Lemekezani Yehova mwa Kusonyeza Ulemu
‘Zochita za Yehova ndi zaulemu ndi zazikulu.’—SAL. 111:3.
1, 2. (a) Kodi mawu akuti “ulemu” amatanthauza chiyani? (b) Kodi tikambirana mafunso otani m’nkhaniyi?
POSONYEZA kuti Mulungu ndi woyenera kulemekezedwa, Baibulo limati: “Yehova, Mulungu wanga . . . muvala ulemu ndi chifumu.” (Sal. 104:1, 2) Mtumwi Paulo anasonyeza kuti anthunso angachite zinthu zimene zingawapangitse kuti alemekezedwe. Ponena za mavalidwe a akazi achikhristu iye anati: “Akazi azidzikongoletsa mwa kuvala moyenera, mwaulemu ndi mwanzeru, osati mwa masitayilo a malukidwe a tsitsi, golide, ngale, kapena zovala zamtengo wapatali.” (1 Tim. 2:9) Koma kuti tilemekeze Yehova chifukwa cha ukulu ndi ulemerero wake, tifunika zambiri osati kuvala mwaulemu kokha.—Sal. 111:3.
2 M’Baibulo mawu achiheberi otanthauza kuti “ulemu” angamasuliridwenso kuti “ukulu,” “ulemerero,” kapena “kulemekezeka.” Malinga ndi buku lina lotanthauzira mawu, mawu akuti “ulemu” amatanthauza “khalidwe labwino lodzilemekeza ndi kulemekezanso ena.” Yehova ndiye wofunika kulemekezedwa kwambiri kuposa wina aliyense. Choncho, popeza kuti ndife atumiki odzipereka a Mulungu, tizilankhula ndi kuchita zinthu mwaulemu. Koma kodi n’chifukwa chiyani anthu amatha kusonyeza ulemu? Kodi ulemerero ndi ukulu wa Yehova umaonekera bwanji? Kodi ulemerero wa Mulungu uyenera kutikhudza bwanji? Kodi tingaphunzire chiyani kwa Yesu Khristu pankhani yosonyeza ulemu? Ndipo kodi ifeyo tingatsanzire bwanji Mulungu posonyeza ulemu?
Chifukwa Chake Anthu Amatha Kusonyeza Ulemu
3, 4. (a) Kodi tizitani chifukwa cha ulemu umene tapatsidwa? (b) Kodi ulosi wa pa Salmo 8:5-9 umanena za ndani? (Onani mawu a m’munsi.) (c) Kodi ndani analemekezedwapo ndi Yehova?
3 Anthu onse amatha kusonyeza ulemu chifukwa chakuti analengedwa m’chifanizo cha Mulungu. Yehova analemekeza munthu woyamba mwa kum’patsa udindo wosamalira dziko lapansi. (Gen. 1:26, 27) Ngakhale pamene anthu anachimwa, Yehova sanawalande udindo wosamalira dziko lapansi. Motero, Mulungu amapatsabe anthu ulemu. (Werengani Salmo 8:5-9.)a Chifukwa choti tapatsidwa ulemu, tifunikanso kusonyeza ulemu mwa kutamanda dzina lalikulu la Yehova.
4 Yehova amalemekeza makamaka anthu amene amamutumikira. Mulungu analemekeza Abele mwa kulandira nsembe imene anapereka koma anakana nsembe ya m’bale wake Kaini. (Gen. 4:4, 5) Mose analangizidwa kuti ‘aike ulemerero wake’ wina pa Yoswa, amene anam’lowa m’malo potsogolera Aisiraeli. (Num. 27:20) Ponena za Solomo, mwana wa Davide, Baibulo limati: “Yehova anakuza Solomo kwakukulu pamaso pa Aisiraeli onse, nam’patsa ulemerero wachifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Isiraeli inali nawo wotero.” (1 Mbiri 29:25) Mulungu amalemekeza mwapadera Akhristu odzozedwa oukitsidwa, amene analengeza mokhulupirika “ulemerero waukulu wa ufumu wake.” (Sal. 145:11-13) Motero, “nkhosa zina” za Yesu nazonso zadalitsidwa ndi kulemekezedwa chifukwa chotamanda Yehova.—Yoh. 10:16.
Kodi Ulemerero ndi Ukulu wa Yehova Umaonekera Bwanji?
5. Kodi Yehova ali ndi ulemerero waukulu motani?
5 M’nyimbo yosonyeza kuti Mulungu ndi wamkulu kuposa anthu, wamasalmo Davide anati: “Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.” (Sal. 8:1) Kuyambira muyaya mpaka muyaya, Yehova Mulungu wakhala wolemekezeka kwambiri m’chilengedwe chonse. Iye wakhala wolemekezeka “kumwamba ndi dziko lapansi” zisanalengedwe, ndipo adzalemekezedwabe ngakhale cholinga chake chachikulu chopanga dziko lapansi kukhala paradaiso chitakwaniritsidwa.—Gen. 1:1; 1 Akor. 15:24-28; Chiv. 21:1-5.
6. Kodi n’chifukwa chiyani wamasalmo ananena kuti Yehova wavala ulemerero?
6 Wamasalmo woopa Mulungu ayenera kuti anakhudzidwa kwambiri ataona nyenyezi zambiri zokongola. Atadabwa kwambiri ndi mmene Mulungu ‘anayalira thambo ngati nsalu,’ iye anati Yehova wavala ulemerero chifukwa cha zinthu zomwe anazilenga mwaluso kwambiri. (Werengani Salmo 104:1, 2.) Ulemerero ndi ukulu wa Mlengi, yemwe sitimuona, zimaoneka m’ntchito zake.
7, 8. Kodi ulemerero ndi ukulu wa Yehova umaonekera bwanji m’zinthu za kumwamba?
7 Mwachitsanzo, taganizirani za mlalang’amba wa Milky Way. Mlalang’amba umenewu uli ndi nyenyezi zambirimbiri ndi mapulaneti amene azungulira dzuwa, moti dziko lathu lapansili limaoneka laling’ono zedi ngati kamchenga mu mlalang’ambawu. Mlalang’amba umodzi wokhawu uli ndi nyenyezi zoposa 100 biliyoni. Ngati mutamawerenga nyenyezi imodzi pa sekondi iliyonse mosalekeza tsiku ndi tsiku, zingakutengereni zaka zoposa 3,000 kuti mumalize kuwerenga nyenyezi 100 biliyoni zimenezi.
8 Ngati mlalang’amba umodzi wa Milky Way uli ndi nyenyezi zoposa 100 biliyoni, nanga milalang’amba yonse ingakhale ndi nyenyezi zochuluka bwanji? Akatswiri ena asayansi ya zakuthambo amati pali milalang’amba 50 biliyoni ndipo ena amati ilipo 125 biliyoni. Nanga kodi nyenyezi zonse zilipo zingati? N’zambiri zedi moti chiwerengero chake sitingathe kuchimvetsa. Koma Yehova ‘amawerenga nyenyezi momwe zili; azitcha mayina zonsezi.’ (Sal. 147:4) Mukaona ulemerero ndi ukulu wa Yehova umenewu, kodi sizikuchititsani kutamanda dzina lake lalikulu?
9, 10. Kodi chakudya chimene Mlengi watipatsa chimasonyeza bwanji nzeru zake?
9 Tiyeni tsopano tichoke ku nkhani ya zinthu zodabwitsa zakuthambo ndipo tikambirane za chakudya. Yehova sanangolenga ‘kumwamba ndi dziko lapansi,’ iye amapatsanso “anjala chakudya.” (Sal. 146:6, 7) ‘Ulemerero ndi ukulu’ wa Mulungu umaonekera m’ntchito zake zazikulu, kuphatikizapo chakudya. (Werengani Salmo 111:1-5.) Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Mutipatse ife lero chakudya chathu cha lero.” (Mat. 6:11) Ndipo chakudya chofunika kwambiri kwa anthu akale, ngakhale Aisiraeli chinali buledi. Ngakhale kuti buledi amaoneka kuti ndi chakudya wamba, mmene zinthu zimene amasakaniza popanga buledi zimagwirira ntchito n’zovuta kumvetsa.
10 Nthawi imene Baibulo linkalembedwa, Aisiraeli popanga buledi ankagwiritsa ntchito ufa wa tirigu kapena wa barele ndi madzi. Ndipo nthawi zina ankagwiritsa ntchito yisiti. Sayansi ya mmene zinthu zimenezi zimagwirira ntchito akazisakaniza kuti mpaka buledi apangidwe, anthu satha kuimvetsa. Komanso anthu samvetsa mmene buledi amagayidwira m’thupi mwathu. N’zosadabwitsa kuti wamasalmo anayimba kuti: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru.” (Sal. 104:24) Kodi zinthu zimenezi nanunso zikukuchititsani kufuna kutamanda Yehova?
Kodi Ulemerero ndi Ukulu wa Mulungu Umakukhudzani Motani?
11, 12. Kodi kusinkhasinkha zimene Mulungu walenga, kumatikhudza motani?
11 Sitikufunikira kukhala asayansi kuti tichite chidwi ndi nyenyezi kapena kuti timve kukoma kwa buledi. Koma kuti timvetse ukulu wa Mlengi wathu, tifunikira kukhala ndi nthawi yosinkhasinkha za ntchito ya manja ake. Kodi kusinkhasinkha kotere kungatithandize bwanji? Timakhudzidwa ngati mmene timachitira tikaganizira za ntchito zinanso za Yehova.
12 Ponena za zinthu zazikulu zimene Yehova anachitira anthu Ake, Davide anayimba kuti: “Ndidzalingalira ulemerero waukulu wa ulemu wanu, ndi ntchito zanu zodabwitsa.” (Sal. 145:5) Timaganizira za ntchito zimenezi tikamawerenga Baibulo ndi kukhala ndi nthawi yosinkhasinkha zimene tikuwerengazo. Zimenezi zimatithandiza kuti timvetse bwino ulemerero ndi ukulu wa Mulungu. Ndithudi, tikatero timalemekeza Yehova mofanana ndi Davide amene anati: “Ukulu wanu ndidzaufotokozera.” (Sal. 145:6) Kusinkhasinkha ntchito zodabwitsa za Yehova kudzalimbitsa ubwenzi wathu ndi iye ndipo kudzatilimbikitsa kuuza ena za iye ndi mtima wonse. Kodi mumalengeza uthenga wabwino mwakhama ndi kuthandiza anthu kumvetsa ulemerero ndi ukulu wa Yehova Mulungu?
Yesu Amatsanzira Mulungu Pankhani Yolemekeza Anthu
13. (a) Malinga ndi Danieli 7:13, 14, kodi Yehova wapatsa Mwana wake chiyani? (b) Monga Mfumu, kodi Yesu amachita motani ndi anthu?
13 Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, analengeza mwakhama uthenga wabwino ndipo analemekeza Atate ake akumwamba. Yehova analemekeza mwapadera mwana wake wobadwa yekha mwa kum’patsa ‘ulamuliro ndi ufumu.’ (Werengani Danieli 7:13, 14.) Koma Yesu si wodzikudza kapena wonyada. Iye ndi wolamulira wachifundo amene amadziwa bwino zimene anthu sangathe kuchita ndipo amawapatsa ulemu. Taganizirani chitsanzo chimodzi chosonyeza mmene Yesu, monga mfumu, anachitira zinthu ndi anthu makamaka amene ankaonedwa osafunika kapena amene sankakondedwa.
14. Kodi kale ku Isiraeli anthu akhate ankaonedwa bwanji?
14 Kale anthu akhate ankafa momvetsa chisoni. Pang’ono ndi pang’ono thupi lawo lonse limagwidwa matenda. Anthu ankaona kuti kuchiritsa munthu wakhate kunali kosatheka ngati kuukitsa munthu wakufa. (Num. 12:12; 2 Maf. 5:7, 14) Anthu akhate ankatengedwa kuti ndi odetsedwa ndipo ankakhala kwaokha. Akamayandikira anthu iwo amafunikira kufuula kuti: “Wodetsedwa, wodetsedwa!” (Lev. 13:43-46) Munthu wakhate ankamuona ngati munthu wakufa. Malinga ndi zolembedwa m’mabuku a arabi, wakhate sankaloledwa kuyandikirana ndi munthu pafupifupi mamita awiri. Akuti mtsogoleri winawake wachipembedzo akaona munthu wakhate, ngakhale ali patali, ankamuthamangitsa ndi miyala.
15. Kodi Yesu anatani ndi munthu wakhate?
15 Koma n’zochititsa chidwi kuona mmene Yesu anachitira munthu wakhate atam’pempha kuti am’chiritse. (Werengani Maliko 1:40-42.) M’malo momuthamangitsa, Yesu anam’chitira chifundo ndi kum’lemekeza. Yesu anaona kuti munthuyu anali womvetsa chisoni ndi wofunika thandizo. Chifukwa chokhudzidwa mtima, Yesu anasonyeza chifundo chake mwa kuchiritsa munthuyu. Iye anatambasula dzanja lake kugwira wakhateyo ndipo nthawi yomweyo anachira.
16. Kodi mmene Yesu anali kuchitira zinthu ndi anthu zikutiphunzitsa chiyani?
16 Monga otsatira a Yesu, kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo chake cholemekeza ena potengera Atate ake? Njira imodzi ndi mwa kuzindikira kuti anthu onse afunikira kupatsidwa ulemu, kaya anthuwo ndi olemera, osauka, odwaladwala kapena okalamba. (1 Pet. 2:17) Makamaka amene ali ndi udindo, monga bambo, makolo ndi akulu mumpingo, ayenera kulemekeza anthu amene akuwayang’anira ndi kuwathandiza kuti asamadzione kukhala osafunika. Potsindika kuti zimenezi n’zofunika kwa Akhristu onse, Baibulo limati: “Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake. Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.”—Aroma 12:10.
Sonyezani Ulemu Polambira
17. Kodi Malemba akutiphunzitsa chiyani pankhani yosonyeza ulemu tikamalambira Yehova?
17 Tifunikira kusonyeza ulemu wapadera polambira Yehova. Lemba la Mlaliki 5:1 limati: “Samalira phazi lako popita ku nyumba ya Mulungu.” Mose ndi Yoswa analamulidwa kuvula nsapato zawo pamalo opatulika. (Eks. 3:5; Yos. 5:15) Iwo amafunika kuchita zimenezi posonyeza ulemu. Ansembe achiisiraeli analamulidwa kuvala zovala za miyendo kuti ‘abise maliseche.’ (Eks. 28:42, 43) Zimenezi zinathandiza kuti azivala modzilemekeza akamatumikira pa guwa la nsembe. Aliyense m’banja la wansembe amafunikira kutsatira malamulo a Mulungu okhudza kudzilemekeza.
18. Kodi timasonyeza bwanji ulemu polambira Yehova?
18 Motero, monga olambira a Yehova tifunikira kusonyeza ulemu m’mbali zonse za moyo wathu. Kuti ena azitipatsa ulemu ifenso tiyenera kuwapatsa ulemu. Tisasonyeze ulemu mwachiphamaso kapena mongodzionetsera chabe. Koma uzikhala ulemu wochokera mu mtima chifukwa Mulungu amaona mumtima. (1 Sam. 16:7; Miy. 21:2) Tiyenera kukhala aulemu nthawi zonse, m’zochita zathu ndi pochita zinthu ndi ena. Ndipo tiyeneranso kumadzilemekeza. Ndithudi, tizisonyeza ulemu polankhula ndi pochita zinthu zina. Pankhani ya khalidwe lathu, kavalidwe ndi kudzikongoletsa, tifunikira kutsatira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu.” (2 Akor. 6:3, 4) Mwa njira imeneyi ‘timakometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu, Mulungu, m’zinthu zonse.’—Tito 2:10.
Pitirizani Kutsanzira Mulungu Posonyeza Ulemu
19, 20. (a) Kodi njira yabwino yolemekezera ena ndi iti? (b) Pankhani yosonyeza ulemu, kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?
19 Akhristu odzozedwa omwe ndi “akazembe m’malo mwa Khristu,” amasonyeza ulemu. (2 Akor. 5:20) A “nkhosa zina” amene amathandiza mokhulupirika odzozedwawa, ndi nthumwi zolemekezeka za Ufumu wa Mesiya. Akazembe kapena nthumwi zimalankhula molimba mtima ndiponso mwaulemu poimira boma lawo. Motero, tiyenera kulankhulanso mwaulemu ndi molimba mtima poimira Ufumu wa Mulungu. (Aef. 6:19, 20) Ndipo tikamalalikira “uthenga wabwino wa zinthu zabwino,” timakhala tikulemekeza anthu ena.—Yes. 52:7.
20 Tiyeni tiyesetse kulemekeza Mulungu mwakuchita zinthu mogwirizana ndi ulemu wake. (1 Pet. 2:12) Nthawi zonse tizim’lemekeza Mulungu kwambiri, tizilemekeza kulambira kwathu ndi Akhristu anzathu. Ndipo Yehova yemwe ndi Mulungu wam’kulu ndi waulemerero, adzasangalala tikamam’lambira mwaulemu.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu a Davide a pa Salmo 8 amaloseranso za Yesu Khristu munthu wangwiro.—Aheb. 2:5-9.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi kumvetsa bwino ulemerero ndi ukulu wa Yehova kuyenera kutikhudza bwanji?
• Kodi tikuphunzira chiyani za kusonyeza ulemu tikaona mmene Yesu anachitira ndi munthu wakhate?
• Kodi tingasonyeze bwanji ulemu polambira Yehova?
[Chithunzi patsamba 12]
Kodi Yehova analemekeza Abele motani?
[Chithunzi patsamba 14]
Ntchito zazikulu za Yehova zimaonekera pa chakudya monga buledi
[Chithunzi patsamba 15]
Mukaona mmene Yesu anachitira ndi munthu wakhate, kodi mukuphunzirapo chiyani pankhani yosonyeza ulemu?
[Chithunzi patsamba 16]
Tifunika kulemekeza Yehova polambira