Zimene Owerenga Amafunsa . . .
Kodi Mulungu Ali ndi Chiyambi?
▪ Baibulo limanena kuti Mulungu alibe chiyambi. Mulungu wakhala alipo nthawi zonse. N’zoona kuti mfundoyi ndi yovuta kuimvetsa, komabe munthu sanganene kuti mfundoyi ndi yabodza chifukwa chakuti iyeyo akulephera kuimvetsa.
Kodi tingayembekezere kumvetsa njira zonse za Mulungu? Mtumwi Paulo anati: “Ha, kuchuluka kwa chuma cha Mulungu! Nzeru zake n’zozama, ndipo kudziwa kwake zinthu n’kozamanso zedi! Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake?” (Aroma 11:33) Sitingamvetse kuchuluka kwa nzeru za Mulungu, mofanana ndi mmene mwana wamng’ono sangamvetse zonse zokhudza makolo ake. Ngakhale kuti palembali Paulo ankatanthauza kuti nzeru ndiponso chifundo cha Mulungu ndi zapadera, mawu amenewa amasonyezanso kuti pali zinthu komanso zochita zina za Yehova Mulungu zimene ndi zozama kwambiri moti sitingazimvetse. Chimodzi mwa zinthu zimenezi ndi mfundo yakuti Mulungu alibe chiyambi. Ngakhale zili choncho, sitingakayikire zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za Mulungu chifukwa Yesu Khristu ponena za Malemba opatulika, anati: “Mawu anu ndiwo choonadi.”—Yohane 17:17.
Popemphera kwa Yehova, Mose anati: “Inu mwakhala mulipo kuyambira kalekale ndipo mudzakhalapo mpaka kalekale.” (Salmo 90:2, The Holy Bible, New Century Version) Palembali, Mose anafotokoza mbali ziwiri. Choyamba, iye ananena kuti Mulungu adzakhalapo mpaka kalekale. Yehova ndi “wokhala ndi moyo kwa muyaya ndi muyaya.” (Chivumbulutso 4:10) Choncho, Mulungu adzakhalapo kwamuyaya. Chachiwiri Mose ananena kuti Mulungu wakhala alipo kuyambira kalekale. M’mawu ena tinganene kuti Mulungu sanachite kulengedwa ndipo alibe chiyambi, koma kuti wakhala alipo kuyambira kalekale.
Choncho m’pomveka kunena kuti Mulungu yekha ndi amene amadziwika ndi dzina lomulemekezera lakuti “Mfumu yosatha.” (1 Timoteyo 1:17) Tangoganizani, Yesu Khristu, miyandamiyanda ya angelo kumwamba komanso anthu onse padziko lapansi ali ndi chiyambi chifukwa anachita kulengedwa. (Akolose 1:15, 16) Koma si mmene Mulungu alili. Kulimbikira kunena kuti Mulungu anachita kulengedwa kumayambitsa mafunso osathandiza, ofuna kudziwa amene analenga Mlengi. Ndi Yehova yekha amene wakhala alipo “kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha.”—Salmo 90:2; Yuda 25.
Komabe mfundo yakuti Mulungu alibe chiyambi ndiponso alibe mapeto ikutithandiza kumvetsa kenakake. Tikaonetsetsa bwinobwino pemphero la Mose, timaona kuti mfundo imeneyi imasonyeza kuti lonjezo la moyo wosatha limene Mulungu anatipatsa ndi lodalirika. Mosiyana ndi moyo wathu umene ndi waufupi, Mulungu amatchedwa “mokhalamo m’mibadwo mibadwo.” Monga Atate wachikondi, Yehova wakhala akuthandiza, amathandiza ndipo adzapitirizabe kuthandiza anthu ake. Mfundo imeneyi ingakulimbikitseni kwambiri.—Salmo 90:1.