Thaŵirani mwa Yehova
‘Ndathaŵira mwa inu, Yehova.’—SALMO 31:1, NW.
1. Kodi lemba la Salmo 31 limasonyeza motani chidaliro m’kukhoza kwa Yehova kupereka pothaŵira?
LIWU lomveka bwino likuimba ponena za munthu amene, ngakhale kuti ali wofooka m’maganizo ndi thupi, akutembenukira kwa Yehova. Chikhulupiriro chimalakika, akutero mawu a nyimbo yopatulika imeneyo. M’mikono yomayembekezera ya Wamphamvuyonse, munthu ameneyu akupeza chitetezo kwa ozunza omlondalonda. ‘Ndathaŵira mwa inu, Yehova,’ likutero salmo lake. “Ndisakhaletu wamanyazi nthaŵi zonse. M’chilungamo chanu perekani pothaŵira panga.”—Salmo 31:1, NW.
2. (a) Kodi chidaliro chathu mwa Yehova monga ngaka yathu chiyenera kuzikidwa pamizati iŵiri iti? (b) Kodi Yehova ali Mulungu wamtundu wotani?
2 Wamasalmoyo ali ndi pothaŵira pamodzi—pabwino koposa! Zivute zitani, chowonadi nchakuti: Yehova ndiye ngaka yake, linga lake. Chidaliro chake nchozikidwa pamizati iŵiri yotsimikizirika. Woyamba, chikhulupiriro chake, chimene Yehova sadzachichititsa manyazi, ndipo wachiŵiri, chilungamo cha Yehova, kutanthauza kuti Iye sadzasiyiratu konse mtumiki Wake. Yehova sali Mulungu amene amachititsa manyazi atumiki ake okhulupirika; iye samaswa lonjezo lake. Mmalo mwake, ali Mulungu wa chowonadi ndipo amapereka mfupo kwa awo omwe amamdalira ndi mtima wonse. Potsirizira pake, chikhulupiriro chidzafupidwa! Chipulumutso chidzadza!—Salmo 31:5, 6.
3. Kodi ndimotani mmene wamasalmo akulemekezera Yehova?
3 Akumapeka nyimbo yake ndi maimbidwe a mawu osiyanasiyana amene akuyamba ndi mawu odandaula ndi achisoni ndi kufika pachimake chosonyeza chidaliro, wamasalmoyo akupeza nyonga yamkati. Iye akulemekeza Yehova kaamba ka chikondi Chake chokhulupirika. “Wolemekezeka Yehova,” iye akuimba motero, “pakuti anandichitira chifundo chake chodabwitsa m’mudzi walinga.”—Salmo 31:21.
Gulu Lalikulu la Oimba la Olengeza Ufumu
4, 5. (a) Kodi ndigulu lalikulu la oimba liti limene likutamanda Yehova lerolino, ndipo kodi iwo achita zimenezo motani m’chaka chautumiki chathachi? (Onani tchati pamasamba 12-15.) (b) Kodi chiŵerengero cha opezeka pa Chikumbutso chikusonyeza motani kuti pali anthu ena ambiri ofuna kugwirizana ndi gulu la oimba la olengeza Ufumu? (Onani tchati.) (c) Kodi ndikagulu kati mumpingo wanu kamene kangakhoze kugwirizana ndi gulu la oimbalo?
4 Lerolino, mawu a salmo limenelo akhala ndi tanthauzo lowonjezereka. Nyimbo zotamanda Yehova sizingaletsedwe ndi wotsutsa woipa aliyense, tsoka lachilengedwe lililonse, kapena mkhalidwe woipa uliwonse wa zachuma; ndithudi, kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova kwakhala kwabwino koposa kwa anthu ake. Kuzungulira dziko lonse m’chaka chatha chautumiki, gulu lalikulu la oimba, la anthu okwanira 4,709,889 m’maiko 231, linaimba nyimbo ya uthenga wa Ufumu wa Mulungu. Boma lakumwamba la Yehova lolamuliridwa ndi Kristu Yesu lili pothaŵira pamene sipadzawagwiritsa mwala. Chaka chatha, olengeza Ufumu ameneŵa a m’mipingo yokwanira 73,070 anathera chiwonkhetso cha maola 1,057,341,972 m’ntchito ya kulengeza. Zimenezi zachititsa anthu 296,004 kusonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi. Ndipo mmene kunaliri kodabwitsa kwambiri nanga kwa opezeka pa Msonkhano Wamitundu Yonse wa Chiphunzitso Chaumulungu ku Kiev, Ukraine, August wapita. Anaona mbiri ikupangika, akumachitira umboni ubatizo waukulu koposa umene sunachitikepo wa Akristu owona! Monga momwe kunanenedweratu pa Yesaya 54:2, 3, anthu a Mulungu akufalikira ponseponse ndi ziŵerengero zosayerekezereka.
5 Komabe, nzika zina zofunitsitsa za Ufumu wa Mulungu zikuyembekezera kugwirizana ndi gulu la oimbalo. Chaka chatha, pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu panapezeka chiwonkhetso cha anthu ochuluka okwanira 11,865,765. Tikhulupirira kuti ambiri mwa ameneŵa adzayeneretsedwa kuimba nyimbo Yaufumu kukhomo ndi khomo mkati mwa chaka chino chautumiki. Ha, mmene chiyembekezo chimenecho chiyenera kukwiyitsira mdani wa chowonadi, Satana Mdyerekezi!—Chivumbulutso 12:12, 17.
6, 7. Fotokozani mmene mwamuna wina mothandizidwa ndi Yehova anagonjetsera kusautsidwa kwake ndi ziŵanda.
6 Satana adzayesa kutsekereza ena kuti asawonjezere mawu awo pagulu lalikulu la oimba limenelo. Mwachitsanzo, ofalitsa ku Thailand amapeza anthu ambiri omawonjezereka akusautsidwa ndi ziŵanda. Komabe, ambiri owona mtima amasulidwa mothandizidwa ndi Yehova. Atachezera sing’anga wina chifukwa cha kukopeka, mwamuna wina anakhala akulamuliridwa ndi ziŵandazo kwa zaka khumi. Iye anayesayesa kumasuka ku ulamulirowo mothandizidwa ndi mtsogoleri wachipembedzo, koma sanawongokere kwenikweni. Mtumiki wanthaŵi yonse wa Mboni za Yehova anayambitsa phunziro Labaibulo kwa mwamunayo namphunzitsa kuchokera m’Baibulo njira yokha yomasukira kuulamuliro wa ziŵanda—kupeza chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi, kukhulupirira Yehova Mulungu, ndi kumchonderera m’pemphero.—1 Akorinto 2:5; Aefeso 4:6, 7; 1 Timoteo 2:3, 4.
7 Usiku wotsatira kukambitsirana kumeneku, mwamunayo analota atate wake wakufa, amene anamuwopseza ngati sakakhalanso wamatsenga. Banja lake linayamba kuvutika. Posafuna kupambutsidwa, mwamunayo anapitiriza maphunziro ake Abaibulo nayamba kumapezeka pamisonkhano. Pa lina la maphunziro amenewo, mpainiyayo anafotokoza kuti nthaŵi zina zinthu zogwiritsiridwa ntchito m’madzoma amatsenga zingapatse ziŵanda mpata wa kuvutitsa anthu amene akuyesayesa kumasuka kuulamuliro wawo. Mwamunayo anakumbukira kuti anali ndi mafuta amene ankawagwiritsira ntchito monga chithumwa. Iye panthaŵiyo anazindikira kuti anafunikira kuwataya. Kuyambira pamene anawataya, sanavutitsidwenso ndi mizimu yoipa. (Yerekezerani ndi Aefeso 6:13; Yakobo 4:7, 8.) Iye ndi mkazi wake akupita patsogolo bwino lomwe ndi phunziro lawo ndipo amapezeka nthaŵi zonse pamisonkhano kulandira malangizo Abaibulo.
8, 9. Kodi nzopinga zina ziti zimene olengeza Ufumu ena agonjetsa?
8 Zopinga zina zingatsekereze mawu a mbiri yabwino. Chifukwa cha mkhalidwe wa zachuma wosautsa kwambiri m’Ghana, antchito ambiri achotsedwa ntchito. Mitengo ya zinthu yakwera kwambiri, ikumakuchititsa kukhala kovuta kwambiri kugula zofunika za moyo zokwanira. Kodi anthu a Yehova akhala akupirira motani? Mwa kudalira Yehova, osati iwo eni. Mwachitsanzo, tsiku lina mwamuna wina anasiya invulopu yomata polandirira alendo pa ofesi yanthambi. Mu invulopumo munali $200 [ya United States], kapena malipiro a miyezi itatu. Invulopuyo inachokera kwa munthu wosadziŵika wopereka mphatsoyo, koma papepala lokuta ndalamazo panali mawu awa: “Ndinachotsedwa pantchito yanga, koma Yehova wandipatsa ntchito ina. Ndiyamikira kwambiri iye ndi Mwana wake, Kristu Yesu. Kuti ndithandizire kufalitsidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu mapeto asanadze, ndikutumiza chopereka changa chochepa.”—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 9:11.
9 Kupezeka pamisonkhano kumathandizira kuphunzitsa awo amene amagwirizana ndi gulu lalikulu la oimba chitamando kwa Yehova. (Yerekezerani ndi Salmo 22:22.) Chotero, kuchigawo cha kummwera kwa Honduras, kuli mpingo wotchedwa El Jordán. Kodi nchiyani chimene chili chapadera ndi kagulu kakang’ono kameneka? Ndicho kupezeka kwawo pamisonkhano mokhulupirika. Mwa ofalitsa 19, okwanira 12 amawoloka mtsinje waukulu kuti akapezeke pamisonkhano mlungu uliwonse. Limeneli silili vuto lalikulu m’chilimwe, popeza amawoloka mtsinjewo pamiyala yowolokera. Komabe, m’nyengo yadzinja, mikhalidwe imasintha. Umene unali mtsinje wosawopsa umakhala chimtsinje chosefukira chomakokolola zonse zimene chipeza. Kuti alake chopinga chimenechi, abale ndi alongo ayenera kukhala odziŵa kusambira. Asanawoloke, amaika zovala zawo za kumsonkhano mu tina (chotengera chachitsulo) ndiyeno amachikuta ndi thumba la pulasitiki. Wosambira wamphamvu koposa amagwiritsira ntchito tina monga choyandamitsa ndi kutsogolera gululo akumawoloka. Atafika tsidya linalo, amadzipukuta, kuvala zovala, ndi kufika pa Nyumba Yaufumu ali okondwa ndi audongodi!—Salmo 40:9.
Ngaka Imene Tingakhalemo
10. Kodi nchifukwa ninji tingatembenukire kwa Yehova m’nthaŵi ya kupsinjika?
10 Kaya mwaukiridwa kotheratu ndi ziŵanda kapena muli wopsinjika maganizo chifukwa cha zinthu zina, Yehova angakhale ngaka yanu. Itanirani pa iye m’pemphero. Iye amamvetsera mosamalitsa ngakhale kubuula kosamveka kwa anthu ake. Wamasalmo anaona zimenezo kukhala zowona nalemba kuti: “Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga: mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga. Pakuti inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa; ndipo chifukwa cha dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni. Mundionjole m’ukonde umene ananditchera mobisika. Pakuti inu ndinu mphamvu yanga.”—Salmo 31:2-4.
11. Fotokozani chifukwa chake ngaka ya Yehova sili malo akanthaŵi.
11 Yehova amapereka osati pothaŵira pakanthaŵi chabe komanso ngaka yosatha kuukiridwa imene tingakhalemo mwachisungiko. Chitsogozo ndi malangizo ake sizinagwiritse mwala anthu ake. Mphamvu yaumulungu idzachititsa machenjera a Satana ndi magulu ake kukhala opanda pake. (Aefeso 6:10, 11) Pamene tidalira Yehova ndi mtima wonse iye adzatipulumutsa kumisampha ya Satana. (2 Petro 2:9) M’zaka zinayi zapitazo, ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova yatsegulidwa m’maiko pafupifupi 35. Ndiponso, kumadera a dziko kumene mikhalidwe ya m’chitaganya, ya zachuma, kapena yandale imadodometsa kulalikidwa kwa mbiri yabwino, anthu ena onga nkhosa asamukira kumene angafikiridwe momasuka. Amodzi a malo otero ndi Japan.
12. Kodi ndimotani mmene mpainiya wina ku Japan anachititsira Yehova kukhala ngaka yake?
12 M’Japan mwakhala anthu ochuluka odzagwira ntchito kwakanthaŵi ochokera kumaiko a kutsidya kwanyanja, ndipo mipingo yambiri ya zinenero zachilendo yakhazikitsidwa. Chokumana nacho cha mbale wina mumpingo wa abale olankhula Japanese chimasonyeza mmene munda wa chinenero chachilendo umenewu ulili wobala zipatso. Mbaleyo anafuna kukatumikira kumene kunali kusoŵa kokulirapo. Komabe, anali kale kuchititsa maphunziro Abaibulo khumi kumene anali. Mmodzi wa mabwenzi ake moseka anati: “Ngati udzapita kumene kuli kusoŵa kokulirapo, udzayenera kumachititsa maphunziro Abaibulo 20 kumeneko!” Analandira gawolo napita ku Hiroshima. Komabe, pambuyo pa miyezi inayi, anali ndi phunziro Labaibulo limodzi lokha. Tsiku lina anafikira mwamuna wina wa ku Brazil wolankhula Chipwitikizi chokha. Popeza kuti mbaleyo anali wosakhoza kukambitsirana ndi mwamunayo, anagula buku lophunzirira Chipwitikizi. Ataphunzira mawu angapo osavuta okambitsirana, anakachezeranso mwamunayo. Pamene mbaleyo anampatsa moni m’chinenero cha Chipwitikizi, mwamunayo anadabwa ndipo, akumwetulira, anatsegula chitseko namuuza kuloŵa. Phunziro Labaibulo linayambidwa. Posapita nthaŵi mbaleyo anali kuchititsa maphunziro okwanira 22, 14 m’Chipwitikizi, 6 m’Chispanish, ndi 2 olankhula Japanese!
Kulalikira ndi Chidaliro
13. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuwopa kuchititsidwa manyazi ndi munthu wina aliyense kukutumikira Yehova?
13 Anthu a Yehova mwachidaliro amaimba nyimbo Yaufumu ndi chikhulupiriro cholimba chakuti Yehova ndiye pothaŵira pawo. (Salmo 31:14) Iwo sadzachita manyazi—Yehova sadzawachititsa manyazi, pakuti adzakwaniritsa mawu ake. (Salmo 31:17) Mdyerekezi ndi magulu ake auchiŵanda adzachita manyazi. Popeza kuti anthu a Yehova apatsidwa ntchito yolalikira uthenga umene suli wochititsa manyazi, kulalikira kwawo sikuli chifukwa chowopa kuchititsidwa manyazi ndi anthu ena. Imeneyo sindiyo njira imene Yehova, kapena Mwana wake, amasonkhezerera anthu kumlambira Iye. Pamene mitima ya anthu idzala ndi chikhulupiriro ndi chiyamikiro kaamba ka ubwino ndi kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova, mkhalidwe wabwino wa mitima yawo ndiwo umene umasonkhezera milomo yawo kulankhula. (Luka 6:45) Chotero, nthaŵi iliyonse imene timathera muutumiki mwezi uliwonse, makamaka ngati nthaŵiyo ili malinga ndi kukhoza kwathu, ili bwino, siyochititsa manyazi. Kodi Yesu ndi Atate wake sanayamikire kwambiri tindalama tamtengo wochepa ta mkazi wamasiye?—Luka 21:1-4.
14. Kodi nchiyani chomwe munganene ponena za ntchito yaupainiya? (Onaninso tchati.)
14 Kwa unyinji womawonjezereka wa ofalitsa, kukhala a moyo wonse m’kulambira kwawo kumaphatikizapo kutumikira monga apainiya—chiŵerengero chapamwamba chaka chatha chinali 890,231! Ngati kupita patsogolo kwa chaka chatha kudzapitirizabe, mothekera chiŵerengero chimenechi chidzaposa pa 1,000,000. Chokumana nacho chotsatira chikusonyeza mmene mlongo wina ku Nigeria analoŵera pamzera wa apainiya. Iye akulemba kuti: “Pamene ndinali pafupi kumaliza sukulu yasekondale, ndinapita kukathandizira kuphika chakudya cha oloŵa sukulu ya apainiya ya Mboni za Yehova. Kumeneko ndinakumana ndi alongo aŵiri okalamba kuposa agogo anga aakazi. Pamene ndinadziŵa kuti anali apainiya amene anali kuloŵa sukuluyo, ndinaganiza kuti, ‘Ngati aŵiri aja akhoza kuchita upainiya, nchifukwa ninji ineyo sindingatero?’ Chotero pamene ndinamaliza sukulu, nanenso ndinakhala mpainiya wokhazikika.”
15. Kodi ndimwanjira yotani imene umboni wamwamwaŵi ungatsegulire ena njira yothaŵira mwa Yehova?
15 Sionse amene angachite upainiya, koma akhoza kuchitira umboni. Ku Belgium mlongo wina wazaka 82 anapita kukagula nyama. Iye anaona kuti mkazi wa wogulitsa nyama anali wovutika kwambiri ndi zipolowe za ndale zaposachedwa. Chotero mlongoyo anapereka trakiti lakuti Kodi Nchiyani Chimene Mboni za Yehova Zimakhulupirira? pamodzi ndi ndalama polipira. Pamene mlongoyo anabwerera kushopuko, mkazi wa wogulitsa nyama, mosazengereza konse, anafunsa zimene Baibulo limanena pa kuthekera kwa nkhondo yadziko yachitatu. Mlongoyo anamubweretsera buku la Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? Patapita masiku angapo, pamene mlongo wachikulireyo analoŵa m’sitoloyo, mkazi wa wogulitsa nyama anali ndi mafunso ochuluka. Mlongoyo anachitira chifundo mkaziyo; anangopempha kuphunzira naye Baibulo, ndipo mkaziyo anavomereza. Tsopano mkazi wa wogulitsa nyama akufuna kubatizidwa. Bwanji za wogulitsa nyama? Iye anaŵerenga trakitilo ndipo nayenso akuphunzira Baibulo tsopano.
‘Chuma cha Ukoma’
16. Kodi ndimotani mmene Yehova wasungira anthu ake chuma cha ukoma?
16 M’masiku otsiriza osautsa ameneŵa, kodi Yehova ‘sanachitire chifundo chodabwitsa’ awo amene athaŵira mwa iye? Monga atate wachikondi ndi wotetezera, Yehova wasungira ana ake a padziko lapansi chuma cha ukoma. Wakhala akuwatsanulira chimwemwe pamaso pa openyerera onse, monga momwe wamasalmo akunenera kuti: “Ha! kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuwopa inu, kumene munachitira iwo [akuthaŵira mwa, NW] inu, pamaso pa ana a anthu!”—Salmo 31:19, 21.
17-19. Ku Ghana, kodi kulembetsa ukwati mwalamulo kwa mwamuna wokalamba kunatulutsa zabwino zotani?
17 Chotero, anthu adziko amakhala mboni zoona ndi maso za kuwona mtima kwa awo amene akulambira Yehova, ndipo amadabwa. Mwachitsanzo, ku Ghana mwamuna wina wazaka 96 anapita ku ofesi ya wolembetsa maukwati napempha kuti ukwati wake wongokhalira limodzi wazaka 70 ulembetsedwe. Wolembetsa maukwatiyo anazizwa nafunsa kuti: “Kodi mukunenetsa kuti mukufuna kuchita zimenezo? Pausinkhu wanu?”
18 Mwamunayo anafotokoza kuti: “Ndifuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova ndi kukhala ndi phande m’ntchito yofunika koposa mapeto adziko asanadze—ntchito yolalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Ntchito imeneyi imatsogolera kumoyo wosatha. Mboni za Yehova zimamvera malamulo a boma, kuphatikizapo lamulo la kulembetsa ukwati. Chotero, chonde tandilemberani mtchato.” Mkuluyo anasoŵa chonena. Analemba mtchatowo, ndipo mwamuna wachikulireyo anapita ali wokondwa kuti wakhala ndi ukwati walamulo tsopano.—Yerekezerani ndi Aroma 12:2.
19 Pambuyo pa zimenezo, wolembetsa maukwati anasinkhasinkha za zinthu zimene anamva. “Mboni za Yehova . . . ntchito yofunika koposa . . . mapeto adziko . . . Ufumu wa Mulungu . . . moyo wosatha.” Pokhala wosadziŵa zimene zonsezi zinatanthauza m’moyo wa nkhalamba ya zaka 96, iye anasankha kufunafuna Mbonizo kuti apende nkhaniyo mowonjezereka. Anavomereza phunziro Labaibulo lapanyumba napita patsogolo. Lerolino, wolembetsa maukwati ameneyu ali Mboni yobatizidwa. Chotero, pamene timvera Yehova ngakhale m’zimene ena angaone kukhala nkhani zazing’ono, kungadzetse ukoma wochuluka kwa ife enife ndi awo amene ali mboni zoona ndi maso za khalidwe lathu.—Yerekezerani ndi 1 Petro 2:12.
20. Ku Myanmar, kodi ndimotani mmene kuwona mtima kwa mlongo wachichepere kunachititsira umboni wabwino kuperekedwa?
20 Achikulire amene alola chowonadi kuwaumba kukhala anthu owona mtima amapereka chitsanzo chabwino kwa achichepere m’dziko losawona mtimali. Ku Myanmar kumakhala mlongo wachichepere wotero. Iye ngwa m’banja wamba losauka ndi lodzichepetsa la ana khumi. Atate wake, opuma pantchito, ndimpainiya wokhazikika. Tsiku lina ali kusukulu, mlongoyo anapeza mphete ya diamondi, imene anapereka kwa mphunzitsi wake panthaŵi yomweyo. Kalasi litasonkhana tsiku lotsatira, mphunzitsiyo anauza kalasilo mmene mpheteyo inapezekera ndi kuperekedwa kuti ibwezeredwe kwa mwini wake. Ndiyeno anauza mlongo wachichepereyo kuimirira pamaso pa kalasi lonselo ndi kufotokoza chifukwa chimene anachitira zimenezi, podziŵa kuti ana ena akanasankha kuisunga. Mlongoyo anafotokoza kuti anali Mboni ya Yehova ndi kuti Mulungu wake samakonda kuba kapena mtundu uliwonse wa kusawona mtima. Zimenezo zinamveka pasukulu ponsepo, zikumapatsa mlongo wathu wachichepere mpata wabwino wa kuchitira umboni kwa aphunzitsi ndi ophunzira omwe.
21. Pamene achichepere adalira Yehova, kodi khalidwe lawo limamyambukira motani?
21 Ku Belgium mphunzitsi anapereka ndemanga yosangalatsa m’kalasi ponena za Mboni za Yehova. Iye anaona khalidwe la mmodzi wa ophunzira ake, yemwenso anali mlongo wachichepere , nati: “Tsopano ndili ndi lingaliro losiyana ponena za Mboni za Yehova. Malingaliro atsankhu anandichititsa kuganiza kuti iwo sangakhale ololera zinthu kwambiri. Iwo analidi ololera zinthu kwambiri, pamene kuli kwakuti sanalolere molakwa malamulo awo a mkhalidwe.” Chaka chilichonse aphunzitsi amafupa ophunzira awo abwino koposa. Ina ya zimenezo ndiyo mphotho ya kosi ya zamakhalidwe abwino. Kwa zaka zitatu zotsatizana, mphoto za magiredi atatu apamwamba zinaperekedwa kwa ana a Mboni za Yehova ndi mphunzitsi ameneyo. Zimatero ndi awo amene chidaliro chawo chokhulupirika chili mwa Yehova.—Salmo 31:23.
22. Kodi mfuu yomalizira yachipambano ya Salmo 31 njotani, ndipo imatithandiza motani m’masiku omalizira a dongosolo ili la zinthu?
22 Mfuu yomalizira yachipambano ya Salmo 31 ikumveka yakuti: “Limbikani, ndipo iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekezera Yehova.” (Salmo 31:24) Chotero, pamene tiyang’anizana ndi masiku omalizira a dongosolo loipa la Satana, mmalo motisiya, Yehova adzayandikira kwambiri pafupi nafe ndi kuika mphamvu yake mwa ife. Yehova ali wokhulupirika ndipo samalephera. Iye ndiye pothaŵira pathu; iye ndiye linga lathu.—Miyambo 18:10.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji mwachidaliro tingapange Yehova kukhala pothaŵira pathu?
◻ Kodi pali umboni wotani wakuti gulu lalikulu la oimba likuimba zitamando Zaufumu molimba mtima?
◻ Kodi nchifukwa ninji tili ndi chidaliro chakuti ukonde wa Satana sudzagwira anthu a Yehova?
◻ Kodi ndichuma chotani chimene Yehova wasungira awo othaŵira mwa iye?
[Tchati pamasamba 12-15]
LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 1993 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Awo amene amathaŵira mwa Yehova amapanga gulu lalikulu la oimba la olengeza Ufumu—4,709,889!
1. Senegal
2. Brazil
3. Chile
4. Bolivia