MUTU 26
Mulungu “Wokonzeka Kukhululuka”
1-3. (a) Kodi ndi katundu wolemera uti amene Davide anasenza, nanga n’chiyani chinamukhazika mtima pansi? (b) Kodi tikachimwa zimakhala ngati tanyamula katundu uti, koma kodi Yehova amatitsimikizira chiyani?
WOLEMBA masalimo Davide anati: “Zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga. Sindingathe kuzisenza chifukwa zikulemera kwambiri ngati katundu wolemera. Thupi langa lonse lachita dzanzi ndipo ndilibiretu mphamvu.” (Salimo 38:4, 8) Davide ankadziwa kuti tikamadziimba mlandu chifukwa chochita tchimo, zimakhala ngati tasenza katundu wolemera kwambiri. Koma panali chinthu china chimene chinkamukhazika mtima pansi. Anazindikira kuti ngakhale kuti Yehova amadana ndi machimo, iye sadana ndi munthu wochimwa amene walapa mochokera pansi pa mtima n’kusiya machimowo. Pokhala ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova ndi wofunitsitsa kuchitira chifundo anthu olapa, Davide anati: “Inu Yehova ndinu . . . wokonzeka kukhululuka.”—Salimo 86:5.
2 Ifenso tikachita tchimo, chikumbumtima chathu chikhoza kumativutitsa kwambiri ndipo zingakhale ngati tanyamula katundu wolemera. Kumva chisoni kotereku n’kwabwino. Kungatichititse kuti tiyesetse kukonza zomwe talakwitsazo. Komabe, nthawi zina tikhoza kumadziimba mlandu mopitirira malire mpaka kufika pomaganiza kuti Yehova sangatikhululukire ngakhale titalapa mochokera pansi pa mtima. Ngati ‘tingakhale ndi chisoni chopitirira malire,’ Satana angayesetse kutichititsa kuti tisiye kutumikira Yehova, potipangitsa kuganiza kuti Yehovayo amationa kuti ndife osafunika ndiponso osayenera kumutumikira.—2 Akorinto 2:5-11.
3 Koma kodi ndi zoona kuti Yehova amationa choncho? Ayi ndithu. Tikutero chifukwa kukhululuka ndi njira imodzi imene Yehova amasonyezera chikondi chake chachikulu. M’Mawu ake, iye amatitsimikizira kuti tikalapa mochokera pansi pa mtima, amakhala wokonzeka kutikhululukira. (Miyambo 28:13) Kuti tisamakayikire kuti Yehova akhoza kutikhululukira, tiyeni tikambirane chifukwa chake amatikhululukira komanso mmene amachitira zimenezi.
Chifukwa Chake Yehova Ndi “Wokonzeka Kukhululuka”
4. Kodi Yehova amakumbukira chiyani chokhudza mmene anatilengera, ndipo zimenezi zimakhudza bwanji mmene amachitira nafe zinthu?
4 Yehova amadziwa zimene sitingathe kuchita. Lemba la Salimo 103:14 limati: “Iye akudziwa bwino mmene anatipangira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” Saiwala kuti tinapangidwa kuchokera kudothi komanso kuti nthawi zambiri timalakwitsa zinthu chifukwa choti ndife ochimwa. Mawu akuti amadziwa bwino “mmene anatipangira” akutikumbutsa zimene Baibulo limanena. Timayerekezera Yehova ndi woumba mbiya ndipo ifeyo limatiyerekezera ndi dongo loumbira zinthu. (Yeremiya 18:2-6) Woumba Wamkuluyu amachita nafe zinthu mokoma mtima poganizira kuti ndife ochimwa komanso potengera zimene timachita akatipatsa malangizo.
5. Kodi buku la Aroma limatithandiza bwanji kudziwa kuti uchimo umagwira anthu mwamphamvu kwambiri?
5 Yehova amadziwa kuti uchimo ndi wamphamvu kwambiri. Baibulo limafotokoza kuti anthufe uchimo umatigwira mwamphamvu kwambiri ndipo umachititsa kuti tizifa. Kodi timadziwa bwanji kuti uchimo ndi wamphamvu kwambiri? M’buku la Aroma, mtumwi Paulo anafotokoza kuti ‘timalamuliridwa ndi uchimo,’ ngati mmene zimakhalira ndi asilikali amene amalamuliridwa ndi mtsogoleri wawo (Aroma 3:9); uchimo ‘umalamulira’ anthu ngati mfumu (Aroma 5:21); ‘umakhala nafe’ (Aroma 7:17, 20) ndiponso “lamulo” lake limagwira ntchito m’thupi mwathu nthawi zonse, n’kumayesa kutichititsa zofuna za uchimowo. (Aroma 7:23, 25) Izitu zikungosonyezeratu kuti uchimo ndi wamphamvu kwambiri kwa anthu omwe si angwirofe.—Aroma 7:21, 24.
6, 7. (a) Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene alapa n’kupempha kuti awakhululukire? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti tikhoza kumachita machimo mwadala ndipo Mulungu atikhululukira chifukwa choti ndi wachifundo?
6 Choncho Yehova amadziwa kuti sitingathe kumumvera osalakwitsa chilichonse, ngakhale titayesetsa bwanji. Mwachikondi amatitsimikizira kuti tikalapa mochokera pansi pa mtima n’kupempha kuti atichitire chifundo, iye adzatikhululukira. Lemba la Salimo 51:17 limati: “Nsembe zimene Mulungu amasangalala nazo ndi kudzimvera chisoni mumtima. Inu Mulungu, simudzakana mtima wosweka ndi wophwanyika.” Yehova sakana munthu yemwe ali ndi “mtima wosweka ndi wophwanyika” chifukwa chodziimba mlandu kwambiri.
7 Komabe, kodi zimenezi zikutanthauza kuti popeza tinabadwa ndi uchimo tikhoza kumachimwa mwadala n’kumaganiza kuti Mulungu ndi wachifundo atikhululukira? Ayi ndithu. Yehova sachita zinthu pongotengera mmene akumvera. Chifundo chake chili ndi malire. Iye sakhululukira anthu amene amachita machimo mwadala koma osalapa n’kuwasiya. (Aheberi 10:26) Komabe, akaona kuti wina ali ndi mtima wolapa amamukhululukira. Tsopano tiyeni tikambirane mawu ena ochititsa chidwi amene Baibulo limagwiritsa ntchito pofotokoza mmene Yehova amasonyezera chikondi chake m’njira yapaderayi.
Kodi Yehova Amakhululuka Mpaka Pati?
8. Kodi tingati Yehova amachita chiyani akatikhululukira, nanga timamva bwanji chifukwa cha zimenezi?
8 Davide atalapa ananena mawu ananena kuti: “Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, sindinabise cholakwa changa. . . . Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.” (Salimo 32:5) Mawu akuti “munandikhululukira” anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chiheberi amene kwenikweni amatanthauza “kunyamula” kapena “kutenga.” Palembali anawagwiritsa ntchito ponena za kuchotsa “cholakwa, tchimo kapena choipa.” Choncho tingati Yehova ananyamula machimo a Davide n’kuwachotsa. N’zosakayikitsa kuti zimenezi zinathandiza Davide kuti asamadziimbe mlandu kwambiri. (Salimo 32:3) Ifenso tingakhulupirire ndi mtima wonse kuti Mulungu akhoza kutichotsera machimo athu ngati titamupempha kuti atikhululukire pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo ya Yesu.—Mateyu 20:28.
9. Kodi Yehova amaika machimo athu kutali bwanji ndi ife?
9 Davide anagwiritsanso ntchito mawu ena amphamvu ofotokoza kukhululuka kwa Yehova. Iye anati: “Mofanana ndi mmene kotulukira dzuwa kwatalikirana ndi kolowera dzuwa, Mulungu waikanso zolakwa zathu kutali ndi ife.” (Salimo 103:12) Dzuwa limatuluka kum’mawa n’kukalowa kumadzulo. Kodi kum’mawa n’kotalikirana bwanji ndi kumadzulo? Nthawi zonse kum’mawa kumakhala kotalikirana kwambiri ndi kumadzulo ndipo mbali ziwirizi sizingakumane. Katswiri wina wa Baibulo anati mawuwa amatanthauza “kutali kwambiri koti sitingakuyerekezere.” Mawu a Davide ouziridwawa amatithandiza kudziwa kuti Yehova akakhululuka, amatenga machimo athu n’kukawataya kutali kwambiri.
10. Yehova akatikhululukira, n’chifukwa chiyani sitifunika kumamva kuti ndife othimbirira ndi machimo kwa moyo wathu wonse?
10 Kodi munayesapo kuchapa chovala choyera chomwe chathimbirira? Mwina munayesetsa kuti muchotse zothimbirirazo koma sizinatheke. Koma taonani zimene Yehova amachita pa nkhani yokhululuka. Iye anati: “Ngakhale kuti machimo anu ndi ofiira kwambiri, adzayera kwambiri. Ngakhale kuti ndi ofiira ngati magazi, adzayera ngati thonje.” (Yesaya 1:18)a Patokha sitingathe kuchotsa uchimo womwe tingati unatithimbiriritsa. Koma Yehova akhoza kuchotseratu kuthimbirira kumeneku. Iye akatikhululukira machimo athu, sitifunikanso kumamva kuti ndife othimbirira ndi machimowo kwa moyo wathu wonse.
11. Kodi Yehova amaponya machimo athu kumbuyo kwake m’njira yotani?
11 Hezekiya atachiritsidwa matenda omwe akanafa nawo, analemba nyimbo yosangalatsa kwambiri. Iye anauza Yehova kuti: “Machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.” (Yesaya 38:17) Lembali likusonyeza kuti Yehova amatenga machimo a munthu wochimwa yemwe walapa n’kuwaponya kumbuyo kwake kumene iye sawaonanso kapena kuwaganiziranso. Mogwirizana ndi zimene buku lina linanena zokhudza lembali, tikhoza kunenanso kuti lembali limanena kuti: “Mwachititsa [machimo anga] kukhala ngati sanachitike.” Kodi zimenezi si zolimbikitsa kwambiri?
12. Kodi mneneri Mika anasonyeza bwanji kuti Yehova akatikhululukira amataya kutali machimo athu ndipo sawaganiziranso?
12 Ponena za lonjezo la Mulungu lobwezeretsa zinthu, Mika anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Yehova adzakhululukira anthu ake omwe alapa. Iye anati: “Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu, amene amakhululukira zolakwa . . . anthu ake otsala omwe ndi cholowa chake? . . . Machimo athu onse mudzawaponya m’nyanja pamalo ozama.” (Mika 7:18, 19) Taganizirani zimene mawu amenewa anatanthauza kwa atumiki a Yehova pa nthawiyo. Kodi zikanatheka kuvuula chinthu chimene chamira “m’nyanja pamalo ozama”? Choncho zimene Mika ananena zikusonyeza kuti Yehova akakhululuka, amataya kutali machimo athu ndipo sawaganiziranso.
13. Kodi mawu a Yesu akuti “mutikhululukire zolakwa zathu” amatanthauza chiyani?
13 Pofuna kutithandiza kumvetsa zimene Yehova amachita akakhululuka, Yesu anafotokoza chitsanzo cha zomwe zimachitika pakati pa munthu wokongoza zinthu ndi wokongola. Iye anatilimbikitsa kupemphera kuti: “Mutikhululukire zolakwa zathu.” (Mateyu 6:12) Mawu a chilankhulo choyambirira omwe anawamasulira kuti “zolakwa,” ankatanthauza ngongole. Choncho Yesu anayerekezera machimo ndi ngongole. (Luka 11:4) Tikachita tchimo timakhala ndi “ngongole” yoti tipereke kwa Yehova. Ponena za mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “mutikhululukire,” buku lina linati amatanthauza “kukhululukira ngongole n’kusiya osadzailonjereranso.” Zimenezi n’zimene Yehova amachita akatikhululukira. Iye amakhala ngati wathetsa ngongole imene timafunika kumubwezera. Izitu n’zolimbikitsa kwambiri kwa anthu ochimwa omwe alapa. Yehova sangalonjerere ngongole imene anaithetsa.—Salimo 32:1, 2.
14. Kodi mawu akuti “machimo anu afafanizidwe” amatithandiza bwanji kumvetsa bwino zimene Yehova amachita akatikhululukira?
14 Zimene Yehova amachita pokhululuka zafotokozedwanso bwino pa Machitidwe 3:19 kuti: “Choncho lapani ndi kutembenuka kuti machimo anu afafanizidwe.” Mawu akuti “afafanizidwe” anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chigiriki amene akhoza kutanthauza “kupukuta, . . . kufufuta kapena kuwononga.” Mogwirizana ndi zimene akatswiri ena a Baibulo amanena, mawuwa amafotokoza za kufufuta zimene munthu walemba. Kodi zimenezi zinkatheka bwanji? Inki imene kale ankaigwiritsa ntchito, nthawi zambiri ankaipanga posakaniza makala, manthova a mitengo, madzi ndiponso zinthu zina. Munthu akangomaliza kulemba ndi inkiyo, ankatha kutenga siponji yonyowa n’kufufuta zimene analembazo. Zimenezitu zikutithandiza kumvetsa bwino chifundo cha Yehova. Iye akatikhululukira machimo athu, zimakhala ngati watenga siponji n’kuwafufuta.
15. Kodi Yehova amafuna kuti tidziwe zinthu ziti zokhudza iyeyo?
15 Tikaganizira mawu ochititsa chidwi osiyanasiyana amenewa, n’zodziwikiratu kuti Yehova amafuna kuti tidziwe kuti iye ndi wokonzeka kutikhululukira akaona kuti talapa mochokera pansi pa mtima. Choncho tisamaope kuti m’tsogolo adzatiimbanso mlandu pa machimo omwewo. Zimenezi zikuonekera bwino mu mfundo inanso imene Baibulo limanena yokhudza chifundo chachikulu cha Yehova, yakuti: Akakhululuka, amaziiwala.
Yehova amafuna kuti tidziwe kuti ndi “wokonzeka kukhululuka”
“Machimo Awo Sindidzawakumbukiranso”
16, 17. Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamati Yehova amaiwala machimo athu, ndipo n’chifukwa chiyani mukuyankha choncho?
16 Ponena za anthu amene ali m’pangano latsopano, Yehova analonjeza kuti: “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.” (Yeremiya 31:34) Kodi izi zikutanthauza kuti Yehova akakhululuka sathanso kukumbukira machimowo? Ayi si choncho. Baibulo limatiuza za anthu amene anachita machimo omwe Yehova anawakhululukira, mwachitsanzo Davide. (2 Samueli 11:1-17; 12:13) N’zodziwikiratu kuti Yehova akudziwabe machimo amene anthuwo anachita. Machimo awo, kulapa kwawo ndiponso mmene Mulungu anawakhululukirira, zonsezi zinalembedwa m’Baibulo kuti zizitithandiza. (Aroma 15:4) Ndiye kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamati Yehova ‘sakumbukira’ machimo a anthu amene anawakhululukira?
17 Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “sindidzawakumbukiranso,” amatanthauza zambiri osati kungokumbukira zinthu zakale. Buku lina limati mawuwa amatanthauzanso “kuchitapo kanthu pa zimene zinachitika.” (Theological Wordbook of the Old Testament) Choncho, ‘kukumbukira’ machimo kukuphatikizapo kulanga wochimwayo. (Hoseya 9:9) Koma pamene Mulungu ananena kuti “machimo awo sindidzawakumbukiranso” akutitsimikizira kuti akakhululukira ochimwa amene alapa, ndiye kuti m’tsogolo sadzawapatsanso chilango chifukwa cha machimo awowo. (Ezekieli 18:21, 22) Choncho Yehova amaiwala m’njira yakuti samangokhalira kutikumbutsa machimowo n’cholinga chakuti azitiimba mlandu kapena kutilanga. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu wathu amakhululuka n’kuiwala.
Nanga Bwanji Zotsatira Zake?
18. N’chifukwa chiyani kukhululukidwa machimo sikutanthauza kuti wochimwa amene walapayo sakumana ndi zotsatira zoipa za machimo akewo?
18 Kodi Yehova akakhululukira wochimwa yemwe walapa, ndiye kuti munthuyo sakumana ndi zotsatira za tchimo lakelo? Ayi si choncho. Sitingachite tchimo n’kumayembekezera kuti sitikumana ndi vuto lililonse. Paulo analemba kuti: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” (Agalatiya 6:7) Tingakumane ndi mavuto ena chifukwa cha zimene tinachita. Zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amatibweretsera mavuto pambuyo poti watikhululukira. Mkhristu akayamba kukumana ndi mavuto, asamaganize kuti, ‘Mwina Yehova akundilanga chifukwa cha machimo amene ndinachita.’ (Yakobo 1:13) Tizikumbukira kuti Yehova samatiteteza ku mavuto onse obwera chifukwa cha machimo omwe tinachita. Kutha kwa banja, mimba yosafunika, matenda opatsirana pogonana, anthu kusiya kukukhulupirira kapena kukulemekeza, zonsezi zingakhale zotsatira zomvetsa chisoni ndiponso zosapeweka za tchimo lomwe munthu anachita. Kumbukirani kuti ngakhale kuti Yehova anakhululukira Davide machimo ake okhudzana ndi Bati-seba ndi Uriya, sanamuteteze ku zotsatira zoipa za machimowo.—2 Samueli 12:9-12.
19-21. (a) Kodi lamulo la pa Levitiko 6:1-7 linkathandiza bwanji wolakwiridwa ndiponso wolakwa? (b) Ngati machimo athu achititsa kuti anthu ena akumane ndi mavuto, kodi Yehova amasangalala tikachita zinthu ziti?
19 Machimo athu angakhale ndi zotsatira zinanso, makamaka ngati zimene tinachitazo zakhudzanso anthu ena. Mwachitsanzo taganizirani zimene zafotokozedwa m’buku la Levitiko, chaputala 6. M’chaputalachi, Chilamulo cha Mose chikufotokoza zimene zinkayenera kuchitika munthu akaba kapena kulanda katundu wa Mwisiraeli mnzake kapenanso kumuchitira zachinyengo kenako n’kukana kuti sanachite zimenezo, mwinanso mpaka kulumbira. Nkhaniyi inkakhala yoti palibe munthu wina amene angapereke umboni. Koma kenako mwina wolakwayo ankavutika ndi chikumbumtima n’kuvomera tchimo lake. Kuti Mulungu amukhululukire, ankafunika kuchita zinthu zinanso zitatu izi: Kubweza zimene anabazo, kupereka chindapusa kwa mwini katunduyo chokwana magawo 20 a magawo 100 alionse a zomwe anabazo ndiponso kupereka nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yakupalamula. Ndiyeno Chilamulo chinkati: “Wansembe aziphimba machimo a munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa.”—Levitiko 6:1-7.
20 Lamulo limeneli linkasonyeza kuti Mulungu ndi wachifundo. Linkathandiza woberedwa chifukwa katundu wake ankabwezedwa komanso ankasangalala kuti wakubayo wavomereza tchimo lake. Lamuloli linkathandizanso munthu wochimwayo, amene chikumbumtima chake chinkamuchititsa kuti avomereze kulakwa kwake n’kukonza zolakwikazo. Ngati akanakana kuchita zimenezi, Mulungu sakanamukhululukira.
21 Ngakhale kuti sititsatira Chilamulo cha Mose, Chilamulochi chimatithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani yokhululuka. (Akolose 2:13, 14) Ngati machimo athu achititsa kuti anthu ena akumane ndi mavuto, Mulungu amasangalala tikachita zomwe tingathe kuti tikonze zolakwazo. (Mateyu 5:23, 24) Zimenezi zingaphatikizepo kuvomera kuti tinachita tchimo, kuvomereza kuti tinalakwa komanso kupepesa munthu amene tinamulakwirayo. Kenako tingapemphe Mulungu kuti atikhululukire pogwiritsa ntchito nsembe ya Yesu ndipo tingayambe kumva kuti watikhululukira.—Aheberi 10:21, 22.
22. Kodi n’chiyani chingachitike ngakhale kuti Yehova watikhululukira?
22 Mofanana ndi kholo lililonse lachikondi, Yehova akatikhululukira akhoza kutipatsanso chilango. (Miyambo 3:11, 12) Ngakhale kuti Mkhristu analapa, akhoza kuluza mwayi womwe anali nawo wokhala mkulu, mtumiki wothandiza kapena kusiya utumiki wa nthawi zonse. Zingakhale zopweteka kwambiri kuti kwa kanthawi sazichitanso utumiki womwe ankaukonda. Komabe chilango chimenechi sichitanthauza kuti Yehova sanamukhululukire. Tizikumbukira kuti Yehova akatipatsa chilango ndi umboni wakuti amatikonda. Kuvomereza chilango chomwe tapatsidwa n’kusintha kumatithandiza kwambiri.—Aheberi 12:5-11.
23. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti Yehova sangatichitire chifundo, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira Yehova pa nkhani yokhululukira ena?
23 N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu wathu ndi “wokonzeka kukhululuka.” Kaya tachita zolakwa zotani, tisamaganize kuti Yehova sangatichitire chifundo. Tikalapa ndi mtima wonse, kuchita zonse zofunika kuti tikonze zolakwikazo ndiponso kupemphera mochokera pansi pa mtima kuti Yehova atikhululukire pogwiritsa ntchito magazi a Yesu, tisamakayikire kuti watikhululukira. (1 Yohane 1:9) Tiyeni tizitsanzira Yehova pa nkhani yokhululukira anzathu. Ngati Yehova amene sachimwa amatikhululukira mwachikondi, kodi si zoyenera kuti anthu ochimwafe tiziyesetsa mmene tingathere kukhululukira ena?
a Katswiri wina wa Baibulo anati kufiira kotchulidwa palembali sikunkasuluka ngakhale pang’ono. Chinthu chamtunduwu sichinkasintha maonekedwe ngakhale atachiika pamame, pamvula, kuchichapa kapena kuchigwiritsa ntchito kwa nthawi yaitali.