-
Kondani Phunziro Laumwini la Mawu a MulunguNsanja ya Olonda—2002 | December 1
-
-
9 Iye akupitiriza kuti: ‘Ukafunafuna [luntha] ngati siliva, ndi kulipwaira ngati chuma chobisika; . . . ’ (Miyambo 2:4) Zimenezi zikutichititsa kuganiza za ntchito za migodi za amuna amene kwa zaka zambiri akhala akufunafuna siliva ndi golidi, miyala imene amati ndi yamtengo wapatali. Anthu aphana chifukwa cha golidi. Ena akhala akufunafuna golidi moyo wawo wonse. Koma kodi golidi ali ndi mtengo wotani? Ngati mutasochera m’chipululu ndipo mwatsala pang’ono kufa ndi ludzu, kodi mungakonde chiyani: golidi kapena madzi? Komatu, anthu afunafuna golidi mwakhama kwambiri, ngakhale kuti mtengo wake ndi wosakhalitsa ndiponso umasinthasintha!a Kuli bwanji nanga kufunafuna nzeru, kuzindikira, ndi kufuna kumvetsa za Mulungu ndi chifuniro chake! Inde, tiyenera kuchita zimenezo mwakhama kwambiri. Koma kodi tingapindule chiyani ndi kufufuza koteroko?—Salmo 19:7-10; Miyambo 3:13-18.
-
-
Kondani Phunziro Laumwini la Mawu a MulunguNsanja ya Olonda—2002 | December 1
-
-
a Kuyambira mu 1979 mtengo wa golidi wakhala ukusinthasintha. Mu 1980, mtengo wa golidi unali madola 850 pa magalamu 31 alionse koma mu 1999 mtengowu unatsika n’kufika pa madola 252.80 pa magalamu 31 alionse.
-