“Mboni Yokhulupirika Kuthambo”
KUYAMBIRA kale kwambiri, anthu akhala akulemba nyimbo ndiponso ndakatulo zotama mwezi chifukwa cha maonekedwe ake. Mwachitsanzo, nyimbo ina youziridwa ndi Mulungu imanena za mkazi “wokongola ngati mwezi.” (Nyimbo ya Solomo 6:10) Ndipo wamasalmo ananena mwandakatulo kuti mwezi ndi “mboni yokhulupirika kuthambo.” (Salmo 89:37) Kodi mawu onena za mweziwa akutanthauza chiyani?
Nthawi zonse mwezi umayenda ulendo wozungulira dziko kwa masiku 27 ndi maola 7 ndipo sulephera kutero ngakhale pang’ono. Motero, n’chifukwa chake wamasalmo anatchula mweziwu kuti mboni yokhulupirika. Komabe, n’zotheka kuti wamasalmoyu sankangotanthauza zokhazi ayi. Iye anatcha mweziwo “mboni yokhulupirika” m’nyimbo yolosera za Ufumu umene Yesu anauza ophunzira ake kuti aziupempherera.—Mateyo 6:9, 10.
Zaka zoposa 3,000 zapitazo, Yehova Mulungu anachita pangano laufumu ndi Mfumu Davide ya Isiraeli. (2 Samueli 7:12-16) Cholinga cha pangano limenelo chinali choika maziko oti Yesu Khristu adzabwere, kudzalowa ufumu wa Davide, n’kudzakhala pa mpando wa ufumuwo kosatha. (Yesaya 9:7; Luka 1:32, 33) Ponena za mpando wa “mbewu” ya Davide, wamasalmo ananena mawu otsatirawa m’nyimbo yake: “Udzakhazikika ngati mwezi ku nthawi yonse, ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo.”—Salmo 89:36, 37.
Mwezi, womwe ndi “chounikira chakulamulira usiku,” umathandiza kwambiri potikumbutsa kuti ulamuliro wa Khristu n’ngosatha. (Genesis 1:16) Ponena za Ufumu wa Yesu, lemba la Danieli 7:14 limati: ‘Ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha . . . ndi ufumu wake sudzawonongeka.’ Mwezi ndi mboni yotikumbutsa za ufumu umenewo ndiponso za madalitso amene ufumuwo udzabweretse kwa anthu.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Moon: NASA photo