Kodi ‘Nkupitiranji kwa Nyerere’?
SOLOMO, mfumu yanzeru ya Israyeli wakale analangiza kuti: “Pita kunyerere.” Kodi ananeneranji zimenezi? Kodi tingaphunzirenji kwa nyerere?
Solomo anawonjezera kuti: “Penya [nyerere] njira zawo nuchenjere; zilibe mfumu, ngakhale kapitao, ngakhale mkulu; koma zitengeratu zakudya zawo m’malimwe; nizituta dzinthu zawo m’masika.” (Miyambo 6:6-8) Mawu akalekale amenewo amasonyeza zowona zopezedwa ndi akatswiri a chibadwa cha zinthu.
Katswiri wa miyambi Aguri amasonyeza kuti nyerere “zipambana kukhala zanzeru.” (Miyambo 30:24, 25) Ndithudi, nzeru yawo simachokera m’kulingalira kwaluntha koma m’mphamvu zachibadwa zimene Mlengi wazipatsa. Mwachitsanzo, chifukwa cha chibadwa, nyerere zimatuta chakudya chake panthaŵi yoyenera.
Nyerere nzolinganizika modabwitsa. Pokhala zogwirizana kwambiri ndi zosamala nyerere zinzawo zogwira nazo ntchito, zimanyamula nyerere zovulala kapena zotopa kumka nazo kuchisa. Mwachibadwa, zimakonzekera mtsogolo ndi kuchita chilichonse chothekera kuti zikwaniritse mathayo awo.
Njira ya kachitidwe ka zinthu ya nyerere imasonyeza kuti anthu ayenera kukonzekera mtsogolo mwawo pasadakhale ndi kukhala ogwira ntchito zolimba. Zimenezi zimagwira ntchito kusukulu, kuntchito, ndi m’ntchito zauzimu. Monga momwe nyerere zimapindulira ndi khama lake, choteronso Mulungu amafuna kuti anthu ‘awone zabwino m’ntchito zawo zonse.’ (Mlaliki 3:13, 22; 5:18) Mofanana ndi nyerere zokangalika, Akristu owona amachita ntchito yabwino ya tsiku. Iwo ‘amachita ndi mphamvu yawo chilichonse dzanja lawo lipeza,’ osati chifukwa chakuti kapitao akuyang’anira, koma chifukwa cha kuwona mtima ndi chikhumbo cha kukhala antchito akhama ndi opindulitsa.—Mlaliki 9:10; yerekezerani ndi Miyambo 6:9-11; onaninso Tito 2:9, 10.
Tidzakhaladi achimwemwe, ngati ‘tipita kwa nyerere’ ndi kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira kwa izo. Ndipo tidzakhala ndi chimwemwe chachikulu koposa ngati tichita chifuniro cha Yehova Mulungu mwakhama, monga momwe Baibulo limasonyezera.