PHUNZIRO 35
N’chiyani Chingatithandize Kuti Tizisankha Zinthu Mwanzeru?
Tonsefe timafunika kusankha zochita pa moyo wathu. Komabe, zimene tingasankhe zingakhudze kwambiri moyo wathu komanso ubwenzi wathu ndi Yehova. Mwachitsanzo, timafunika kusankha komwe tikufuna kukakhala, mmene tingapezere ndalama komanso ngati tikufuna kukhala pabanja kapena ayi. Tikamasankha zinthu mwanzeru tikhoza kumakhala mosangalala komanso tingamasangalatse Yehova.
1. Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji kuti muzisankha zinthu mwanzeru?
Musanasankhe zochita pa nkhani inayake, muzipemphera kwa Yehova ndipo muzifufuza m’Baibulo kuti mudziwe maganizo a Yehova pa nkhaniyo. (Werengani Miyambo 2:3-6.) Nthawi zina Yehova amapereka lamulo lomveka bwino lokhudza nkhani inayake. Zikatero, mungachite bwino kwambiri kumvera lamulolo.
Ndiye kodi mungasankhe bwanji zochita pa nkhani imene m’Baibulo mulibe lamulo lachindunji lokhudza nkhaniyo? Yehova sadzasiya kukutsogolerani “m’njira imene muyenera kuyendamo.” (Yesaya 48:17) Kodi angachite bwanji zimenezi? M’Baibulo muli mfundo zimene zingakuthandizeni kusankha zochita. Mfundo za choonadi zomwe zimapezeka m’Baibulo zingakuthandizeni kudziwa maganizo a Mulungu pa nkhani yomwe mukufuna kusankhayo. Tikamawerenga Baibulo, nthawi zambiri timapeza mfundo zotithandiza kudziwa mmene Mulungu amaonera nkhani inayake. Choncho, tikazindikira mmene Yehova amamvera, timasankha zimene zimamusangalatsa.
2. Kodi muyenera kuganizira zinthu ziti musanasankhe zochita?
Baibulo limanena kuti: “Wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Zimenezi zikutanthauza kuti tifunika kuganiza kaye mofatsa tisanasankhe zochita. Choncho, musanasankhe zochita pa nkhani inayake, muzidzifunsa kuti: ‘Ndi mfundo ziti za m’Baibulo zomwe zingandithandize kusankha mwanzeru zoyenera kuchita pa nkhaniyi? Kodi zimene ndingasankhe zikhudza bwanji moyo wanga? Nanga anthu ena ziwakhudza bwanji?’ Chofunika kwambiri, muzidzifunsanso kuti, ‘Kodi zimene ndingasankhe zisangalatsa Yehova?’—Deuteronomo 32:29.
Yehova ali ndi ufulu wotiuza zoyenera kuchita ndi zosayenera kuchita. Tikadziwa bwino malamulo ndi mfundo zake n’kumayesetsa kuzigwiritsa ntchito pa moyo wathu, timakhala tikudziphunzitsa kuti chikumbumtima chathu chikhale chabwino. Chikumbumtima ndi chimene chimatithandiza kuzindikira kuti zomwe tikufuna kuchita kapena zomwe tachita ndi zolondola kapena zolakwika. (Aroma 2:14, 15) Choncho, tikamaphunzitsa bwino chikumbumtima chathu, chidzatithandiza kusankha zochita mwanzeru.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti muone mmene mfundo za m’Baibulo komanso chikumbumtima zingatithandizire kuti tizisankha zinthu mwanzeru.
3. Muzitsatira mfundo za m’Baibulo
Kodi mfundo za m’Baibulo zingatithandize bwanji tikamasankha zochita? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Kodi Yehova anatipatsa mphatso yamtengo wapatali iti?
N’chifukwa chiyani Yehova anatipatsa mphatso imeneyi?
Kodi Yehova watipatsa chiyani pofuna kutithandiza kusankha zinthu mwanzeru?
Kuti muone chitsanzo cha mfundo ya m’Baibulo, werengani Aefeso 5:15, 16. Kenako mukambirane mmene ‘mungagwiritsire ntchito bwino nthawi yanu’ . . .
powerenga Baibulo tsiku lililonse.
kuti mukhale mwamuna kapena mkazi wabwino, kholo kapenanso mwana wabwino.
kuti muzichita nawo misonkhano yampingo.
4. Muziphunzitsa chikumbumtima chanu kuti muzisankha zinthu mwanzeru
Sitimavutika kusankha zochita pa nkhani inayake ngati m’Baibulo muli lamulo lomveka bwino lokhudza nkhaniyo. Nanga bwanji ngati m’Baibulo mulibe lamulo lotithandiza kusankha zochita pa nkhani inayake? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Muvidiyoyi, kodi mlongoyu anachita chiyani kuti aphunzitse chikumbumtima chake komanso kuti asankhe zinthu zomwe zingasangalatse Yehova?
Tikafuna kusankha zochita pa nkhani inayake, n’chifukwa chiyani sitiyenera kupempha anthu ena kuti atisankhire zochita? Werengani Aheberi 5:14, kenako mukambirane mafunso awa:
Zingakhale zosavuta kupempha anthu ena kuti atisankhire zochita pa nkhani inayake. Koma kodi ifeyo patokha tiyenera kusiyanitsa chiyani?
N’chiyani chomwe chingakuthandizeni kuti muziphunzitsa chikumbumtima chanu komanso kuti muzisankha zochita mwanzeru?
5. Muzilemekeza zikumbumtima za anthu ena
Anthu amene ndi osiyana amasankhanso zinthu mosiyana. Ndiye tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza zikumbumtima za anthu ena? Taganizirani zochitika ziwiri izi:
Chochitika choyamba: Mlongo amene anazolowera kuphoda wasamukira mumpingo wina umene alongo amumpingomo amaona kuti kuphoda si koyenera.
Werengani Aroma 15:1 ndi 1 Akorinto 10:23, 24, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Malinga ndi mavesiwa, kodi mlongoyo angasankhe kuchita chiyani? Nanga inuyo mungatani ngati muli ndi munthu wina amene chikumbumtima chake sichikumulola kuchita zimene inuyo chikumbumtima chanu chikukulolani kuchita?
Chochitika chachiwiri: M’bale akudziwa bwino kuti Baibulo silimaletsa kumwa mowa mosapitirira malire, koma iyeyo wasankha kuti asamamwe mowa n’komwe. Kenako m’baleyo waitanidwa kuphwando ndipo akuona kuti abale ena akumwa mowa.
Werengani Mlaliki 7:16 ndi Aroma 14:1, 10, kenako mukambirane mafunso awa:
Malinga ndi mavesiwa, kodi m’baleyu angasankhe kuchita chiyani? Nanga inuyo mungatani ngati mwaona munthu wina amene chikumbumtima chake chikumulola kuchita zimene inuyo chikumbumtima chanu sichikukulolani kuchita?
Kodi ndi zinthu ziti zimene zingathandize munthu kusankha zinthu mwanzeru?
1. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kusankha zoyenera kuchita.—Yakobo 1:5.
2. Muzifufuza m’Baibulo, mabuku ndi zinthu zina zimene gulu lathu limafalitsa kuti mupeze mfundo zimene zingakuthandizeni. Mukhozanso kulankhulana ndi Akhristu okhwima mwauzimu.
3. Muziganizira mmene zosankha zanu zingakhudzire chikumbumtima chanu komanso zikumbumtima za anthu ena.
ZIMENE ENA AMANENA: “Aliyense ali ndi ufulu wochita zimene akufuna. Kaya anthu ena azinena zotani, ndi zawo zimenezo!”
N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mmene zochita zathu zingakhudzire Mulungu komanso anthu ena?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Tikadziwa maganizo a Yehova pa nkhani inayake timasankha zochita mwanzeru, kenako timaganizira mmene zochita zathuzo zingakhudzire anthu ena.
Kubwereza
Kodi mungasankhe bwanji zochita zimene zingasangalatse Yehova?
Kodi mungaphunzitse bwanji chikumbumtima chanu?
Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumalemekeza zikumbumtima za anthu ena?
ONANI ZINANSO
Mungatani kuti muzisankha zinthu zomwe zingakuthandizeni kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu?
“Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu” (Nsanja ya Olonda, April 15, 2011)
Dziwani zambiri zokhudza mmene Yehova amatipatsira malangizo.
Onani zimene zinathandiza munthu wina kusankha zochita mwanzeru pa nkhani yovuta.
Onani zimene tingachite kuti tizisangalatsa Yehova ngakhale pa nkhani zimene palibe lamulo lachindunji.
“Kodi Mumafunikira Lamulo la M’Baibulo Nthawi Zonse?” (Nsanja ya Olonda, December 1, 2003)