‘Ndi Nzeru Masiku Athu Adzachuluka’
NDANI angakane kuti nzeru n’njofunika kwambiri pothetsa mavuto m’moyo? Nzeru yeniyeni ndiyo kugwiritsa ntchito moyenera zomwe tadziŵa ndi kuzindikira. Wopanda nzeru amati ndi chitsiru, wopusa, kapena kuti chidzete. Choncho, Malemba akutilimbikitsa kuti tipeze nzeru. (Miyambo 4:7) Buku la m’Baibulo la Miyambo linalembedwa makamaka kuti litipatse nzeru ndi mwambo. Mawu oyambirira a bukuli amati: “Miyambo ya Solomo mwana wa Davide, mfumu ya Israyeli. Kudziŵa nzeru ndi mwambo; kuzindikira mawu ozindikiritsa.”—Miyambo 1:1, 2.
Tangoganizirani ziphunzitso zomveka bwino ndi zodalirika m’machaputala ochepa oyambirira a Miyambo. Monga atate wachikondi polangiza mwana wake, Solomo akulimbikitsa oŵerenga ake kulandira mwambo ndi kumvetsera nzeru. (Chaputala 1 ndi 2) Akutilangiza mmene tingakulitsire ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi mmene tingatetezere mtima wathu. (Chaputala 3 ndi 4) Akutilimbikitsa kukhalabe ndi makhalidwe abwino. (Chaputala 5 ndi 6) Inde, n’kofunika kwambiri kudziŵa njira zomwe munthu wakhalidwe loipa amagwiritsa ntchito. (Chaputala 7) Ndipotu pempho lomwe nzeru yotchulidwa ngati munthu imeneyi ikupempha aliyense n’lochititsa chidwi. (Chaputala 8) Asanapitirize ndi miyambo yomveka bwino m’machaputala a m’tsogolo, Mfumu Solomo akumaliza zimene walemba kale ndi mawu ochititsa chidwi.—Chaputala 9.
‘Idzani, Mudye Chakudya Changa Nimumwe Vinyo Wanga’
Mawu omaliza a chigawo choyamba cha buku la Miyambo si chidule wamba cha malangizo omwe atchulidwa kale ayi. Koma ndi fanizo losangalatsa ndi logwira mtima, losonkhezera oŵerenga kufunafuna nzeru.
Chaputala 9 cha buku la m’Baibulo la Miyambo chikuyamba ndi mawu akuti: “Nzeru yamanga nyumba yake, yasema zoimiritsa zake zisanu ndi ziŵiri.” (Miyambo 9:1) Wophunzira wina anati, mawu akuti “zoimiritsa zisanu ndi ziŵiri akusonyeza nyumba yaikulu yomangidwa pafupi ndi bwalo. Nyumba ya nsanamira zitatu mbali iliyonse, ndi nsanamira imodzi pakatikati pa mbali yachitatu yoyang’anizana ndi bwalo lomwe lili kumaso kwake.” Kaya izi n’zoona kapena ayi, nzeru yeniyeni yamanga nyumba yolimba yolandirira alendo ambiri.
Chakudya chakonzedwa kale m’nyumbayi. Nyama ndi vinyo zilipo. Nzeru ndiyo yakonza chakudyacho ndi kuchiika patebulo. “Yaphera nyama yake, nisanganiza vinyo wake, nilongosolanso pa gome lake.” (Miyambo 9:2) Tebulo lophiphiritsa limeneli liyenera kukhala ndi chakudya chauzimu chofunika kuchiganizira mosamala.—Yesaya 55:1, 2.
Kodi ndani akuitanidwa ku phwando lomwe nzeru yeniyeni yakonza? “Yatuma anamwali ake, iitana pa misanje ya m’mudzi. Wachibwana yense apambukire kuno; iti kwa yense wosowa nzeru, tiyeni, idyani chakudya changa; nimumwe vinyo wanga ndam’sanganiza. Lekani, achibwana inu, nimukhale ndi moyo; nimuyende m’njira ya nzeru.”—Miyambo 9:3-6.
Nzeru yatuma adzakazi ake kukaitana anthu. Adzakaziwa akupita kumalo opezeka anthu ambiri kuti akaitane ochuluka. Onse “osoŵa nzeru” kapena osazindikira, komanso achibwana akuitanidwa. (Miyambo 9:4) Ndipo akuwalonjeza moyo. Ndithudi, pafupifupi aliyense angapeze nzeru ya m’Mawu a Mulungu, kuphatikizapo ya m’buku la Miyambo. Masiku ano, monga amithenga a nzeru yeniyeni, Mboni za Yehova n’zotanganidwa kuitana anthu, kulikonse komwe angapezeke kuti aphunzire Baibulo. Ndithudi, kuliphunzira kungatitsogolere ku moyo wosatha.—Yohane 17:3.
Akristu ayenera kulandira modzichepetsa mwambo womwe nzeru ikupereka. Izi n’zofunika makamaka kwa achinyamata ndi omwe angoyamba kumene kuphunzira za Yehova. Chifukwa chosadziŵa zambiri pa njira za Mulungu angakhale “osoŵa nzeru.” Si kuti maganizo awo onse amakhala oipa, koma kuti zimatenga nthaŵi ndi khama kupangitsa mtima kukhala wokondweretsadi Yehova Mulungu. Izi zimafuna kugwirizanitsa maganizo, zikhumbo, ndi zolinga zawo ndi zimene Mulungu amavomereza. N’kofunikatu kwambiri kuti ‘akulitse chilakolako cha mkaka wosasukuluka wa mawu.’—1 Petro 2:2.
Koma kodi tonsefe sitiyenera kuphunzira zoposa “mawu a chiyambidwe”? Ndithudi, tiyenera kukulitsa chidwi pa “zakuya za Mulungu” ndi kudya chakudya chotafuna cha anthu aakulu msinkhu. (Ahebri 5:12–6:1; 1 Akorinto 2:10) “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” amene Yesu Kristu akumuyang’anira, ndi wotanganidwa kupereka chakudya chauzimu kwa aliyense panthaŵi yoyenera. (Mateyu 24:45-47) Tiyenitu tidye pa tebulo la nzeru mwa kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndi zofalitsa zofotokoza Baibulo zomwe gulu la kapolo lapereka.
“Usadzudzule Wonyoza”
Kulangiza ndi kudzudzula, ndi zina mwa zomwe nzeru imaphunzitsa. Si onse omwe amakondwera ndi mbali imeneyi ya nzeru. N’chifukwa chake mawu omaliza a chigawo choyamba cha buku la Miyambo ali ndi chenjezo ili: “Woweruza munthu wonyoza adzichititsa yekha manyazi; yemwe adzudzula wochimwa angodetsa mbiri yake. Usadzudzule wonyoza kuti angakude; dzudzula wanzeru adzakukonda.”—Miyambo 9:7, 8a.
Wonyoza amasungira udani amene akuyesa kum’thandiza kuwongolera njira zake. Munthu woipa sadziŵa kufunika kwa kudzudzulidwa. N’kupandatu nzeru kuyesa kuphunzitsa choonadi chogwira mtima cha Mawu a Mulungu munthu yemwe amadana ndi choonadi kapena wongofuna kuchinyoza! Pamene mtumwi Paulo anali kulalikira ku Antiokeya, anakumana ndi gulu la Ayuda osakonda choonadi. Anayesa kukangana naye mwa kum’tsutsa motonza. Koma Paulo anangoti: “Popeza muwakankha [Mawu a Mulungu], nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.”—Machitidwe 13:45, 46.
Poyesetsa kufikira anthu oona mtima ndi uthenga wabwino wa Ufumu, tiyeni tikhale osamala kuti tisayambe kutsutsana ndi kukangana ndi onyoza. Kristu Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “Ndipo poloŵa m’nyumba muwalankhule. Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mawu anu, pamene mulikutuluka m’nyumbayo, kapena m’mudzimo, sansani fumbi m’mapazi anu.”—Mateyu 10:12-14.
Munthu wanzeru amaona kudzudzulidwa mosiyana ndi mmene wonyoza amakuonera. Solomo anati: “Dzudzula wanzeru adzakukonda. Ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake.” (Miyambo 9:8b, 9a) Munthu wanzeru amadziŵa kuti “chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwe[re]tsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.” (Ahebri 12:11) Ngakhale uphungu ukhale wopweteka, kodi pali chifukwa chochitira ukali kapena kuukana ngati kuulandira kudzatiwonjezera nzeru?
“Ukaphunzitsa wolungama adzawonjezera kuphunzira,” ikupitiriza motero mfumu yanzeru. (Miyambo 9:9b) Aliyense ayenera kupitiriza kuphunzira kaya wanzeru kwambiri kapena wokalamba kwambiri. N’zosangalatsa kwambiritu kuona ngakhale okalamba akulandira choonadi ndi kudzipatulira kwa Yehova! Nafenso tiyeni tiyesetse kukhalabe ndi mtima wofuna kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito ubongo wathu.
“Zaka za Moyo Wako Zidzawonjezedwa”
Potsindika mfundo yaikulu ya nkhaniyi, Solomo akutchula chinthu chofunika kuti tipeze nzeru. Iye analemba kuti: “Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova; kudziŵa Woyerayo ndiko luntha.” (Miyambo 9:10) Sitingapeze nzeru yaumulungu popanda kuopa ndi kulemekeza Mulungu woona. Munthu akhoza kudziŵa zambiri, koma ngati saopa Yehova, adzalephera kugwiritsa ntchito zomwe akudziŵazo kulemekeza Mlengi. Akhoza kuganiza molakwa pa zinthu zodziŵika bwino, kudzipangitsa kuoneka wopusa. Komanso, kudziŵa Yehova Woyerayo, n’kofunika kwambiri kuti tipeze mbali yodziŵika bwino ya kukhala wanzeru yomwe ndi kuzindikira.
Kodi nzeru imabala zipatso zotani? (Miyambo 8:12-21, 35) Mfumu ya Aisrayeli ikuti: “Mwa ine masiku ako adzachuluka, zaka za moyo wako zidzawonjezedwa.” (Miyambo 9:11) Masiku ndi zaka zambiri za moyo ndizo zotsatira za kukhala ndi nzeru. Inde, “nzeru isunga moyo wa eni ake.”—Mlaliki 7:12.
Ndi udindo wa aliyense kuyesetsa kupeza nzeru. Ponenetsa mfundo imeneyi, Solomo anati: “Ukakhala wanzeru, si yakoyako nzeruyo? Ndipo ukanyoza udzasauka wekha.” (Miyambo 9:12) Munthu wanzeru amapindula nayo yekha, koma wonyoza adzavutika yekha. Ndithudi, timakolola zomwe tinafesa. Tsono tiyenitu ‘titchere makutu athu ku nzeru.’—Miyambo 2:2.
“Mkazi Wautsiru N’ngolongolola”
Posiyanitsa, kenako Solomo akuti: ‘Mkazi wautsiru amalongolola, n’ngwa chibwana wosadziŵa kanthu. Akhala pakhomo la nyumba yake, pampando pa misanje ya m’mudzi, kuti aitane akupita panjira, amene angonkabe m’kuyenda kwawo, Wachibwana ndani? Apambukire kuno.’—Miyambo 9:13-16a.
Utsiru ukufotokozedwa monga mkazi wolongolola, wopanda khalidwe, ndi wopusa. Nayenso wamanga nyumba. Ndipo wadzipatsa ntchito yoitana aliyense wosazindikira. Choncho odutsa m’njira ali ndi ufulu wosankha. Kodi avomera kuitana kwa nzeru kapena kwa utsiru?
“Madzi Akuba Atsekemera”
Nzeru ndi utsiru zikuitana omvetsera kuti “apambukire kuno.” Koma kuitana kwake n’kosiyana. Nzeru ikuitana anthu kuti akamwe vinyo, kudya nyama, ndi mkate. Zomwe utsiru ukuitanira anthu zikutikumbutsa mkazi wachiwerewere. Solomo akuti: “Ati kwa yense wopanda nzeru, madzi akuba atsekemera, ndi chakudya chobisika chikoma.”—Miyambo 9:16b, 17.
Mmalo mwa vinyo wosanganiza, “mayi Utsiru” akuitanira anthu madzi akuba. (Miyambo 9:13, New International Version) M’Malemba, kusangalala pogona ndi mkazi wokondedwa amakufanizira ndi kumwa madzi otsitsimula. (Miyambo 5:15-17) Choncho, madzi akuba akuimira kuchita chiwerewere mwamtseri. Madzi otero, amaoneka kukhala otsekemera kuposa vinyo chifukwa n’ngakuba ndiponso umaganiza kuti zidzakhalabe zachinsinsi. Mkate wodyedwa mwachinsinsi ukuoneka kukhala wokoma kwambiri kuposa mkate ndi nyama yomwe nzeru ikupereka chifukwa chakuti ndi wopezeka mwachinyengo basi. Kukopeka ndi zinthu zoletsedwa zochitika mwamtseri, ndi chizindikiro cha uchitsiru.
Pamene kuitana kwa nzeru kukuphatikizapo lonjezo la moyo, mkazi wautsiru sakutchula chilichonse pa zotsatira za njira yake. Koma Solomo akuchenjeza kuti: “Mwamunayo sadziwa kuti akufa ali konko; omwe achezetsa utsiru ali m’manda akuya.” (Miyambo 9:18) “Nyumba ya [mkazi wautsiru] si yeniyeni koma chiliza chachikulu chapamanda. Ngati ulowamo, sutulukamo wamoyo,” analemba motero wophunzira wina. Kukhala ndi moyo wachiwerewere si nzeru; n’kusewera ndi imfa.
Yesu Kristu anati: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Tiyenitu nthaŵi zonse tizidya pa tebulo la nzeru ndi kukhala nawo panjira yopita ku moyo.
[Chithunzi patsamba 31]
Munthu wanzeru amavomereza malangizo
[Chithunzi patsamba 31]
Kupeza nzeru ndi udindo wa aliyense payekha