“Mitima Yanu Isavutike”
“Mitima yanu isavutike. Sonyezani chikhulupiriro mwa Mulungu, sonyezani chikhulupiriro mwa inenso.”—YOHANE 14:1, NW.
1. Nchifukwa ninji mawu a Yesu pa Yohane 14:1 anali a pa nthaŵi yake?
PANALI pa Nisan 14 m’chaka cha 33 C.E. Gulu lochepa la amuna linasonkhana m’chipinda chapamwamba m’Yerusalemu pambuyo pa kuloŵa kwa dzuŵa. Mtsogoleri wawo anali kuwapatsa iwo uphungu ndi chilimbikitso chowatsanzika. Mbali ina iye ananena kuti: “Mitima yanu isavutike.” (Yohane 14:1, NW) Mawu ake anali apanthaŵi yake, popeza kuti zochitika zosakaza zinayenera kuchitika mwamsanga. Usiku umenewo iye anagwidwa, kuyesedwa, ndi kulamulidwa kuphedwa.
2. Nchifukwa ninji tsiku limenelo linali lowopsya, ndipo nchiyani chimene chinawathandiza ophunzira?
2 Muli ndi chifukwa chabwino cha kuwonera tsiku limenelo kukhala lowopsya kwambiri m’mbiri, kuyambukira mtsogolo monse mwa mtundu wa munthu. Imfa ya nsembe ya Mtsogoleriyo, Yesu, inakwaniritsa maulosi ambiri akale ndipo inapereka maziko kaamba ka moyo wosatha kwa awo okhulupirira mwa iye. (Yesaya 53:5-7; Yohane 3:16) Koma atumwiwo, ododometsedwa ndi kuzizwitsidwa ndi zochitika zoŵaŵa za usiku umenewo, anasokonezeka ndi kuwopa kwa kanthaŵi. Petro anafikira ngakhale pa kumukana Yesu. (Mateyu 26:69-75) Komabe, pambuyo pa kulandira kwa atumwiwo mthandizi wolonjezedwa, mzimu woyera, iwo anakhala olimba mtima ndi osavutitsidwa. (Yohane 14:16, 17) Chotero, pamene Petro ndi Yohane anayang’anizana ndi chitsutso chovuta ndipo anaikidwa m’ndende, iwo anapemphera kwa Mulungu kaamba ka thandizo m’kulankhula mawu ake “ndi kulimbika mtima konse.” Pemphero lawo linayankhidwa.—Machitidwe 4:1-3, 29-31.
3. Nchifukwa ninji anthu ambiri ali ovutitsidwa moipa lerolino?
3 Lerolino, tikukhala m’dziko limene liri lovutitsidwa kotheratu. Mapeto a dongosolo iri lakale la kachitidwe ka zinthu akuyandikira mofulumira. (2 Timoteo 3:1-5) Mamiliyoni akuyambukiridwa mwaumwini kapena kusokonezedwa mozama ndi kusweka kowopsya kwa moyo wa banja ndi miyezo ya makhalidwe abwino, chiwonjezeko chochititsa mantha cha matenda achilendo, kusakhazikika kwa ndale zadziko, kusowa ntchito, kupereŵera kwa zakudya, uchigawenga, ndi chiwopsyezo cha nkhondo ya nyukiliya. Mitima yambiri ikuvutitsidwa ndi kukulakula kwa mantha a mtsogolo. Monga mmene Yesu ananeneratu, pali “chisauko cha mitundu . . . anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi.”—Luka 21:25, 26.
4. Ndi nsonga zotani zimene zingapangitse Akristu kupsyinjika?
4 Ngakhale Akristu angayambukiridwe moipa ndi zinthu zotsendereza zoterozo. Iwo angayang’anizanenso ndi kupsyinjika chifukwa cha kunyada kwa chipembedzo kapena chitsutso kuchokera kwa achibale, anansi, ogwira nawo ntchito, ophunzira nawo, ndi maulamuliro a boma. (Mateyu 24:9) Chotero ndimotani mmene tingakhalire abata, osavutitsidwa, m’nthaŵi zovuta zimenezi? Ndimotani mmene tingasungire mtendere wa maganizo pamene zinthu zavuta? Ndimotani mmene tingayang’anizirane ndi mtsogolo ndi chidaliro? Nchiyani chimene chidzatithandiza ife kulaka kudera nkhaŵa kokulira komwe kukukhala kofala? Tiri m’nyengo imene Yesu anapereka uphungu pa Yohane 14:1, chotero lolani kuti tiyang’ane pa uwo mosamalitsa.
Kodi Tingagonjetse Motani Kudera Nkhaŵa?
5. Ndi machenjezo olimbikitsa otani amene Malemba amatipatsa ife?
5 Pokhala atapereka chilimbikitso chachikondi ‘kusalola mitima yawo kuvutika,’ Yesu anauza atumwi ake kuti: “Sonyezani chikhulupiriro mwa Mulungu, sonyezani chikhulupiriro mwa inenso.” (Yohane 14:1, NW) Malemba ouziridwa amatipatsa ife machenjezo ambiri ofananawo: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo iye adzakugwiriziza.” “Pereka njira yako kwa Yehova, khulupiriranso iye, adzachichita.” (Masalmo 55:22; 37:5) Paulo anapatsa Afilipi chenjezo lofunika iri: “Musadere nkhaŵa konse, komatu m’zonse ndi pemphero ndi pembedzero pamodzi ndi chiyamiko zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afilipi 4:6, 7.
6, 7. (a) Ndi iti imene iri njira imodzi ya kuchepetserako kupsyinjika? (b) Ndimotani mmene tingakulitsire chomangira chathithithi ndi Yehova?
6 Kudera nkhaŵa kapena kuchulukidwa maganizo kopangitsidwa ndi mavuto ndi mathayo olemera nthaŵi zina kungayambukire umoyo wathu limodzinso ndi uzimu wathu. Komabe, katswiri wa za mankhwala, m’buku lakuti Don’t Panic, akuchitira ndemanga kuti: “Ngati anthu ali okhoza kulankhula mavuto awo ndi winawake amene amamlemekeza . . . , ukulu wa kupsyinjika kaŵirikaŵiri umachepetsedwa mokulira.” Ngati chimenecho chiri tero m’chigwirizano ndi kusinthana ndi munthu wina, lingakhale thandizo lokulira chotani nanga lochokera ku kulankhula ndi Mulungu. Popeza kodi ndani amene tingakhale naye ndi ulemu wokulira kuposa Yehova?
7 Chimenecho ndicho chifukwa chake unansi waumwini wathithithi ndi iye uli wofunika kwambiri kaamba ka Akristu lerolino. Atumiki achikulire a Yehova amadziŵa ichi bwino lomwe, chotero iwo ali osamalira kupewa kufuna mayanjano ndi anthu a kudziko kapena kutha nthaŵi kumene kungafooketse unansi umenewo. (1 Akorinto 15:33) Iwonso amayamikira mmene chiriri chofunika kufikira Yehova m’pemphero, osati kokha kamodzi kapena kaŵiri patsiku, koma mobwerezabwereza. Akristu achichepere kapena achatsopano mwapadera afunikira kukulitsa chomangira chathithithi chimenechi ndi Yehova mwa phunziro lokhazikika ndi kusinkhasinkha pa Mawu ake ndiponso mwa mayanjano a Chikristu ndi utumiki. Tikufulumizidwa kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”—Yakobo 4:8.
Uphungu Umene Yesu Anapereka
8, 9. Tingagwiritsire ntchito uphungu wabwino uti wonena za mavuto a chuma?
8 M’maiko ambiri, kusowa ntchito ndi kupsyinjika kwa chuma kuli zopangitsa kudandaula zazikulu. Yesu anapereka uphungu wabwino wonena za zodera nkhaŵa zimenezi: “Musadere nkhaŵa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa, kapena thupi lanu chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?” (Mateyu 6:25) Inde, moyo ndi thupi, kapena munthu yense, ali wofunika mokulira kuposa chakudya ndi chovala. Atumiki a Mulungu angakhale otsimikizira kuti adzawathandiza iwo kupeza zosowa zawo zenizeni. Yesu anapereka chitsanzo ichi: “Yang’anirani mbalame za kumwamba, kuti sizifesa ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?” (Mateyu 6:26) Chiri chosalingalirika kuti Mulungu angapereke kaamba ka zinthu zokhala ndi mapiko koma kunyalanyaza atumiki ake aumunthu, amene ali amtengo wapatali kwa iye ndi kaamba ka amene Kristu anataya moyo wake.
9 Yesu kenaka anagogomezera chimenechi mwakulozera ku akakombo a m’munda omwe sagwira ntchito ndiponso sapota, komabe “ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la amenewa.” Ulamuliro wa Mfumu Solomo unadziŵika kaamba ka ulemerero wake. Yesu kenaka motonthoza anafunsa kuti: “Kodi [Mulungu] sadzaveka inu moposa?”—Mateyu 6:28-32, NW; Nyimbo ya Solomo 3:9, 10.
10. (a) Ndi kwa ndani kumene mawu otonthoza a Yesu anaperekedwa? (b) Ndi uphungu wotani umene iye anapereka ponena za mtsogolo?
10 Komabe, Yesu akupitiriza kusonyeza kuti ichi chiri kokha kaamba ka awo “ofuna choyamba ufumu ndi chilungamo chake.” Pa dziko lonse, Akristu owona oterowo amayamikira chimene kwenikweni Ufumu wa Mulungu uli ndi kuika iwo choyamba m’miyoyo yawo. Kwa iwo, chenjezo la Yesu limagwira ntchito: “Musadere nkhaŵa za mawa, pakuti mawa adzadzidera nkhaŵa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.” (Mateyu 6:33, 34) M’mawu ena, chitani ndi vuto lirilonse pamene libuka, ndipo musadere nkhaŵa mopambanitsa ponena za mtsogolo.
11, 12. Ndimotani mmene Akristu ena adzimverera kuti Yehova wawathandiza iwo kuyankha ku mapemphero awo?
11 Anthu ambiri, ngakhale kuli tero, ali oyedzamira ku kudandaula ponena za mtsogolo, makamaka pamene zinthu zilakwika. Koma Akristu angatembenukire ndipo ayenera kutembenukira m’chikhulupiriro kwa Yehova. Lingalirani nkhani ya Eleanor. Mwamuna wake anali kudwala kwambiri, ndipo kwa chaka chimodzi iye anali wosakhoza kugwira ntchito. Iye anali ndi ana aŵiri a ang’ono ndi tate wokalamba woyenera kusamalira, chotero iye sakanatha kusungilira ntchito ya nthaŵi zonse. Iwo anapempha Yehova kaamba ka thandizo. M’mawa wina, mwamsanga pambuyo pa ichi, iwo anapeza enivulupu pansi pa chitseko. Inali ndi unyinji wa ndalama—zokwanira kuwasunga iwo kufikira mwamuna wake anali wokhoza kugwiranso ntchito. Iwo anadzimva oyamikira mokulira kaamba ka thandizo la panthaŵi yake limeneli. Palibe maziko a Baibulo kaamba ka kuyembekezera chinthu chofananacho kuchitika kwa Mkristu aliyense wosowa, koma tingakhale otsimikizira kuti Yehova adzamva kulira kwathu ndipo kuti iye ali ndi kuthekera kwa kutithandiza ife m’njira zosiyanasiyana.
12 Mkazi wamasiye Wachikristu kum’mwera kwa Africa anayenera kufuna ntchito kuti apeze zosowa za ana ake a ang’ono aŵiri. Koma iye mwamphamvu anakhumba kugwira ntchito kokha theka la tsiku ndi cholinga chofuna kuthera nthaŵi ina ndi iwo. Pambuyo pa kupeza ntchito, iye anakakamizidwa kusiya iyo pamene manejala wake analingalira kuti anafuna mlembi wa nthaŵi zonse. Atasowa ntchito kachiŵirinso, mlongo ameneyo anapemphera mofunitsitsa kwa Yehova kaamba ka thandizo. Milungu itatu pambuyo pake, manejala wake wakale anamufunsa iye kubwereranso pa maziko a theka la tsiku. Iye anali wachimwemwe chotani nanga! Anadzimva kuti Yehova anayankha pemphero lake.
Pembedzerani Yehova
13. (a) Nchiyani chimene chikutanthauzidwa mwakuti “kupembedzera”? (b) Ndi zitsanzo za m’Malemba zotani za kupembedzera zimene tiri nazo?
13 Chonde dziŵani kuti pambuyo pa kuchenjeza kuti, “Musadere nkhaŵa konse,” Paulo akuwonjezera kuti, “komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” (Afilipi 4:6) Nchifukwa ninji akutchula “pembedzero”? Liwulo limatanthauza “kupembedzera mofunitsitsa,” kapena ‘pemphero lochonderera.’ Limaphatikizapo kupembedzera Mulungu mofunitsitsa, monga m’nthaŵi ya chitsenderezo chachikulu kapena tsoka. Pamene anali wandende, Paulo anapempha Akristu anzake kupembedzera iye kotero kuti akalalikire mopanda mantha “mbiri yabwino . . . monga mtumiki wa m’unyolo.” (Aefeso 6:18-20) Nduna ya nkhondo ya Chiroma Korneliyo nayenso “anapemphera Mulungu kosaleka.” Iye anali wosangalatsidwa chotani nanga pamene mngelo ananena kuti: “Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu”! Ndipo iye anali ndi mwaŵi wotani nanga kukhala pakati pa Akunja oyambirira kudzozedwa ndi mzimu woyera!—Machitidwe 10:1-4, 24, 44-48.
14. Ndimotani mmene tingadziŵire kaya kuchonderera kofunitsitsa kwa Yehova kufunikira kuchitidwa kamodzi kokha?
14 Chiri chofunika kudziŵa kuti kuchonderera kofunitsitsa koteroko kwa Yehova kaŵirikaŵiri sikuchitidwa kamodzi kokha. Yesu anaphunzitsa mu Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri: “Pitirizani kupempha, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza; pitirizani kugogoda, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu.” (Mateyu 7:7, NW) Malembedwe ambiri a Baibulo amapereka motere: “Pemphani . . . funani . . . gogodani.” Koma Chigriki choyambirira chimapereka lingaliro la kachitidwe kopitirizabe.a
15. (a) Nchifukwa ninji Nehemiya anali wachisoni pamene anali kuperekera vinyo kwa Mfumu Aritasasta? (b) Ndimotani mmene Nehemiya anachitira zowonjezereka kuposa kupereka pemphero lachidule?
15 Pamene Nehemiya anali kutumikira mfumu ya ku Perisiya Aritasasta monga woperekera chikho, mfumu inafunsa chifukwa chimene nkhope yake inali yachisoni. Nehemiya ananena kuti chinali chifukwa chakuti iye anali atadziŵa kuti Yerusalemu anali mumkhalidwe wosakazidwa. Mfumuyo kenaka inafunsa kuti: “Ufunanji iwe?” Pomwepo Nehemiya anafunsa Yehova kaamba ka thandizo, mosakaikira mwachidule, mwachete. Iye kenaka anapempha chilolezo cha kubwerera ku Yerusalemu kukamanganso mzinda wake wokondedwa. Pempho lake linaloledwa. (Nehemiya 2:1-6) Komabe, kusanafike kufunsidwa kowopsya kumeneko, Nehemiya anali atatha masiku angapo kuchonderera, kupembedzera, Yehova kaamba ka thandizo. (Nehemiya 1:4-11) Kodi mukuliwona phunziro mu ichi kaamba ka ena?
Yehova Amayankha
16. (a) Ndi mwaŵi wapadera wotani umene Abrahamu anasangalala nawo? (b) Ndi zothandizira zamphamvu zotani zimene tiri nazo zimene zingaphatikizidwe m’kuyankha mapemphero athu?
16 Pa chochitika china, Abrahamu anasangalala ndi mwaŵi wa kulankhula ndi Yehova kupyolera mwa angelo. (Genesis 22:11-18; 18:1-33) Ngakhale kuti chimenecho sichichitika lerolino, tiri odalitsidwa ndi zothandizira za mphamvu zimene Abrahamu analibe. Chimodzi chiri Baibulo lathunthu—magwero osatopetsedwa a chitsogozo ndi chitonthozo. (Masalmo 119:105; Aroma 15:4) Kaŵirikaŵiri, Baibulo lingatipatse ife chitsogozo kapena chilimbikitso chimene timachifuna, Yehova amatithandiza ife kukumbukira ndime zokhumbikazo. Kaŵirikaŵiri, concordance kapena chimodzi cha zofalitsidwa zambiri za Baibulo zimene Mulungu wapereka kupyolera mwa gulu lake zingatipatse ife yankho. Chosonyezera chatsatanetsatane ndi choyenera ku zofalitsidwa zimenezi chirinso thandizo lina lofunika koposa m’kupeza chidziŵitso chofunika.
17. Ndi mwanjira zina zotani mmene Yehova angayankhire mapemphero athu, ndipo ndimotani mmene Akristu achifundo, omvera chisoni angathandizire?
17 Ngati tivutitsidwa ndi vuto kapena kudzimva wokwiya kapena wokhumudwitsidwa, mayankho ku mapemphero athu angabwere m’njira zinanso. Mwachitsanzo, nkhani ya Baibulo pa mpingo kapena pa msonkhano wa Mboni za Yehova ingakhale ndi “mankhwala” okha amene tikuwafunikira. Panthaŵi zina, kucheza ndi Mkristu wina kungapereke chimene tifuna. Nthaŵi zambiri akulu mu mpingo angapereke chilimbikitso kapena uphungu. Ngakhale kungokhuthula mitima yathu kwa Mkristu wachikulire, wachifundo, ndi womvera chisoni yemwe ali mvetseri wabwino kaŵirikaŵiri kungatipange ife kumva bwino. Icho chiridi tero ngati bwenzi limeneli litithandiza ife kuwunikira pa malingaliro a Baibulo. Kusinthana koteroko kungachotse katundu wolemetsa pa maganizo ndi mtima wathu.—Miyambo 12:25; 1 Atesalonika 5:14.
18. Ndi ntchito yapadera yotani imene ingathandize Akristu kugonjetsa nyengo zokhumudwa, ndipo ndimotani mmene ichi chinathandizira mpainiya wachichepere?
18 Mikhalidwe yosiyanasiyana ya mkhalidwe wopsyinjidwa iri yofala mkati mwa “nthaŵi zino zovuta.” (2 Timoteo 3:1) Anthu akukhala okhumudwitsidwa ndi kuchita tondovi kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana. Ichi chingachitikenso kwa Akristu, ndipo chingakhale chokumana nacho choipa kwambiri. Ambiri apeza, ngakhale kuli tero, kuti kulalikira mbiri yabwino kwawathandiza iwo kuchotsako pang’ono mavuto awo.b Kodi mwayesera chimenecho? Pamene mudzimva kukhala wokhumudwitsidwa, yeserani kugawanamo mu mtundu winawake wa utumiki wa Ufumu. Kulankhula kwa ena ponena za Ufumu wa Mulungu kaŵirikaŵiri kudzakuthandizani kusintha mkhalidwe wanu wa maganizo kuchokera ku woipa kupita ku wabwino. Kulankhula ponena za Yehova ndi kugwiritsira ntchito Mawu ake kungakupatseni chimwemwe—chipatso cha mzimu wake—ndi kukupangitsani kudzimva mosiyana. (Agalatiya 5:22) Mpainiya wachichepere anapezanso kuti kukhala wotanganitsidwa m’ntchito ya Ufumu kunamupangitsa iye kuzindikira kuti “m’kuyerekeza ndi mavuto a ena, [ake] anali ochepa kwambiri ndipo apa kanthaŵi.”
19. Ndimotani mmene Mkristu wa mkhalidwe wa umoyo woipa anagonjetsera malingaliro olakwa?
19 Pa nthaŵi zina, mkhalidwe wa kuthupi wotsika, mwinamwake woyambitsidwa ndi nkhaŵa kapena mavuto, ungatsogolere ku mkhalidwe wopsyinjika. Ichi chingapangitse wina kuwuka usiku wovutitsidwa, monga mmene nthaŵi zina zinachitikira kwa Mkristu wa zaka zapakati yemwe anali ndi umoyo woipa. Koma iye anapeza kuti pemphero lochokera mu mtima linali thandizo lenileni. Nthaŵi zonse pamene anauka akudzimva wopsyinjika, iye anapemphera kwa Yehova mofatsa. Ichi mwamsanga chinampangitsa iye kumva bwino. Iyenso anapeza icho kukhala chotonthoza kubwereza kuchokera m’kukumbukira ndime zotonthoza za Baibulo, monga ngati Masalmo 23. Mosasunthika, mzimu wa Yehova, wogwira ntchito m’kuyankha ku pemphero kapena kupyolera m’Mawu ake, udzatithandiza kubwezeretsa mkhalidwe wa maganizo wopsyinjika ndi wachimwemwepo. Pambuyo pake, munthuyo akalingalira ponena za mavuto ake ndi kulinganizika ndi bata, kuwona mmene angawalakire iwo kapena kudzimva kukhala wolimbikitsidwa kupirira nawo.
20. Nchifukwa ninji yankho ku pemphero nthaŵi zina lingawoneke kukhala likuchedwa?
20 Ichi chiri chitsanzo cha mmene pemphero lingabweretsere yankho. Koma nthaŵi zina pamawonekera kuchedwa mkupeza yankho. Chifukwa ninji? Mwinamwake yankho liyenera kudikira nthaŵi yoikika ya Mulungu. Chikuwoneka kuti nthaŵi zina Mulungu amalola opembedzera ake kuchitira chitsanzo kuzama kwa kudera nkhaŵa kwawo, ukulu wa chikhumbo chawo, kuwona mtima kwa kudzipereka kwawo. Mmodzi wa amasalmo anali ndi chokumana nacho choterocho!—Masalmo 88:13, 14; yerekezani ndi 2 Akorinto 12:7-10.
21. Nchifukwa ninji uli mwaŵi waukulu kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova lerolino, ndipo ndimotani mmene tingasonyezere chiyamikiro?
21 M’chochitika chirichonse, kulankhuzana ndi Mulungu Wamphamvuyonse m’pemphero chiri chokumana nacho cholimbikitsa chikhulupiriro chomwe chingatichotse ife ku kusowa chochita kufika ku chidaliro. Chiri chotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti iye amamva ndi kuyankha! Monga mmene Paulo analembera mpingo wa mu Filipi, tiyenera kupereka mapemphero athu ndi mapembedzero “pamodzi ndi chiyamiko.” (Afilipi 4:6) Inde, tsiku lirilonse tiyenera kutsegula mitima yathu m’chiyamiko kwa Yehova ndi “m’zonse yamikani.” (1 Atesalonika 5:18) Ichi chidzagawirako ku chomangira chapafupi, chotentha ndipo chidzabweretsa mtendere kwa ife. Nkhani yotsatira idzasonyeza mmene ichi chiriri chofunika kwa atumiki a Yehova m’nthaŵi zino zovutitsa, ndi zowopsya.
[Mawu a M’munsi]
a M’kugwirizana ndi kulondola kwa New World Translation of the Holy Scriptures, Charles B. Williams akutembenuza versilo motere: “Pitirizani kupempha . . . pitirizani kufuna . . . pitirizani kugogoda, ndipo chitseko chidzatsegulidwa kwa inu.”—The New Testament: A Translation in the Language of the People.
b Kuchita tondovi kwa pa kanthaŵi kuli kosiyana ndi kwakukulu, kupsyinjika kopitiriza, kumene kuli kowopsya ndi mkhalidwe wocholowanacholowana wa malingaliro kapena maganizo. Onani Galamukani! ya October 22, 1987, Chingelezi, masamba 3-16.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Ndi nsonga zotani zimene zingapangitse Akristu kuvutitsidwa?
◻ Nchiyani chimene chingatithandize ife kugonjetsa kudera nkhaŵa?
◻ Nchifukwa ninji Akristu angatsimikizire kuti Mulungu adzawathandiza iwo ndi zosowa zawo zazikulu?
◻ Nchiyani chimene “pembedzero” limatanthauza, ndipo ndimotani mmene zitsanzo zakale zimachitira chitsanzo mmene Yehova amayankhira?
◻ Ndi njira zosiyana zotani mu zimene Yehova angayankhire mapemphero athu?
[Chithunzi patsamba 12]
‘Atate wanu wakumwamba amadyetsa mbalame. Kodi simuli oyenera kuposa izo?’