Pezani Nzeru Ndipo Landirani Mwambo
YEHOVA MULUNGU ndi Mlangizi Wamkulu wa anthu ake. Amawaphunzitsa za iye komanso za moyo. (Yesaya 30:20; 54:13; Salmo 27:11) Mwachitsanzo, Yehova anapatsa mtundu wa Israyeli, aneneri, Alevi—makamaka ansembe—ndi amuna ena anzeru kuti akhale aphunzitsi. (2 Mbiri 35:3; Yeremiya 18:18) Aneneri ankaphunzitsa anthu za chifuno cha Mulungu ndi makhalidwe ake ndiponso analongosolera iwo choyenera kuchita kuti apulumuke. Ansembe ndi Aleviwo anali ndi udindo wophunzitsa Chilamulo cha Yehova. Ndipo amuna anzeru, kapena akulu, ankapereka uphungu woyenera pa kakhalidwe kawo ka tsiku ndi tsiku.
Solomo, mwana wa Davide, anali wanzeru zochuluka mwa amuna onse a m’Israyeli. (1 Mafumu 4:30, 31) Ataona ulemerero ndi chuma chake, mmodzi wa alendo ake odziŵika bwino, mfumukazi ya ku Seba, inachitira umboni kuti: “Anangondiuza dera lina lokha. Nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.” (1 Mafumu 10:7) N’chiyani chomwe chinali chinsinsi cha nzeru za Solomo? Pamene anakhala mfumu ya Israyeli mu 1037 B.C.E., Solomo anapempha “nzeru ndi chidziŵitso.” Yehova anakhutira ndi pempho lakelo, ndipo anam’patsa chidziŵitso, nzeru, ndi mtima wozindikira. (2 Mbiri 1:10-12; 1 Mafumu 3:12) N’zosadabwitsa kuti Solomo “ananena miyambi zikwi zitatu”! (1 Mafumu 4:32) Ina mwa imeneyi, limodzinso ndi “mawu a Aguli” ndi a “Mfumu Lemueli,” analembedwa m’Buku la Baibulo la Miyambo. (Miyambo 30:1; 31:1) Choonadi chonenedwa m’miyambi imeneyi chimasonyeza nzeru ya Mulungu ndipo n’njamuyaya. (1 Mafumu 10:23, 24) Miyambi imeneyi ili yofunika kwambiri kwa amene akufuna moyo wachimwemwe ndi wachipambano lerolino, monga mmene inalili panthaŵi imene imalankhulidwa.
Chipambano, ndi Chiyero cha Makhalidwe—Motani?
Mawu oyamba a buku la Miyambo, afotokoza cholinga chenicheni cha bukuli: “Miyambo ya Solomo mwana wa Davide, mfumu ya Israyeli. Kudziŵa nzeru ndi mwambo; kuzindikira mawu ozindikiritsa; kulandira mwambo wakusamalira machitidwe, chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika; kuchenjeza achibwana, kuphunzitsa mnyamata kudziŵa ndi kulingalira.”—Miyambo 1:1-4.
Cholinga cha “miyambo ya Solomo” n’chapamwamba zedi! N’njawofuna “kudziŵa nzeru ndi mwambo.” Nzeru zimaphatikizamo kuona zinthu mmene zilili ndi kugwiritsa ntchito chidziŵitso pothetsa mavuto, kukwanitsa zolinga, kupewa ngozi, kapenanso kuthandiza ena kuchita zimenezi. Buku lina la maumboni linati: “M’buku la Miyambo,” “‘nzeru’ zimasonyeza mmene mungakhalire ndi moyo wapamwamba—kukhoza kusankha mwanzeru ndi kukhala ndi moyo wopambana.” Kupeza nzeru n’kofunika zedi!—Miyambo 4:7.
Miyambo ya Solomo imatipatsanso mwambo. Kodi maphunziro ameneŵa n’ngofunika kwa ife? M’Malemba liwu lakuti mwambo limapereka lingaliro loongolera, kudzudzula, ngakhale kulanga. Katswiri wina wa Baibulo anati, “limatanthauza kuphunzira chikhalidwe chabwino chachibadwa, chokhudza kuwongolera mchitidwe wa munthu womwe ungam’tsogolere kuchita kapena kuganiza mopusa.” Mwambo wodzipatsa tokha, kapena wotipatsa ena, umatithandiza osati kupewa tchimo kokha, komanso umatisonkhezera kusintha kuti tikhale ndi makhalidwe abwino. Inde, mwambo n’ngwofunika kwa ife ngati tikufuna kukhalabe oyera mwa makhalidwe.
Choncho cholinga cha miyambo chili ndi mbali ziŵiri—kuzindikiritsa nzeru ndi kupereka mwambo. Mwambo wophunzitsa chikhalidwe ndi luso la kulingalira bwino zili ndi mbali zochuluka. Mwachitsanzo, chilungamo ndi khalidwe labwino ndipo chimatithandiza kutsatira miyezo yapamwamba ya Yehova.
Nzeru imaphatikiza mbali zambiri monga kumvetsa, chidziŵitso, kuchenjera, ndi luso la kulingalira. Kumvetsa ndiko kukhoza kuona chimene nkhaniyo ikutanthauza ndi kuzindikira nkhani yonseyo mwa kumvetsa kugwirizana kwa mbali zake zonse ndi mutu wa nkhaniyo, potero mukumamvetsa tanthauzo lake. Chidziŵitso chimafuna kudziŵa ndi kumvetsa chifukwa chake kuchita zinthu zina zake n’kwabwino kapena ayi. Mwachitsanzo, munthu womvetsa angazindikire pamene winawake akufuna kulakwa, ndipo nthaŵi yomweyo angam’chenjeze za kuwopsa kwa chomwe akufuna kuchitacho. Koma adzafunikira chidziŵitso kuti azindikire chifukwa chake munthu ameneyo akuchitira zimenezo kuti athe kupeza njira yabwino yom’pulumutsira.
Anthu ochenjera amakhalanso anzeru—samanyengeka msanga. (Miyambo 14:15) Amatha kuona zovuta za m’tsogolo ndi kuzikonzekera. Ndipo nzeru zimatitheketsa kulingalira bwino ndipo timapanga mfundo zothandiza m’moyo. Kuphunzira miyambo ya m’Baibulo n’kopindulitsadi chifukwa inalembedwa kuti tidziŵe nzeru ndi mwambo. Ngakhale “wachibwana” amene angamvetsere miyambo adzakhala wochenjera, ndipo “wamng’ono,” adzapeza chidziŵitso ndi luso la kulingalira.
Miyambo Ndi ya Anzerunso
Komabe miyambo ya m’Baibulo si ya achibwana ndi ana okha. Ndi ya anzeru onse ofuna kumvera. Mfumu Solomo inati: “Wanzeru amve, nawonjezere kuphunzira, ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu, kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lake, mawu a anzeru ndi zophiphiritsa zawo.” (Miyambo 1:5, 6) Munthu amene anazindikira kale nzeru, adzawonjezera kuphunzira mwa kukhala womvetsera kwambiri miyambi, ndipo munthu wozindikira adzanola luntha lake ndi kupanga moyo kukhala wopambana.
Nthaŵi zonse mwambi umalongosola nzeru yeniyeni yakuya m’mawu ochepa kwambiri. Miyambi ya m’Baibulo nthaŵi zina ingakhale yokuluwika. (Miyambo 1:17-19) Miyambo ina imakhala mawu ophiphiritsa—yokuluwika ndi yovuta kumva imene ingafune kumasulira kuti mudziŵe tanthauzo lake. Mwambi ungakhalenso ndi ntchedzero, mafanizo, ndi mawu ena okuluwika. Kuti umvetsetse zimenezi pamafunika nthaŵi yokwanira ndi kusinkhasinkha. Solomo, yemwe analemba miyambi yambiri, mwachionekere anali wokhoza kuzindikira bwino tanthauzo la mwambi. M’buku la Miyambo, anayesetsa kutheketsa oŵerenga kukhala ozindikira tanthauzo la mwambi monga mmene iye analiri, chinachake chimene munthu wanzeru angafune kukhala wochimvetsera kwambiri.
Chiyambi Chotsogolera ku Cholinga
Kodi n’kuti kumene munthu angayambire kufunako nzeru ndi mwambo? Solomo akuyankha kuti: “Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziŵa. Opusa anyoza nzeru ndi mwambo.” (Miyambo 1:7) Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha chidziŵitso. Popanda chidziŵitso sipangakhale nzeru kapena mwambo. Choncho kuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru ndi mwambo.—Miyambo 9:10; 15:33.
Kuopa Mulungu sikutanthauza mantha achinthenthe. M’malomwake kumatanthauza kum’patsa ulemu waukulu. Popanda mantha ameneŵa, sipangakhale chidziŵitso chenicheni. Moyo n’ngwochokera kwa Yehova Mulungu, ndipo moyowu n’ngwofunikadi kuti tikhale ndi chidziŵitso. (Salmo 36:9; Machitidwe 17:25, 28) Kuwonjezera pamenepo, Mulungu analenga zinthu zonse; choncho chidziŵitso chonse cha anthu n’chozikidwa pa ntchito za manja ake. (Salmo19:1, 2; Chivumbulutso 4:11) Mulungu anauziranso Mawu ake olembedwawo, omwe ‘amapindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.’ (2 Timoteo 3:16, 17) Choncho, wofunika kwambiri pa chidziŵitso choona ndi Yehova, ndipo munthu amene akufuna chidziŵitso ayenera kumuwopa.
Kodi chidziŵitso cha anthu ndi nzeru za dziko, zingakhale ndi phindu lanji popanda kuopa Mulungu? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Alikuti wanzeru? Mlembi alikuti? Alikuti wotsutsana wa nthaŵi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitsa nzeru ya dziko lapansi?” (1 Akorinto 1:20) Posoŵa mantha a umulungu, anthu anzeru zadziko, amagamula molakwa pa mfundo zodziŵika bwino ndipo mapeto ake amangokhala ‘zitsiru.’
“Mkanda Pakhosi Pako”
Mfumu yanzeru imeneyi ikulangizanso achinyamata kuti: “Mwananga, tamvera mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amako. Pakuti izi ndi korona wa chisomo pam’tu pako, ndi mkanda pakhosi pako.”—Miyambo 1:8, 9.
Mu Israyeli wakale, Mulungu anapereka udindo wophunzitsa ana kwa makolo. Mose analangiza atate kuti: “Ndipo mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:6, 7) Amayi nawonso ankachita zofunika zedi. Pansi pa ulamuliro wa mwamuna wake, mkazi wachihebri ankalimbikitsa malamulo a m’banja.
Monga mmene Baibulo lonseli likusonyezera, m’banja ndi mmene munthu amaphunziramo zambiri. (Aefeso 6:1-3) Ngati ana akumvera makolo awo okhulupirira, ndiye kuti akudzikongoletsa ndi korona wokongola ndi mkanda waulemu.
“Chilanda Moyo wa Eni Ake”
Mmwenye wina yemwe anatumiza mwana wake wamwamuna wa zaka 16 kukapitiriza maphunziro ku United States, anapereka malangizo kwa mwana wakeyo kuti akapewe kuyanjana ndi anthu oipa. Malangizo ameneŵa n’ngofanana ndi chenjezo la Solomo lakuti: “Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.” (Miyambo 1:10) Pano Solomo akusonyeza nyambo imene amagwiritsa ntchito kuti anyengerere anthu: “Idza nafe, tibisalire mwazi, tilalire osachimwa opanda chifukwa; tiwameze ali ndi moyo ngati manda, ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje, tidzapeza chuma chonse chamtengo wake, tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha, udzachita nafe maere, tonse tidzakhala ndi chibeti chimodzi.”—Miyambo 1:11-14.
Mwachionekere, chuma chochuluka ndicho nyambo. Pofuna kupeza phindu mofulumira, “ochimwa” amakopa ena kuwapangitsa kuchitira anthu upandu kapena zonyansa. Anthu oipa amenewa, samaopa kukhetsa mwazi ndi cholinga chongofuna kupeza chuma. ‘Amawameza ali amoyo ngati manda, ali amphumphu,’ kuwalanda zawo zonse anali nazo, monga mmene manda amalandirira thupi lonse. Amaitanira ena ku ntchito ya upandu—amangofuna “kudzaza nyumba zawo ndi zofunkha,’ ndipo amafuna achibwana kuti ‘achite nawo maere.’ Chenjezo ili labweradi panthaŵi yake kwa ife! Kodi magulu a achinyamata aupandu ndi ogulitsa mankhwala ozunguza bongo, samagwiritsa ntchito njira zomwezo pokopa ena? Kodi lonjezo lopeza chuma mwansangalo, silingakhale chiyeso kwa amene akufuna kuyamba bizinesi?
Mfumu yanzeru ikutilangiza kuti: “Mwananga, usayende nawo m’njira; letsa phazi lako ku mayendedwe awo; pakuti mapazi awo athamangira zoipa, afulumira kukhetsa mwazi.” Poneneratu za mapeto ake oopsawo, iye anapitiriza ndi kuti: “Pakuti kutchera msampha pamaso pa mbalame ndi chabe, ndipo awa abisalira mwazi wawowawo, alalira miyoyo yawoyawo. Mayendedwe a yense wopindula chuma monyenga n’ngotere; chilanda moyo wa eni ake.”—Miyambo 1:15-19.
“Yense wopindula chuma monyenga” adzawonongedwa m’njira yake yomwe. Misampha yomwe anthu oipawo amatcherera anthu ena, adzakodwa nayo eni okha. Kodi ochita zoipa mwadala adzasiya njira zawo? Ayi. Msampha ungakhale poonekera, koma mbalame—zolengedwa za mapiko—zimaulukirabe m’msamphawo. Chimodzimodzinso oipa, achititsidwa khungu ndi umbombo wawo, ndipo amangopitirizabe kuchita zaupandu, komabe posakhalitsa adzagwidwa.
Adzamvetsera Mawu Anzeru Ndani?
Kodi ochimwa ameneŵa amadziŵadi kuti njira zawozo n’zovulaza? Kodi achenjezedwa za zotsatira za zochita zawozo? Kusadziwa sikuli chodzikhululukira nacho, chifukwa uthenga ndiye ukulengezedwa konse kumene kumapezeka anthu.
Solomo anati: “Nzeru ifuula panja; imveketsa mawu ake pabwalo; iitana posonkhana anthu poloŵera pachipata; m’mudzi inena mawu ake.” (Miyambo 1:20, 21) Nzeru ikufuula momveka bwino zedi, kuti aliyense amene ali pabwalo amve. Mu Israyeli wakale amuna achikulire ankapereka uphungu wanzeru ndi kupereka zigamulo zachiweruzo m’zipata za mizinda. Kwa ife lerolino, Yehova wapangitsa nzeru yeniyeni kulembedwa m’Mawu ake, Baibulo, lomwe lili lofala tsopano. Ndipo atumiki ake ali otanganidwa ndi kufalitsa uthenga wake ponseponse. Ndithudi Mulungu wafalitsa nzeru zake kwa onse.
Kodi nzeru yoona imati chiyani? Ndi iyi: “Kodi mudzakonda zachibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, . . . ? ndaitana, ndipo munakana; ndatambasula dzanja langa, ndipo panalibe analabadira.” Opusa samvera mawu anzeru. Ndipo pambuyo pake, “adzadya zipatso za mayendedwe awo . . . kubwerera m’mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwayi za opusa zidzawawononga.”—Miyambo 1:22-32.
Nanga bwanji kwa amene amvetsera mawu anzeru amenewa? “Adzakhala osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.” (Miyambo 1:33) Khalani m’gulu la amene anapeza nzeru ndi kulandira mwambo mwa kumvetsera miyambi ya m’Baibulo.
[Chithunzi patsamba 15]
Nzeru yeniyeni n’njofala ponseponse