Kulitsani Mkhalidwe wa Kulolera
“Lolani kuti kulolera kwanu kudziŵike kwa anthu onse. Ambuye ali pafupi.”—AFILIPI 4:5, NW.
1. Kodi nchifukwa ninji kuli kovuta kukhala wololera m’dziko lamakono?
“MUNTHU wololera”—Mtolankhani Wachingelezi Bwana Alan Patrick Herbert anamutcha kukhala munthu wa m’nthano chabe. Ndithudi, nthaŵi zina kungaoneke kuti kulibenso anthu ololera omwe adakalipo m’dziko lino logaŵanika ndi mikangano. Baibulo linaneneratu kuti mu “masiku otsiriza” ano oŵaŵitsa, anthu akakhala “aukali,” “aliuma olimbirira,” ndi “osayanjanitsika”—m’mawu ena, osalolera mpang’ono pomwe. (2 Timoteo 3:1-5) Komabe, Akristu oona amalemekeza kwambiri mkhalidwe wa kulolera, podziŵa kuti kuli chizindikiro cha nzeru yaumulungu. (Yakobo 3:17) Sitimalingalira kuti kuli kosatheka kukhala wololera m’dzikoli losalolerena. Mmalomwake, tikulandira ndi manja aŵiri chitokosocho cha mu uphungu wouziridwa wa Paulo wopezeka pa Afilipi 4:5 wakuti: “Lolani kuti kulolera kwanu kudziŵike kwa anthu onse.”
2. Kodi mawu a mtumwi Paulo pa Afilipi 4:5 amatithandiza motani kudziŵa kaya ngati tili ololera?
2 Onani mmene mawu a Paulo akutithandizira kudziyesa kuona ngati tili ololera. Siili kwenikweni nkhani ya mmene timadzionera ife eni; ndi nkhani ya mmene ena amationera, mmene tikudziŵikira. Matembenuzidwe a Phillips amamasulira vesili motere: “Khalani ndi mbiri ya kukhala wololera.” Aliyense wa ife angadzifunse kuti, ‘Kodi ndimadziŵika motani? Kodi ndili ndi mbiri ya kukhala wololera, wogonja, wodekha? Kapena kodi ndimadziŵika kukhala woumirira, waukali, kapena waliuma?’
3. (a) Kodi liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kuti “kulolera” limatanthauzanji, ndipo kodi nchifukwa ninji mkhalidwe umenewu uli wokhumbirika? (b) Kodi ndimotani mmene Mkristu angaphunzirire kukhala wololera moposerapo?
3 Mbiri ya mkhalidwe wathu m’nkhani imeneyi idzangosonyeza mlingo umene timatsanzirira Yesu Kristu. (1 Akorinto 11:1) Pamene anali padziko lapansi pano, Yesu anasonyeza bwino lomwe chitsanzo chopambana cha Atate wake cha kulolera. (Yohane 14:9) Kwenikweni, pamene Paulo analemba za “kufatsa ndi kukoma mtima kwa Kristu,” liwu Lachigiriki limene anamasulira kuti kukoma mtima (e·pi·ei·kiʹas) limatanthauzanso “kulolera” kapena, m’lingaliro lenileni, “kugonja.” (2 Akorinto 10:1, NW) The Expositor’s Bible Commentary limatcha limeneli kukhala “limodzi la mawu aakulu olongosola mkhalidwe wa munthu mu NT [Chipangano Chatsopano].” Limalongosola mkhalidwe wokhumbirika kwambiri kwakuti katswiri wina anamasulira liwulo kukhala “kulolera kokoma.” Motero, tiyeni tikambitsirane njira zitatu zimene Yesu, mofanana ndi Atate wake, Yehova, anasonyezeramo mkhalidwe wa kulolera. Tikatero tingaphunzire mmene tingakhalire ololera mokulirapo ife eni.—1 Petro 2:21.
“Wofunitsitsa Kukhululukira”
4. Kodi ndimotani mmene Yesu anadzisonyezera kukhala “wofunitsitsa kukhululukira”?
4 Mofanana ndi Atate wake, Yesu anasonyeza mkhalidwe wa kulolera mwa kukhala “wofunitsitsa kukhululukira” mobwerezabwereza. (Salmo 86:5) Talingalirani nthaŵi pamene Petro, mnzake wapamtima, anakana Yesu katatu pausiku umene Yesu anamangidwa ndi kuzengedwa mlandu. Yesu iye mwini anali atanena poyamba kuti: “Yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.” (Mateyu 10:33) Kodi Yesu anagwiritsira ntchito lamulo limeneli mouma khosi ndi mopanda chifundo kwa Petro? Iyayi; pambuyo pa kuuka Kwake, Yesu anakachezera Petro mwaumwini, mosakayikira anakamtonthoza ndi kukalimbikitsa mtumwi wolapa wosweka mtima ameneyu. (Luka 24:34; 1 Akorinto 15:5) Pasanapite nthaŵi yaitali, Yesu analola Petro kukhala ndi thayo lalikulu. (Machitidwe 2:1-41) Panopa tikuona kulolera kokoma kukusonyezedwa bwino koposa! Kodi sikuli kotonthoza mtima kuganiza kuti Yehova waika Yesu kukhala woweruza mtundu wonse wa anthu?—Yesaya 11:1-4; Yohane 5:22.
5. (a) Kodi ndi mbiri yotani imene akulu ayenera kukhala nayo pakati pa nkhosa? (b) Kodi ndi nkhani ziti zimene akulu angapendenso asanasamalire nkhani zachiweruzo, ndipo chifukwa ninji?
5 Pamene akulu achita monga oweruza mumpingo, amayesayesa kutsatira chitsanzo cha Yesu cha kulolera. Samafuna kuti nkhosa ziwawope monga opereka chilango. Mmalo mwake, amafuna kutsanzira Yesu kotero kuti nkhosazo zimve kukhala zosungika kwa iwo monga abusa achikondi. M’nkhani zachiweruzo, amapanga kuyesayesa kulikonse kwa kukhala ololera, ofunitsitsa kukhululukira. Asanasamalire nkhani yoteroyo, akulu ena akuona kukhala kothandiza kupendanso nkhani za mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1992 zakuti “Yehova, ‘Woweruza wa Dziko Lonse’ Wopanda Tsankhu” ndi “Akulu, Weruzani Mwachilungamo.” Motero iwo amakumbukira chidule cha njira yoweruzira ya Yehova chakuti: “Kusagwedezeka pamene kuli kofunikira, chifundo pamene kuli kotheka.” Sikulakwa kukhotherera pa chifundo poweruza mlandu pamene pali maziko abwino ochitira zimenezo. (Mateyu 12:7) Kuli kulakwa kwakukulu kukhala waukali ndi wopanda chifundo. (Ezekieli 34:4) Motero akulu amapeŵa kulakwa mwa kufunafuna mwakhama njira yachikondi koposa ndi yachifundo yotheka mkati mwa malire a chilungamo.—Yerekezerani ndi Mateyu 23:23; Yakobo 2:13.
Kusinthika Poyang’anizana ndi Mikhalidwe Yomasintha
6. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kulolera pochita ndi mkazi Wachikunja amene mwana wake wamkazi anagwidwa ndi chiŵanda?
6 Mofanana ndi Yehova, Yesu anasonyeza kukhala wofulumira kusintha kachitidwe kapena kusinthira ku mikhalidwe yatsopano pamene inabuka. Panthaŵi ina mkazi Wachikunja anampempha kuchiritsa mwana wake wamkazi wogwidwa ndi chiŵanda moipitsitsa. M’njira zitatu zosiyanasiyana, Yesu poyamba anasonyeza kuti sakamthandiza—yoyamba, mwa kukana kumyankha; yachiŵiri, mwa kutchula mwachindunji kuti anatumizidwa, osati kwa Akunja, koma kwa Ayuda; ndipo yachitatu, mwa kupereka fanizo limene mokoma mtima linamveketsa mfundo imodzimodziyo. Komabe, mkaziyo anaumirira m’zonsezi, akumapereka umboni wa chikhulupiriro chapadera. Poona mkhalidwe wapadera umenewu, Yesu anakhoza kuona kuti iyi siinali nthaŵi ya kugwiritsira ntchito lamulo logwira ntchito kwa onse; inali nthaŵi ya kusintha molingana ndi malamulo apamwamba.a Chifukwa chake, Yesu anachita chimene anali atasonyeza katatu konse kuti sakachita. Anachiritsa mwana wamkazi wa mayiyo!—Mateyu 15:21-28.
7. Kodi ndi njira zotani zimene makolo angasonyezeremo kulolera, ndipo chifukwa ninji?
7 Kodi nafenso timadziŵika ndi kufunitsitsa kwathu kusintha pamene kuli koyenera? Makolo kaŵirikaŵiri amafunikira kusonyeza kulolera koteroko. Popeza kuti mwana aliyense ali wosiyana, njira zimene zimagwira ntchito kwa wina zingakhale zosayenera kwa winayo. Ndiponso, pamene ana akukula, zosoŵa zawo zimasintha. Kodi nthaŵi yofika panyumba iyenera kusinthidwa? Kodi phunziro la banja lingakhale lopindulitsa litakhala mu mpangidwe wosangalatsa koposerapo? Pamene kholo lichita mopambanitsa pa kulakwa kwakung’ono, kodi lili lofunitsitsa kudzichepetsa ndi kuwongolera nkhaniyo? Makolo amene amagonja mwa njira zimenezo amapeŵa kukwiitsa ana awo mosafunikira ndi kuwapambutsa kwa Yehova.—Aefeso 6:4.
8. Kodi ndimotani mmene akulu a mpingo angatsogolere m’kusinthira ku zosoŵa za m’gawo?
8 Akulu nawonso, afunikira kusintha pamene mikhalidwe yatsopano ibuka, pamene kuli kwakuti safunikira konse kulolera molakwa malamulo achindunji a Mulungu. Poyang’anira ntchito yolalikira, kodi mumakhala atcheru pa masinthidwe a m’gawo? Pamene njira za moyo m’chitaganya zisintha, mwinamwake umboni wa madzulo, umboni wa m’khwalala, kapena umboni wapafoni uyenera kulimbikitsidwa. Kusinthira ku njira zimenezi kumatithandiza kuchita ntchito yathu yolalikira mogwira mtima kwambiri. (Mateyu 28:19, 20; 1 Akorinto 9:26) Paulonso anakhaladi akumasinthira kwa anthu onse mu utumiki wake. Kodi nafenso timachita chimodzimodzi, mwachitsanzo, mwa kuphunzira zokwanira ponena za zipembedzo za kumalo athuwo ndi miyambo kuti tikhale okhoza kuthandiza anthu?—1 Akorinto 9:19-23.
9. Kodi nchifukwa ninji mkulu sayenera kuumirira nganganga pa kusamalira nkhani nthaŵi zonse mwa njira imene anachitira kale?
9 Pamene masiku otsirizawa akupitiriza kukhala ovuta, abusa angafunikirenso kusintha molingana ndi kucholoŵana komvetsa chisoni ndi kosautsa kwa mavuto amene nkhosa zikuyang’anizana nawo tsopano. (2 Timoteo 3:1) Akulu, ino sinthaŵi ya kukhala oumirira nganganga! Ndithudi mkulu safunikira kuumirira nganganga pa njira za kusamalira mavuto zimene anagwiritsira ntchito kale ngati kuti tsopano zakhala zosagwira ntchito kapena ngati “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wakuona kukhala koyenera kufalitsa mfundo zatsopano pa nkhanizo. (Mateyu 24:45; yerekezerani ndi Mlaliki 7:10; 1 Akorinto 7:31.) Mkulu wina wokhulupirika anayesa moona mtima kuthandiza mlongo wopsinjika maganizo yemwe anafunikira kwambiri munthu womvetsera. Komabe, iye anaona kupsinjika maganizo kwa mlongoyo ndi lingaliro losasamala kwambiri motero anangopereka chithandizo chachisawawa. Ndiyeno Watch Tower Society inafalitsa mfundo zozikidwa pa Baibulo zimene zinakhudza vuto lenilenilo la mlongoyo. Mkuluyo anatsimikizira kulankhulanso naye, koma tsopano akumagwiritsira ntchito mfundo zatsopano ndi kusonyeza chifundo pa mkhalidwe wakewo. (Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 5:14, 15.) Ha, ndi chitsanzo chabwino chotani nanga cha mkhalidwe wa kulolera!
10. (a) Kodi ndimotani mmene akulu ayenera kusonyezera mkhalidwe wa kugonja kulinga kwa wina ndi mnzake ndi kulinga kwa bungwe la akulu lonse? (b) Kodi ndimotani mmene bungwe la akulu liyenera kuonera awo amene amadzisonyeza kukhala osalolera?
10 Akulu nawonso amafunikira kusonyeza mkhalidwe wa kugonja kwa wina ndi mnzake. Pamene bungwe la akulu likumana, nkofunika chotani nanga kuti pasakhale mkulu mmodzi yemwe akulamulira makambitsiranowo! (Luka 9:48) Makamaka amene akutsogoza ayenera kukhala wodziletsa pambali imeneyi. Ndipo pamene mkulu mmodzi kapena aŵiri sakugwirizana ndi chosankha cha bungwe lonse la akululo, sadzafunikira kuumirira panjira yawoyo. Mmalomwake, malinga ngati palibe lamulo la mkhalidwe la Malemba limene likuswedwa, iwo adzafunikira kugonja, akumakumbukira kuti kulolera kuli kofunikira kwa akulu. (1 Timoteo 3:2, 3) Kumbali ina, bungwe la akulu liyenera kukumbukira kuti Paulo anadzudzula mpingo wa Akorinto kaamba ka ‘kuyanja anthu osalolera’ omwe anadzisonyeza okha kukhala ‘atumwi oposa.’ (2 Akorinto 11:5, 19, 20, NW) Motero iwo ayenera kukhala ofunitsitsa kupatsa uphungu mkulu mnzawo amene achita mwa njira yaliuma ndi yosalolera, koma iwo eniwo ayenera kukhala odekha ndi okoma mtima pochita zimenezo.—Agalatiya 6:1.
Kulolera Pochita Ulamuliro
11. Kodi ndi kusiyana kotani kumene kunali pakati pa kuchita ulamuliro kwa atsogoleri achipembedzo Achiyuda a m’tsiku la Yesu ndi mmene Yesu anachitira?
11 Pamene Yesu anali padziko lapansi, kulolera kwake kunaonekeradi mwa njira imene anachitira ulamuliro wake wopatsidwa ndi Mulungu. Anali wosiyana chotani nanga ndi atsogoleri achipembedzo a m’tsiku lake! Talingalirani chitsanzo. Lamulo la Mulungu linali litalamula kuti palibe ntchito imene inayenera kuchitidwa pa Sabata, ngakhale kutola nkhuni. (Eksodo 20:10; Numeri 15:32-36) Atsogoleri achipembedzo anafuna kulamulira mmene kwenikweni anthu anagwiritsirira ntchito lamulo limenelo. Chotero modzichitira okha analamula zimene kwenikweni munthu anafunikira kunyamula pa Sabata. Iwo analamula kuti: Osati chilichonse cholemera koposa nkhuyu ziŵiri zouma. Anapereka ngakhale chiletso cha kusavala nsapato zokhomedwa ndi misomali, akumanena kuti kunyamula kulemera kowonjezerako kwa misomali kukatanthauza kugwira ntchito! Kukunenedwa kuti, arabi anawonjezera malamulo 39 onse pamodzi, pa lamulo la Mulungu la Sabata napanganso timalamulo towonjezereka tambirimbiri. Komabe, Yesu sanafune kulamulira anthu mwakuwachititsa manyazi mwa kupereka malamulo oletsa ambirimbiri kapena kuika miyezo yokhwima yosafikirika.—Mateyu 23:2-4; Yohane 7:47-49.
12. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Yesu sanagwedere pochita ndi miyezo yolungama ya Yehova?
12 Pamenepo, kodi tifunikira kulingalira kuti Yesu sanachirikize mwamphamvu miyezo yolungama ya Mulungu? Iye anaichirikizadi! Anazindikira kuti malamulo amakhala ogwira ntchito kwambiri pamene anthu avomereza mikhalidwe yokhala kumbuyo kwa malamulowo. Pamene kuli kwakuti Afarisiwo anali otanganitsidwa ndi kufuna kulamulira anthu ndi malamulo ambirimbiri, Yesu anayesayesa kufikira mitima ya anthu. Mwachitsanzo, iye anadziŵa bwino lomwe kuti sipafunikira kugonja pa malamulo aumulungu onga lakuti “thaŵani dama.” (1 Akorinto 6:18) Chotero Yesu anachenjeza anthu ponena za malingaliro amene akatsogolera ku chisembwere. (Mateyu 5:28) Kuphunzitsa koteroko kunaloŵetsamo nzeru yakuya ndi kulingalira mmalo mwa kungopereka malamulo okhwima osalingalira mkhalidwe.
13. (a) Kodi nchifukwa ninji akulu ayenera kupeŵa kupanga malamulo ndi miyezo yosasinthika? (b) Kodi ndi m’mbali zina ziti m’zimene kuli kofunika kulemekeza chikumbumtima cha munthu?
13 Abale a thayo lerolino alinso ofunitsitsa mofananamo kufikira mitima. Chotero, iwo amapeŵa kupereka malamulo odzifunira ndi osasinthika kapena kupanga malingaliro awo aumwini ndi maganizo kukhala lamulo. (Yerekezerani ndi Danieli 6:7-16.) Nthaŵi ndi nthaŵi, zikumbutso zokoma mtima pankhani zonga mavalidwe ndi mapesedwe zingakhale zoyenera ndi zapanthaŵi yake, koma mkulu angawononge mbiri yake ya kukhala munthu wololera ngati nthaŵi zonse angoimba nkhani zimenezo kapena ngati ayesa kuumiriza zimene kwenikweni zimaonekera kukhala zokonda zake. Ndithudi, onse mumpingo ayenera kupeŵa kulamulira ena.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 1:24; Afilipi 2:12.
14. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuti anali wololera pa zimene anayembekezera kwa ena?
14 Akulu angafune kudzipenda okha pankhani inanso: ‘Kodi ndili wololera pazimene ndimayembekezera kwa ena?’ Yesu analidi wotero. Iye nthaŵi zonse anasonyeza otsatira ake kuti sanayembekezere zoposa zoyesayesa zawo za mtima wonse ndi kuti analemekeza kwambiri zimenezi. Anatamanda mkazi wamasiye wosaukayo kaamba ka kupereka timakobiri tiŵiri ta mtengo wochepa kwambiri. (Marko 12:42, 43) Anadzudzula ophunzira ake pamene anasuliza chopereka cha mtengo wapamwamba cha Mariya, akumati: “Mlekeni, . . . Iye wachita chimene wakhoza.” (Marko 14:6, 8) Iye anali wololera ngakhale pamene otsatira ake anamgwiritsa mwala. Mwachitsanzo, ngakhale kuti iye analimbikitsa atumwi ake apamtima atatu kukhalabe maso ndi kuyang’anira limodzi naye pausiku wa kumangidwa kwake, iwo anamgwiritsa mwala mwa kugona tulo mobwerezabwereza. Komabe, iye mwachifundo ananena kuti: “Mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.”—Marko 14:34-38.
15, 16. (a) Kodi nchifukwa ninji akulu ayenera kukhala osamala kuti asapanikize kapena kutsendereza nkhosa? (b) Kodi ndimotani mmene mlongo wina wokhulupirika anasinthira pa zimene anayembekezera kwa ena?
15 Zoona, Yesu analimbikitsa otsatira ake ‘kuyesetsa’ mwamphamvu. (Luka 13:24) Koma sanawaumirize konse kuti achite zimenezo! Iye anawasonkhezera, anapereka chitsanzo, anawatsogolera, ndipo anayesayesa kufikira mitima yawo. Anadalira mphamvu ya mzimu wa Yehova kuchita zotsalazo. Mofananamo, akulu lerolino ayenera kulimbikitsa nkhosa kutumikira Yehova ndi mtima wonse koma ayenera kupeŵa kuwachititsa kudzimva aliwongo kapena achisoni, akumapereka lingaliro lakuti zimene akuchita panthaŵi ino mu utumiki wa Yehova zili zosakwanira mwanjira inayake kapena zosalandirika. Njira ya chisonkhezero choumiriza, yakuti “chita zowonjezereka, chita zowonjezereka, chita zowonjezereka!” ingalefule amene akuchita zonse zimene angathe. Kukakhala kwachisoni chotani nanga ngati mkulu akhala ndi mbiri ya kukhala “wovuta kukondweretsa”—mkhalidwe wosiyana kutalitali ndi kukhala wololera!—1 Petro 2:18.
16 Tonsefe tiyenera kukhala ololera m’zimene timayembekezera kwa ena! Mlongo wina, pamene iye ndi mwamuna wake analeka ntchito yaumishonale kuti akasamalire amayi ake odwala, analemba kuti: “Nthaŵi zino nzovuta kwambiri kwa ife ofalitsa kuno ku mipingo. Pokhala tinali m’ntchito ya m’dera ndi m’chigawo, ochinjirizidwa ku mavuto ambiri otero, tachititsidwa kudziŵa zimenezi mwanjira yomvetsa chisoni ndi yopweteka. Mwachitsanzo, ndinkaganiza kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji mlongo uja sagaŵira buku loyenera la mwezi uno? Kodi samaŵerenga Utumiki Wathu Waufumu?’ Tsopano ndikudziŵa chifukwa chake. Kwa ena zokha zimene atha kuchita ndizo kungopita [mu utumiki].” Kuli kwabwinopo chotani nanga kuthokoza abale athu pa zimene amachita mmalo mwa kuwaweruza pazimene samachita!
17. Kodi ndimotani mmene Yesu anaperekera chitsanzo kwa ife cha kukhala ololera?
17 Talingalirani chitsanzo chabwino cha mmene Yesu anachitira ulamuliro wake mwa njira yololera. Mofanana ndi Atate wake, Yesu samatetezera ulamuliro wake mwansanje. Nayenso ali wogaŵira mathayo wamkulu, akumasankha gulu lake la kapolo wokhulupirika kuti lisamalire “zinthu zake zonse” padziko lapansi pano. (Mateyu 24:45-47) Ndipo iye samawopa kumvetsera malingaliro a ena. Kaŵirikaŵiri anafunsa omvetsera ake kuti; “Uganiza bwanji?” (Matthew 17:25; 18:12; 21:28; 22:42) Ziyenera kukhala moteronso pakati pa otsatira a Kristu onse lerolino. Palibe mlingo uliwonse wa ulamuliro umene uyenera kuwapangitsa kukhala osafuna kumvetsera. Makolo inu, mvetserani! Amuna inu, mvetserani! Akulu inu, mvetserani!
18. (a) Kodi tingadziŵe motani kaya ngati tili ndi mbiri ya kukhala wololera? (b) Kodi tonsefe tingachite bwino kutsimikizira za chiyani?
18 Mwachionekere, aliyense wa ife amafuna “kukhala ndi mbiri ya kukhala wololera.” (Afilipi 4:5, Phillips) Koma kodi tingadziŵe motani ngati tili ndi mbiri imeneyo? Chabwino, pamene Yesu anafuna kudziŵa zimene anthu ankanena za iye, anafunsa anzake odalirika. (Mateyu 16:13) Bwanji osatsatira chitsanzo chake? Mukhoza kufunsa munthu amene mungamdalire kukhala woona mtima kuti akuuzeni ngati muli ndi mbiri ya kukhala munthu wololera ndi wogonja. Ndithudi pali zambiri zimene tonsefe tingachite kuti titsanzire kwambiri chitsanzo changwiro cha Yesu cha kukhala wololera! Makamaka ngati tili ndi ulamuliro winawake pa anthu ena, tiyeni nthaŵi zonse titsatire chitsanzo cha Yehova ndi Yesu, nthaŵi zonse tikumauchita mwa njira yololera, tili ofunitsitsa nthaŵi zonse kukhululukira, kusintha, kapena kugonja pamene kuli koyenera. Ndithudi, aliyense wa ife ayeseyesetu “kukhala wololera”!—Tito 3:2, NW.
[Mawu a M’munsi]
a Buku lakuti New Testament Words limanena kuti: “Munthu amene ali wa epieikēs [wololera] amadziŵa kuti pali nthaŵi zimene chinthu chikhoza kukhala cholungama kwenikweni mwalamulo komabe nkukhala cholakwa kwenikweni mwamakhalidwe. Munthu amene ali wa epieikēs amadziŵa pamene pafunikira kufeŵetsa lamulo mokakamizika ndi mphamvu yapamwamba ndi yaikulu kuposa lamulolo.”
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kufuna kukhala ololera?
◻ Kodi ndimotani mmene akulu angatsanzirire Yesu m’kukhala ofunitsitsa kukhululukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji tifunikira kuyesetsa kukhala osinthika monga momwe Yesu analiri?
◻ Kodi tingasonyeze motani mkhalidwe wa kulolera mwa njira imene timachitira ulamuliro wathu?
◻ Kodi ndimotani mmene tingadzipendere tokha kuona ngati tilidi ololera?
[Chithunzi patsamba 15]
Yesu mofunitsitsa anakhululukira Petro wolapayo
[Chithunzi patsamba 16]
Pamene mkazi anasonyeza chikhulupiriro chapadera, Yesu anaona kuti siinali nthaŵi ya kugwiritsira ntchito lamulo logwira ntchito kwa onse
[Chithunzi patsamba 18]
Makolo inu mvetserani!
[Chithunzi patsamba 18]
Amuna inu mvetserani!
[Chithunzi patsamba 18]
Akulu inu mvetserani!