“Pita ku Nyerere”
“PITA kunyerere, wolesi iwe,” analemba tero Mfumu Solomo, ‘penya njira zawo nuchenjere.’ Kodi nchiyani chimene munthu waulesi—kapena munthu aliyense kunena kwake titero—angaphunzire ku nyerere? Solomo anapitiriza kuti: ‘Ziribe mfumu, ngakhale kapitao, ngakhale mkulu; koma zitengeratu zakudya zawo m’malimwe.’—Miyambo 6:6-8.
Mwachiwonekere mfumu yanzeruyo inkalozera ku nyerere yotuta. Mu Israyeli, monga mmene zinakhalira m’malo ena, sichachilendo kuwona nyerere yotuta ikumadzandiradzandira, itanyamula mbewu zazikulu pafupifupi mofanana nayo. (Onani pamwamba chakumanzere.) Iyo imapereka zakudya zosonkhanitsidwa ku nkhokwe ya kunsi kwa nthaka.
Pokhala kunsi kwa nthaka, “nkhokweyo” ingakhale yachinyontho m’nyengo ya mvula, ndipo mbewuzo zidzaphuka kapena kukhala ndi nkhungu ngati sizinasamaliridwe. Chotero nyerere ziri ndi ntchito yowonjezereka. Mwamsanga dzuŵa litatuluka, nyerere zogwira ntchito zimanyamula mbewuzo kunka nazo panja kuti ziume ndi mphepo. (Onani pamwamba.) Ndipo dzuŵa lisanaloŵe, nyererezo zimafunikira kunyamula mbewu zonsezo ndikuzibweza. Nyerere zina nzosamalira kwenikweni kwakuti zimadula mbali yophukirayo ya mbewuzo mwamsanga zitasonkhanitsidwa kapena pamene ziyamba kuphukira.
Ntchito ya nyerere simathera pa kukonzekera zakudya. Izo zirinso ndi ntchito yosamalira zachichepere. Mazira ayenera kuikidwa m’magulumagulu. Mbozi zochokera m’mazira ofungatiridwa ziyenera kudyetsedwa. Ana aang’ono ayenera kusamaliridwa. Nyerere zina zimasamalira ntchito ya mpweya. Kutatentha mkati mwa tsiku, izo zimapititsa ana aang’onowo kunsi kwenikweni ku zisa zawo. Pamene kuzizira kwamadzulo kuyandikira, izo zimabweretsanso ana aang’onowo pamwamba. Ntchito yambiridi, kodi sitero?
Pamene banjalo likula, zipinda zatsopano ziyenera kumangidwa. Nyerere zogwira ntchito zimagwiritsira ntchito nsagwada zawo kukumba ndi kutulutsa dothi kunja. Kaŵirikaŵiri izo zimachita ichi pambuyo pa mvula pamene nthakayo idakali yofeŵa. Izo zimawumbanso nthakayo kukhala “njerwa” kaamba ka maprojekiti awo omanga—kumanga makoma ndi madenga a migodi yawo yakunsiko ndi zipinda.
Nyerere zimachita zonsezi ‘popanda mfumu, kapitao kapena mkulu.’ Bwanji ponena za mfumukazi? Iye samalamulira. Iye amangoikira mazira ndipo ndi mfumukazi m’lingaliro lakuti ndiye nakubala wa banjalo. (Onani pamwambapo.) Ngakhale popanda woyang’anira wozifufuza kapena mkulu wozikhamanitsa, nyerere zimagwirabe ntchito mosatopa. Nyerere imodzi inawonedwa ikugwira ntchito kuyambira pa 6 koloko m’mawa kufikira 10 koloko usiku!
Kodi mungaphunzire phunziro mwakupenyetsetsa nyerere? Kodi mumagwira ntchito zolimba ndi kukalamira kuwongolera ntchito yanu kaya mukuyang’aniridwa kapena ayi? (Miyambo 22:29) Inu mudzafupidwa m’kupita kwa nthaŵi ngakhale ngati bwana wanuyo sakukuwonani. Inu mungasangalale ndi chikumbumtima chabwino ndi chikhutiro chaumwini. Monga mmene Solomo ananenera kuti: “Tulo ta munthu wogwira [ntchito] ntabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri.”—Mlaliki 5:12.
Izi sizokhazo zimene tingaphunzire ku nyerere. Nyerere zimagwira ntchito zolimba mwachibadwa. Kwenikweni, nyerere zina zimawonedwa zikutsatira mwakhungu nkukuluzi umene zinazo zinazisiya m’mbuyo. Zimangothera zikuthamangathamanga, kuyenda mozungulirazungulira, kufikira zitagwa ndi kufa.
Kodi nthaŵi zina mumalingalira kuti mukuthamangathamanga, mukumakhala wotanganitsidwa nthaŵi zonse ndi kutopa komatu osaphula kanthu? Ngati nditero, iyi ndiyo nthaŵi yosanthula chifuno cha ntchito yanu yolimba ndikuwona phindu lenileni la zonulirapo zanu. Kumbukirani uphungu uwu wa Mfumu Solomo yanzeru: ‘Opa Mulungu, nusunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.’—Mlaliki 12:13.