Khalani Ndi Moyo Wopambana!
“Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa . . . Zonse azichita apindula nazo [“zipambana,” NW].”—SALMO 1:1, 3.
1. (a) Kodi achinyamata ambiri m’dziko amaona kuti kupambana n’chiyani? (b) Kodi Baibulo limam’longosola motani munthu wopambana?
CHIPAMBANO—kodi liwu limeneli limatanthauzanji kwa inu? Mnyamata wina anati: “Cholinga changa chachikulu koposa ndi kupambana m’bizinesi.” Msungwana wina anati: “Chimene ndimalakalaka kwambiri ndicho kukhala ndi banja lachimwemwe.” Koma msungwana winanso anati: “Ineyo ndimangofuna kukhala ndi nyumba yangayanga yokongola, galimoto yokongola . . . ndingofuna zanga basi.” Koma vuto n’lakuti chipambano chenicheni sichidalira ndalama, kupeza banja, osatinso ngakhale ntchito yamalipiro abwino. Pa Salmo 1:1-3, timaŵerenga kuti: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa . . . M’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake . . . Zonse azichita apindula nazo [“zipambana”].”
2. Kodi chipambano chenicheni tingachipeze kuti, ndipo njira yokha yochipezera ndi yotani?
2 Baibulo pano likulonjeza chinthu chimene munthu wina aliyense sangachipereke—chipambano chenicheni! Koma silikunena za phindu la ndalama ayi. Baibulo lokhalokhalo limachenjeza kuti: “Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama.” (1 Timoteo 6:10) Chipambano chenicheni chili m’kukondweretsa Mulungu—komanso kutsatira chimalulo cha Yehova. Zokhazo n’zimene zingadzetse chikhutiro ndi chimwemwe chenicheni! Mwinamwake sizikukusangalatsani kumva za kutsatira chilamulo cha Yehova ndi kuuzidwa zochita. Komabe, Yesu anati: “Odala ali osauka mumzimu [“ali awo ozindikira zosoŵa zawo zauzimu,” NW].” (Mateyu 5:3) Kaya mukudziŵa kapena ayi, munalengedwa muli ndi zosoŵa zauzimu—kuphatikizapo chosoŵa chozikika kwambiri chofuna kudziŵa Mulungu ndi kumvetsa zolinga zake. Chifukwa chake, mutha kupeza chimwemwe chenicheni kokha mwa kukwaniritsa zosoŵazo ndi kutsatira “chilamulo cha Yehova.”
Chifukwa Chake Tifunikira Malamulo a Mulungu
3. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osangalala polola Yehova ‘kulongosola mapazi athu’?
3 Mneneri Yeremiya analemba kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Zimenezi n’zoona ponena za anthu onse, aang’ono ndi achikulire omwe. Sitimangosoŵa nzeru yokha ndi chidziŵitso kuti tilongosole mapazi athu; koma tilibe ngakhale kuyenera komwe kochita chimenecho. Pa Chivumbulutso 4:11, Baibulo limati: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” Monga Mlengi wathu, Yehova ndiye “chitsime cha moyo.” (Salmo 36:9) N’chifukwa chake iye ndiye akudziŵa bwino kuposa wina aliyense za mmene tingakhalire bwino ndi moyo. Choncho, iye anapanga malamulo, osati kuti atisoŵetse chisangalalo, koma kuti atithandize kupindula. (Yesaya 48:17) Mukakana chilamulo cha Mulungu, dziŵani pamenepo kuti zonse mwalephera.
4. N’chifukwa chiyani achinyamata ambiri akuwononga miyoyo yawo?
4 Mwachitsanzo, kodi mumadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani achinyamata ambiri amawononga moyo wawo ndi mankhwala osokoneza bongo, chiwerewere, ndi makhalidwe ena oipa? Salmo 36:1, 2 limanena kuti: “Cholakwa cha woipayo chimati mkati mwa mtima wanga [“wake,” NW], Palibe kuopa Mulungu pamaso pake. Pakuti adzidyoletsa yekha m’kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.” Pokhala alibe mantha oyenera a “kuopa Mulungu,” achinyamata ambiri amadzipusitsa mwa kuganiza kuti khalidwe lawo loŵaika pachiswelo silikhala ndi zotsatirapo. Komabe pamapeto pake, amadzakumana ndi choonadi chosasinthika chakuti: “Chimene munthu achifesa, chimenenso, adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.”—Agalatiya 6:7, 8.
‘Kuŵerenga Masiku’
5, 6. (a) N’chifukwa chiyani achinyamata ayenera ‘kuŵerenga masiku awo,’ ndipo kumatanthauzanji kuchita zimenezo? (b) Kodi ‘kukumbukira Mlengi wathu’ kumatanthauzanji?
5 Kodi mungatani kuti mukhale ndi moyo wopambana ndi ‘kututa moyo wosatha’? Mose analemba kuti: “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi aŵiri, kapena tikakhala nayo mphamvu ndi zaka makumi asanu ndi atatu . . . Kumapitako msanga ndipo tithaŵa ife tomwe.” (Salmo 90:10) Nthaŵi zina simungaganizenso kuti kuli imfa. Ndipo achinyamata ambiri amachita ngati kuti ndi osakhoza kufa. Koma Mose akutikumbutsa choonadi choŵaŵa chakuti moyo n’ngwaufupi. Tilibe ndi chitsimikizo chomwe chakuti tidzakhala ndi moyo zaka 70 kapena 80. ‘Zotigwera’ zosadziŵika zimadula ngakhale moyo wa achinyamata athanzi lawo. (Mlaliki 9:11) Nanga tsopano mungaugwiritse ntchito motani moyo wamtengo wapatali umene muli nawowu? Mose anapemphera kuti: “Mutidziŵitse kuŵerenga masiku athu motero, kuti tikhale nawo mtima wanzeru.”—Salmo 90:12.
6 Kodi kuŵerenga masiku kumatanthauzanji? Sikutanthauza kungoganizira za utali wa zaka umene mungakhale ndi moyo. Mose anali kupemphera kuti Yehova aphunzitse anthu Ake mmene angagwiritsire ntchito masiku awo otsalawo m’njira yopereka ulemu kwa Iye. Kodi inuyo mukuŵerenga masiku a moyo wanu—mwa kuona tsiku lililonse kukhala mwayi wapadera wotamandira Mulungu? Baibulo limalimbikitsa achinyamata kuti: ‘Chotsa zopweteka m’mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata n’ngwachabe. Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.’ (Mlaliki 11:10–12:1) Kukumbukira Mlengi wathu sikumangotanthauza kusaiŵala kuti aliko. Pamene m’pandu uja anapempha Yesu kuti, “ndikumbukireni mmene muloŵa Ufumu wanu,” anafuna Yesu kuchita zoposa kungokumbukira dzina lake. Anafuna kuti Yesu akachitepo kanthu, kuti akamuukitse! (Luka 23:42; yerekezani ndi Genesis 40:14, 23; Yobu 14:13.) Mofananamo, kukumbukira Yehova kumafuna kuchitapo kanthu, kuchita zimene iye amafuna. Kodi tingatero kuti inuyo mumam’kumbukira Yehova?
Peŵani Kuwasirira Ochita Zoipa
7. N’chifukwa chiyani achinyamata ena amasankha kumuiŵala Mlengi wawo? Perekani chitsanzo.
7 Achinyamata ambiri amasankha kumuiŵala Yehova chifukwa amaona ngati kukhala Mboni ndi chimtolo chachikulu kwambiri. Mbale wina ku Spain akukumbukira mmene anali kuganizira adakali wachinyamata kuti: “Ndinkakopeka ndi dziko chifukwa choonadi chinkaoneka kukhala chovuta ndi chokhwimitsa zinthu kwambiri. Kukhala pansi, kuphunzira, kupita ku misonkhano, ndi kuvala tayi, ndi zinthu zimene ndinkadana nazo kwambiri.” Kodi nthaŵi zina mumaona kuti kutumikira Mulungu kumakumanitsani zinthu zina? Mwina mudzadabwa kudziŵa kuti wina mwa olemba Baibulo anakhalanso ndi maganizo amenewo. Tatsegulani Baibulo lanu ndi kuŵerenga Salmo 73.
8. N’chifukwa chiyani Asafu ‘anachitira nsanje anthu odzitamandira’?
8 Tiyeni tilipende mwatsatanetsatane salmo limeneli. Mavesi 2 ndi 3 amanena kuti: “Koma ine, ndikadagwa; mapazi anga akadaterereka. Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa.” Timawu tapamwamba pa vesi 1 tikusonyeza kuti salmo limeneli linalembedwa ndi Asafu. Iye anali Mlevi woimba nyimbo ndipo anakhalapo ndi moyo m’nthaŵi ya Mfumu Davide. (1 Mbiri 25:1, 2; 2 Mbiri 29:30) Ngakhale kuti iye anali ndi mwayi wapadera wotumikira m’kachisi wa Mulungu, ‘anachita nsanje’ ndi anthu amene anadzitamandira ndi mphulupulu zawo. Zinthu zinaoneka ngati kuti zinawayendera iwowo; anaoneka kukhala pamtendere komanso otetezeka. Ndipo kupambana kwawoko kunaoneka kukhala koposa “malingaliro a mitima yawo.” (Mavesi 5, 7) Iwo ankalankhula za zoipa zawo “modzitama,” kapena kuti mwamwano. (Vesi 8) ‘Pakamwa pawo ankanena zam’mwamba, ndipo lilime lawo linkayendayenda m’dziko lapansi,’ posaopa aliyense—kaya kumwamba kapena padziko lapansi.—Vesi 9.
9. N’chifukwa chiyani Akristu ena achinyamata lero angaganize mofanana ndi Asafu?
9 Mwina ndi mmenenso zinthu zilili ponena za anzanu kusukulu. Mwina mungaŵamve akudzitama mopanda manyazi za khalidwe lawo lachiwerewere, mapwando omwerekera, ndi kumwetsa moŵa komanso mankhwala osokoneza bongo. Pamene muyerekeza moyo wawo wooneka ngati wosangalatsawo ndi njira yopapatiza imene muyenera kuyendamo monga Mkristu, nthaŵi zina ‘mungachitire nsanje odzitamandira.’ (Mateyu 7:13, 14) Asafu anafika mpaka ponena kuti: “Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe, ndipo ndinasamba m’manja mosalakwa; popeza andisautsa tsiku lonse.” (Mavesi 13, 14) Inde, anayamba kukayikira za phindu la kutumikira Mulungu ndi kutsata moyo wolungama.
10, 11. (a) N’chiyani chinathandiza Asafu kusintha maganizo ake? (b) Ndi motani mmene ochita zoipa alili “poterera”? Perekani chitsanzo.
10 Mwamwayi wake, Asafu sanakhale ndi maganizo otaya mtima ameneŵa kwa nthaŵi yaitali. Mwamsanga anazindikira kuti mtendere wa oipawo unali wachiphamaso—komanso wosakhalitsa! Iye anati: “Indedi muwaika poterera: Muwagwetsa kuti muwawononge. Ha! m’kamphindi ayesedwa bwinja; athedwa konse ndi zoopsa.” (Mavesi 18, 19) Anzanunso ambiri ali “poterera.” M’kupita kwa nthaŵi, khalidwe lawo lopanda umulungulo lidzawatembenukira, zotsatira zake zikumakhala mwina mimba zapathengo, matenda opatsirana mwa kugonana, ngakhalenso kumangidwa kapena kufa kumene! Koma choipitsitsa pa zonse n’chakuti Mulungu amawakana.—Yakobo 4:4.
11 Mboni ina yachitsikana ku Spain inadzionera yokha zoona zake za mfundo imeneyo. Monga mtsikana, iye anali ndi moyo wachiphamaso, akumagwirizana kwambiri ndi gulu lina la achinyamata opanda umulungu. Posapita nthaŵi, iye anakhala pachibwenzi ndi mmodzi wa iwo—womwerekera ndi mankhwala osokoneza bongo. Ngakhale kuti iye amakana kugwiritsa ntchito mankhwalawo, amangogulira chibwenzi chakecho. Iye anavomereza kuti: “Ndimam’thandizanso kum’baya jakisoni ya mankhwalawo.” Mwamwayi wake, mlongoyu anazindikira msanga nabwereranso ku moyo wake wauzimu. Koma patapita nthaŵi, iye anadabwa ndi kuchita mantha kwambiri atamva kuti mnyamata wogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo uja, amene anali chibwenzi chake, anamwalira ndi AIDS. Inde, monga ananenera wamasalmo, anthu opanda umulungu ali “poterera.” Ena akhoza kumwalira mosayembekezeka chifukwa cha moyo wawo wosadziletsa. Koma ponena za enawo amene mwina sangamwalire, ayenera kusintha moyo wawo, apo phuluzi, posachedwa adzakumana ndi “vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu.”—2 Atesalonika 1:7, 8.
12. Kodi mnyamata wina ku Japan anazindikira motani kupusa kosirira anthu ochita zoipa?
12 Choncho kungakhale kupusa kwenikweni kusirira “iwo osam’dziŵa Mulungu”! Ndithudi, oyenera kuwasirira ndi aja amene amam’dziŵa Yehova amenenso ali ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha. Mbale wina wachinyamata ku Japan anazindikira zimenezo atakumana nazo. Monga wachinyamata, iyenso “anali kufuna ufulu waukulu.” Iye akufotokoza kuti: “Ndimaganiza kuti ndikutsalira pa zinthu zina. Ndiyeno ndinalingalira za mmene moyo wanga ukanakhalira ndikanakhala kuti sindinaphunzire choonadi. Ndimayesa kuoneratu moyo wanga wam’tsogolo n’tafika zaka 70 kapena 80 kenako n’kumwalira. Koma Yehova amapereka chiyembekezo cha moyo wosatha! Kuzindikira zimenezi kunandithandiza kumvetsa chimenedi ndinali nacho.” Ngakhale ndi choncho, n’kovuta kukhalabe wokhulupirika ngati wazingidwa ndi anthu osadziŵa malamulo a Mulungu. Kodi zinthu zina zimene mungachite ndi ziti kuti mukane mikhalidwe yoipa imeneyo?
Samalani Mabwenzi Anu!
13, 14. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kusankha mabwenzi mwanzeru?
13 Tiyeni tionenso mmene am’fotokozera munthu wopambana pa Salmo 1:1-3: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m’njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo [“zipambana”].”
14 Choyamba dziŵani kuti mabwenzi anu amachita mbali yaikulu. Miyambo 13:20 imati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” Izi sizikutanthauza kuti muyenera kukhala amphwayi, achidani, kapena amwano kwa achinyamata amene si Mboni za Yehova ayi. Baibulo limatilimbikitsa kukonda anansi athu komanso ‘kukhala mwamtendere ndi anthu onse.’ (Aroma 12:18; Mateyu 22:39) Komabe, ngati mugwirizana kwambiri ndi aja amene satsatira miyezo ya Baibulo, mungapeze kuti ‘mukuyenda mu uphungu’ wawo.
Mapindu a Kuŵerenga Baibulo
15. Kodi achinyamata angakulitse motani chilakolako cha kuŵerenga Baibulo?
15 Wamasalmo anaonanso kuti munthu wopambana amakonda kuŵerenga chilamulo cha Mulungu mwa ‘kuchilingalira usana ndi usiku.’ (Salmo 1:1, 2) N’zoona kuti Baibulo si buku lofeŵa kwambiri kuliŵerenga, chifukwa mmenemo muli “zina zovuta kuzizindikira.” (2 Petro 3:16) Koma kuŵerenga Baibulo sikuyenera kukhala kotopetsa. N’kotheka ‘kukulitsa chilakolako cha mkaka wosasukuluka’ wa Mawu a Mulungu. (1 Petro 2:2, NW) Yesani kuŵerenga pang’ono pokha tsiku lililonse. Ngati pali mfundo zimene simukumvetsa, zifufuzeni. Mukatero, sinkhasinkhani zimene mwaŵerengazo. (Salmo 77:11, 12) Ngati zikuvutani kuti musumike maganizo pazimene mukuŵerenga, yesani kuŵerenga motulutsa mawu koma apansipansi. M’kupita kwa nthaŵi, chidwi chanu poŵerenga Baibulo chidzakula. Mlongo wina wachitsikana ku Brazil anakumbukira kuti: “Nthaŵi zonse ndimaona ngati Yehova ali patali ndi ine. Koma pamiyezi ingapo yapitayi, ndakhala ndikuwongolera phunziro langa laumwini ndi kaŵerengedwe kanga ka Baibulo. Tsopano ndikuona kuti unansi wanga ndi Yehova wakhala wolimbirapo. Tsopano ali pafupi kwambiri ndi ine.”
16. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tipindule kwambiri ndi misokhano ya mpingo?
16 Kufika pamisonkhano ya mpingo kumathandizanso kuti mukule mwauzimu. Ngati ‘muyang’anira mamvedwe anu,’ mungalimbikitsidwe kwambiri. (Luka 8:18) Kodi nthaŵi zina mumaona kuti misonkhano sikukusangalatsani kwambiri? Chabwino, dzifunseni kuti, ‘Kodi ineyo ndimachitaponji pofuna kuti misonkhano indisangalatse? Kodi ndimatchera khutu? Kodi ndimakonzekera? Kodi ndimayankhapo?’ Ndi iko komwe, Baibulo limatiuza kuti ‘tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, . . . tikumadandaulirana’ wina ndi mnzake. (Ahebri 10:24, 25) Kuti muchite zimenezo muyenera kutengamo mbali! Komanso, kuti mutengemo mbali muyenera kukonzekereratu. Mlongo wachitsikana anavomereza kuti: “Kuyankha pamisonkhano n’kosavuta ukakonzekera.”
Kutsatira Njira ya Mulungu Kumathandiza Munthu Kupambana
17. N’chifukwa chiyani muŵerengi wa Baibulo wakhama “akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi”?
17 Wamasalmo akupitiriza kufotokoza munthu wopambana kuti “akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi.” Mitsinje ya madzi imene anali kutanthauza iyenera kuti ndi ngalande zimene panthaŵiyo amazigwiritsa ntchito pothirira minda yampesa. (Yesaya 44:4) Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kuli ngati kutunga madzi mumtsinje wosaphwa umenewo wa madzi ochirikiza moyo komanso otsitsimutsa. (Yeremiya 17:8) Tsiku ndi tsiku mudzalandira nyonga yokulimbikitsani pokumana ndi mayesero ndi zovuta zina. Pokhala mutaphunzira malingaliro a Yehova, mudzapeza nzeru yokuthandizani kusankha zinthu mwanzeru.
18. Kodi n’chiyani chingatheketse wachinyamata kupambana potumikira Yehova?
18 Nthaŵi zina kutumikira Yehova kungaoneke kukhala kovuta. Koma musaganize konse kuti simungakwanitse. (Deuteronomo 30:11) Baibulo likukulonjezani kuti ‘zonse zimene muchita zidzapambana’ m’kupita kwa nthaŵi, malinga ngati cholinga chanu chachikulu chikhala kukondweretsa mtima wa Yehova! (Miyambo 27:11) Ndipo kumbukirani, simudzakhala nokha pochita zinthu zimenezo. Yehova ndi Yesu Kristu adzakuchirikizani. (Mateyu 28:20; Ahebri 13:5) Iwo amadziŵa zovuta zimene mukumana nazo, ndipo sadzakusiyani. (Salmo 55:22) Komanso gulu lonse la “abale” lidzakuchirikizani, komanso makolo anu ngati ali oopa Mulungu. (1 Petro 2:17) Pokhala ndi okuchirikizani onsewo, limodzi ndi kutsimikiza mtima kwanu komanso khama lanu, mutha kukhala ndi moyo wopambana, osati lero lokha komanso ku umuyaya wonse!
Mafunso Obwereramo
◻ Kodi chipambano chenicheni n’chiyani?
◻ N’chifukwa chiyani timafunikira Yehova kuti alongosole mapazi athu?
◻ Kodi achinyamata ‘angaŵerenge motani masiku awo’?
◻ N’chifukwa chiyani kuli kupusa kusirira anthu ochita zoipa?
◻ Kodi kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku komanso kufika pamisonkhano nthaŵi zonse kungathandize motani achinyamata kukhala ndi moyo wopambana?
[Chithunzi patsamba 20]
Posoŵa mantha oyenera a “kuopa Mulungu,” achinyamata ambiri amadziloŵetsa m’khalidwe lowawononga
[Chithunzi patsamba 22]
Kaŵirikaŵiri, achinyamata amaiŵala kuti zochita zawo zimakhala ndi zotsatirapo zake
[Chithunzi patsamba 23]
Kulitsani chidwi choŵerenga Baibulo
[Chithunzi patsamba 23]
Mudzasangalala kwambiri ndi misonkhano ngati muyankhapo