Kuongoka Mtima Kumatsogolera Olungama
“MUNTHU wobadwa ndi mkazi n’ngwa masiku oŵerengeka, nakhuta mavuto,” limatero Baibulo (Yobu 14:1) Anthu amakumanadi ndi mavuto. Ngakhale pa moyo wa tsiku ndi tsiku, tikhoza kukhala ndi nkhaŵa ndi mavuto osaneneka. Kodi n’chiyani chingatitsogolere kudutsa bwinobwino m’mavuto ndi kutithandiza kukhalabe olungama pamaso pa Mulungu?
Tiyeni tione chitsanzo cha Yobu, mwamuna wolemera kwambiri amene anakhalako zaka pafupifupi 3,500 zapitazo m’dziko limene pakalipano amati Arabia. Satana anavutitsa munthu woopa Mulungu ameneyu kwadzaoneni. Ziŵeto zake zonse zinawonongeka ndipo ana ake onse anamwalira. Ndiyeno, Satana anazunza Yobu ndi zilonda zoŵaŵa kuyambira kumutu mpaka kuphazi. (Yobu, machaputala 1 ndi 2) Yobu sanali kudziŵa chifukwa chake zonsezi zinam’chitikira. Komabe, “Yobu sanachimwa ndi milomo yake.” (Yobu 2:10) Iye anati: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.” (Yobu 27:5) Inde, ungwiro wake kapena kuti kuwongoka mtima kwake kunam’thandiza Yobu panthaŵi ya mayesero ake.
Kuwongoka mtima kumatanthauza kukhala ndi makhalidwe abwino komanso okwanira ndipo kumaphatikizapo kukhala wopanda chifukwa ndiponso wosalakwa pamaso pa Mulungu. Komabe, liwuli silitanthauza kuti anthu opanda ungwiro angalankhule ndi kuchita zinthu zangwiro, popeza iwo sangakwanitse kuchita zinthu mogwirizana ndendende ndi miyezo ya Mulungu. M’malo mwake, tikamati munthu ali ndi mtima woongoka ndiye kuti amadzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova ndi pochita zofuna ndi zolinga za Yehovayo. Kudzipereka kwa Mulungu kumeneko kumatsogolera olungama nthaŵi zonse pamene zinthu zili bwino ndi pamene zikuvuta. Mbali yoyamba ya chaputala 11 cha buku la m’Baibulo la Miyambo ikusonyeza mmene kuwongoka mtima kungatitsogolere m’mbali zosiyanasiyana za moyo ndiponso phindu limene tingapeze chifukwa cha zimenezo. Ndiyetu popeza tachita chidwi, tiyeni tione zimene zili m’chaputala chimenechi.
Kuwongoka Mtima Kumafuna Kukhulupirika pa Malonda
Mfumu Solomo ya Israyeli wakale pofotokoza mfundo ya kukhulupirika, inagwiritsa ntchito mawu a ndakatulo m’malo mwa mawu ogwiritsidwa ntchito pa za malamulo. Inati: “Muyeso wonyenga unyansa Yehova; koma mulingo wamphumphu um’sekeretsa.” (Miyambo 11:1) Aŵa ndi malo oyamba mwa malo anayi m’buku la Miyambo mmene anagwiritsa ntchito miyeso ndi milingo kusonyeza kuti Yehova amafuna kuti anthu amene amamulambira akhale okhulupirika pankhani za malonda.—Miyambo 16:11; 20:10, 23.
Munthu angakopeke chifukwa cha kutukuka kwa anthu amene amagwiritsa ntchito miyeso yonyenga, kapena osakhulupirika. Koma kodi tingakonde kusiya miyezo ya Mulungu ya chabwino ndi choipa mwa kuchita malonda achinyengo? Sitingatero ngati tili oongoka mtima. Timapeŵa chinyengo chifukwa Yehova amasangalala ndi mwala wonse woyesera, kutanthauza mulingo wolungama woimira kukhulupirika.
“Nzeru Ili ndi Odzichepetsa”
Mfumu Solomo inapitiriza kuti: “Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; koma nzeru ili ndi odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Kudzikuza, kaya mwa kunyada, mwano, kapena nsanje, kumadzetsa manyazi. Koma ngati modzichepetsa tizindikira kuti tili ndi zofooka, imeneyo ndi nzeru. Zitsanzo za m’Malemba zimasonyeza bwino kuti mwambi umenewu ndi woona.
Kora, Mlevi wansanje, anatsogolera gulu lopanduka kutsutsa ulamuliro wa Mose ndi Aroni, atumiki amene Yehova anawaika. Kodi n’chiyani chinachitika chifukwa cha kudzikuza kumeneko? “Dziko linayasama pakamwa pake ndi kuwameza” ena mwa oukirawo, pamene ena, kuphatikizapo Kora, ananyeka ndi moto. (Numeri 16:1-3, 16-35; 26:10; Deuteronomo 11:6) Zinalidi zamanyazi. Taganizaninso za Uza, amene podzikuza anagwira likasa la chipangano pofuna kuti lisagwe. Anam’kantha n’kufera pomwepo. (2 Samueli 6:3-8) Choncho, tiyeni tipeŵe kudzikuza.
Munthu wodzichepetsa sachita manyazi ngakhale atalakwa. Yobu anali munthu wopanda ungwiro ngakhale kuti iye ali chitsanzo chabwino m’njira zambiri. Mayesero ake anavumbula chofooka chachikulu pa zinthu zina zimene anali kuganiza. Pofuna kudziteteza kwa anthu amene anali kumuimba mlandu, Yobu sanasamale penapake. Anafika podziona ngati anali wolungama kuposa Mulungu. (Yobu 35:2, 3) Kodi Yehova anakonza bwanji maganizo a Yobu?
Yehova anam’phunzitsa Yobu kuti munthu ndi wamng’ono poyerekeza ndi ukulu wa Mulungu. Anatero mwa kum’fotokozera za dziko lapansi, nyanja, nyenyezi za kumwamba, nyama zina, ndi zodabwitsa zina za chilengedwe. (Yobu, machaputala 38-41) Polankhula, Yehova sanatchulepo chifukwa chake Yobu anali kuvutika. Sanafunikire kutero. Yobu anali wodzichepetsa. Anazindikira modzichepetsa kusiyana kwakukulu pakati pa iye ndi Mulungu, pakati pa kupanda ungwiro komanso kufooka kwake ndi chilungamo komanso mphamvu za Yehova. Iye anati: “Ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m’fumbi ndi mapulusa.” (Yobu 42:6) Chifukwa cha mtima wake woongoka, Yobu analandira chidzudzulo mosazengereza. Bwanji nanga ifeyo? Kodi kuwongoka mtima kumatithandiza kulandira chidzudzulo kapena chilango mosazengereza ngati zimenezi zikufunika?
Mose analinso wodzichepetsa. Mmene anayamba kutopa posamala mavuto a anthu ena, apongozi ake, a Yetero, anamuuza mfundo yothandiza yakuti agaŵe maudindo ena kwa amuna ena oyenerera. Mose pozindikira kuti panali zinthu zina zimene sakanatha kuchita, anavomera mwanzeru mfundo imeneyo. (Eksodo 18:17-26; Numeri 12:3) Munthu wodzichepetsa saumira kugaŵira ena maudindo ndiponso saopa kuti ulamuliro wake uchepa chifukwa chogaŵa maudindo kwa amuna ena oyenerera. (Numeri 11:16, 17, 26-29) M’malo mwake, iye amawathandiza ndi mtima wonse kuti apite patsogolo mwauzimu. (1 Timoteo 4:15) Kodi ifenso sitiyenera kuchita zimenezo?
‘Njira ya Wangwiro Ndi Yoongoka’
Solomo pozindikira kuti kuwongoka mtima sikuteteza olungama kuti asakumane ndi ngozi kapena mavuto, anati: “Kuwongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera; koma kukhota kwa achiwembu kudzawawononga.” (Miyambo 11:3) Kuwongoka mtima kumatsogoleradi anthu olungama kuti achite zoyenera pamaso pa Mulungu, ngakhale panthaŵi zovuta, ndipo kumawapindulitsa m’kupita kwa nthaŵi. Yobu anakana kutaya mtima wake woongoka, ndipo Yehova “anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake.” (Yobu 42:12) Anthu amene amachita zinthu mwachinyengo angaone ngati akupindula mwa kudyera masuku pamutu anthu ena ndipo kwakanthaŵi angaoneke ngati zinthu zikuwayendera bwino. Komabe nthaŵi ina iliyonse, chinyengo chawocho chidzawawononga.
Mfumu yanzeruyo inati: “Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo; koma chilungamo chipulumutsa ku imfa.” (Miyambo 11:4) N’kupusatu kugwira ntchito zolimba kuti tipeze chuma koma n’kunyalanyaza phunziro laumwini, pemphero, misonkhano, ndi utumiki wa kumunda—zinthu zimene zingatithandize kukonda kwambiri Mulungu ndi kulimbitsa kudzipereka kwathu kwa iye. Chuma, ngakhale chingachuluke bwanji, sichidzapulumutsa munthu pa chisautso chachikulu chimene chikubwera. (Mateyu 24:21) Chilungamo cha wolungama n’chimene chidzam’pulumutse. (Chivumbulutso 7:9, 14) Motero, timachita mwanzeru tikamamvera pempho la Zefaniya lakuti: ‘Lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova, funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso.” (Zefaniya 2:2, 3) Pakalipano cholinga chathu chikhale ‘kulemekeza Yehova ndi chuma chathu.’—Miyambo 3:9.
Solomo popitiriza kutsindika kufunika kotsata chilungamo, akufotokoza zimene zimachitikira wabwino ndi woipa. Akuti: “Chilungamo cha wangwiro chimawongola njira yake; koma woipa adzagwa ndi zoipa zake. Chilungamo cha oongoka mtima chidzawapulumutsa; koma achiwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yawo. Pomwalira woipa chidikiro chake chiwonongeka; chiyembekezo cha uchimo [“chokhalapo chifukwa cha mphamvu,” NW] chiwonongeka. Wolungama apulumuka kuvuto; woipa naloŵa m’malo mwake.” (Miyambo 11:5-8) Wolungama sagwa m’njira zake ndipo sakodwa ndi zochita zake. Njira yake ndi yowongoka. Mapeto ake, oongoka mtima amapulumuka ku mavuto. Oipa angaoneke ngati ndi amphamvu, koma sadzapulumuka.
“Mudzi Usekera”
Kuwongoka mtima kwa olungama ndiponso zimene woipa amachita zimakhudzanso anthu ena. Mfumu ya Israyeli inati: “Wonyoza Mulungu awononga mnzake ndi m’kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziŵa.” (Miyambo 11:9) Kodi alipo angatsutse zoti bodza, miseche, mawu otukwana, ndi njerengo zachabe zimavulaza ena? Kusiyana ndi zimenezi, wolungama amalankhula zabwino, amaganiza kaye asanalankhule, ndiponso amaganizira ena. Wolungama amapulumuka mwa zimene akudziŵa chifukwa kuwongoka mtima kwake kumam’thandiza kukhala ndi umboni wofunika kusonyeza kuti anthu amene akumuimba mlandu ndi abodza.
Mfumuyo inapitiriza kuti: “Olungama akapeza bwino, mudzi usekera; nufuula pakuwonongeka oipa.” (Miyambo 11:10) Olungama nthaŵi zambiri anthu amawakonda ndipo amachititsa anansi awo kusekera—kusangalala ndi kukhala achimwemwe. Palibe amene amakonda “oipa.” Anthu nthaŵi zambiri salira oipa akamwalira. Ndithudi, sipadzakhala kulira Yehova ‘akadzalikha oipa m’dziko ndi kuzulamo achiwembu.’ (Miyambo 2:21, 22) M’malo mwake, padzakhala chisangalalo chifukwa sadzakhalakonso. Koma bwanji nanga ifeyo? Tingachite bwino kuona ngati zimene timachita zimasangalatsa anthu ena.
“Akuza Mudzi”
Solomo akupitiriza kufotokoza mmene zochita za wolungama ndi woipa zimakhudzira anthu. Akuti: “Madalitso a olungama akuza mudzi; koma m’kamwa mwa oipa muupasula.”—Miyambo 11:11.
Anthu amene amachita zinthu zolungama pamudzi amalimbikitsa mtendere ndi moyo wabwino ndiponso amalimbikitsa ena. Motero, amakuza mudzi, zinthu zimayenda bwino pamudzipo. Amene amalankhula zojeda anzawo, zokhumudwitsa, ndiponso zinthu zachabe amayambitsa chisokonezo, chisoni, kusagwirizana ndi mavuto. Zimenezi zimakhala choncho makamaka ngati amene akuchita zimenezo ndi anthu amene ali ndi udindo pamudzipo. Pamudzi wotero pamakhala chisokonezo, katangale, makhalidwe oipa ndiponso mwina mavuto a zachuma.
Mfundo ya pa Miyambo 11:11 imagwiranso ntchito chimodzimodzi kwa anthu a Yehova akamasonkhana pamodzi m’mipingo yawo yonga midzi. Anthu auzimu—amene amatsatira kuwongoka mtima—akamatsogolera mpingo, anthu mumpingomo amakhala achimwemwe, okangalika ndiponso amakhala othandiza. Zimenezi zimalemekeza Mulungu. Yehova amadalitsa mpingowo, ndipo umayenda bwino mwauzimu. Nthaŵi zina, anthu ochepa odandaula ndi osakondwa, omwe amapeza anzawo zifukwa ndipo amalankhula moipidwa ndi mmene zinthu zikuyendera, ali ngati ‘muzu woŵaŵa’ umene ungafalikire ndi kuipitsa anthu ena amene poyamba analibe maganizo otero. (Ahebri 12:15) Nthaŵi zambiri anthu oterowo amafuna mpando ndi kutchuka. Amayambitsa mphekesera zakuti mumpingomo kapena akulu sakuchita chilungamo, pali kusankhana mafuko, kapena zinthu zina. Pakamwa pawo pangagaŵanitsedi mpingo. Kodi si bwino kusamvera zimene akunena ndi kuyesetsa kukhala anthu auzimu amene tingalimbikitse mtendere ndi mgwirizano mumpingo?
Solomo akupitiriza kuti: “Wopeputsa mnzake asoŵa nzeru; koma wozindikira amatonthola. Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi; koma wokhulupirika mtima abisa mawu.”—Miyambo 11:12, 13.
Inde, munthu wosazindikira, kapena ‘wosoŵa nzeru’ amayambitsa mavuto aakulu. Kulankhula kwake kosadziletsa amafika nako pochita miseche kapena kuchita chipongwe. Akulu oikidwa ayenera kuthetsa zinthu zoipa ngati zimenezi mwamsanga. Kusiyana ndi ‘wosoŵa nzeru,’ munthu wozindikira amadziŵa pamene afunikira kutonthola. Amabisa mawu, m’malo mowanditsa zinsinsi. Munthu wozindikira amakhala “wokhulupirika mtima” chifukwa amadziŵa kuti lilime lingavulaze kwambiri ngati salilamulira. Amakhulupirika kwa okhulupirira anzake ndipo saulula nkhani zachinsinsi zimene zingawaike pangozi. Anthu oongoka mtima ameneŵa amapindulitsa mpingo.
Pofuna kutithandiza kuyenda m’njira ya olungama, Yehova amatipatsa chakudya chauzimu chambiri chimene amachikonza kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Munthu aliyense payekha amalandiranso thandizo lalikulu kudzera mwa akulu achikristu m’mipingo yathu yonga midzi. (Aefeso 4:11-13) Tikuyamikira kwambiri zimenezi, chifukwa “popanda upo wanzeru anthu amagwa; koma pochuluka aphungu pali chipulumutso.” (Miyambo 11:14) Tiyenitu titsimikize mtima kuti ngakhale zitavuta bwanji, ‘tidzayendabe mu ungwiro wathu.’—Salmo 26:1.
[Mawu Otsindika patsamba 26]
N’kupusatu Kugwira Ntchito Zolimba Kuti Tipeze Chuma Koma N’kunyalanyaza Zinthu Zauzimu
[Zithunzi patsamba 24]
Kuwongoka mtima kunam’tsogolera Yobu ndipo Yehova anam’dalitsa
[Chithunzi patsamba 25]
Uza anafa chifukwa cha kudzikuza kwake