Kulapa Komwe Kumachiritsa
“PAMENE ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.” (Salmo 32:3, 4) Mawu odandaula ameneŵa, angakhale akusonyeza kuvutika mtima kwa Davide, Mfumu yamakedzana ya Israyeli, kuvutika chifukwa cha kubisa m’malo moulula tchimo lalikulu.
Davide anali munthu waluso kwambiri. Anali msilikali wolimba mtima, waluso la kulamulira, wandakatulo, ndi wanyimbo. Koma sanadzidalire yekha, anadalira Mulungu wake. (1 Samueli 17:45, 46) Anadziŵika monga munthu yemwe mtima wake unali “wangwiro ndi Yehova.” (1 Mafumu 11:4) Koma anachita tchimo limodzi loipa kwambiri. Mwina ndilo linali m’maganizo mwake polemba Salmo 32. Tingaphunzire zambiri mwa kuona zomwe zinam’pangitsa kuchimwa. Tizindikira mbuna zoyenera kupeŵa ndi kuona kufunika kwa kuulula machimo athu kuti tikhalebe abwenzi a Mulungu.
Mfumu Yokhulupirika Inachita Tchimo
Fuko la Aisrayeli linali pankhondo ndi Aamoni, koma Davide anali kunyumba kwake ku Yerusalemu. Tsiku lina akuyendayenda padenga la nyumba yake, anaona mkazi wokongola akusamba chapafupi ndi nyumba yakeyo. Analephera kudziletsa, nayamba kum’khumba. Atadziŵa kuti ndi Bateseba mkazi wa Uriya yemwe anali msilikali wa m’gulu lake lankhondo, Davide anamuitanitsa ndi kuchita naye chigololo. Patapita kanthaŵi, Bateseba anatumiza uthenga kwa Davide kuti ali ndi pakati.—2 Samueli 11:1-5.
Zinthu zinamuipira Davide. Ngati tchimo lawo liululika, chilango cha onsewo chinali imfa. (Levitiko 20:10) Choncho anakonza nzeru. Anaitanitsa Uriya mwamuna wa Bateseba yemwe anali kunkhondo. Atam’funsa mmene nkhondo inali kuyendera, Davide anauza Uriya kuti apite kunyumba kwake. Davide anakhulupirira kuti zimenezi zidzapangitsa Uriya kuoneka ngati bambo wa mwana yemwe Bateseba adzabale.—2 Samueli 11:6-9.
Koma Davide anakhumudwa poona kuti Uriya sanapite kwa mkazi wake. Uriya anati si nzeru kupita kunyumba pamene asilikali anzake anali kunkhondo yoopsa. Asilikali a Aisrayeli akapita kunkhondo, amuna ankapeŵa kugona ndi akazi ngakhale akazi awo enieni. Ankafunikira kukhala oyera mwamwambo. (1 Samueli 21:5) Ndiyeno Davide anaitanira Uriya chakudya ndi moŵa. Koma ngakhale ataledzera, sanapite kunyumba kwa mkazi wake. Kukhulupirika kwa Uriya, kunatsimikizira kukula kwa tchimo la Davide.—2 Samueli 11:10-13.
Zotsatira za tchimo lake lomwe, zinayamba kum’soŵetsa mtendere Davide. Posoŵa pogwira, anapeza njira imodzi yokha yobisira tchimolo. Anam’bweza Uriya kunkhondo limodzi ndi kalata kwa m’tsogoleri wa asilikaliwo Yoabu. Cholinga cha kalata yaifupiyo chinali chomveka bwino kuti: “Mumuike Uriya pa msongwe wa nkhondo yolimba, ndipo mum’lekerere kuti akanthidwe nafe.” Mwa kungolemba kalata, mfumu yamphamvuyo inaoneka ngati yabisa tchimo lake ndi kuphetsa Uriya.—2 Samueli 11:14-17.
Nyengo yomwe Bateseba analira mwamuna wake itangotha, Davide anamukwatira. Panapita nthaŵi ndipo mwana wawo anababwa. Panthaŵi yonseyi, Davide sanachitepo kanthu pa machimo ake. Mwina ankadzipezera zifukwa zoti alibe mlandu, monga kuti: Kodi Uriya sanafe imfa yolemekezeka ya kunkhondo monga anafera ena? Komanso, kodi anamvera mfumu pokana kupita kwa mkazi wake? ‘Mtima wonyenga,’ ungapeze zifukwa zosiyanasiyana pofuna kuchepetsa tchimo.—Yeremiya 17:9; 2 Samueli 11:25.
Zotsogolera ku Uchimo
Zinatheka bwanji kuti Davide munthu wokonda chilungamo achite chigololo ndi kupha? Mbewu za uchimo wake, ziyenera kuti zinafesedwa kwa kanthaŵi. N’zodabwitsa kuti Davide sanali ndi asilikali ake, kukawathandiza pankhondo yomenyana ndi adani a Yehova. M’malo mwake Davide anali kunyumba kwake kumangokhala, osaganizako m’pang’ono pomwe za nkhondoyo moti sanathenso kuleka kulakalaka mkazi wa msilikali wokhulupirika. Masiku ano, kutanganidwa ndi ntchito zauzimu m’mipingo ndi kugwira nawo ntchito yolalikira, n’chitetezo kwa Akristu oona.—1 Timoteo 6:12.
Mfumu ya Israyeli inauzidwa kukopera buku la Chilamulo ndi kumaliŵerenga tsiku ndi tsiku. Popereka chifukwa chake, Baibulo limati: “Kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake, kusunga mawu onse a chilamulo ichi ndi malemba aŵa, kuwachita; kuti mtima wake usadzikuze pa abale ake, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere.” (Deuteronomo 17:18-20) Zikuoneka kuti Davide sanali kutsatira langizo limeneli panthaŵi yomwe anachita machimo oopsaŵa. Kuphunzira Mawu a Mulungu kaŵirikaŵiri ndi kuwasinkhasinkha, kudzatithandizadi kupewa kuchita zoipa m’nthaŵi zowawa zino.—Miyambo 2:10-12.
Kuwonjezera apo, lamulo lomaliza pa Malamulo Khumi limanena mosapita m’mbali kuti: ‘Usasirire mkazi wa mnzako.’ (Eksodo 20:17) Panthaŵiyi, Davide anali ndi akazi angapo ndiponso akazi aang’ono ambiri. (2 Samueli 3:2-5) Koma zimenezo sizinamuletse kulakalaka mkazi winanso wokongola. Nkhaniyi ikutikumbutsa kufunika kwa mawu a Yesu akuti: “Yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28) M’malo mopitiriza kulakalaka zoipa ngati zimenezi, tiyeni tizifulumira kuzichotsa mumtima mwathu.
Kulapa ndi Chifundo
Cholinga cha nkhani ya m’Baibulo yosapita m’mbaliyi yonena za tchimo la Davide si kudzutsa chilakolako cha kugonana cha munthu ayi. Nkhaniyi ikutipatsa mwayi woona mkhalidwe wamphamvu ndi wochititsa chidwi wa Yehova womwe ndi chifundo.—Eksodo 34:6, 7.
Bateseba atabala mwana wamwamuna, Yehova anatumiza mneneri Natani kukam’funsa Davide za nkhaniyi. Chimenechi chinali chifundo. Davide akanapanda kufunsidwa za nkhaniyi ndi kungokhala chete osachitapo kanthu, mtima wake ukanaumitsidwa pa uchimo. (Ahebri 3:13) N’zosangalatsa kuti Davide anagwirizana ndi chifundo cha Mulungu. Kulankhula mwaluso kwa Natani kunakhudza chikumbumtima cha Davide ndipo modzichepetsa anavomereza kuti anachimwira Mulungu. Komanso atalapa ndi kuvomereza tchimo lake loopsa, Davide analemba Salmo 51 lomwe limafotokoza kuchimwa kwake ndi Bateseba. Tisaloletu mtima wathu kuuma pamene tachita tchimo lalikulu.—2 Samueli 12:1-13.
Ngakhale kuti Davide anakhululukidwa, anadzudzulidwa ndiponso anakumana ndi zotsatira za tchimo lake. (Miyambo 6:27) Kodi Mulungu akanachitira mwina? Kukanakhala kutsutsana ndi miyezo yake ya makhalidwe ngati Mulungu akanangozinyalanyaza zonse. Akanafanana ndi Eli, Mkulu wa Ansembe wolekerera yemwe ankadzudzula ana ake mopanda mphamvu ndi kungowayang’ana akupitirizabe kuchita zoipa. (1 Samueli 2:22-25) Komabe, Yehova saleka kusonyeza kukoma mtima kwa munthu wolapa. Chifundo chake, chotsitsimula ngati madzi ozizira, chidzathandiza wochimwayo kupirira mavuto omwe kuchimwako kungadzetse. Kudziŵa kuti Mulungu amakhululukira ndiponso kuyanjana kolimbikitsa ndi olambira anzathu n’kothandiza mwauzimu. Inde, mwa nsembe ya dipo la Kristu, olapa angaone “kulemera kwa chisomo cha [Mulungu].”—Aefeso 1:7.
“Mtima Woyera” ndi ‘Mzimu Watsopano’
Davide atavomereza machimo ake sanadzione monga wopanda pake. Mawu ake m’masalmo omwe analemba onena za kuulula machimo, akusonyeza kuti anali womasuka ndi wotsimikiza kutumikira Mulungu mokhulupirika. Mwachitsanzo, taonani Salmo 32. Vesi 1 limati: “Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake.” Ngakhale tchimo litakhala lalikulu bwanji, zotsatira zake zimakhala zosangalatsa ngati munthu alapa moona mtima. Njira imodzi yosonyeza kuona mtima kumeneku, ndiyo kuvomereza zomwe tachita monga anachitira Davide. (2 Samueli 12:13) Iye sanapeze zifukwa zopeputsira kuchimwa kwake kwa Yehova kapena kuyesa kuloza ena chala. Vesi 5 likuti: “Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.” Kulapa kwenikweni kumakhazikitsa mtima pansi, choncho munthu savutikanso ndi chikumbumtima chake poganiza zomwe anachita kale.
Atapempha Yehova kuti am’khululukire, Davide anapemphanso kuti: “Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mundipatse mzimu watsopano, wokhazikika m’kati mwanga.” (Salmo 51:10, NW) Kupempha “mtima woyera” ndi “mzimu watsopano,” kukusonyeza kuti Davide ankadziŵa za chizoloŵezi chake chauchimo ndi kuti anafuna kuti Mulungu am’thandize kuyeretsa mtima wake ndi kuyambanso kum’tumikira. M’malo modzimvera chisoni, anatsimikiza mtima kupitirizabe kutumikira Mulungu. Iye anapemphera kuti: “Ambuye, tsegulani pa milomo yanga; ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemerero wanu.”—Salmo 51:15.
Kodi Yehova anatani pamene Davide analapa moona mtima ndi kutsimikiza kum’tumikira? Anam’limbikitsa Davide kuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” (Salmo 32:8) Pano Yehova akutsimikiza kuti adzayang’anira maganizo ndi zosowa za munthu wolapa. Yehova anachita zotheka kumuwonjezera Davide nzeru, kuti azitha kuoneratu zotsatira zenizeni za nkhani. Ngati akakumana ndi mayesero m’tsogolo, akatha kuona zotsatira za zomwe angachite ndi mmene zidzakhudzira ena, choncho akachita mwanzeru.
Zochitika pa moyo wa Davidezi, n’zolimbikitsa onse amene anachitapo tchimo lalikulu. Mwa kuulula machimo athu ndi kusonyeza kulapa koona mtima, tingakhalenso pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu. Ubwenziwu ndiwo chinthu chofunika kwambiri kwa ife. Kuli bwino kwambiri kuwawidwa mtima ndi kuchita manyazi kwakanthaŵi kusiyana ndi ululu womwe tingamve chifukwa chongokhala chete osachitapo kanthu, kapena zotsatira zoopsa za njira yopanduka ya kuumitsa mitima yathu. (Salmo 32:9) Koma m’malo mwake tingakhululukidwe ndi Mulungu wachikondi, wachifundo, “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.”—2 Akorinto 1:3.
[Chithunzi patsamba 31]
Davide anaganiza kuti angapewe zotsatira za tchimo lake mwa kuphetsa Uriya