“Nthaŵi Yolankhula”—Liti?
MARY amagwira ntchito monga wothandiza wa mankhwala pa chipatala. Chofunika chimodzi chimene ayenera kugwirizana nacho mu ntchito yake chiri kusunga chinsinsi. Iye amafunikira kusunga zolembera ndi chidziŵitso chogwirizana ndi ntchito yake kusapita kwa anthu osayeneretsedwa. Malamulo a mu boma lake amaletsanso kunena chidziŵitso cha chinsinsi cha odwala.
Tsiku lina Mary anakumana ndi kupanikizidwa. Pamene anali kugwirira ntchito pa zolembera za mankhwala, iye anafika pa chidziŵitso chosonyeza kuti wodwala, Mkristu mnzake, anali atalembetsa ku kuchotsa mimba. Kodi iye anali ndi thayo la m’Malemba la kuvumbula chidziŵitsochi kwa akulu mu mpingo, ngakhale kuti chikakhoza kutsogolera ku kutaya ntchito yake, ku kuzengedwa kwake mlandu, kapena ku kukhala ndi mavuto a lamulo a omulemba ntchito ake? Kapena kodi Miyambo 11:13 ikalungamitsa kusunga nkhaniyo kukhala yobisidwa? Ipo pamaŵerenga kuti: “Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi; koma wokhulupirika mtima abisa mawu.”—Yerekezani ndi Miyambo 25:9, 10.
Mikhalidwe yonga uwu imayang’anizana ndi Mboni za Yehova nthaŵi ndi nthaŵi. Monga Mary, iwo amakhala ozindikira kotheratu za chimene Mfumu Solomo anawona: “Kanthu kali konse kali ndi nthaŵi yake ndi chifuno chiri chonse cha pansi pa thambo: . . . mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:1, 7) Kodi iyi inali nthaŵi ya Mary yakutonthola, kapena inali nthaŵi yakulankhula ponena za zimene iye anadziŵa?a
Mikhalidwe ingasiyane mokulira. Chotero, chingakhale chosatheka kukhazikitsa njira ya makhalidwe yoyenera kutsatiridwa mu mkhalidwe uliwonse, ngati kuti aliyense adzasamalira nkhaniyi mu njira yofanana ndi Mary. Ndithudi, Mkristu aliyense, ngati angakumane ndi mkhalidwe wonga ngati uwu, ayenera kukonzekeretsedwa kuyesa mbali zonse zokhudzidwa ndi kufikira chosankha chomwe amalingalira maprinsipulo a Baibulo limodzinso ndi zolowetsedwamo za lamulo zomwe zidzamusiya iye kapena winayo ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Yehova. (1 Timoteo 1:5, 19) Pamene machimo ali ochepa ndipo kaamba ka kupanda ungwiro kwa munthu, prinsipulo ili limagwira ntchito: “Chikondi chikwirira unyinji wa machimo.” (1 Petro 4:8) Koma pamene pawonekera kuti pali cholakwa chachikulu, kodi Mkristu wokhulupirika kokha chifukwa cha chikondi cha Mulungu ndi mnansi wake Wachikristu ayenera kuvumbulutsa chomwe akudziŵa kotero kuti wochimwayo angalandire thandizo ndi kuti kuyera kwa mpingo kusungidwe?
Kugwiritsira Ntchito Maprinsipulo la Baibulo
Kodi ndi maprinsipulo okulira a Baibulo ena ati amene angagwire ntchito? Choyamba, aliyense wochita cholakwa chachikulu sayenera kuyesa kuchibisa icho. “Obisa machimo ake [sadzapambana], koma wakuvomereza nawasiya adzachitidwa chifundo.” (Miyambo 28:13) Palibe chirichonse chimapulumuka chidziŵitso cha Yehova. Machimo obisidwa mkupita kwanthaŵi adzaŵerengeredwa. (Miyambo 15:3; 1 Timoteo 5:24, 25) Nthaŵi zina Yehova amabweretsa chobisidwa choipacho ku chidziŵitso cha chiwalo cha mpingo kotero kuti ichi chibweretsedwe ku chisamaliro choyenera.—Yoswa 7:1-26.
Chitsogozo china cha Baibulo chimapezeka pa Levitiko 5:1: “Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mawu akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuwona, kapena wakudziŵa, koma osaulula, azisenza mphulupulu yake.” “Kumva mawu akulumbiritsa” kumeneku sikunali koipa kapena konyansa. M’malo mwake, kaŵirikaŵiri chinali kuti pamene winawake analakwiridwa anakakamiza kuti mboni yoyenerera imthandiza iye kupeza chilungamo, pamene anali kulumbiritsa—mwachidziŵikire kuchokera kwa Yehova—pa wina wake, mwinamwake mosazindikiritsidwa, amene adamulakwira iye. Unali mtundu wakuika ena pansi pa chilumbiro. Wochitira umboni aliyense wa cholakwacho akadziŵa amene anavutika ndi kupanda chilungamo ndipo akakhala ndi thayo la kubwera kudzakhazikitsa cholakwacho. Kupanda apo, iwo anayenera ‘kuyankha kaamba ka zolakwa zawo’ pamaso pa Yehova.b
Chiweruzo chimenechi chochokera ku Malo Apamwamba koposa aulamuliro mu chilengedwe amaika thayo pa aliyense wa Aisrayeli kupereka ripoti kwa oweruza cholakwa chirichonse chowopsya chomwe anawona kotero kuti nkhaniyo isamaliridwe. Pamene kuli kwakuti Akristu sali mokakamizika pansi pa Chilamulo cha Mose, maprinsipulo ake amagwirabe ntchito ku mpingo Wachikristu. Chotero, pangakhale nthaŵi pamene Mkristu amakhala ndi thayo lakubweretsa nkhani ku chisamaliro cha akulu. Zowona, chiri cholakwa m’maiko ambiri kudziŵitsa anthu osayeneretsedwa zinthu zomwe zikupezedwa mu zolembera za mseri. Koma ngati Mkristu adzimva, pambuyo pa kulingalira kwa pemphero, kuti iye akuyang’anizana ndi mkhalidwe umene lamulo la Mulungu likumufuna iye kupereka ripoti la chimene iye akudziŵa mosasamala kanthu za malamulo a olamulira ocheperako, pamenepo liri thayo limene alandira kwa Yehova. Pamakhala nthaŵi pamene Akristu “ayenera kumvera Mulungu osati anthu.”—Machitidwe 5:29.
Pamene kuli kwakuti zilumbiro kapena malonjezo enieni sayenera kutengedwa mopepuka, pangakhale pamene malonjezo ofunikira kwa anthu ali owombana ndi chifuno chakupereka kudzipereka kotheratu kwa Mulungu wathu. Pamene winawake achita chimo lalikulu, iye, m’chenicheni, amafika pansi pa ‘kulumbiritsidwa kwapoyera’ kuchokera kwa mmodzi wa wolakwiridwayo, Yehova Mulungu. (Deuteronomo 27:26; Miyambo 3:33) Onse amene amakhala mbali ya mpingo Wachikristu amadziika iwo eni pansi pa “lumbiro” kusunga mpingo kukhala woyera, ponse paŵiri mwa zimene iwo amachita mwaumwini ndi njira imene iwo amathandizira ena kukhalabe oyera.
Thayo la Umwini
Awa ali ena a maprinsipulo a Baibulo amene Mary mwachiwonekere analingalira m’kupanga chosankha chaumwini. Nzeru inalamulira kuti iye sayenera kuchita zinthu mwamsanga, popanda kuyesa nkhaniyo mosamalitsa. Baibulo limapereka uphungu: “Usachitire mnzako umboni womtsutsa popanda chifukwa. Ndiyeno udzapusa ndi milomo yako.” (Miyambo 24:28, NW) Kuti mukhazikitse nkhani kotheratu, umboni wa chifupifupi mboni ziŵiri zowona ndi maso umafunikira. (Deuteronomo 19:15) Ngati Mary anawona kokha kutchulidwa kwachidule kwa kuchotsa mimba, iye angakhale analingalira mosamalitsa kuti chitsimikiziro cha kulakwa kulikonse chinali chosakwanira nkomwe kotero kuti iye sakanapitiriza. Pangakhale panali cholakwika mu kulemba kwa matenda, kapena mu njira ina yake zolemberazo zingakhale zinawunikira mkhalidwe wina wolakwika.
M’chochitika ichi, ngakhale kuli tero, Mary anali ndi chidziŵitso chinachake chodziŵika. Mwachitsanzo, iye anadziŵa mwaumwini kuti mlongoyo anali atapereka ndalama, mwachidziŵikire kudziŵitsa kuti iye anali atalandira utumiki wotchulidwawo. Ndiponso, iye anadziŵa kuti mlongoyo ali wosakwatiwa, chotero kudziŵitsa kuthekera kwa kuchita chigololo. Mary anamva chikhumbo chachikondi chakuthandiza wina yemwe angakhale atalakwa ndipo ndi kusunga chiyero cha gulu la Yehova, kukumbukira Miyambo 14:25: “Mboni yowona imalanditsa miyoyo, koma wolankhula zonama angonyenga.”
Mary mwanjira ina yake anali wodziŵa ponena za mbali za lamulo koma anadzimva kuti mu mkhalidwe umenewu maprinsipulo a Baibulo ayenera kutenga mphamvu yokulira kuposa zofunikira zomwe zimachirikiza chinsinsi cha zolembera za mankhwala. Motsimikizirika mlongoyo sakafuna kukhala wolapa ndi kuyesa kubwezera mwakupanga mavuto kaamba ka iye, iye analingalira. Chotero pamene Mary anabwereramo mu nsonga zonse zomwe zinalipo kwa iye, iye analingalira mosamalitsa kuti iyi inali nthaŵi ya “kulankhula,” osati “kutonthola.”
Tsopano Mary anayang’anizana ndi funso lowonjezereka: Kodi nkwadani kumene iye akalankhula, ndipo ndimotani mmene iye akachitira icho mochenjera? Iye akanatha kupita mwachindunji kwa akulu, koma iye analingalira choyamba kumufikira mlongoyo mwamseri. Kameneka kanali kafikiridwe kachikondi. Mary analingalira kuti uyu yemwe anali pansi pa kukaikiridwa angakhoze kulandira mwaŵi wa kumveketsa nkhaniyo kapena, ngati anali wolakwa, kutsimikizira kukaikiridwako. Ngati mlongoyo anali atalankhula kale kwa akulu ponena za nkhaniyo, mwachiwonekere iye akanena tero, ndipo Mary sakafunikira kupitiriza ndi nkhaniyo. Mary analingalira, ngati mlongoyo analembetsa kuti achotse mimba ndipo sanalape ku kulakwira lamulo la Mulungu kowopsya kumeneku, iye akamlimbikitsa iye kuchita tero. Kenaka akulu akamthandiza iye m’chigwirizano ndi Yakobo 5:13-20. Mwachimwemwe, mmenemo ndi mmene zinthu zinachitikira. Mary anapeza kuti mlongoyo anali atalembetsa kuti achotse mimba pansi pa chitsenderezo chokulira ndi chifukwa cha kukhala wofooka mwauzimu. Manyazi limodzi ndi mantha anampangitsa iye kubisa chimo lake, koma iye anali wachimwemwe kupeza thandizo kuchokera kwa akulu kulinga ku kuchira kwauzimu.
Ngati Mary anali atachita ripoti ku bungwe la akulu choyamba, iwo akanayang’anizidwa ndi chosankha chofananacho. Kodi ndimotani mmene iwo akanasamalirira chidziŵitso cha chinsinsi chobwera ku chisamaliro chawo? Iwo akanayenera kupanga chosankha chozikidwa pa zimene iwo anawona kuti Yehova ndi Mawu ake anafuna iwo kuchita monga abusa a gulu. Ngati ripoti linaphatikizapo Mkristu wobatizidwa yemwe anali kuyanjana mokangalika ndi mpingo, iwo akanayenera kuyesa chidziŵitsocho monga mmene anachitira Mary mu kugamulapo ngati iwo akafunikira kupitirizabe. Ngati iwo analingalira kuti panali kuthekera kwamphamvu kuti mkhalidwe wa “kuwola” unalimo mu mpingo, iwo akanasankha kugawira komiti ya chiweruzo kuwona m’nkhaniyo. (Agalatiya 5:9, 10) Ngati mmodzi amene anali pansi pa kukaikiridwayo anali, m’chenicheni, wochotsedwa kukhala chiwalo, wosapezeka pa msonkhano uliwonse kwanthaŵi ina ndipo wosadzizindikiritsa iyemwini monga mmodzi wa Mboni za Yehova, iwo akanasankha kulola nkhaniyo kudikira kufikira panthaŵi imene iye akayamba kudzizindikiritsa kachiŵirinso monga Mboni.
Kulingalira Zamtsogolo
Olemba ntchito ali ndi kuyenera kwa kuyembekezera kuti olembedwa ntchito awo Achikristu ‘adzasonyeza chikhulupiriro chonse chabwino,’ kuphatikizapo kusamalira malamulo awo pa kusunga chinsinsi. (Tito 2:9, 10) Ngati chilumbiro chatengedwa, sichiyenera kutengedwa mopepuka. Lumbiro limapangitsa lonjezo kukhala lamphamvu ndi lomangirira. (Masalmo 24:4) Ndipo kumene lamulo limalimbikitsa chifuno chakukhala osunga chinsinsi, nkhaniyo imakhala yovutirapo koposa. Chotero, Mkristu asanatenge chilumbiro kapena kudziika mwini pansi pa chitsenderezo cha kusunga chinsinsi, kaya m’chigwirizano ndi ntchito kapena mwinamwake, chikakhala chanzeru kulingalira ndi ku utali wotani wothekera kumene ichi chingabweretsere chifukwa cha kuwombana kuli konse kwa zofuna za Baibulo. Ndimotani mmene wina angasamalire nkhani pamene mbale kapena mlongo akhala kasitomala wake? Kaŵirikaŵiri ntchito zonga ngati kugwira ndi adokotala, m’chipatala, bwalo la milandu, ndi maloya uli mtundu wa ntchito mmene mavuto angabuke. Sitinganyalanyaze malamulo a Kaisara kapena kuwopsya kwa lumbiro, koma malamulo a Yehova ali okulira.
Kuyembekezera vuto, abale ena omwe ali maloya, madokotala, oŵerengera ndalama, ndi ena otero, akonzekera njira zothandizira mwakulemba ndipo afunsa abale omwe angawafikire kuŵerenga zimenezi asanavumbulutse chirichonse chachinsinsi. Chotero kumvetsetsa kuli kofunika pasadakhale kuti ngati cholakwa chowopsya chifikira kukudziŵidwa, wolakwayo angalimbikitsidwe kupita kukawonana ndi akulu mu mpingo wake ponena za nkhaniyo. Chidzamveketsedwa kuti ngati iye sanachite tero, phunguyo adzadzimva kukhala wathayo kupita kwa akuluwo iyemwini.
Pangakhale nthaŵi pamene mtumiki wokhulupirika wa Mulungu amafulumizidwa ndi zitsimikiziro zake zaumwini, zozikidwa pa chidziŵitso chake cha Mawu a Mulungu, kuvutika kapena ngakhale kunyalanyaza kufunika kwa kusunga chinsinsi chifukwa cha malamulo apamwamba a lamulo laumulungu. Kulimba mtima ndi kuchenjera kudzafunikira. Cholinga sichidzafunikira kukhala kuzonda pa ufulu wa wina koma kuthandiza olakwawo ndi kusunga mpingo Wachikristu kukhala woyera. Zolakwa zazing’ono chifukwa chauchimo ziyenera kunyalanyazidwa. Pano, “chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo,” ndipo tiyenera kukhululuka “nthaŵi makumi asanu ndi aŵiri kuchulukitsa zisanu ndi ziŵiri.” (Mateyu 18:21, 22) Iyi iri “nthaŵi yakutonthola.” Koma pamene pali kuyesera kwakubisa machimo a akulu, iyi ingakhale “nthaŵi yakulankhula.”
[Mawu a M’munsi]
a Mary ndi munthu woyerekezera molingana ndi mkhalidwe umene Akristu ena akumana nawo. Njira imene iye amachitira ndi mkhalidwe imaimira mmene ena agwiritsira ntchito maprinsipulo a Baibulo pa mikhalidwe yofananayo.
b Mu Commentary on the Old Testament, Keil ndi Delitzsch ananena kuti munthu angakhale wolakwa kapena kuchimwa ngati “anadziŵa upandu wa wina, kaya anawona iwo, kapena anafika kuchidziŵitso chinachake cha icho mwanjira ina yake, ndipo kuti chotero anali woyeneretsedwa kuwonekera pabwalo la mlandu monga mboni kaamba ka kutsimikizira upanduwo, ananyalanyaza kuchita tero, ndipo sananene chimene iye anawona kapena kudziŵa, pamene iye anamva chiweruzo chotheratu cha woweruza pa kufufuza kwapoyera kwa upanduwo, pa chimene anthu onse amene alipo, omwe anadziŵa chirichonse cha nkhaniyo, anafulumizidwa kubwera monga mboni.”
[Chithunzi patsamba 15]
Iri njira yolondola ndi yachikondi kulimbikitsa Mboni yolakwa kulankhula ndi akulu, kutsimikizira kuti iwo adzasamalira vutolo mu njira yachifundo ndi momvetsetsa