Musalole Chilichonse Kukulepheretsani Kupeza Ulemerero
“Wa mtima wodzichepetsa adzapeza ulemerero.”—MIY. 29:23.
1, 2. (a) Kodi mawu amene anawamasulira kuti “ulemerero” amanena za chiyani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhani ino?
KODI inuyo mukamva mawu akuti “ulemerero” mumaganiza za chiyani? Kodi mumaganiza za kukongola kwa chilengedwe? (Sal. 19:1) Kapena kodi mumaganizira ulemu umene anthu amapatsidwa chifukwa choti ndi achuma, anzeru kapena akwanitsa kuchita zinazake? M’Baibulo, mawu amene anawamasulira kuti “ulemerero” amanena za kulemera kwa chinthu. Kale ndalama zinkapangidwa ndi zinthu ngati golide kapena siliva. Ndalamayo ikakhala yolemera kwambiri inkakhalanso yamtengo wapatali. Choncho mawu amene ankatanthauza kulemera anayamba kugwiritsidwa ntchito ponena za zinthu zamtengo wapatali kapena zochititsa kaso.
2 Anthufe timalemekeza anthu audindo kapena otchuka. Koma kodi Mulungu amaona kuti munthu amakhala wolemekezeka pa zifukwa ziti? Malemba amasonyeza kuti Mulungu amapereka ulemerero kwa anthu. Mwachitsanzo, pa Miyambo 22:4 timawerenga kuti: “Zotsatirapo za kudzichepetsa ndiponso kuopa Yehova ndizo chuma, ulemerero, ndi moyo.” Nayenso Yakobo analemba kuti: “Dzichepetseni pamaso pa Yehova, ndipo iye adzakukwezani.” (Yak. 4:10) Kodi ulemerero umene Yehova amapereka kwa anthu ndi wotani? Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kupeza ulemerero umenewo? Nanga tingathandize bwanji anthu ena kuupeza?
3-5. Kodi Yehova angatitsogolere ku ulemerero wotani?
3 Wamasalimo ankakhulupirira kuti Yehova adzagwira dzanja lake lamanja n’kumutsogolera ku ulemerero. (Werengani Salimo 73:23, 24.) Kodi Yehova amapatsa bwanji anthu ulemerero? Iye amatsogolera anthu ake odzichepetsa ku ulemerero powadalitsa m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, amawathandiza kumvetsa cholinga chake. (1 Akor. 2:7) Iye amalolanso kukhala pa ubwenzi wolimba ndi anthu amene amamumvera.—Yak. 4:8.
4 Yehova amalemekezanso atumiki ake powapatsa mwayi wolalikira uthenga wabwino. (2 Akor. 4:1, 7) Utumiki umenewu umatipatsa ulemerero. Anthu amene amachita utumikiwu n’cholinga choti alemekeze Yehova ndiponso kuthandiza anthu ena, akulonjezedwa kuti: “Amene akundilemekeza ndiwalemekeza.” (1 Sam. 2:30) Anthu oterewa amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo nthawi zambiri amalemekezedwa ndi atumiki anzawo.—Miy. 11:16; 22:1.
5 Kodi tsogolo la anthu amene ‘amayembekezera Yehova, ndi kusunga njira zake’ ndi lotani? Baibulo limawalonjeza kuti: “[Yehova] adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi. Pamene oipa akuphedwa, iwe udzaona.” (Sal. 37:34) Iwo amayembekezera kuti Mulungu adzawapatsa moyo wosatha.—Sal. 37:29.
“SINDIFUNA ULEMERERO WOCHOKERA KWA ANTHU”
6, 7. N’chifukwa chiyani anthu ambiri sankakhulupirira Yesu?
6 Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kulandira ulemerero umene Yehova akufuna kutipatsa? Chinthu chimodzi ndi kulemekeza kwambiri maganizo a anthu amene sali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Taonani zimene mtumwi Yohane analemba pofotokoza za olamulira m’nthawi ya Yesu. Iye anati: “Ambiri, ngakhalenso olamulira anamukhulupirira [Yesu], koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze poyera, poopa kuti angawachotse musunagoge. Pakuti anakonda kwambiri ulemerero wa anthu kuposa ulemerero wa Mulungu.” (Yoh. 12:42, 43) Olamulirawo akanakhala kuti sankalemekeza kwambiri maganizo a Afarisi, zinthu zikanawayendera bwino.
7 Yesu anali atafotokoza kale zinthu zimene zinkalepheretsa anthu ambiri kumukhulupirira. (Werengani Yohane 5:39-44.) Aisiraeli ankayembekezera Mesiya kwa zaka zambiri. Pamene Yesu anayamba kuphunzitsa, n’kutheka kuti anthu ena anazindikira kuchokera mu ulosi wa Danieli kuti nthawi yoti Khristu aonekere yafika. Miyezi ingapo Yesu asanayambe kuphunzitsa, Yohane Mbatizi ankalalikira ndipo anthu ankadzifunsa kuti: “Kodi Khristu uja si ameneyu?” (Luka 3:15) Koma Mesiya amene ankamuyembekezera kwa nthawi yaitali uja atafika, anthu odziwa bwino Chilamulo sanamulandire. Posonyeza chifukwa chake, Yesu anawafunsa kuti: “Mungakhulupirire bwanji, pamene mumalandira ulemerero kuchokera kwa anthu anzanu, koma osayesetsa kupeza ulemerero wochokera kwa Mulungu yekhayo?”
8, 9. N’chiyani chimachititsa munthu kuona kuti ulemerero wochokera kwa anthu ndi wofunika kuposa wochokera kwa Mulungu? Perekani chitsanzo.
8 Tiyeni tione chitsanzo chimene chingatithandize kumvetsa kuti anthu angaone kuti ulemerero wochokera kwa anthu ndi wofunika kuposa wochokera kwa Mulungu. Kumwamba kuli nyenyezi zambirimbiri zimene zimawala. “Ulemerero wa nyenyezi” ndi wochititsa kaso. (1 Akor. 15:40, 41) Koma mukayang’ana kumwamba muli mumzinda wokhala ndi magetsi ambiri, nyenyezizo sizioneka kwenikweni. N’chifukwa chiyani sizioneka? Kodi kuwala kwa magetsi kumakhala kwamphamvu kapena kokongola kwambiri kuposa kwa nyenyezi? Ayi. Koma zimachitika chifukwa chakuti magetsiwo ali pafupi kwambiri ndipo amatilepheretsa kuona nyenyezizo. Choncho kuti tione kuwala kwa nyenyezi, tiyenera kupita kumalo kumene kulibe magetsi.
9 Ndi mmene zililinso ndi ulemerero. Ngati ulemerero wochokera kwa anthu uli pafupi ndi mtima wathu, ungatilepheretse kuona kuti ulemerero wochokera kwa Yehova ndi wofunika. Anthu ambiri salandira uthenga wa Ufumu chifukwa choopa zimene anzawo kapena achibale awo angaganize. Koma kodi atumiki a Yehova angakhalenso ndi mtima wofuna ulemerero wochokera kwa anthu? Tiyerekeze kuti wachinyamata wapemphedwa kuti alalikire m’dera limene anthu ambiri amamudziwa koma sadziwa kuti ndi wa Mboni za Yehova. Kodi iye adzaopa? Nanga bwanji ngati munthu akunyozedwa chifukwa chofuna kuchita zambiri potumikira Yehova? Kodi adzasintha zolinga zake chifukwa cha anthuwo? Nanga ngati Mkhristu wachita tchimo lalikulu? Kodi adzabisa poopa zimene zingamuchitikire mu mpingo kapena poopa kukhumudwitsa anzake? Ngati iye akufunitsitsa kukonza ubwenzi wake ndi Yehova, ‘adzaitana akulu a mpingo’ kuti amuthandize.—Werengani Yakobo 5:14-16.
10. (a) Kodi kuganizira kwambiri mmene anthu ena angationere kungatisokoneze bwanji? (b) Kodi chidzachitike n’chiyani tikakhala odzichepetsa?
10 Tiyerekeze kuti inuyo mukuona kuti mukuyesetsa ndithu kukhala Mkhristu wabwino, koma m’bale wina wakupatsani uphungu. Malangizo ake akhoza kukuthandizani ngati mupewa kuwanyalanyaza chifukwa cha kunyada, kusafuna kunyozeka kapena kufuna kudziikira kumbuyo. Tiyerekezenso kuti mukugwira ntchito inayake ndi Mkhristu mnzanu. Kodi mudzaganizira kwambiri za amene adzalemekezedwe chifukwa cha ntchitoyo? Nthawi zonse muzikumbukira kuti munthu “wa mtima wodzichepetsa adzapeza ulemerero.”—Miy. 29:23.
11. Kodi tiyenera kumva bwanji mumtima mwathu tikamayamikiridwa ndipo n’chifukwa chiyani?
11 Oyang’anira ndiponso amene “akuyesetsa kuti akhale” oyang’anira ayeneranso kusamala kuti asayambe kufuna ulemerero wochokera kwa anthu. (1 Tim. 3:1; 1 Ates. 2:6) Kodi m’bale ayenera kuchita chiyani akayamikiridwa chifukwa cha zimene wachita? N’zodziwikiratu kuti sangafune kuimika chipilala cha chikumbutso chake ngati mmene anachitira Mfumu Sauli. (1 Sam. 15:12) Koma kodi amazindikira kuti ndi Yehova amene wamuthandiza kukwanitsa zimene wachitazo? Kodi amadziwanso kuti zinthu zingamuyendere bwino m’tsogolo pokhapokha Yehova atamudalitsa ndiponso kumuthandiza? (1 Pet. 4:11) Mmene timamvera mumtima mwathu tikamayamikiridwa zimasonyeza ulemerero umene timafuna kwambiri.—Miy. 27:21.
“MUKUFUNA KUCHITA ZOKHUMBA ZA ATATE WANU”
12. N’chiyani chinalepheretsa Ayuda ena kumvetsera uthenga wa Yesu?
12 Zokhumba zathu zingatilepheretsenso kupeza ulemerero wochokera kwa Mulungu. Ngati timakhumba zinthu zolakwika mwina sitingafune n’komwe kumvetsera choonadi. (Werengani Yohane 8:43-47.) Yesu anauza Ayuda ena kuti sankafuna kumva uthenga wake chifukwa chakuti ‘ankafuna kuchita zokhumba za atate wawo Mdyerekezi.’
13, 14. (a) Kodi akatswiri amanena kuti chimachitika n’chiyani ngati anthu akutilankhula? (b) N’chiyani chimachititsa munthu kusankha woti amumvetsere?
13 Nthawi zina anthufe timangomva zimene tikufuna kumva. (2 Pet. 3:5) Yehova anatilenga m’njira yoti tizitha kunyalanyaza phokoso losafunika. Panopa tangoyesani kukhala phee kuti muone zinthu zosiyanasiyana zimene mungamve. N’kutheka kuti zina zimene mwazimva panopa simunkazimva poyamba. Ngakhale kuti mungathe kumva zonsezo, mbali ina ya ubongo wanu inkakuthandizani kuti muzingoika maganizo anu pa chinthu chimodzi. Koma akatswiri ena anapeza kuti ubongo umavutika kuchita zimenezi ngati phokoso limene tikumva ndi la kulankhula kwa anthu. Izi zikutanthauza kuti ngati anthu awiri akulankhula, mumafunika kusankha amene mukufuna kumumvetsera. Ayuda amene ankafuna kuchita zokhumba za atate wawo, Mdyerekezi, sanamvetsere Yesu.
14 Anthufe timamva uthenga kuchokera ‘kunyumba ya nzeru’ komanso ‘nyumba ya kupusa.’ (Miy. 9:1-5, 13-17) Zili ngati nzeru ndiponso kupusa zikutiitana pa nthawi imodzi ndipo tiyenera kusankha kumvetsera mbali imodzi. Kodi timvetsera ndani? Zimadalira amene tikufuna kumutsanzira. Nkhosa za Yesu zimamvetsera mawu ake ndi kumutsatira. (Yoh. 10:16, 27) Zimakhala “kumbali ya choonadi.” (Yoh. 18:37) “Sizidziwa mawu a alendo.” (Yoh. 10:5) Anthu odzichepetsa chonchi amapeza ulemerero.—Miy. 3:13, 16; 8:1, 18.
MASAUTSO ANGAWA “AKUTANTHAUZA ULEMERERO KWA INU”
15. Kodi zinatheka bwanji kuti masautso a Paulo ‘atanthauze ulemerero’ kwa anthu ena?
15 Tikamayesetsa kupirira pochita zimene Yehova amafuna, timathandiza anthu ena kupezanso ulemerero. Paulo analembera mpingo wa ku Efeso kuti: “Ndikukupemphani kuti musabwerere m’mbuyo poona masautso angawa, amene ndikukumana nawo chifukwa cha inu, pakuti akutanthauza ulemerero kwa inu.” (Aef. 3:13) Kodi zinatheka bwanji kuti masautso a Paulo ‘atanthauze ulemerero’ kwa Aefeso? Paulo anali wofunitsitsa kuwatumikirabe ngakhale kuti ankakumana ndi mayesero. Izi zinathandiza Aefeso kuzindikira kuti mwayi wawo wotumikira Mulungu unali wamtengo wapatali kwambiri. Ngati Paulo akanafooka, iwo akanaona kuti ubwenzi wawo ndi Yehova, utumiki wawo komanso chiyembekezo chawo n’zopanda ntchito. Koma kupirira kwa Paulo kunasonyeza kuti Chikhristu ndi chofunika kwambiri ndipo munthu ayenera kulolera kutaya chilichonse kuti akhale wophunzira wa Yesu.
16. Kodi Paulo anakumana ndi masautso otani ku Lusitara?
16 Kodi khama ndiponso kupirira kwa Paulo zinathandiza bwanji? Lemba la Machitidwe 14:19, 20 limati: “Ayuda anafika kuchokera ku Antiokeya ndi ku Ikoniyo ndipo anakopa anthuwo. Choncho anaponya Paulo miyala ndi kumukokera kunja kwa mzindawo, poganiza kuti wafa. Koma pamene ophunzira anamuzungulira, anadzuka ndi kukalowa mumzinda. Tsiku lotsatira iye pamodzi ndi Baranaba anachoka ndi kupita ku Debe.” Tangoganizani zimene Paulo anachita. Iye atamenyedwa mpaka kutsala pang’ono kufa, mawa lake anayamba ulendo wa makilomita 100 wapansi.
17, 18. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Timoteyo ankadziwa bwino zimene Paulo anakumana nazo ku Lusitara? (b) Kodi kupirira kwa Paulo kunathandiza bwanji Timoteyo?
17 Kodi Timoteyo analipo pamene Paulo ankaponyedwa miyala? Nkhani ya m’buku la Machitidwe sinena zimenezi koma n’kutheka kuti analipo. Taonani zimene Paulo analembera Timoteyo m’kalata yake yachiwiri. Iye anati: “Iwe wayesetsa kutsatira chiphunzitso changa, moyo wanga . . . . Ukudziwanso mazunzo ndi masautso amene ndinakumana nawo ku Antiokeya [anamuponya kunja kwa mzinda], ku Ikoniyo [ankafuna kumuponya miyala], ndi ku Lusitara [anamuponya miyala]. Komabe, Ambuye anandipulumutsa m’mazunzo onsewa.”—2 Tim. 3:10, 11; Mac. 13:50; 14:5, 19.
18 Timoteyo ankadziwa kuti Paulo anapirira mavuto onsewa. Iye ayenera kuti anaphunzira zambiri kwa Paulo. Pamene Paulo anapita ku Lusitara, anapeza Timoteyo akuchita bwino kwambiri mu mpingo moti “abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo anamuchitira umboni wabwino.” (Mac. 16:1, 2) Patapita nthawi, Timoteyo anayenerera maudindo ena akuluakulu.—Afil. 2:19, 20; 1 Tim. 1:3.
19. Kodi kupirira kwathu kungathandize bwanji ena?
19 Nafenso tikamapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika, tidzapereka chitsanzo chabwino kwa achinyamata moti akhoza kudzakhala atumiki a Mulungu odalirika kwambiri. Achinyamata samangotiyang’ana n’kutengera kalankhulidwe kathu kapena kaphunzitsidwe kathu mu utumiki. Amaonanso zimene timachita tikakumana ndi mavuto. Paulo ‘anapirirabe zinthu zonse’ n’cholinga choti anthu ena okhulupirika ‘alandire chipulumutso ndiponso ulemerero wosatha.’—2 Tim. 2:10.
20. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kufunafuna ulemerero wochokera kwa Mulungu?
20 Tiyeni tonse tipitirize kufunafuna “ulemerero wochokera kwa Mulungu yekhayo.” (Yoh. 5:44; 7:18) Yehova amapereka ‘moyo wosatha kwa anthu amene akuyesetsa kupeza ulemerero.’ (Werengani Aroma 2:6, 7.) Ngati ‘tipirira m’ntchito yabwino’ tidzathandizanso anthu ena kukhala okhulupirika n’kudzapezanso moyo wosatha. Choncho tisalole chilichonse kutilepheretsa kupeza ulemerero wochokera kwa Mulungu.