‘Kondwerani mwa Yehova’
“Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.”—SALMO 37:4.
1, 2. Kodi ndani amene ali Gwero la chimwemwe chenicheni, ndipo Mfumu Davide inafotokoza bwanji mfundo imeneyi?
“ODALA ali osauka mumzimu; . . . odala ali akuchitira chifundo; . . . odala ali akuchita mtendere.” Mawu ameneŵa pamodzinso ndi mawu ena asanu ndi amodzi ofotokoza za anthu amene ali odala, kapena kuti achimwemwe, ndi mawu oyamba ochititsa chidwi kwambiri a Ulaliki wa pa Phiri wotchuka wa Yesu, monga mmene wolemba Uthenga Wabwino, Mateyu, analembera. (Mateyu 5:3-11) Mawu a Yesu ameneŵa akutitsimikizira kuti tingathe kukhala achimwemwe.
2 Salmo limene Mfumu Davide ya Israyeli wakale inalemba likutisonyeza kuti Yehova ndiye Gwero la chimwemwe chenicheni. Davide anati: “Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.” (Salmo 37:4) Koma kodi n’chiyani chingachititse kudziŵa Yehova ndiponso kudziŵa makhalidwe ake osiyanasiyana kukhala ‘kokondweretsa’? Kodi kuganizira zimene wachita ndiponso zimene adzachite m’tsogolo pokwaniritsa zolinga zake kungakuthandizeni bwanji kuyembekezera kudzalandira ‘zokhumba mtima wanu’? Kupenda mosamala Salmo 37, mavesi 1 mpaka 11, kuyankha mafunso ameneŵa.
“Usachite Nsanje”
3, 4. Kodi Davide akutilangiza chiyani malinga ndi mmene Salmo 37:1 likunenera, ndipo n’chifukwa chiyani kumvera langizo limeneli n’koyenera masiku ano?
3 Tikukhala ‘m’nthaŵi zoŵaŵitsa’ ndipo pali zoipa zambiri zimene zikuchitika. Takhala tikuona zimene mtumwi Paulo ananena zikuchitikadi. Iye anati: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.” (2 Timoteo 3:1, 13) Tikhoza kukhudzidwa mosavuta ndi mmene anthu oipa akuonekera ngati zinthu zikuwayendera bwino ndiponso akutukuka. Zonsezi zingatidodometse, kutichititsa kuti kuona kwathu zinthu mwauzimu kusokonezeke. Onani mmene mawu oyamba a Salmo 37 akutichenjezera za ngozi imeneyi yomwe tikhoza kukumana nayo. Akuti: “Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.”
4 Tsiku ndi tsiku, mawailesi, ma TV, ndi manyuzipepala amatiuza zinthu zambirimbiri zosonyeza kusoŵa chilungamo. Anthu amalonda osaona mtima salangidwa chifukwa cha chinyengo chawo. Zigaŵenga zimapezerera anthu osavuta kuwadyera masuku pamutu. Anthu amene amapha anzawo satulukiridwa kapena salangidwa. Zitsanzo zonsezi za kusoŵa chilungamo zingatikwiyitse ndi kusokoneza mtendere wathu wa maganizo. Popeza anthu oipa akuoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino, zimenezi zikhoza kutichititsa kukhala ndi mtima wa nsanje. Koma kodi kuipidwa kwathu kudzathandiza kuti zinthu zisinthe? Kodi kuchitira nsanje anthu oipa omwe akuoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino kudzasintha zinthu kuti zisawayendere bwino? Ayi! Ndipo palibedi chifukwa choti ‘tivutike mtima.’ N’chifukwa chiyani sitiyenera kutero?
5. N’chifukwa chiyani anthu oipa anawayerekezera ndi udzu?
5 Wamasalmo akuyankha kuti: “Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi.” (Salmo 37:2) Msipu wauwisi ungaoneke wokongola kwambiri, koma suchedwa kufota ndi kufa. N’chimodzimodzinso ndi anthu ochita zoipa. Angaoneke kuti zinthu zikuwayendera bwino, koma zimenezi n’zosakhalitsa. Akamwalira, chuma chawo chimene anachipeza m’njira zosayeneracho sichiwathandiza. Mapeto ake, aliyense amakumana ndi zotsatira za zochita zake. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mphotho yake ya uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Anthu oipa ndi onse amene sachita chilungamo pomaliza palibe chilichonse chimene adzalandire kupatulapo “mphotho” yawo. Inde, zochita za anthu oipa n’zopanda phindu!—Salmo 37:35, 36; 49:16, 17.
6. Kodi tikuphunzira chiyani pa Salmo 37:1, 2?
6 Motero, kodi tilole kuti kutukuka kosakhalitsa kwa anthu oipa kutidodometse? Phunziro limene lili m’mavesi aŵiri oyambirira a Salmo 37 n’lakuti: Musalole kusiya njira imene munasankha yotumikira Yehova chifukwa chakuti anthu oipa zinthu zikuwayendera bwino. M’malo mwake, ikani mtima pa madalitso ndi zolinga zauzimu.—Miyambo 23:17.
“Khulupirira Yehova, Ndipo Chita Chokoma”
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Yehova?
7 Wamasalmoyo akutilimbikitsa kuti: “Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma.” (Salmo 37:3a) Tikakhala ndi nkhaŵa kapena ngati tikukayika, tifunika kudalira kwambiri Yehova. Iye ndi amene amapereka chitetezo chauzimu chokwanira. Mose analemba kuti: “Iye amene akhala pansi m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.” (Salmo 91:1) Tikakhumudwa ndi kuwonjezeka kwa kusoŵa chilungamo kumene kuli padziko lapansili, tifunika kudalira kwambiri Yehova. Tikabinya phazi, timasangalala kwambiri mnzathu akatithandiza. Mofanana ndi zimenezi, pamene tikuyesetsa kukhala okhulupirika, timafunika thandizo la Yehova.—Yesaya 50:10.
8. Kodi kuchita utumiki wachikristu kungatithandize bwanji kupeŵa kudodometsedwa mopambanitsa ndi kutukuka kwa oipa?
8 Chinthu chimodzi chimene chingatithandize kuti tisadodometsedwe ndi kutukuka kwa oipa ndicho kudzitangwanitsa ndi ntchito yofunafuna ndi kuthandiza anthu onga nkhosa kuti adziŵe zinthu zolondola zokhudza Yehova ndi zolinga zake. Popeza zinthu zoipa zikuwonjezeka, tifunika kudzitangwanitsa kwambiri ndi ntchito yothandiza ena. Mtumwi Paulo anati: “Musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.” Chinthu “chokoma” kwambiri chimene tingachite ndicho kuuza ena uthenga wabwino waulemerero wa Ufumu wa Mulungu. Kulalikira kwathu anthu onse kulidi “nsembe yakuyamika.”—Ahebri 13:15, 16; Agalatiya 6:10.
9. Fotokozani mfundo zokhudza langizo la Davide lakuti “khala m’dziko.”
9 Davide anapitiriza kuti: “Khala m’dziko, ndipo tsata choonadi [“khulupirika,” NW].” (Salmo 37:3b) “Dziko” la m’masiku a Davide linali dera limene Yehova anapatsa Aisrayeli, Dziko Lolonjezedwa. Panthaŵi imene Solomo anali kulamulira, malire a dzikoli ku mbali ya kumpoto anafika ku Dani ndipo kumbali ya kum’mwera anafika ku Beereseba. Kumeneku ndiko kunali kwawo kwa Aisrayeli. (1 Mafumu 4:25) Masiku ano, kulikonse kumene tikukhala padziko lapansi, tikuyembekezera nthaŵi imene dziko lonse lapansili lidzakhala paradaiso m’dziko latsopano lachilungamo. Koma pakadali pano, tikukhala m’malo otetezeka auzimu.—Yesaya 65:13, 14.
10. Kodi chimachitika n’chiyani ‘tikakhulupirika’?
10 Kodi n’chiyani chidzachitika ‘tikakhulupirika’? Mwambi wina wouziridwa umatikumbutsa kuti: “Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri.” (Miyambo 28:20) Mosakayika, Yehova adzatidalitsa pamene tichita khama kulalikira uthenga wabwino mokhulupirika kulikonse kumene tikukhala ndiponso kwa munthu aliyense amene tingathe kumulalikira. Mwachitsanzo, Frank ndi mkazi wake, Rose, anayamba upainiya zaka 40 zapitazo m’tauni ina kumpoto kwa dziko la Scotland. Anthu ochepa amene m’mbuyomo anasonyeza chidwi ndi choonadi kumeneko anali atasiya. Apainiya aŵiriŵa sanakhumudwe nazo zimenezi ndipo anayamba ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira. Panopa tsopano m’tauni imeneyi muli mpingo umene ukuyenda bwino kwambiri. Mosakayika, Yehova wadalitsa kukhulupirika kwa apainiya aŵiriŵa. Frank anafotokoza modzichepetsa kuti: “Dalitso lalikulu kwambiri n’lakuti tikadali m’choonadi mpaka pano ndipo Yehova akutigwiritsa ntchito.” Inde, ‘tikamakhulupirika,’ timalandira madalitso ambiri.
“Udzikondweretsenso mwa Yehova”
11, 12. (a) Kodi ‘tingakondwere mwa Yehova’ motani? (b) Kodi mungadziikire zolinga zotani pankhani yophunzira panokha, ndipo pangakhale zotsatira zotani?
11 Kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova ndiponso kuti tipitirize kumudalira, tiyenera ‘kudzikondweretsa mwa Yehova.’ (Salmo 37:4a) Kodi timachita bwanji zimenezo? M’malo mongoganizira kwambiri mmene zinthu zilili pa moyo wathu, ngakhale zitakhala zovuta, tiyenera kuganizira kwambiri za Yehova. Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndiyo kupatula nthaŵi yoŵerenga Mawu ake. (Salmo 1:1, 2) Kodi mumakondwera mukaŵerenga Baibulo? Mungakondwere ngati muŵerenga n’cholinga choti muphunzire zambiri za Yehova. Bwanji osaima kaye mukaŵerenga ndime inayake n’kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndime imeneyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova’? Mwina mungaone kuti kukhala ndi kope kapena pepala pafupi pamene mukuŵerenga Baibulo kungakuthandizeni. Nthaŵi iliyonse mukaima kuti musinkhesinkhe tanthauzo la zimene mwaŵerenga, lembani mawu amene akukumbutsani khalidwe linalake lokopa la Mulungu. M’salmo lina, Davide anaimba kuti: “Mawu a m’kamwa mwanga ndi maganizo a m’mtima wanga avomerezeke pamaso panu [“zikukondweretseni,” NW], Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.” (Salmo 19:14) Kuŵerenga Mawu a Mulungu moikirapo mtima kwambiri ‘kumakondweretsa’ Yehova, ndipo kumatikondweretsanso eni akefe.
12 Kodi tingapeze bwanji chimwemwe pophunzira ndi kusinkhasinkha? Tingadziikire cholinga chakuti tiphunzire zambiri monga mmene tingathere zokhudza Yehova ndi njira zake. Mabuku monga a Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako ndi Yandikirani kwa Yehovaa amatipatsa mfundo zambiri zimene tingazisinkhesinkhe moyamikira. Ndiyeno Davide akutsimikizira munthu wolungama kuti, Yehova “adzakupatsa zokhumba mtima wako.” (Salmo 37:4b) Kudalira kotereku kuyenera kuti n’kumene kunachititsa mtumwi Yohane kulemba kuti: “Uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; ndipo ngati tidziŵa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziŵa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.”—1 Yohane 5:14, 15.
13. Kodi ntchito yolalikira Ufumu yakula motani m’mayiko ambiri m’zaka zaposachedwapa?
13 Ife monga anthu okhulupirika, chinthu chimene chimatisangalatsa kwambiri ndicho kuona anthu akutsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. (Miyambo 27:11) Kodi mitima yathu sidzaza ndi chimwemwe tikamamva za ntchito yaikulu yolalikira imene abale athu akuchita m’mayiko amene munali maboma opondereza ndi ankhanza? Tikuyembekezera kuona ufulu wina umene ungapezeke dongosolo la zinthu lino lisanathe. Atumiki ambiri a Yehova a ku mayiko a azungu akulalikira mwakhama kwa ophunzira, anthu othaŵa kwawo, ndi ena amene akukhala m’mayiko amenewo kwa nthaŵi yochepa ndipo ali ndi ufulu wolambira. Tikulakalaka kuti anthu ameneŵa akabwerera kwawo, akapitirize kuwalitsa kuunika kwa choonadi mu mdima wa ndiweyani.—Mateyu 5:14-16.
“Pereka Njira Yako kwa Yehova”
14. Kodi ndi umboni wotani umene ulipo wotsimikizira kuti tingadalire Yehova?
14 N’zokhazika mtima pansi kudziŵa kuti nkhaŵa zathu ndiponso zilizonse zimene zingaoneke kuti zikutilemetsa kwambiri zingachotsedwe. Motani? Davide anati: “Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye.” Ndiyeno anawonjezera kuti, “adzachichita.” (Salmo 37:5) M’mipingo yathu, tili ndi umboni wokwanira wotsimikizira kuti tingadalire Yehova kuti atithandize. (Salmo 55:22) Onse amene ali mu utumiki wa nthaŵi zonse kaya monga apainiya, oyang’anira oyendayenda, amishonale, kapena ogwira ntchito yodzipereka pa Beteli, angachitire umboni kuti Yehova ndi wodalirika pankhani yothandiza anthu ake. Bwanji osalankhula ndi ena amene mukuwadziŵa ndi kuwafunsa mmene Yehova wawathandizira? Mosakayika, mudzamva zinthu zambiri zimene akumana nazo zosonyeza kuti dzanja la Yehova silifupika ngakhale panthaŵi zovuta. Iye nthaŵi zonse amapereka zofunika pa moyo.—Salmo 37:25; Mateyu 6:25-34.
15. Kodi chilungamo cha anthu a Mulungu chimaŵala bwanji?
15 Tikamadalira Yehova ndi kumukhulupirira ndi mtima wonse, zingatichitikire zimene wamasalmo ananena m’mawu ake otsatira. Iye anati: “Adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika, ndi kuweruza kwako monga usana.” (Salmo 37:6) Monga Mboni za Yehova, nthaŵi zambiri anthu amatiipitsira mbiri yathu. Koma Yehova amatsegula maso a anthu oona mtima, kuwathandiza kuona kuti utumiki wathu umene timachita kwa anthu onse timachita chifukwa chakuti timakonda Yehova ndiponso timakonda anzathu. Komanso, makhalidwe athu abwino amaonekera ngakhale kuti ena amaipitsa mbiri yathu ya makhalidwe abwino. Yehova amatithandiza pamene tikukumana ndi otsutsa osiyanasiyana ndiponso pamene tikuzunzidwa m’njira zosiyanasiyana. Chifukwa cha zimenezi, chilungamo cha anthu a Mulungu chimaŵala monga mmene limachitira dzuŵa masana.—1 Petro 2:12.
“Khala Chete . . . Num’lindirire”
16, 17. Malinga ndi Salmo 37:7, kodi ino ndi nthaŵi yochita chiyani, ndipo chifukwa chiyani?
16 Mawu otsatira a wamasalmoyo akuti: “Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye: usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m’njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.” (Salmo 37:7) Apa Davide akutsindika kufunika koti tidikire moleza mtima kuti Yehova adzachitepo kanthu. Ngakhale kuti dongosolo la zinthu lino silinafike kumapeto, chimenechi sichiyenera kukhala chifukwa chodandaulira. Kodi sitinaone kuti chifundo cha Yehova ndi kuleza mtima kwake n’zazikulu kwambiri kuposa mmene tinali kuganizira poyamba? Kodi ifenso sitiyenera tsopano lino kusonyeza kuti tikudikira moleza mtima pamene tikudzitangwanitsa ndi kulalikira uthenga wabwino mapeto asanafike? (Marko 13:10) Tsopano ndi nthaŵi yofunika kupeŵa kuchita zinthu mopupuluma zimene zingatiwonongere chimwemwe chathu ndiponso chitetezo chathu chauzimu. Ino ndi nthaŵi yokanitsitsa zinthu zoipa za m’dziko la Satanali zimene zingatisokoneze. Ndiponso ino ndi nthaŵi yoti tikhale ndi makhalidwe abwino ndipo tisaike pangozi kulungama kwathu pamaso pa Yehova. Tiyenera kupitiriza kupeŵa kuganizira zinthu zoipa ndiponso kuchita zinthu mosayenera kwa anthu amene si amuna kapena akazi anzathu kapenanso ngakhale anthu amene ndi amuna kapena akazi anzathu.—Akolose 3:5.
17 Davide akutilangiza kuti: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: usavutike mtima ungachite choipa. Pakuti ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.” (Salmo 37:8, 9) Inde, tingayembekezere ndi chikhulupiriro chonse nthaŵi imene tsopano yatsala pang’ono pamene Yehova adzachotsa padziko lapansi zoipa zonse ndi anthu amene amachita zoipazo.
“Katsala Kanthaŵi”
18, 19. Kodi lemba la Salmo 37:10 likukulimbikitsani bwanji?
18 “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe.” (Salmo 37:10) Mawu ameneŵa akutilimbikitsa kwambiri pamene tikuyandikira mapeto a dongosolo lino la zinthu ndiponso mapeto a kudziimira paokha kwa anthu m’malo modalira Yehova kumene kwabweretsa mavuto ambiri. Maboma kapena maulamuliro a mtundu uliwonse amene anthu apanga alephera momvetsa chisoni. Ndipo tsopano tikuyandikira nthaŵi imene tidzabwerera ku ulamuliro wa Mulungu, Ufumu wa Yehova womwe uli m’manja mwa Yesu Kristu. Udzakhala ndi mphamvu pa chilichonse chokhudza dziko lapansi ndipo udzachotsa anthu onse otsutsa Ufumu wa Mulungu.—Danieli 2:44.
19 M’dziko latsopano limene lidzalamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu, ngakhale mutadzafufuza motani simudzapezamo munthu “woipa.” Inde, aliyense amene adzapandukira Yehova panthaŵiyo adzamuchotsa nthaŵi yomweyo. Simudzakhala munthu aliyense woukira ulamuliro wake kapena wokana kugonjera ulamuliro wa Mulungu. Anthu onse amene muzidzakhala nawo pafupi adzakhala ndi maganizo ofanana ndi anu ofuna kusangalatsa Yehova. Kudzakhala chitetezo champhamvu, sikudzakhala maloko, zitsulo zotchingira kuopa akuba, kapena china chilichonse chimene chidzalepheretsa kukhulupirira ena ndi mtima wonse ndiponso palibe chimene chidzasokoneza chimwemwe.—Yesaya 65:20; Mika 4:4; 2 Petro 3:13.
20, 21. (a) Kodi “ofatsa” amene awatchula pa Salmo 37:11 ndani, ndipo amapeza kuti “mtendere wochuluka”? (b) Kodi tidzapeza madalitso otani ngati titsanzira Davide Wamkulu?
20 Ndiyeno, “ofatsa adzalandira dziko lapansi.” (Salmo 37:11a) Koma kodi “ofatsa” ameneŵa ndani? Liwu limene analimasulira kuti “ofatsa” likuchokera ku liwu limene limatanthauza “kuzunza, kuchepetsa, kunyozetsa.” Inde, “ofatsa” ndi anthu amene amadikira Yehova modzichepetsa kuti adzakonza kupanda chilungamo kumene anthu ena akuwachitira. ‘Adzakondwera nawo mtendere wochuluka.’ (Salmo 37:11b) Ngakhale pakadali pano, tikupeza mtendere wochuluka m’paradaiso wauzimu amene ali mumpingo wachikristu woona.
21 Ngakhale kuti pakadali pano sitinamasuke ku mavuto, timathandizana ndi kulimbikitsa ovutika maganizo. Zimenezi zimathandiza kuti pakati pa anthu a Yehova pazikhala chisangalalo chenicheni chamumtima. Abale amene aikidwa kukhala abusa amatithandiza mwachikondi kupeza zimene tikufunikira mwauzimu ndiponso nthaŵi zina ngakhale zofunika za moyo wa tsiku ndi tsiku, zimene zimatithandiza kupirira mavuto amene timakumana nawo chifukwa chochita chilungamo. (1 Atesalonika 2:7, 11; 1 Petro 5:2, 3) Mtendere umenewu ndi chinthu chamtengo wapatali chimene tili nacho. Tikuyembekezeranso kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso wamtendere posachedwapa. Ndiyetu tiyeni titsanzire Davide Wamkulu, Kristu Yesu, amene changu chake kwa Yehova chinamuchititsa kutumikira mokhulupirika mpaka mapeto. (1 Petro 2:21) Mwakuchita zimenezo, tidzapitiriza kukhala achimwemwe, kutamanda amene timakondwera naye, Mulungu wathu, Yehova.
[Mawu a M’munsi]
a Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mungayankhe?
• Kodi mwaphunzira zotani pa Salmo 37:1, 2?
• Kodi ‘mungakondwere mwa Yehova’ motani?
• Kodi pali umboni wotani wotsimikizira kuti tingadalire Yehova?
[Chithunzi patsamba 9]
Akristu ‘sachita nsanje chifukwa cha ochita chosalungama’
[Chithunzi patsamba 10]
“Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma”
[Chithunzi patsamba 11]
Kondwerani mwa Yehova mwa kuphunzira zambiri za iye mmene mungathere
[Chithunzi patsamba 12]
“Ofatsa adzalandira dziko lapansi”