PHUNZIRO 10
Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakuthandizeni Bwanji?
Kodi munaitanidwapo kumsonkhano wa Mboni za Yehova? Ngati simunayambe mwapitako, mwina mukhoza kumachita mantha mukaganiza zopitako. Mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi pamisonkhano imeneyi pamachitika zotani? N’chifukwa chiyani ili yofunika? Nanga n’chifukwa chiyani ndikuyenera kupezekapo?’ M’phunziroli, muona mmene misonkhano ingakuthandizireni pa moyo wanu komanso mmene ingakuthandizireni kuti mukhale mnzake wa Mulungu.
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kusonkhana?
Wolemba Baibulo wina anasonyeza kuti kusonkhana ndi kofunika kwambiri. Iye anati: “Pamsonkhano, ndidzatamanda Yehova.” (Salimo 26:12) Nawonso a Mboni za Yehova amasangalala kwambiri ndi misonkhano. Padziko lonse lapansi, iwo amasonkhana mlungu uliwonse kuti atamande Mulungu, aimbe nyimbo ndiponso apemphere. Ndipo maulendo angapo chaka chilichonse, iwo amalambira Mulungu pamisonkhano ikuluikulu.
2. Kodi mudzaphunzira chiyani pamisonkhano yathu?
Pamisonkhano, timakambirana kwambiri Mawu a Mulungu, kuwafotokozera “ndi kumveketsa tanthauzo lake.” (Werengani Nehemiya 8:8.) Mukadzapezeka pamisonkhano, mudzaphunzira za Yehova ndiponso makhalidwe ake abwino. Mukamaphunzira zinthu zambiri zosonyeza kuti Yehova amakukondani, nanunso mudzayamba kumukonda. Mudzaphunziranso mmene Mulungu angakuthandizireni kuti mukhale wosangalala.—Yesaya 48:17, 18.
3. Kodi anthu amene mungakumane nawo pamisonkhano yathu angakuthandizeni bwanji?
Yehova akutiuza kuti “tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.” (Aheberi 10:24, 25) Pamisonkhano yathu, mudzakumana ndi anthu amene amakondanadi zenizeni ndipo mofanana ndi inuyo, amafuna kuphunzira zambiri zokhudza Mulungu. Mudzamva anthu akukambirana mfundo zolimbikitsa zochokera m’Baibulo. (Werengani Aroma 1:11, 12.) Mudzathanso kucheza ndi anthu ena omwe akukwanitsa kulimbana ndi mavuto amene anthu apabanja komanso amene sali pabanja amakumana nawo. Apatu tangoona zifukwa zochepa chabe zimene Yehova amatiuzira kuti tizisonkhana nthawi zonse.
FUFUZANI MOZAMA
Onani mmene misonkhano ya Mboni za Yehova imachitikira ndiponso chifukwa chake tiyenera kuyesetsa kupezekapo.
4. Misonkhano ya Mboni za Yehova
Mu nthawi ya atumwi, Akhristu ankasonkhana nthawi zonse kuti alambire Yehova. (Aroma 16:3-5) Werengani Akolose 3:16, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Akhristu oyambirira ankalambira bwanji Yehova?
Masiku ano, a Mboni amasonkhananso nthawi zonse. Kuti muone mmene amapangira misonkhano yawo, onerani VIDIYO. Kenako onani chithunzi chosonyeza mmene misonkhano imachitikira, n’kukambirana mafunso otsatirawa:
Kodi zimene zimachitika pa Nyumba ya Ufumu zikufanana bwanji ndi zimene munawerenga pa Akolose 3:16?
Muvidiyoyi kapena pachithunzipa, ndi zinthu ziti zokhudza misonkhano zimene zakusangalatsani?
Werengani 2 Akorinto 9:7, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani misonkhano ya Mboni za Yehova imakhala yaulere?
Limodzi ndi mphunzitsi wanu, onani zina mwa nkhani zimene zidzakambidwe pamsonkhano umodzi wa mlungu uno.
Ndi nkhani iti pamsonkhanowu imene yakusangalatsani kapena imene mukuona kuti ingakuthandizeni kwambiri?
Kodi mukudziwa?
Pa jw.org, mukhoza kupeza malo amene misonkhano imachitikira komanso nthawi imene imachitikira padziko lonse.
Pamisonkhano yathu pamakhala nkhani, zitsanzo ndi mavidiyo. Misonkhano imayamba ndiponso kutha ndi nyimbo ndi pemphero
Pa nthawi ina anthu amakhala ndi mwayi wolankhulapo
Aliyense ndi wolandiridwa—mabanja, anthu omwe sali pabanja, achikulire ndiponso ana
Misonkhano yathu ndi yaulere. A Mboni za Yehova salipiritsa polowa komanso sayendetsa mbale ya zopereka
5. Pamafunika khama kuti muzipezeka pamisonkhano
Taganizirani chitsanzo cha banja la Yesu. Kuti akapezeke pamsonkhano wapachaka, ankafunika kuyenda mtunda wa makilomita 100 m’dera lamapiri kuchokera ku Nazareti kukafika ku Yerusalemu. Werengani Luka 2:39-42, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi mukuganiza kuti pankafunika khama kuti ayende ulendo wopita ku Yerusalemu umenewu?
N’chifukwa chiyani mungafunike kuchita khama kuti mupezeke pamisonkhano?
Kodi mukuganiza kuti kuchita khama limenelo ndi kothandiza? N’chifukwa chiyani mukutero?
Baibulo limanena kuti kusonkhana ndi kofunika kwambiri. Werengani Aheberi 10:24, 25, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani tiyenera kusonkhana nthawi zonse?
ZIMENE ENA AMANENA: “Kusonkhana ndi anthu ena si kofunika kwenikweni. Kuphunzira Baibulo pawekha n’kokwanira.”
Tchulani lemba kapena chitsanzo cha m’Baibulo chimene chimatithandiza kudziwa zimene Yehova amafuna.
ZOMWE TAPHUNZIRA
Kupezeka pamisonkhano kungakuthandizeni kuti muphunzire zambiri zokhudza Yehova, muzimukonda kwambiri monga mnzanu wapamtima ndiponso kuti muzimulambira limodzi ndi anthu ena.
Kubwereza
N’chifukwa chiyani Yehova amatilimbikitsa kuti tizisonkhana?
Kodi mudzaphunzira zotani pamisonkhano ya Mboni za Yehova?
Kodi mukuganiza kuti kupezeka pamisonkhano kungakuthandizeni m’njira zinanso ziti?
ONANI ZINANSO
Ngati mukuchita mantha kupezeka pamsonkhano, onani mmene munthu wina amene ankamvanso chimodzimodzi anayambira kukonda misonkhano.
Onani zimene zinachititsa kuti mnyamata wina asangalale ndi misonkhano komanso asasiye kupezekapo.
Onani mmene ena amaonera nkhani yopezeka pamisonkhano.
“N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupezeka Pamisonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani mmene chigawenga china chinasinthira pambuyo popezeka pamsonkhano wa Mboni za Yehova.
“Ndinkayenda ndi Mfuti Kulikonse” (Nsanja ya Olonda, July 1, 2014)