‘Zimene Yehova Watsimikiza’ Sizingalephereke
“Ndidzauza za chitsimikizo [cha Yehova, NW]: Yehova ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga . . . Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale choloŵa chako.”—SALMO 2:7, 8.
1. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa zolinga za Mulungu ndi za amitundu?
YEHOVA MULUNGU ali n’cholinga chokhudza anthu ndiponso dziko lapansi. Nawonso amitundu ali ndi cholinga. Koma zolingazi n’zosiyana kwambiri! Izi n’zosadabwitsa chifukwa Mulungu ananena kuti: “Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.” Cholinga cha Mulungu chidzachitika mosakayika, chifukwa iye ananenanso kuti: “Monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbewu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m’mene ndinawatumizira.”—Yesaya 55:9-11.
2, 3. Kodi ndi mfundo iti imene yafotokozedwa momveka bwino m’salmo lachiŵiri, koma kodi pali mafunso otani?
2 Mfundo imeneyi yakuti cholinga cha Mulungu chokhudza Mfumu yake ya Umesiya chidzakwaniritsidwa yafotokozedwa momveka bwino m’salmo lachiŵiri. Wolemba salmo limeneli, yemwe ndi Mfumu Davide ya Israyeli wakale, anauziridwa ndi Mulungu kuti alosere za nthaŵi ina pamene amitundu adzasokosera chifukwa chosokonezeka. Owalamulira awo adzatsutsana ndi Yehova Mulungu pamodzi ndi Wodzozedwa wake. Komabe, wamasalmoyu anaimbanso kuti: “Ndidzauza za chitsimikizo cha Yehova: Yehova ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga . . . Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale choloŵa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako.”—Salmo 2:7, 8.
3 Kodi zimene Yehova watsimikiza kuchitazi zikukhudza bwanji amitundu? Kodi zikukhudza motani anthu onse? Kodi zimenezi zikukhudza bwanji makamaka anthu oopa Mulungu amene amaŵerenga salmo lachiŵirili?
Amitundu Aphokosera
4. Kodi mungafotokoze motani mwachidule mfundo zikuluzikulu za pa Salmo 2:1, 2?
4 Ponena za zochita za amitundu pamodzi ndi owalamulira awo, wamasalmoyu akuyamba nyimbo yakeyi mwa kuimba kuti: “Aphokoseranji amitundu, nalingiriranji anthu zopanda pake? Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake.”—Salmo 2:1, 2.a
5, 6. Kodi anthu akhala ‘akulingalira zopanda pake’ zotani?
5 Kodi anthu a masiku ano akhala ‘akulingalira zopanda pake’ zotani? M’malo movomereza Wodzozedwa wa Mulungu, yemwe ndi Mesiya, kapena kuti Kristu, amitundu akhala ‘akulingalira,’ kapena kuti kusinkhasinkha zopitiriza ulamuliro wawo. Mawu ameneŵa a salmo lachiŵirili anakwaniritsidwanso m’zaka 100 zoyambirira Kristu Atabwera pamene atsogoleri a Ayuda ndi Aroma anagwirizana kuti aphe Yesu Kristu, Mfumu Yosankhidwiratu ya Mulungu. Komabe, mawuŵa anayamba kukwaniritsidwa kwambiri mu 1914 pamene Yesu anadzozedwa kukhala Mfumu yakumwamba. Kuchokera nthaŵi imeneyo, palibe gulu landale lililonse padziko pano limene lavomereza Mfumu yoikidwa ya Mulungu.
6 Kodi wamasalmo anatanthauzanji pamene anafunsa kuti ‘amitundu akulingiriranji zopanda pake’? Cholinga chawo ndiye chopanda pake; sangaphule nacho kanthu ndipo n’zodziŵikiratu kuti sichidzatheka ndipo chidzalephereka. Sangabweretse mtendere ndi mgwirizano padziko lapansili. Komano, iwo akupitirizabe zochita zawozo mpaka kufika potsutsa ulamuliro wa Mulungu. Ndipo mogwirizana akuchita zamtopola ndipo asonkhana kuti alimbane ndi Wam’mwambamwamba pamodzi ndi Wodzozedwa wake. Koma ndiye n’kupusa bwanji!
Mfumu Yopambana ya Yehova
7. Kodi otsatira oyambirira a Yesu anagwiritsira ntchito motani Salmo 2:1, 2 m’pemphero lawo?
7 Otsatira a Yesu anagwiritsira ntchito mawu a Salmo 2:1, 2 pa Yesuyo. Pamene anali kuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, iwo anapemphera kuti: “Mfumu [Yehova], Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili mmenemo; amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davide mtumiki wanu, mudati, Amitundu anasokosera chifukwa chiyani? Nalingirira zopanda pake anthu? Anadzindandalitsa mafumu a dziko, ndipo oweruza anasonkhanidwa pamodzi, kutsutsana ndi Ambuye ndi Kristu wake. Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m’mudzi muno Herode [Antipa], ndi Pontiyo Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israyeli kum’chitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munam’dzoza.” (Machitidwe 4:24-27; Luka 23:1-12)b Inde, m’zaka 100 zoyambirira anthu anam’chitira chiwembu Yesu, mtumiki wodzozedwa wa Mulungu. Komabe, salmo limeneli linadzakwaniritsidwanso patatha zaka zambiri m’tsogolo mwake.
8. Kodi lemba la Salmo 2:3 likugwira ntchito motani kwa amitundu a masiku ano?
8 M’nthaŵi imene mfumu ya Israyeli wakale inkakhala munthu, monga Davide, mitundu yachikunja pamodzi ndi owalamulira awo ankasonkhana kuti alimbane ndi Mulungu ndi mfumu yake yodzozedwa. Koma bwanji masiku athu ano? Amitundu a masiku ano safuna kumvera malamulo a Yehova ndi Mesiya. Motero iwo amakhala ngati akunena kuti: “Tidule zomangira zawo, titaye nsinga zawo.” (Salmo 2:3) Olamulira pamodzi ndi amitundu amatsutsa chilichonse chimene Mulungu pamodzi ndi Wodzozedwa wake amaletsa. Koma chilichonse chomwe angachite pofuna kudula zomangira zimenezo ndi kutaya nsinga zimenezo sichingaphule kanthu.
Yehova Amawanyoza
9, 10. N’chifukwa chiyani Yehova amanyoza amitundu?
9 Yehova sada nkhaŵa ndi chinthu chilichonse chimene olamulira a amitundu angachite pofuna kukhazikitsa ulamuliro wawo. Salmo lachiŵirili likupitiriza motere: “Wokhala m’mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza.” (Salmo 2:4) Mulungu akupitiriza cholinga chake ngati kuti olamuliraŵa sanunkha kanthu n’komwe. Iye akuwaseka chifukwa cha mwano umene akuchita ndipo akuwanyoza. Alekeni azidzitamandira pa zimene akufuna kuchita. Yehova amangowaseka. Amawaseka chifukwa chakuti amalimbana naye mopanda kuphula kanthu.
10 Davide m’masalmo ake anafotokoza penapake za anthu ndiponso mitundu yodana ndi mtundu wake ndipo anaimba kuti: “Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli, ukani kukazonda amitundu onse: Musachitire chifundo mmodzi yense wakuchita zopanda pake monyenga. Abwera madzulo, auwa ngati galu, nazungulira mudzi. Onani abwetuka pakamwa pawo; m’milomo mwawo muli lupanga, pakuti amati, Amva ndani? Koma Inu, Yehova, mudzawaseka; mudzalalatira amitundu onse.” (Salmo 59:5-8) Yehova amaseka kudzitamandira ndiponso kusokonezeka kwa amitundu pa zochita zawo zopusa zofuna kulimbana naye.
11. Kodi chimachitika n’chiyani amitundu akamayesa kutsutsana ndi cholinga cha Mulungu?
11 Mawu a Salmo 2 amalimbitsa chikhulupiriro chathu chakuti Mulungu angathetse vuto lililonse. Tisakayike kuti iye nthaŵi zonse amakwaniritsa zofuna zake ndipo sataya atumiki ake. (Salmo 94:14) Ndiyeno, chimachitika n’chiyani amitundu akamatsutsana ndi cholinga cha Yehova? Malinga ndi salmo limeneli, Mulungu “adzalankhula nawo mu mkwiyo wake,” ngati kugunda kwa bingu lalikulu. Komanso, ‘adzawaopsa m’ukali wake,’ ngati kung’anima kwa mphenzi.—Salmo 2:5.
Mfumu ya Mulungu Iikidwa
12. Kodi Salmo 2:6 limanena za kuika pampando mfumu iti?
12 Mosakayikira amitundu akukhumudwa ndi zimene Yehova akunena tsopano kudzera mwa wamasalmoyu. Mulungu akulengeza kuti: “Ine ndadzoza mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.” (Salmo 2:6) Ziyoni linali phiri ku Yerusalemu kumene Davide anadzozedwa kapena kuti anaikidwa kukhala mfumu ya Israyeli yense. Koma sikuti Mfumu ya Umesiya idzaikidwa pampando mu mzinda umenewo kapena wina uliwonse padziko lapansi pano. Ndipotu, Yehova anaika kale Yesu Kristu kukhala Mfumu yake yosankhidwa ya Umesiya pa phiri la Ziyoni lakumwamba.—Chivumbulutso 14:1.
13. Kodi Yehova anapanga pangano lotani ndi Mwana wake?
13 Mfumu ya Umesiyayi ikulankhula tsopano. Ikuti: “Ndidzauza za chitsimikizo cha Yehova: Yehova [amene anapanga pangano la Ufumu ndi Mwana wake] ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga; ine lero ndakubala.” (Salmo 2:7) Kristu ankanena za pangano la Ufumu limeneli pamene anauza atumwi ake kuti: “Inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine.”—Luka 22:28, 29.
14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu ndi woyenereradi kukhala Mfumu?
14 Mogwirizana ndi ulosi wa pa Salmo 2:7, Yehova anasonyeza kuti Yesu ndi Mwana Wake pamene Yesuyo ankabatizidwa ndiponso pamene anamuukitsa kwa akufa n’kukhala ndi moyo wauzimu. (Marko 1:9-11; Aroma 1:4; Ahebri 1:5; 5:5) Inde, Mfumu ya Ufumu wakumwamba ndiye Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. (Yohane 3:16) Monga mwana wa m’banja lachifumu la Mfumu Davide, Yesu ndi woyenereradi kukhala Mfumu. (2 Samueli 7:4-17; Mateyu 1:6, 16) Malinga ndi salmo limeneli, Mulungu akuuza Mwana wakeyu kuti: “Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale choloŵa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako.”—Salmo 2:8.
15. N’chifukwa chiyani Yesu akupempha amitundu kuti akhale choloŵa chake?
15 Mfumuyi, yemwe ndi Mwana weniweni wa Mulungu, ndi yachiŵiri kwa Yehova. Yesu ndi munthu amene atayesedwa m’njira zosiyanasiyana, Yehova anaona kuti ndi wabwino, wokhulupirika ndiponso wodalirika. Kuwonjezera pamenepo, Yesu ali ndi choloŵa popeza ndi Woyamba Kubadwa wa Mulungu. Inde, Yesu Kristu “ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Akangopempha basi, Mulungu ‘adzam’patsa amitundu akhale choloŵa chake, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akeake.’ Yesu akupempha izi monga munthu amene amakonda ana a anthu ndiponso chifukwa chofunitsitsa kuchita chifuniro cha Atate wake wakumwamba chokhudza dziko lapansi ndiponso anthu.—Miyambo 8:30, 31.
Zimene Yehova Watsimikiza Kuchita kwa Amitundu
16, 17. Malinga ndi Salmo 2:9, kodi amitundu adzaona zotani?
16 Popeza kuti salmo lachiŵirili likukwaniritsidwa nthaŵi inoyi, yomwe ndi nthaŵi ya kukhalapo kosaoneka kwa Yesu Kristu, kodi amitundu adzaona zotani? Posachedwapa, Mfumuyi idzachita zimene Mulungu akulengeza, kuti: “Udzawathyola [amitundu] ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.”—Salmo 2:9.
17 Ndodo za mafumu a m’nthaŵi zakale zinkakhala chizindikiro cha ufumu. Ndodo zina zinkakhala zachitsulo, monga ndodo yomwe ikutchulidwa m’salmoli. Mawu ophiphiritsira omwe agwiritsiridwa ntchito apa akusonyeza kuti Kristu Mfumu sizidzamuvuta kuwononga amitundu. Mbiya yadongo ingasweke moti singakonzedwenso itamenyedwa mwamphamvu ndi ndodo yachitsulo.
18, 19. Kodi mafumu a dziko lapansi ayenera kuchitanji kuti Mulungu awayanje?
18 Kodi olamulira a amitundu sangapeŵe kuwonongedwa pachiwonongeko choopsa chimenechi? Ayi, angathe kupeŵa, chifukwa wamasalmoyu akuwachonderera motere: “Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru: Langikani, oweruza inu a dziko lapansi.” (Salmo 2:10) Mafumu akupemphedwa kuganizira mozama za nkhaniyi. Ayenera kuona kuti zomwe iwo akuganizira kuchita n’zosaphula kanthu poziyerekezera ndi zinthu zimene Ufumu wa Mulungu udzachite zomwe anthu adzapindule nazo.
19 Kuti Mulungu awayanje, mafumu a dziko lapansi akuyenera kusintha zochita zawo. Iwo akulimbikitsidwa “kutumikira Yehova ndi mantha, ndi kukondwera ndi chinthenthe.” (Salmo 2:11) N’chiyani chingachitike atati achite zimenezi? M’malo mochita phokoso, kapena kuti kusokonezeka maganizo, iwo angathe kukhala osangalala poyembekezera zinthu zimene Mfumu ya Umesiya idzawapatse. M’pofunika kuti olamulira a dziko lapansi asiye kunyada ndiponso kudzikuza kumene amasonyeza m’maulamuliro awo. Kuwonjezera apo, ayeneranso kusintha mwamsanga ndi kuchita zinthu mwanzeru pankhani yokhudza ulamuliro wosayerekezeka wa Yehova ndiponso mphamvu zosagonjetseka zimene Mulungu ndi Mfumu yake ya Umesiya ali nazo.
“Mpsompsoneni Mwanayo”
20, 21. Kodi ‘kumpsompsona Mwanayo’ kukutanthauza kuchita chiyani?
20 Salmo 2 tsopano likupempha mwachifundo olamulira a amitundu kuchita kanthu kenakake. M’malo mosonkhana pamodzi n’kupanga mgwirizano wotsutsa, iwo akulangizidwa kuti: “Mpsompsoneni Mwanayo, kuti [Yehova Mulungu] angakwiye, ndipo mungatayike m’njira, ukayaka pang’ono pokha mkwiyo wake.” (Salmo 2:12a) Anthu ayenera kumvera Ambuye Mfumu Yehova akapereka lamulo. Mulungu atakhazika Mwana wake pampando wachifumu, olamulira a dziko lapansi anayenera kusiya ‘kulingalira zopanda pake.’ Anayenera kuzindikira Mfumuyi mwamsanga ndi kuimvera ndi mtima wonse.
21 N’chifukwa chiyani ayenera ‘kumpsompsona Mwanayo’? Panthaŵi yomwe salmoli linkalembedwa, kumpsompsona munthu kunkasonyeza kugwirizana naye komanso kunkachitika munthu akamalandira alendo kunyumba yake, komwe akanatha kuchezeredwa. Kumpsompsona kunkasonyezanso kukhulupirika. (1 Samueli 10:1) M’vesi la salmo lachiŵirili, Mulungu akulamula amitundu kuti ampsompsone, kapena kuti alandire, Mwana wake monga Mfumu yodzozedwa.
22. Kodi olamulira a amitundu akufunika kumvera chenjezo liti?
22 Anthu omwe amakana kuvomereza mphamvu za Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu amanyoza Yehova. Amakana kuti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse ndiponso kuti angathe kusankha Mfumu yabwino kwambiri yoyenera kulamulira anthu. Olamulira a amitundu adzazindikira mwadzidzidzi kuti Mulungu wawakwiyira, panthaŵi yomwe iwowo atanganidwa ndi zolinga zawo. ‘Umayaka pang’ono pokha mkwiyo wake,’ kapena kuti mkwiyo wake suchedwa kuyaka ndiponso kuti sungaletsedwe. Olamulira a amitundu akufunika kuyamikira ndi kutsatira chenjezo limeneli. Adzapeza moyo akachita zimenezo.
23. Kodi padakali nthaŵi yoti anthu achite chiyani?
23 Salmo lochititsa chidwili likumaliza motere: “Odala onse akum’khulupirira Iye [Yehova].” (Salmo 2:12b) Nthaŵi idakalipo kuti anthu apeze chitetezo. Izi zilinso choncho ngakhale kwa olamulirawo pawokhapawokha, amene akhala akutsatira zolinga za amitundu. Iwo angathaŵire kwa Yehova, amene amateteza pogwiritsira ntchito ulamuliro wa Ufumu. Koma akufunika kuchita izi Ufumu Waumesiya usanawononge amitundu otsutsa.
24. Kodi tingatani kuti tikhale moyo wosangalala kwambiri ngakhale m’dziko lamavutoli?
24 Ngati timaphunzira Malemba mwakhama ndi kumatsatira malangizo ake, tingathe kukhala ndi moyo wosangalala kwambiri ngakhale panopa m’dziko lamavutoli. Kutsatira malangizo a m’Malemba kumathandiza kuti mabanja akhale achimwemwe ndiponso kumathetsa nkhaŵa ndi mantha amene dzikoli likuvutika nawo. Kutsatira malangizo a m’Baibulo kumatipatsa chikhulupiriro chakuti tikukondweretsa Mlengi. Palibe winanso kusiyapo Wolamulira wa Chilengedwe Chonse amene angatitsimikizire kuti tikhala “moyo uno, ndi . . . moyo ulinkudza” akadzachotsa padzikoli anthu amene amakana ulamuliro wa Ufumu ndipo motero amasonyeza kuti safuna kuchita zabwino.—1 Timoteo 4:8.
25. Popeza kuti zimene Yehova watsimikiza sizingalephereke, kodi tingayembekezere kuti m’masiku athu kuchitika zotani?
25 Zimene Yehova watsimikiza sizingalephereke. Popeza Mulungu ndiye Mlengi wathu, iye amadziŵa zinthu zomwe zingatipindulitse kwambiri ndipo adzakwaniritsa cholinga chake chakuti anthu okhulupirika akhale pamtendere, akhale osangalala, ndi otetezeka kwamuyaya mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Ponena za nthaŵi yathu ino, mneneri Danieli analemba kuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Motero ino ndiyedi nthaŵi ‘yompsompsona Mwanayo’ ndi kutumikira Ambuye Mfumu Yehova!
[Mawu a M’munsi]
a Poyamba, Mfumu Davide ndiye anali “wodzozedwa,” ndipo “mafumu a dziko lapansi” anali olamulira a Afilisti omwe anasonkhanitsa asilikali awo kuti alimbane naye.
b Mavesi ena a Malemba Achigiriki Achikristu amasonyezanso kuti Yesu ndiye Wodzozedwa wa Mulungu wotchulidwa m’salmo lachiŵirili. Timaona zimenezi tikayerekezera Salmo 2:7 ndi Machitidwe 13:32, 33 komanso tikaliyerekezera ndi Ahebri 1:5; 5:5. Onaninso Salmo 2:9 ndi Chivumbulutso 2:27.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi anthu akhala ‘akulingalira zopanda pake’ zotani?
• N’chifukwa chiyani Yehova amanyoza amitundu?
• Kodi Mulungu watsimikiza kuchita chiyani kwa amitundu?
• Kodi ‘kumpsompsona Mwanayo’ kumatanthauza chiyani?
[Chithunzi patsamba 16]
Davide anaimba za Mfumu yopambana ya Umesiya
[Chithunzi patsamba 17]
Olamulira ndi anthu a Israyeli anachitira chiwembu Yesu Kristu
[Chithunzi patsamba 18]
Kristu anaikidwa kukhala Mfumu pa phiri la Ziyoni lakumwamba