Lingaliro la Baibulo
Kodi Mulungu Amatidalitsa ndi Chuma?
“Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”—MIYAMBO 10:22.
KODI lemba la m’Baibulo lili pamwambali likutanthauza kuti Mulungu amadalitsa atumiki ake powapatsa chuma? Anthu ena amakhulupirira choncho. Talingalirani zimene ananena mlaliki wina wa tchalitchi cha Pentekositi ku Australia yemwenso amalemba mabuku. Iye anati: “M’buku [langa] ndikuuzani chifukwa chake mufunikira kukhala ndi ndalama zambiri ndipo chachiŵiri ndikuuzani mmene mungapezere ndalama zambiri . . . Ngati mungasinthe zoganiza zanu n’kuyamba kuganizira bwino za ndalama, ndikukhulupirira kuti Mulungu adzakudalitsani ndi kukulemeretsani ndipo simudzavutikanso kupeza ndalama.”
Komatu zonena zoterezi zimasonyeza kuti anthu osauka sayanjidwa ndi Mulungu. Kodi kukhala wolemera ndichodi chizindikiro chakuti Mulungu akukudalitsa?
Anawadalitsa ndi Cholinga
Zina mwa nkhani za m’Baibulo zimasimba za mmene Mulungu anadalitsira atumiki ake okhulupirika powapatsa chuma. Mwachitsanzo, Yakobo anachoka kwawo ali chabe ndi ndodo, koma patatha zaka 20 anabwerera ali ndi nkhosa, ng’ombe, ndi abulu zokwanira kupanga makamu aŵiri. Malinga n’kunena kwa Baibulo, kulemera kwa Yakobo inali mphatso yochokera kwa Mulungu. (Genesis 32:10) Nachi chitsanzo china: Katundu yense wa Yobu anawonongeka, koma kenako Yehova anadzamudalitsa ndi “nkhosa zikwi khumi ndi zinayi, ndi ngamila zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi ng’ombe zamagoli chikwi chimodzi, ndi abulu akazi chikwi chimodzi.” (Yobu 42:12) Yehova anapatsa Mfumu Solomo chuma chambiri zedi moti amatchuka nachobe mpaka pano.—1 Mafumu 3:13.
Komanso, m’Baibulo muli nkhani zambirimbiri za anthu olambira Mulungu okhulupirika ndi omvera amene anali osauka. Ndithudi, sitinganene kuti Mulungu anali kulanga anthu ena ndi umphaŵi ndi kudalitsa ena ndi chuma. Nangano cholinga cha Mulungu chinali chiyani popatsa anthu ena chuma?
Yankho lake ndi losiyana pa nkhani iliyonse. Chuma cha Yakobo chinali maziko oyambitsira mtundu winawake wa anthu pokonzekera kudza kwa Mbewu imene inalonjezedwa. (Genesis 22:17, 18) Kulemera kwa Yobu kunaonetsa poyera amene anamubweretsera masoka, motero dzina la Yehova linayeretsedwa. (Yakobo 5:11) Ndipo Solomo anagwiritsa ntchito chuma chake chochuluka chomwe anamupatsa Mulungu kumangira kachisi wokongola kwambiri. (1 Mafumu 7:47-51) N’zochititsa chidwi kuti Yehova anagwiritsanso ntchito Solomo kulemba, kuchokera pa zimene iye mwini anaziona, kuti chuma chilibe phindu lokhalitsa.—Mlaliki 2:3-11; 5:10; 7:12.
Mmene Mulungu Amatidalitsira
Yesu anaphunzitsa omutsatira kuti asamaganize kwambiri za ndalama pamene anawauza kuti ‘asadere nkhaŵa’ zokhala ndi chuma. Anawafotokozera kuti ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavale mokongola ngati mmene alili maluŵa a kuthengo. Ndiyeno Yesu anati: ‘Koma ngati Mulungu aveka chotero maudzu a kuthengo, nanga si inu opambana ndithu, inu akukhulupirira pang’ono?’ Yesu anatsimikizira Akristu kuti ngati omutsatira atafuna choyamba Ufumu ndi chilungamo cha Mulungu, ndiye kuti adzawapatsanso chakudya, zovala ndi pogona. (Mateyu 6:25, 28-33) Kodi lonjezo limeneli limakwaniritsidwa motani?
Munthu akamatsatira malangizo a m’Baibulo, makamaka amapindula mwauzimu. (Miyambo 10:22) Komabe, palinso phindu lina. Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu amalangiza Akristu kuti: “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito.” (Aefeso 4:28) Limanenanso kuti “wochita ndi dzanja laulesi amasauka; koma dzanja la akhama lilemeretsa.” (Miyambo 10:4) Akristu oona mtima ndiponso olimbikira ntchito amene amatsatira malangizo ameneŵa nthaŵi zambiri anthu amakonda kuwalemba ntchito. Limenelitu lingakhale dalitso.
Baibulo limaphunzitsanso Akristu kupeŵa chizoloŵezi chadyera chotchova njuga, khalidwe lodetsa thupi losuta fodya, ndiponso chizoloŵezi chofooketsa thupi cha kuledzera. (1 Akorinto 6:9, 10; 2 Akorinto 7:1; Aefeso 5:5) Amene amatsatira malangizo ameneŵa amaona kuti sakuwononganso ndalama zambiri ndiponso thanzi lawo limakhala labwinopo.
Chamtengo Wapatali Kuposa Siliva Kapena Golidi
Komabe, sikuti kupeza bwino ndicho chizindikiro chokhacho chosonyeza kuti Mulungu akuyanja ndi kudalitsa munthu winawake. Mwachitsanzo, Yesu anavumbula kuti Akristu ena a ku Laodikaya anali osauka mwauzimu pamene anawauza kuti: “Unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasoŵa kanthu; ndipo sudziŵa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiŵa.” (Chivumbulutso 3:17) Komano kwa Akristu osauka koma opeza bwino mwauzimu a ku Smurna, Yesu anati: “Ndidziŵa chisautso chako, ndi umphaŵi wako (komatu uli wachuma).” (Chivumbulutso 2:9) Mosakayikira Akristu ameneŵa anali ndi mavuto a zachuma chifukwa cha anthu amene ankawazunza chifukwa cha kukhulupirika kwawo, komatu iwo anali ndi chuma chamtengo wapatali kuposa siliva kapena golidi.—Miyambo 22:1; Ahebri 10:34.
Yehova Mulungu amadalitsa khama la anthu amene amayesetsa kuchita zimene iye amafuna. (Salmo 1:2, 3) Amawapatsa mphamvu ndiponso zinthu zofunikira kuti apirire ziyeso, kuti azisamalira mabanja awo, ndi kuti azitha kufuna Ufumu wake choyamba. (Salmo 37:25; Mateyu 6:31-33; Afilipi 4:12, 13) Choncho, m’malo moona kuti chuma ndicho dalitso lalikulu la Mulungu, Akristu oona amayesetsa kukhala ‘ochuluka ndi ntchito zabwino.’ Mwa kukulitsa ubwenzi wawo ndi Mlengi, Akristu ‘amadzikundikira okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi.’—1 Timoteo 6:17-19; Marko 12:42-44.