-
Yehova, Wochita Zinthu ZodabwitsaNsanja ya Olonda—1992 | December 15
-
-
8. Kodi ndikuzoloŵerana kotani kumene tingakhale nako ndi Yehova, ndipo kodi iye wasonyeza motani ubwino wake?
8 Davide akupereka pemphero lina lochonderera kuti: “Inu, O Yehova, ndinu wabwino ndi wokhululuka msanga; ndi wachifundo chochuluka kwa onse oitanira pa inu. Tcherani khutu, O Yehova, kupemphero langa; ndipo mvetserani mawu a mapembedzero anga. M’tsiku la nsautso yanga ndidzaitana pa inu, pakuti mudzandiyankha.” (Salmo 86:5-7, NW) “O Yehova”—mobwerezabwereza tikuchita chidwi chotani nanga ndi mawu osonyeza kuzoloŵerana amenewa! Ndiko kuzoloŵerana kumene kungakulitsidwe mosalekeza kupyolera mwa pemphero. Davide anapemphera panyengo ina kuti: “Musakumbukire zolakwa zaubwana wanga kapena zopikisana nanu: mundikumbukire monga mwachifundo chanu, chifukwa chaubwino wanu, Yehova.” (Salmo 25:7) Yehova ndiye chitsanzo chenicheni chaubwino—m’kupereka dipo la Yesu, m’kusonyeza chifundo kwa ochimwa olapa, ndi m’kusonyeza kukoma mtima kwachikondi kwa Mboni zake zokhulupirika ndi zoyamikira.—Salmo 100:3-5; Malaki 3:10.
9. Kodi nchitsimikiziro chotani chimene ochimwa olapa ayenera kulingalira mwamphamvu?
9 Kodi tiyenera kudera nkhaŵa zophophonya zapitazo? Ngati ife tsopano tiri kulambulira mapazi athu njira zowongoka, timalimbikitsidwa pamene tikumbukira chitsimikiziro cha mtumwi Petro kwa olapawo chakuti “nyengo za kutsitsimutsa” zidzadza kuchokera kwa Yehova. (Machitidwe 3:19) Tiyeni tiyandikire kwa Yehova m’pemphero kupyolera mwa Wopereka Dipo wathu, Yesu, amene mwachikondi anati: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.” Pamene Mboni zokhulupirika zipemphera kwa Yehova lerolino m’dzina lokondedwa la Yesu, izo zimapezadi mpumulo.—Mateyu 11:28, 29; Yohane 15:16.
-
-
Yehova, Wochita Zinthu ZodabwitsaNsanja ya Olonda—1992 | December 15
-
-
13. Kodi ndimotani mmene makolo ndi ana awo angapindulire ndi ubwino wa Yehova?
13 Mosakaikira, Davide anakhomereza mu mtima wa mwana wake Solomo kufunika kwa kudalira pa ubwino wa Yehova. Chotero, Solomo anakhoza kulangiza mwana wake kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; Umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako. Usadziyese wekha wanzeru; Wopa Yehova, nupatuke pa zoipa.” (Miyambo 3:5-7) Mofananamo makolo lerolino ayenera kuphunzitsa ana awo mmene angapempherere modalira Yehova ndi mmene angagonjetsere ziukiro zokakala za dzikoli—monga chitsenderezo cha a msinkhu wofanana ku sukulu ndi ziyeso zakuchita chisembwere. Kukhalira moyo chowonadi limodzi ndi ana anu tsiku lirilonse kungathe kukhomereza pa mitima yawo yachichepereyo chikondi chowona cha pa Yehova ndi kudalira pa iye mwapemphero.—Deuteronomo 6:4-9; 11:18, 19.
-