Umphumphu Wanu Umakondweretsa Mtima wa Yehova
“Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.”—MIY. 27:11.
1, 2. (a) Kodi buku la Yobu limafotokoza kuti Satana anati chiyani poneneza anthu? (b) N’chiyani chimene chikusonyeza kuti Satana anapitirizabe kutsutsa Yehova ngakhale kuti Yobu anali atafa kale?
YEHOVA analola Satana kuyesa umphumphu wa mtumiki wake wokhulupirika Yobu. Choncho, ziweto zake zinaphedwa ndipo zina zinabedwa, ana ake anafa ndipo iye anayamba kudwala. Pa nthawi imene Satana ankakayikira umphumphu wa Yobu, sikuti ankangoganiza za Yobu yekhayo. Satana anati: “Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.” Mawu amenewa anayambitsa nkhani imene imakhudza anthu ena osati Yobu yekhayo, ndipo nkhani imeneyi ikupitirirabe ngakhale kuti Yobu anafa kale.—Yobu 2:4.
2 Patapita zaka pafupifupi 600 kuchokera pamene Yobu anakumana ndi mayesero, Mulungu anamuuzira Solomo kulemba kuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miy. 27:11) Izi zikusonyeza kuti pa nthawiyi n’kuti Satana akupitirizabe kutsutsa Yehova. Komanso mtumwi Yohane anaona masomphenya. M’masomphenyawo, Satana anali atachotsedwa kumwamba pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu m’chaka cha 1914 ndipo ankaneneza atumiki a Mulungu. Inde, ngakhale masiku ano pamene tili kumapeto kwa masiku otsiriza a dongosolo loipali, Satana akupitirizabe kukayikira umphumphu wa atumiki a Mulungu.—Chiv. 12:10.
3. Kodi ndi mfundo zofunika kwambiri ziti zimene tikuphunzira m’buku la Yobu?
3 Tsopano tiyeni tikambirane mfundo zitatu zofunika kwambiri zimene tikuphunzira m’buku la Yobu. Yoyamba, mayesero a Yobu akutithandiza kudziwa mdani weniweni wa anthu onse ndiponso kuti mdani ameneyu ndi amenenso amachititsa kuti anthu a Mulungu azitsutsidwa. Mdani ameneyu ndi Satana Mdyerekezi. Yachiwiri, kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu kungatithandize kusunga umphumphu ngakhale titakumana ndi mayesero aakulu. Yachitatu, pamene takumana ndi mavuto ndipo tikuyesedwa m’njira ina yake, Mulungu amatithandiza monga mmene anathandizira Yobu. Masiku ano Yehova amatithandiza pogwiritsa ntchito Mawu ake, gulu lake ndiponso mzimu wake woyera.
Tisamaiwale Mdani Wathu Weniweni
4. Kodi ndani amene akuchititsa mavuto padzikoli?
4 Anthu ambiri sakhulupirira kuti Satana aliko. Choncho, ngakhale kuti iwo angachite mantha akamaona mavuto apadziko lapansili, sadziwa kuti Satana Mdyerekezi ndi amene amawayambitsa. Komanso mbali ina anthu ndi amene amayambitsa ambiri mwa mavuto amene timakumana nawo. Makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, sanafune kulamuliridwa ndi Mlengi wawo. Kuyambira pamenepo mibadwo yonse ya anthu yakhala ikuchita zinthu zosalongosoka. Komabe, Mdyerekezi ndi amene ananyenga Havayo kuti apandukire Mulungu. Iye ndi amene wakhazikitsa dongosolo la dzikoli pa anthu opanda ungwiro amenenso amafa. Chifukwa chakuti Satana ndi “mulungu wa dongosolo lino la zinthu,” anthu padziko lonse amasonyeza makhalidwe amene iye ali nawo monga kunyada, ndewu, nsanje, dyera, chinyengo komanso mzimu woukira. (2 Akor. 4:4; 1 Tim. 2:14; 3:6; werengani Yakobe 3:14, 15.) Makhalidwe amenewa ayambitsa mikangano yandale ndiponso yachipembedzo, udani, katangale komanso chiwawa. Zimenezi zabweretsa mavuto ambiri kwa anthu.
5. Kodi tiyenera kuchita chiyani ndi zinthu zamtengo wapatali zimene tikudziwa?
5 Ife atumiki a Yehova timadziwa zinthu zamtengo wapatali. Tikudziwa amene akuchititsa kuti zinthu ziipe kwambiri padzikoli. Kudziwa zimenezi kumatilimbikitsa kugwira ntchito yolalikira, kuti anthu adziwe amene amayambitsa mavuto onsewa. Ndipo timasangalatsa kwambiri kukhala kumbali ya Mulungu woona Yehova ndiponso kuwafotokozera ena mmene iye adzawonongera Satana komanso mmene adzathetsera mavuto a anthu.
6, 7. (a) Kodi ndani amene amachititsa kuti olambira oona azizunzidwa? (b) Kodi tingatengere bwanji chitsanzo cha Elihu?
6 Kuwonjezera pa kuyambitsa mavuto a dzikoli, Satana ndi amenenso amasonkhezera anthu kuti azitsutsa atumiki a Mulungu. Iye angachite chilichonse kuti atiyese. Yesu Khristu anauza mtumwi Petulo kuti: “Simoni, Simoni! Ndithu Satana akufuna anthu inu, kuti akupeteni ngati tirigu.” (Luka 22:31) Choncho wina aliyense amene amatsatira mapazi a Yesu, adzakumana ndi mayesero osiyanasiyana. Petulo anati Mdyerekezi ali ngati “mkango wobangula, wofunitsitsa kuti wina umudye.” Ndipo Paulo anati: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.”—1 Pet. 5:8; 2 Tim. 3:12.
7 Kodi pamene wokhulupirira mnzathu akumana ndi mavuto, tingasonyeze bwanji kuti sitikuiwala mdani wathu weniweni? M’malo momusiya yekha m’bale wathuyo, tiyenera kukhala ngati Elihu amene analankhula ndi Yobu monga bwenzi lenileni. M’bale wathu akagweredwa mavuto timamuthandiza kulimbana ndi mdani watonsefe, Satana. (Miy. 3:27; 1 Ates. 5:25) Cholinga chathu chimakhala kuthandiza mtumiki mnzathuyo kusungabe umphumphu zivute zitani, chifukwa akatero adzakondweretsa mtima wa Yehova.
8. Kodi n’chifukwa chiyani Satana sanathe kuletsa Yobu kulemekeza Yehova?
8 Chinthu choyamba chimene Satana anamuwonongera Yobu chinali ziweto. Ziweto zimenezo zinali za ndalama zambiri ndipo mwina iye ankadalira ziwetozo kuti azipeza zosowa za banja lake. Yobu ankagwiritsanso ntchito ziwetozo polambira. Yobu atapatula kapena kuti kuyeretsa ana ake, anauka “mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m’mtima mwawo. Anatero Yobu masiku onse.” (Yobu 1:4, 5) Choncho nthawi zonse Yobu ankapereka nsembe za nyama kwa Yehova. Ndiyeno atakumana ndi mayesero aja, sakanathanso kuchita zimenezi. Pa nthawiyo, Yobu analibe “chuma” choti alemekezere Yehova. (Miy. 3:9) Komabe iye akanatha kulemekeza Yehova ndi milomo yake, ndipo anachitadi zimenezi.
Khalani pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova
9. Kodi chinthu chofunika kwambiri kwa ife n’chiyani?
9 Kaya ndife olemera kapena osauka, ana kapena achikulire, athanzi kapena odwala, tingathe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Ngakhale titakumana ndi mayesero aakulu, kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu kudzatithandiza kusungabe umphumphu ndi kukondweretsa mtima wa Yehova. Ngakhale anthu amene ankadziwa zochepa chabe za choonadi analimba mtima n’kusungabe umphumphu wawo.
10, 11. (a) Kodi mlongo wina anatani atakumana ndi mayesero? (b) Kodi mlongoyu anapereka yankho losatsutsika lotani kwa Satana?
10 Taganizirani chitsanzo cha Mlongo Valentina Garnovskaya. Iye ndi chitsanzo chimodzi cha Mboni zambiri za ku Russia, zomwe mofanana ndi Yobu wokhulupirikayo, zinasungabe umphumphu ngakhale zinakumana ndi mayesero oopsa. Pamene iye anali ndi zaka 20 m’chaka cha 1945, analalikiridwa ndi m’bale wina. M’baleyu anabwera kwa mlongoyu kudzakambirana naye za Baibulo kawiri kokha, kenako sanadzakumanenso. Ngakhale zinali choncho, Valentina anayamba kulalikira kwa anthu ena. Zotsatirapo zake, iye anamangidwa ndipo analamulidwa kuti akhale kumalo ogwirira ukaidi kwa zaka 8. Atangotuluka m’chaka cha 1953, anayambiranso ntchito yake yolalikira. Kenako anamangidwanso ndipo analamulidwa kuti akhale m’ndende zaka 10. Atakhala zaka zingapo kumalo amodzi ogwirira ukaidi, anamusamutsiranso kumalo ena. Kumalo atsopanowa, anakumana ndi alongo ena amene anali ndi Baibulo. Tsiku lina mlongo wina anamuonetsa Valentina Baibulolo. Izitu zinali zosangalatsa kwambiri chifukwa kuchokera m’chaka cha 1945 pamene analalikidwa ndi m’bale uja, iye sanaonenso Baibulo.
11 M’chaka cha 1967, Valentina anamasulidwa ndipo kenako anabatizidwa posonyeza kudzipereka kwake kwa Yehova. Pa nthawi imene iye anali pa ufulu umenewu, anagwira ntchito yolalikira mwachangu mpaka m’chaka cha 1969. Komabe m’chaka chimenechi, iye anamangidwanso ndipo pa nthawiyi analamulidwa kuti akhale m’ndende kwa zaka zitatu. Koma Valentina sanasiye kulalikira. Iye asanamwalire m’chaka cha 2001, anali atathandiza anthu okwana 44 kuphunzira choonadi. Mlongoyu anali atatha zaka 21 ali m’ndende komanso m’malo osiyanasiyana ogwirira ukaidi. Iye analolera kusiya chilichonse, kuphatikizapo ufulu wake, kuti asunge umphumphu. Atatsala pang’ono kumwalira Valentina ananena kuti: “Sindinakhalepo ndi nyumba yangayanga. Katundu wanga yense anali m’sutikesi imodzi basi, komabe ndinali wosangalala ndiponso wokhutira ndi zimene ndinali nazo potumikira Yehova.” Apatu Valentina anatsutsa bodza la Satana, amene amanena kuti anthu sangakhale okhulupirika kwa Mulungu atakumana ndi mayesero. (Yobu 1:9-11) Sitikukayika kuti iye anakondweretsa mtima wa Yehova ndiponso kuti Yehova akufunitsitsa kudzaukitsa Valentina limodzi ndi anthu ena onse amene anafa ali okhulupirika.—Yobu 14:15.
12. Kodi chikondi chimatithandiza bwanji pa ubwenzi wathu ndi Yehova?
12 Tili pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa chakuti timamukonda. Timasirira makhalidwe a Mulungu ndipo timachita chilichonse chimene tingathe kuti makhalidwe athu akhale ogwirizana ndi zolinga zake. Mosiyana ndi zimene Mdyerekezi amanena, timakonda Yehova mwakufuna kwathu osati chifukwa cha dyera. Chikondi chochokera pansi pa mtima chimenechi chimatithandiza kusunga umphumphu tikamayesedwa. Nayenso Yehova ‘amadikirira khwalala la opatulidwa ake,’ kapena anthu ake okhulupirika.—Miy. 2:8; Sal. 97:10.
13. Kodi Yehova amaziona bwanji zimene timamuchitira?
13 Chikondi chimatithandiza kuti tizilemekeza dzina la Yehova, ngakhale kuti nthawi zina tingaganize kuti sitingakwanitse kuchita zambiri. Yehova amadziwa zolinga zathu zabwino ndipo satiimba mlandu ngati sitikwanitsa zonse zimene tingafune kuchita. Chofunika kwambiri kwa iye si zimene timachita zokha, komanso chifukwa chimene timachitira zinthuzo. Ngakhale kuti Yobu anali pa chisoni chachikulu ndiponso anavutika kwambiri, anauza anthu amene ankamutsutsa kuti iye ankakonda malamulo a Yehova. (Werengani Yobu 10:12; 28:28.) M’chaputala chomaliza cha buku la Yobu, Mulungu ananena kuti anakwiya ndi Elifazi, Bilidadi ndiponso Zofari chifukwa iwo sananene zoona. Komanso, Yehova anasonyeza kuti anakondwera ndi Yobu pomutchula kanayi kuti “mtumiki wanga” ndiponso anamuuza kuti awapempherere anthu atatu opalamula aja. (Yobu 42:7-9) Tiyeni nafenso tizichita zinthu zokondweretsa Yehova kuti azitiyanja.
Yehova Amathandiza Atumiki Ake Okhulupirika
14. Kodi Yehova anamuthandiza bwanji Yobu kusintha maganizo ake?
14 Yobu anasungabe umphumphu ngakhale anali wopanda ungwiro. Koma nthawi zina chifukwa chopanikizika kwambiri, iye ankaona zinthu molakwika. Mwachitsanzo, iye ananena kwa Yehova kuti: “Ndifuula kwa Inu, koma simundiyankha . . . Ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza.” Komanso Yobu ananyanyira podzilungamitsa pamene ananena kuti: “Sindili woipa,” ndipo “palibe chiwawa m’manja mwanga, ndi pemphero langa ndi loyera.” (Yobu 10:7; 16:17; 30:20, 21) Komabe Yehova anamuthandiza Yobu mokoma mtima. Iye anamufunsa mafunso osiyanasiyana amene anamuthandiza kuti asamangoganiza za iye mwini ndipo izi zinamuthandiza kudziwa kuti Mulungu ndi wamkulu kwambiri kuposa anthu. Yobu atadzudzulidwa chonchi analabadira ndipo anasintha maganizo ake.—Werengani Yobu 40:8; 42:2, 6.
15, 16. Kodi Yehova amathandiza bwanji atumiki ake masiku ano?
15 Masiku anonso Yehova amalangiza atumiki ake mokoma mtima komanso mosabisa mawu. Kuwonjezera pamenepa timapindulanso m’njira zambiri. Mwachitsanzo, Yesu Khristu anapereka nsembe ya dipo ndipo machimo athu amakhululukidwa chifukwa cha nsembe imeneyi. Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, tingathe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu chifukwa cha nsembe imeneyi. (Yak. 4:8; 1 Yoh. 2:1) Komanso tikamakumana ndi mayesero, timapempha mzimu woyera wa Mulungu kuti utithandize ndi kutilimbitsa. Ndiponso tili ndi Baibulo lathunthu limene tikamaliwerenga ndi kusinkhasinkha zimene tawerenga, timakhala okonzeka kulimbana ndi zinthu zoyesa chikhulupiriro chathu. Kuphunzira Mawu a Mulungu kumatithandiza kumvetsa nkhani yaikulu yokhudza ulamuliro wa Mulungu m’chilengedwe chonse ndiponso yokhudza umphumphu wathu.
16 Kuwonjezera pamenepa, timathandizidwa kwambiri chifukwa chakuti tili m’gulu la padziko lonse la abale limene Yehova amalipatsa chakudya chauzimu kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) M’mipingo pafupifupi 100,000 ya Mboni za Yehova mumachitika misonkhano imene imatiphunzitsa ndi kutikonzekeretsa kuti tizikhalabe okhulupirika tikakumana ndi mayesero. Chitsanzo cha Mboni ina yachitsikana ya ku Germany, dzina lake Sheila, chikutsimikizira zimenezi.
17. Fotokozani chitsanzo chosonyeza ubwino wotsatira malangizo amene gulu la Yehova limapereka masiku ano.
17 Tsiku lina Sheila ali kusukulu, aphunzitsi ake anatuluka m’kalasi yawo, ndiye ophunzirawo anaganiza zoyesa kugwiritsa ntchito thabwa lina lamatsenga. Sheila atangomva zimenezi anatuluka m’kalasimo. Ndipo atamva zimene zinachitika iye atatulukamo, anaona kuti anachita bwino kwambiri. Anzakewo atayamba kugwiritsa ntchito thabwa lamatsengalo, ena mwa iwo anazindikira kuti m’kalasimo mwabwera ziwanda ndipo anagwidwa mantha kwambiri n’kuyamba kuthawa. Koma kodi n’chiyani chinamuthandiza Sheila kuganiza zotuluka m’kalasimo mwamsangamsanga? Iye ananena kuti: “Tinali titangophunzira kumene pamsonkhano wina ku Nyumba ya Ufumu kuti matabwa amatsenga ndi oopsa. Ndiye ndinadziwiratu zoyenera kuchita. Ndiponso ndinkafuna kukondweretsa Yehova, monga mmene Baibulo limatiuzira pa Miyambo 27:11.” Sheila anachita bwino kwambiri kupezeka komanso kumvetsera mwachidwi pamsonkhanowu.
18. Kodi inuyo panokha mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?
18 Tiyeni tonsefe tizitsatira malangizo onse amene gulu la Mulungu limapereka. Kuti tipeze malangizo ndiponso thandizo limene timafunikira, tiyenera kumapezeka pamisonkhano nthawi zonse, kuwerenga Baibulo, kuphunzira mabuku ofotokoza Baibulo, kupemphera ndiponso kucheza ndi Akhristu okhwima mwauzimu. Yehova amafuna kuti tipambane ndipo ali ndi chikhulupiriro kuti tidzakhalabe okhulupirika. Ndi mwayi waukulu kwambiri kulemekeza dzina la Yehova, kusunga umphumphu komanso kukondweretsa mtima wa Yehova.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi Satana amayambitsa mavuto ndi mayesero otani?
• Kodi chinthu chofunika kwambiri kwa ife n’chiyani?
• Kodi n’chifukwa chiyani tili pa ubwenzi ndi Yehova?
• Kodi Yehova amatithandiza m’njira zotani masiku ano?
[Chithunzi patsamba 8]
Kodi mumafunitsitsa kuuza ena choonadi chamtengo wapatali chimene mwachidziwa?
[Chithunzi patsamba 9]
Tingathandize okhulupirira anzathu kuti asunge umphumphu wawo
[Chithunzi patsamba 10]
Valentina analolera kutaya chilichonse pofuna kusungabe umphumphu