Anthu Onse Alengeze Ulemerero wa Yehova
“M’patseni Yehova ulemerero ndi mphamvu. M’patseni Yehova ulemerero wa dzina lake.”—SALMO 96:7, 8.
1, 2. Kodi n’chiyani chimene chikupatsa Yehova ulemerero, ndipo ndani amene akulimbikitsidwa kupereka nawo ulemerero umenewo?
DAVIDE, mwana wa Jese, anakula monga mbusa ku dera la ku Betelehemu. Ayenera kuti nthaŵi zambiri ankayang’anitsitsa kumwamba kodzaza ndi nyenyezi zambirimbiri usiku, kunja kuli zii, akuyang’anira ziweto za atate wake m’malo odyetserako nkhosa amene ankakhala kwaokha. Mosakayikira, anakumbukira zinthu zosaiŵalika zimenezi pamene, motsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, analemba ndi kuyimba mawu ochititsa chidwi a mu Salmo 19, amene amati: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Muyeso wawo wapitirira pa dziko lonse lapansi, ndipo mawu awo ku malekezero a m’dziko muli anthu.”—Salmo 19:1, 4.
2 Zakumwamba zochititsa chidwi zolengedwa ndi Yehova zimalengeza ulemerero wa Yehova usana ndi usiku popanda kulankhula, popanda mawu, popanda liwu lawo kumveka. Chilengedwe sichisiya kulengeza ulemerero wa Mulungu, ndipo tikaganizira kuti umboni wopanda mawu umenewu umapita “pa dziko lonse lapansi” kuti anthu onse okhalamo awuone, zimatichititsa kuzindikira kuti ndife ochepa mphamvu kwambiri. Komabe, umboni wopanda mawu wa chilengedwe si wokwanira. Anthu okhulupirika akulimbikitsidwa kulengeza nawo umboni umenewu ndi mawu awo. Wolemba salmo wina, amene dzina lake silinatchulidwe, anauza olambira okhulupirika kuti: “M’patseni Yehova ulemerero ndi mphamvu. M’patseni Yehova ulemerero wa dzina lake.” (Salmo 96:7, 8) Anthu amene ali ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova amasangalala kumvera langizo limeneli. Koma kodi kupatsa Mulungu ulemerero kumatanthauza chiyani?
3. N’chifukwa chiyani anthu amapatsa Mulungu ulemerero?
3 Kupatsa Mulungu ulemerero kumafuna zambiri, osati mawu okha. Aisrayeli mu nthaŵi ya Yesaya analemekeza Mulungu ndi milomo yawo, koma ambiri a iwo sankachita zimenezi kuchokera mumtima. Kudzera mwa Yesaya, Yehova anati: “Anthu aŵa ayandikira ndi Ine ndi m’kamwa mwawo, nandilemekeza ndi milomo yawo, koma mtima wawo uli kutali ndi Ine.” (Yesaya 29:13) Mawu olemekeza Mulungu alionse amene anthu ameneŵa ankanena anali opanda tanthauzo. Kuti akhale atanthauzo, mawu olemekeza Mulungu ayenera kuchokera mu mtima wokonda kwambiri Yehova ndipo munthuyo ayenera kuvomereza moona mtima kuti Yehova ali ndi ulemerero wapadera. Yehova yekha ndiye Mlengi. Iye ndi Wamphamvuyonse, Wachilungamo, kuchimake kwa chikondi. Iye ndiye gwero la chipulumutso chathu ndiponso Wolamulira Wamkulu woyenerera, amene aliyense yemwe ali kumwamba ndi padziko lapansi ayenera kumugonjera. (Chivumbulutso 4:11; 19:1) Ngati timakhulupiriradi zimenezi, tiyeni tim’patse ulemerero ndi mtima wathu wonse.
4. Kodi Yesu anatipatsa malangizo otani a mmene tingalemekezere Mulungu, ndipo kodi tingawakwaniritse motani?
4 Yesu Kristu anatiuza mmene tingalemekezere Mulungu. Iye anati: “Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga.” (Yohane 15:8) Kodi timabala chipatso chambiri motani? Choyamba, mwakugwira nawo ndi mtima wonse ntchito yolalikira “uthenga . . . wabwino wa Ufumu” ndipo mwakutero timathandizana ndi zolengedwa zonse “kunena” “zosaoneka” za Mulungu. (Mateyu 24:14; Aroma 1:20) Kuwonjezera pamenepo, tikamachita zimenezi tonsefe timatengako mbali, mwachindunji kapena ayi, popanga ophunzira atsopano amene nawonso amalemekeza Yehova Mulungu. Chachiŵiri, timakulitsa chipatso chimene mzimu woyera umayambitsa mwa ife, ndipo timayesetsa kutsanzira makhalidwe abwino kwambiri a Yehova Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23; Aefeso 5:1; Akolose 3:10) Zotsatirapo zake n’zakuti khalidwe lathu tsiku lililonse limalemekeza Mulungu.
“Ku Dziko Lonse Lapansi”
5. Fotokozani mmene Paulo anagogomezera za udindo wa Akristu wolemekeza Mulungu mwa kuuza ena chikhulupiriro chawo.
5 M’kalata imene Paulo analembera Aroma, anagogomezera za udindo umene Akristu ali nawo wolemekeza Mulungu mwa kuuza ena chikhulupiriro chawo. Nkhani yaikulu m’buku la Aroma ndi yakuti anthu amene angapulumutsidwe ndi okhawo amene amasonyeza chikhulupiriro mwa Yesu Kristu. M’chaputala 10 cha bukuli, Paulo anasonyeza kuti Aisrayeli a mu nthaŵi yake anali akuyeserabe kukhala olungama mwa kutsatira Chilamulo cha Mose, koma “Kristu a[na]li chimaliziro cha lamulo.” Choncho, Paulo anati: “Ngati udzavomereza mkamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.” Kuyambira nthaŵi imeneyo kupita m’tsogolo, “kulibe kusiyana Myuda ndi Mhelene; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa iye; pakuti, amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”—Aroma 10:9-13.
6. Kodi Paulo anagwiritsa ntchito bwanji Salmo 19:4?
6 N’zosadabwitsa kuti kenaka Paulo anafunsa kuti: “Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanam’khulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?” (Aroma 10:14) Ponena za Aisrayeli, Paulo anati: “Sanamvera uthenga wabwino onsewo.” N’chifukwa chiyani Aisrayeli sanamvere? Sanamvere chifukwa cha kusoŵa chikhulupiriro, osati chifukwa cha kusoŵa mpata. Paulo anasonyeza zimenezi mwa kugwira mawu amene ali pa Salmo 19:4 n’kuwagwiritsa ntchito pokamba za ntchito yachikristu yolalikira mmalo mwa umboni wopanda mawu wa chilengedwe. Iye anati: “Indetu, liwu lawo linatulukira ku dziko lonse lapansi, ndi maneno awo ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.” (Aroma 10:16, 18) Indedi, monga momwe chilengedwe chopanda moyo chimalemekezera Yehova, Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino analalikira uthenga wabwino wa chipulumutso kulikonse ndipo analemekeza Mulungu “ku dziko lonse lapansi.” M’kalata yake yopita kwa Akolose, Paulo anafotokozanso mmene uthenga wabwino unafalikira. Anati uthenga wabwino unali utalalikidwa kwa “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.”—Akolose 1:23.
Mboni Zachangu
7. Malinga ndi zimene Yesu ananena, kodi Akristu ali ndi udindo wotani?
7 Mwachiwonekere, Paulo analemba kalata yake yopita kwa Akolose patapita zaka pafupifupi 27 Yesu Kristu atafa. Kodi zikanatheka bwanji kuti ntchito yolalikira ifalikire mpaka ku Kolose mu nthaŵi yochepa ngati imeneyo? Zinatheka chifukwa Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anali achangu, ndipo Yehova anadalitsa changu chawocho. Yesu anali ataneneratu kuti otsatira ake adzakhala alaliki achangu pamene ananena kuti: “Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Kuwonjezera pa ulosi umenewo, Yesu anapereka lamulo limene linalembedwa m’mavesi omalizira a uthenga wabwino wa Mateyu loti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Patangopita nthaŵi yochepa Yesu atakwera kumwamba, otsatira ake anayamba kukwaniritsa mawu amenewo.
8, 9. Malinga ndi buku la Machitidwe, kodi Akristu anachita chiyani potsatira malamulo a Yesu?
8 Mzimu woyera utatsanulidwa pa Pentekoste wa mu 33 C.E., chinthu choyamba chimene otsatira okhulupirika a Yesu anachita chinali kupita kokalalikira, kukauza anthu amene anasonkhana ku Yerusalemu “zazikulu za Mulungu.” Kulalikira kwawoko kunali kogwira mtima kwambiri, ndipo “anthu ngati zikwi zitatu” anabatizidwa. Ophunzirawo anapitiriza kulemekeza Mulungu pamaso pa anthu onse ndiponso mwachangu, ndipo zotsatirapo zake zinali zabwino.—Machitidwe 2:4, 11, 41, 46, 47.
9 Pasanapite nthaŵi yaitali, atsogoleri achipembedzo anamva zimene Akristuwo anali kuchita. Posasangalala ndi kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane, anauza atumwi aŵiriwo kuti asiye kulalikira. Atumwiwo anayankha kuti: “Sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.” Atawaopseza kenaka n’kuwamasula, Petro ndi Yohane anabwerera kwa abale awo, ndipo onse pamodzi anapemphera kwa Yehova. Molimba mtima anapempha Yehova kuti: “Patsani kwa akapolo anu alankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse.”—Machitidwe 4:13, 20, 29.
10. Kodi ndi chitsutso chotani chimene chinayamba, ndipo kodi Akristu oona anachita chiyani?
10 Pemphero limenelo linali logwirizana ndi cholinga cha Yehova, monga momwe zinadzaonekera patapita nthaŵi yochepa. Atumwiwo anamangidwa ndipo kenaka anamasulidwa mozizwitsa ndi mngelo. Mngeloyo anawauza kuti: “Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule m’kachisi kwa anthu onse mawu a Moyo umene.” (Machitidwe 5:18-20) Chifukwa chakuti atumwiwo anamvera, Yehova anapitiriza kuwadalitsa. Choncho, “masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.” (Machitidwe 5:42) Mwachiwonekere, chitsutso cholimba chinalephereratu kusiyitsa otsatira a Yesu kupatsa Mulungu ulemerero pamaso pa anthu.
11. Kodi Akristu oyambirira ankaiona bwanji ntchito yolalikira?
11 Posakhalitsa Stefano anamangidwa ndi kuponyedwa miyala mpaka kufa. Imfa yakeyo inayambitsa chizunzo choopsa ku Yerusalemu, ndipo ophunzira onse, kupatulapo atumwi, anakakamizika kuthaŵira kumadera ena. Kodi iwo analefuka chifukwa cha chizunzocho? Ayi. Timaŵerenga kuti: “Iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mawuwo.” (Machitidwe 8:1, 4) Changu chimenecho polengeza ulemerero wa Mulungu chinaonekera nthaŵi zambiri. M’buku la Machitidwe chaputala 9, timaŵerenga kuti Mfarisi wotchedwa Saulo wa ku Tariso akupita ku Damasiko kuti akayambitse chizunzo cha ophunzira a Yesu, anaona masomphenya a Yesu ndipo anachititsidwa khungu. Ku Damasiko, Ananiya anachiza khungu la Saulo mozizwitsa. Kodi chinthu choyamba chimene Saulo, amene anadzatchedwa mtumwi Paulo, anachita chinali chiyani? Nkhaniyo imati: ‘Pomwepo m’masunagoge analalikira Yesu, kuti iye ndiye Mwana wa Mulungu.’—Machitidwe 9:20.
Aliyense Ankalalikira Nawo
12, 13. (a) Malinga ndi zimene anena olemba mbiri, kodi n’chiyani chinali chochititsa chidwi mu mpingo woyambirira wachikristu? (b) Kodi buku la Machitidwe ndiponso zimene ananena Paulo zikugwirizana bwanji ndi zimene ananena olemba mbiri?
12 N’zodziŵika bwino kuti aliyense mu mpingo wachikristu woyambirira ankalalikira nawo. Ponena za Akristu m’masiku amenewo, Philip Schaff analemba kuti: “Mpingo uliwonse unali ndi cholinga chochita utumiki, ndipo Mkristu wokhulupirira aliyense anali mtumiki.” (History of the Christian Church) W. S. Williams anati: “Umboni wochuluka umene ulipo ukusonyeza kuti Akristu onse m’tchalitchi choyambirira, makamaka amene anali ndi mphatso yapadera [mphatso za mzimu], ankalalikira uthenga wabwino.” (The Glorious Ministry of the Laity) Iye ananenanso mosapita m’mbali kuti: “Yesu Kristu sanafune kuti kulalikira kukhale ntchito ya atumiki a udindo winawake okha.” Ngakhale Celsus, mdani wakale wa Chikristu, analemba kuti: “Anthu oomba nsalu pogwiritsa ntchito ubweya, osoka nsapato, ofufuta zikopa, ndi anthu wamba osaphunzira anali alaliki achangu a uthenga wabwino.”
13 Nkhani zochitikadi zimene zinalembedwa m’buku la Machitidwe zimasonyeza kuti mawu amenewo ndi oonadi. Pambuyo pa Pentekoste wa mu 33 C.E., mzimu woyera utatsanulidwa, ophunzira onse, amuna ndi akazi, analengeza pamaso pa anthu onse zinthu zazikulu za Mulungu. Pambuyo pa chizunzo chimene chinachitika Stefano ataphedwa, Akristu onse amene anabalalitsidwa m’madera akunja analengeza uthenga wabwino m’madera ambiri. Patatha zaka 28, Paulo analembera kalata Akristu onse Achihebri, osati kagulu ka atsogoleri achipembedzo kokha, ndipo anati: “Mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” (Ahebri 13:15) Pofotokoza mmene iye mwiniyo ankaionera ntchito yolalikira, Paulo anati: “Ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.” (1 Akorinto 9:16) Mwachiwonekere, Akristu okhulupirika onse a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino ankamva chimodzimodzi.
14. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa chikhulupiriro ndi kulalikira?
14 Zoonadi, Mkristu woona ayenera kugwira nawo ntchito yolalikira chifukwa ndi yogwirizana kwambiri ndi chikhulupiriro. Paulo anati: “Ndi mtima munthu akhulupira kutengapo chilungamo; ndi mkamwa avomereza kutengapo chipulumutso.” (Aroma 10:10) Kodi ndi kagulu kochepa kokha mu mpingo wachikristu, monga kagulu ka atsogoleri achipembedzo, kamene kali ndi chikhulupiriro, n’kukhala ndi udindo wolalikira? Ayi ndithu. Akristu oona onse amakulitsa chikhulupiriro cholimba mwa Ambuye Yesu Kristu ndipo amafuna kulengeza poyera chikhulupiriro chimenecho kwa ena. Akapanda kutero ndiye kuti chikhulupiriro chawo n’chakufa. (Yakobo 2:26) Chifukwa chakuti Akristu onse okhulupirika a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anasonyeza chikhulupiriro chawo mwa njira imeneyi, anthu ambiri anamva za dzina la Yehova ndipo analilemekeza kwambiri.
15, 16. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti ntchito yolalikira inapita patsogolo ngakhale kuti panali mavuto.
15 M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, Yehova anadalitsa anthu ake ndipo anawonjezeka ngakhale kuti anali ndi mavuto ochokera mkati ndi kunja kwa mpingo. Mwachitsanzo, m’buku la Machitidwe chaputala 6 analembamo za kusagwirizana kumene kunalipo pakati pa Akristu ongotembenuzidwa kumene olankhula Chihebri ndi olankhula Chigiriki. Atumwi anachitapo kanthu pa vuto limeneli. Zotsatirapo zake n’zimene timaŵerenga, zakuti: “Mawu a Mulungu anakula; ndipo chiŵerengero cha akuphunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.”—Machitidwe 6:7.
16 Kenaka panadzabuka kusamvana chifukwa cha ndale pakati pa Mfumu Herode Agripa ya ku Yudeya, ndi anthu a ku Turo ndi Sidoni. Anthu a m’mizinda imeneyo anachita mapangano a mtendere achinyengo ongofuna kum’sangalatsa Herode, ndipo chifukwa cha zimenezi Herode analankhula pamaso pa anthuwo. Anthu amene anasonkhana pamenepo anayamba kufuula kuti: “Ndiwo mawu a Mulungu, si a munthu ayi.” Nthaŵi yomweyo, mngelo wa Yehova anakantha Herode Agripa, ndipo anafa “chifukwa sanam’patsa Mulungu ulemerero.” (Machitidwe 12:20-23) Zinali zokhumudwitsa kwambiri kwa anthu amene anali kudalira atsogoleri a anthu! (Salmo 146:3, 4) Koma Akristu anapitiriza kulemekeza Yehova. Chifukwa cha kuchita zimenezo, “mawu a Mulungu anakula, nachulukitsa,” ngakhale kuti kunali mavuto a ndale oterowo.—Machitidwe 12:24.
Mmene Zinthu Zinalili Kalelo ndi Mmene Zilili Masiku Ano
17. Kodi m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anthu ambiri anayamba kuchita nawo chiyani?
17 Zoonadi, mu mpingo wachikristu wapadziko lonse m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino munali anthu achangu, olemekeza Yehova Mulungu. Akristu onse okhulupirika ankafalitsa nawo uthenga wabwino. Ena anakumana ndi anthu omvetsera, ndipo anawaphunzitsa kumvera zinthu zonse zimene Yesu analamula, monga mmene iye ananenera. (Mateyu 28:19, 20) Zotsatirapo zake n’zakuti mpingowo unakula, ndipo anthu ambiri anayamba kupatsa Yehova ulemerero monga momwe anachitira Mfumu Davide wakale. Onse anagwirizana ndi mawu ouziridwa akuti: “Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthaŵi zonse. Pakuti chifundo chanu cha pa ine n’chachikulu.”—Salmo 86:12, 13.
18. (a) Kodi pali kusiyana kotani pakati pa Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino ndi Matchalitchi Achikristu masiku ano? (b) Kodi tidzakambirana chiyani mu nkhani yotsatira?
18 Poona zimenezi, mawu amene ananena pulofesa wa maphunziro apamwamba a zaumulungu Allison A. Trites ndi ofunika kuwaganizira. Poyerekezera Matchalitchi Achikristu amasiku ano ndi Chikristu cha m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, iye anati: “Masiku ano mipingo imakula chifukwa cha kubadwa kwa anthu (pamene ana a m’banja lina la mu mpingowo ayamba kusonyeza chikhulupiriro) kapena chifukwa cha kusamuka (pamene munthu asamuka ku mpingo wa kudera kwina n’kupita ku mpingo wa kudera kwina.) Koma m’buku la Machitidwe, mpingo unali kukula chifukwa cha kutembenuza anthu, chifukwa mpingowo unali ukungoyamba kumene ntchito yake.” Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Chikristu choona sichikukulanso m’njira imene Yesu ananena kuti chiyenera kukulira? Ayi. Akristu oona masiku ano akulemekeza Mulungu pamaso pa anthu onse mwachangu mofanana ndi Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Tiona zimenezi mu nkhani yotsatira.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi timalemekeza Mulungu m’njira ziti?
• Kodi Paulo anagwiritsa ntchito bwanji Salmo 19:4?
• Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa chikhulupiriro ndi kulalikira?
• Kodi n’chiyani chinali chochititsa chidwi mu mpingo wachikristu wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino?
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Kumwamba nthaŵi zonse kumachitira umboni za ulemerero wa Yehova
[Mawu a Chithunzi]
Mwachilolezo cha Anglo-Australian Observatory, chojambulidwa ndi David Malin
[Zithunzi patsamba 10]
Pali kugwirizana kwakukulu pakati pa ntchito yolalikira ndi pemphero