa Mwana wake kuti: ‘Ndikondwera nawe.’—Luka 3:22; Yohane 6:27; Yakobo 1:12.
Kodi Munganenenji?
◻ Kodi nchifukwa ninji kaŵirikaŵiri Yehova amaona atumiki ake mosiyana ndi mmene anthu amawaonera?
◻ Kodi nchiyani chingatithandize kudziŵa zimene Mulungu amaona pamene asanthula mtima wathu?
◻ Kodi ndikaphunziridwe kotani kamene kamatithandiza kudziŵa zenizeni ndi kuchinjiriza mtima wathu?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kudziŵa zimene Mulungu amanena ndiponso kukhala ndi malingaliro ake?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupemphera patokha kuti: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga”?
[Chithunzi patsamba 16]
Pamene mukuphunzira, yesayesani kukhala ndi malingaliro a Mulungu ndi kumva mmene amamvera
[Chithunzi patsamba 18]
Zolingalira za Yehova “zichuluka koposa mchenga”
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.