-
“Sunga Malangizo Anga, Nukhale ndi Moyo”Nsanja ya Olonda—2000 | November 15
-
-
“Tiye tikondwere ndi chikondano mpaka mamaŵa,” iye akupitiriza motero, “tidzisangalatse ndi chiyanjano,” [“tisangalatsane ndi chikondi,” NW]. Akumuitanira zinazake osati chakudya chokoma chokha cha anthu aŵiri. Akum’lonjeza kukasangalala mwa kugonana. Kwa mnyamatayu, pempholitu n’lochititsa chidwi ndi losangalatsa! Popitiriza kum’nyengerera, akunena kuti: “Pakuti mwamuna kulibe kwathu, wapita ulendo wa kutali; watenga thumba la ndalama m’dzanja lake, tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.” (Miyambo 7:18-20) Akum’tsimikizira kuti palibe aliyense adzawapezerera, chifukwa chakuti mwamuna wake wachoka wapita kukachita bizinesi ndipo akakhala kumeneko kwakanthaŵi ndithu asanabwerere kunyumba. N’katswiridi pokopa mnyamata ndi mawu onyengerera! “Am’kakamiza ndi kukoka kwa mawu ake, am’patutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake.” (Miyambo 7:21) Munthu wanzeru ndi wakhalidwe labwino ngati Yosefe, ndi yekhayo angathe kupeŵa mawu onyengerera ngati ameneŵa. (Genesis 39:9, 12) Kodi mnyamata uyu angathe kupeŵa mkhalidwewu?
-
-
“Sunga Malangizo Anga, Nukhale ndi Moyo”Nsanja ya Olonda—2000 | November 15
-
-
“Mkazi wachiwerewere” yemwe mfumu inamuona anakopa mnyamata mochenjera mwa kumuitana kuti “asangalatsane ndi chikondi.” Kodi achinyamata ambiri—makamaka atsikana—sakukakamizidwa kuchita zosayenera m’njira ngati imeneyi? Koma taganizani: Pamene winawake ayesa kukukopani kuti mugone naye, kodi chimakhaladi chikondi chenicheni kapena amangofuna kukhutiritsa chilakolako chake chadyeracho? Kodi mwamuna yemwe amakondadi mkazi angam’kakamizirenji kuchita zosemphana ndi miyezo yachikristu ndi chikumbumtima chake? “Mtima wako usapatukire ku njira” zimenezo, akuchenjeza motero Solomo.
-