“Khalanibe M’chikondi cha Mulungu”
“Khalanibe m’chikondi cha Mulungu. Teroni pamene mukuyembekezera chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pokhala ndi cholinga cha moyo wosatha.”—YUDA 21.
1, 2. Kodi Yehova wasonyeza motani chikondi chake kwa ife, ndipo tikudziwa bwanji kuti sikuti iye azingotikondabe kaya tichite zotani?
YEHOVA MULUNGU wasonyeza chikondi chake kwa ife m’njira zambirimbiri. Njira yapamwamba kwambiri imene Yehova wasonyezera chikondi chake ndiyo kupereka nsembe ya dipo. Iye amakonda kwambiri anthu moti mpaka anatumiza Mwana wake wokondedwa padziko lapansi kuti adzatifere. (Yoh. 3:16) Yehova anachita zimenezi chifukwa chakuti amafuna kuti tikhale ndi moyo wosatha ndiponso kuti tipindule ndi chikondi chake kosatha.
2 Koma kodi tiyenera kuganiza kuti Yehova azitikondabe mosasamala kanthu za zimene tikuchita? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti palemba la Yuda vesi 21 timalangizidwa kuti: “Khalanibe m’chikondi cha Mulungu. Teroni pamene mukuyembekezera chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pokhala ndi cholinga cha moyo wosatha.” Mawu akuti “khalanibe m’chikondi cha Mulungu,” amasonyeza kuti pali zimene tiyenera kuchita. Ndiyeno kodi tifunika kutani kuti tikhalebe m’chikondi cha Mulungu?
Kodi Tingatani Kuti Tikhalebe M’chikondi cha Mulungu?
3. Kodi Yesu anati n’chiyani chinali chofunika kuti iye akhalebe m’chikondi cha Atate ake?
3 Yankho la funso limeneli likupezeka m’mawu amene Yesu ananena, usiku womaliza wa moyo wake padziko lapansi. Iye anati: “Ngati musunga malamulo anga, mudzakhalabe m’chikondi changa, mmenenso ine ndasungira malamulo a Atate ndi kukhalabe m’chikondi chake.” (Yoh. 15:10) N’zoonekeratu kuti Yesu ankadziwa kuti ayenera kusunga malamulo a Yehova kuti akhalebe woyanjidwa ndi Atate akewo. Ngati zinali choncho ndi Mwana wa Mulungu yemwe anali wangwiro, ndiye kuli bwanji ifeyo?
4, 5. (a) Kodi njira yaikulu imene tingasonyezere kuti timakonda Yehova ndi iti? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kudana ndi mfundo yakuti tizimvera malamulo a Yehova?
4 Njira yaikulu imene tingasonyezere kuti timakonda Yehova ndiyo kumumvera. Pofotokoza mfundo imeneyi, mtumwi Yohane anati: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake; ndipo malamulo akewo si olemetsa.” (1 Yoh. 5:3) N’zoona kuti anthu ambiri masiku ano sakonda kumvera. Koma taganizirani mawu akuti: “Ndipo malamulo akewo si olemetsa.” Yehova satipempha kuchita zinthu zimene sitingakwanitse.
5 Tiyerekezere motere: Kodi inu mungapemphe mnzanu wapamtima kuti akunyamulireni katundu wolemera kwambiri amene mukudziwa kuti sangamukwanitse? Ayi ndithu simungatero. Yehova ndi wokoma mtima kwambiri kuposa ifeyo ndipo amadziwa bwino kwambiri zimene tingathe ndi zimene sitingathe kuchita. Baibulo limatiuza mawu olimbikitsa akuti Yehova ‘amakumbukira kuti ife ndife fumbi.’ (Sal. 103:14) Iye sangatiuze kuchita zinthu zimene sitingakwanitse. Motero palibe chifukwa choti tizidana ndi mfundo yakuti tiyenera kumvera malamulo a Yehova. M’malomwake timadziwa kuti kumvera Yehova kumatipatsa mwayi wosonyeza Atate wathu wakumwamba kuti timamukonda kwambiri ndipo timafuna kukhalabe m’chikondi chake.
Mphatso Yapadera Yochokera kwa Yehova
6, 7. (a) Kodi chikumbumtima n’chiyani? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza mmene chikumbumtima chingatithandizire kukhalabe m’chikondi cha Mulungu.
6 M’dziko lovuta limene tikukhalali, timafunika kupanga zosankha ndipo zosankha zimenezi zimasonyeza ngati timamvera Mulungu kapena ayi. Kodi tingatsimikize bwanji kuti zosankha zathu zikugwirizana ndi chifuniro cha Mulungu? Yehova watipatsa mphatso yapadera imene ingatithandize kwambiri pa nkhani ya kumvera. Mphatso imeneyi ndi chikumbumtima. Kodi chikumbumtima n’chiyani? Chikumbumtima ndi luso lotha kudzidziwa tokha. Chili ngati woweruza wa mumtima mwathu amene amatithandiza kuona zosankha zimene timapanga pa moyo wathu ndiponso amatithandiza kuganizira zimene tachita kale, n’kutiuza ngati zili zabwino kapena zoipa, ngati ndi zoyenera kapena zolakwika.—Werengani Aroma 2:14, 15.
7 Kodi tingatani kuti chikumbumtima chathu chizigwira bwino ntchito? Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti munthu wina ali paulendo ndipo akudutsa m’chipululu. M’chipululumo mulibe tinjira, misewu kapena zikwangwani koma iye akulondola bwinobwino kumene akupita. Kodi chikumuthandiza n’chiyani? Iye ali ndi kampasi. Kampasi imafanana ndi wotchi yamivi, koma imakhala ndi muvi umodzi wa maginito umene nthawi zonse umaloza kumpoto. Popanda kampasi munthuyo akhoza kusochera. Mofanana ndi munthu ameneyu, munthu wopanda chikumbumtima nthawi zambiri amasochera, osadziwa zimene angasankhe pa nkhani zokhudza makhalidwe abwino, chikhalidwe, komanso zoyenera kuchita.
8, 9. (a) Pa nkhani ya chikumbumtima chathu, kodi tiyenera kukumbukira chiyani? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti chikumbumtima chathu chizitithandiza?
8 Koma chikumbumtima, mofanana ndi kampasi, chingathe kutisokoneza. Ngati munthu woyenda m’chipululu uja ataika maginito pafupi ndi kampasi, muvi wa kampasiyo sungalozenso kumpoto. Ngati ifenso titatengeka kwambiri ndi zofuna za mtima wathu, kodi chingachitike n’chiyani? Mtima wathu wodzikonda ungasokoneze chikumbumtima chathu. Baibulo limatichenjeza kuti “mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.” (Yer. 17:9; Miy. 4:23) Komanso ngati munthu uja atakhala wopanda mapu olondola ndiponso odalirika, kampasi yake singamuthandize. Ifenso tikapanda kudalira kwambiri Baibulo, lomwe ndi lodalirika ndiponso ndi Mawu a Mulungu, chikumbumtima chathu sichingatithandize. (Sal. 119:105) N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri m’dzikoli amatengeka kwambiri ndi zofuna za mtima wawo, ndipo sasamalira kwenikweni kapenanso sasamalira n’komwe mfundo zimene Mulungu wapereka m’Mawu ake. (Werengani Aefeso 4:17-19.) N’chifukwa chake anthu ambiri amatha kuchita zinthu zoipa, ngakhale kuti ali ndi chikumbumtima.—1 Tim. 4:2.
9 Tiyenera kuyesetsa kuti tisakhale anthu otero. M’malomwake, tiyeni tipitirize kulola Mawu a Mulungu kuphunzitsa chikumbumtima chathu kuti chikhaledi chothandiza. Tiyenera kumvera chikumbumtima chathu chophunzitsidwa bwino Baibulo, m’malo mongotsatira zofuna za mtima wathu wodzikonda. Ndiponso tiyenera kumayesetsa kulemekeza chikumbumtima cha abale ndi alongo athu. Timayesetsa kuti tisawakhumudwitse, ndipo timakumbukira kuti chikumbumtima chawo chingawaletse kuchita zinthu zina zimene chikumbumtima chathu chingatilole kuchita.—1 Akor. 8:12; 2 Akor. 4:2; 1 Pet. 3:16.
10. Kodi tikambirana njira zitatu ziti zimene tingasonyezere kuti timakonda ndiponso kumvera Yehova?
10 Timasonyeza kuti timakonda Yehova mwa kukhala omvera, ndipo tiyeni tikambirane njira zitatu zimene tingachitire zimenezi. M’njira zonsezi chikumbumtima chiyenera kutitsogolera. Koma kuti zimenezi zitheke, chofunika kwambiri ndi chakuti chikumbumtimacho chiyenera kutsogoleredwa ndi mfundo zouziridwa za m’Baibulo zokhudza makhalidwe abwino. Njira zitatu zimene tingasonyezere kuti timam’konda Yehova ndiponso kumumvera ndi izi: (1) Kukonda anthu amene Yehova amawakonda, (2) kulemekeza ulamuliro, ndiponso (3) kuyesetsa kukhalabe oyera pamaso pa Mulungu.
Muzikonda Anthu Amene Yehova Amawakonda
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda anthu amene Yehova amawakonda?
11 Choyamba, tiyenera kukonda anthu amene Yehova amawakonda. Pa nkhani ya mayanjano, anthufe tili ngati thonje. Likaikidwa m’madzi, limayamwa madziwo. Nafenso timakonda kutengera anthu otizungulira. Mlengi wathu amadziwa bwino kuti anthu opanda ungwirofe tingathe kusokonezedwa kapena kuthandizidwa ndi anthu amene timacheza nawo. Motero amatipatsa malangizo anzeru awa: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33) Palibe amene amafuna ‘kupwetekedwa.’ Tonsefe timafuna kukhala “anzeru.” Yehova sangachititsidwe kukhala wanzeru kwambiri kuposa mmene alili, komanso palibe amene angawononge khalidwe lake labwino. Ngakhale zili choncho, iye amatipatsa chitsanzo chabwino pa nkhani ya mayanjano. Ndiyeno taganizirani izi: Kodi ndi anthu opanda ungwiro ati amene Yehova amawasankha kuti akhale mabwenzi ake?
12. Kodi Yehova amasankha anthu otani kukhala mabwenzi ake?
12 Yehova ananena kuti Abulahamu anali ‘bwenzi lake.’ (Yes. 41:8) Abulahamu anali chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kukhulupirika, chilungamo ndi kumvera. Iye anali munthu wa chikhulupiriro. (Yak. 2:21-23) Masiku anonso, anthu oterewa ndi amene Yehova amawasankha kuti akhale mabwenzi ake. Ngati Yehova amasankha mabwenzi oterewo, ndiye kuli bwanji ifeyo? Kodi si kofunika kuti tiziyenda ndi anthu anzeru kuti tikhalenso anzeru?
13. Pa nkhani yosankha mabwenzi, kodi n’chiyani chingatithandize?
13 Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kusankha bwino pa nkhani imeneyi? Kuphunzira zitsanzo za m’Baibulo n’kumene kungakuthandizeni. Taganizirani ubwenzi umene unalipo pakati pa Naomi ndi mpongozi wake Rute, Davide ndi Jonatani, kapenanso pakati pa Timoteyo ndi Paulo. (Rute 1:16, 17; 1 Sam. 23:16-18; Afil. 2:19-22) Chifukwa chachikulu chimene chinachititsa kuti anthu amenewa akhale mabwenzi apamtima, n’chakuti onse ankakonda Yehova. Kodi mungapeze mabwenzi amene amakonda Yehova ngati mmene inuyo mumachitira? Khalani otsimikiza kuti mungathe kupeza mabwenzi oterewa mumpingo wachikhristu. Mabwenzi oterewa sangakupweteketseni mwauzimu. M’malomwake angakuthandizeni kuti muzimvera Yehova, muzikula mwauzimu ndiponso kuti muzifesera mzimu. (Werengani Agalatiya 6:7, 8.) Mabwenzi oterewa adzakuthandizani kuti mukhalebe m’chikondi cha Mulungu.
Muzilemekeza Ulamuliro
14. Kodi ndi zinthu ziti zimene kawirikawiri zimachititsa kuti tizivutika kulemekeza ulamuliro?
14 Njira yachiwiri imene timasonyezera kuti timakonda Yehova, imakhudza ulamuliro. Tiyenera kulemekeza ulamuliro. Kodi n’chifukwa chiyani nthawi zina zimakhala zovuta kuti tichite zimenezi? Chifukwa chakuti anthu amene ali ndi ulamuliro ndi opanda ungwiro. Kuwonjezera pamenepo, ifenso ndife opanda ungwiro. Nthawi zonse timalimbana ndi chibadwa chathu chofuna kupanduka.
15, 16. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza anthu amene Yehova wawapatsa udindo wosamalira anthu ake? (b) Kodi ndi phunziro lofunika kwambiri liti limene tikupeza tikaganizira mmene Yehova anamvera Aisiraeli atapandukira Mose?
15 Mwina mungadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera ulamuliro ngati kuchita zimenezo kuli kovuta choncho?’ Yankho la funso limeneli limakhudza nkhani ya ulamuliro wachilengedwe chonse. Kodi inuyo mungasankhe ndani kukhala wolamulira wanu? Ngati mwasankha Yehova monga wolamulira wanu, muyenera kulemekeza ulamuliro wake. Kodi zingakhale zoona kunena kuti iye ndi wolamulira wathu, ngati sitilemekeza ulamuliro wake? Ndipotu Yehova amalamulira pogwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro amene iye wawapatsa udindo wosamalira anthu ake. Ndiyeno kodi Yehova angamve bwanji ngati ifeyo titapandukira anthu amenewa?—Werengani 1 Atesalonika 5:12, 13.
16 Mwachitsanzo, pamene Aisiraeli anang’ung’udza ndi kupandukira Mose, Yehova anaona kuti anthuwo akum’pandukira iyeyo. (Num. 14:26, 27) Mulungu sanasinthe. Ngati tingapandukire anthu amene iye wawapatsa udindo, ndiye kuti tikum’pandukira iyeyo.
17. Kodi tiyenera kuyesetsa kusonyeza mzimu wotani kwa anthu amene apatsidwa udindo mumpingo?
17 Mtumwi Paulo anafotokoza mmene tiyenera kuonera anthu amene apatsidwa udindo mumpingo wachikhristu. Iye analemba kuti: “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankha mlandu. Teroni kuti achite ntchito yawo mwa chimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuwonongani.” (Aheb. 13:17) N’zoona kuti pamafunika khama kuti tikhale ndi mzimu womvera ndiponso wogonjera. Koma kumbukirani kuti cholinga chathu ndi kuyesetsa kukhalabe m’chikondi cha Mulungu. Ndiye kodi sitiyenera kuchita chilichonse chimene tingathe kuti tikwaniritse cholinga chimenechi?
Khalanibe Oyera Pamaso pa Mulungu
18. N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizikhala oyera?
18 Njira yachitatu imene timasonyezera kuti timakonda Yehova ndi yakuti timayesetsa kukhalabe oyera pamaso pake. Makolo amayesetsa kwambiri kuti ana awo azioneka aukhondo. N’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Chifukwa chakuti ukhondo umathandiza kuti mwanayo akhale wathanzi labwino. Chifukwa chinanso n’chakuti mwana waukhondo amasonyeza kuti banja limene akuchokera ndi laukhondo ndiponso kuti makolo ake amam’konda ndi kumusamalira. Yehova amafunanso kuti tizikhala oyera pa zifukwa zomwezi. Iye amadziwa kuti kukhala oyera kumatithandiza kukhala ndi thanzi labwino. Iye amadziwanso kuti tikakhala oyera, timasonyeza mmene Atate wathu wakumwambayu alili. Zimenezi ndi zofunika kwambiri chifukwa anthu angakopeke ndi Mulungu amene timam’tumikira poona kuti ndife osiyana kwambiri ndi anthu odetsedwa a m’dzikoli.
19. Kodi tikudziwa bwanji kuti ukhondo ndi wofunika?
19 Kodi tifunika kukhala oyera m’mbali ziti? M’mbali zonse za moyo wathu. Mu Isiraeli wakale, Yehova anauza anthu ake kuti ukhondo ndi wofunika kwambiri. (Lev. 15:31) M’Chilamulo cha Mose munali malamulo ena okhudza kutaya zinyalala, kutsuka ziwiya, kusamba m’manja ndi mapazi ndiponso kuchapa zovala. (Eks. 30:17-21; Lev. 11:32; Num. 19:17-20; Deut. 23:13, 14) Zimenezi zinakumbutsa Aisiraeli kuti Yehova Mulungu wawo ndi woyera, kutanthauza kuti ndi “wosadetsedwa” ndiponso “wopatulika.” Motero atumiki a Mulungu, yemwe ndi woyera, afunikanso kukhala oyera.—Werengani Levitiko 11:44, 45.
20. Kodi tifunika kukhala oyera m’mbali ziti?
20 Choncho, tiyenera kukhala oyera mwauzimu ndi mwakuthupi. Timayesetsa kukhala oyera mwa kupewa kuganizira zinthu zoipa. Timatsatira mokhulupirika mfundo za Yehova za makhalidwe abwino, ngakhale kuti dzikoli likuipiraipira pa nkhani ya chiwerewere. Chofunika kwambiri n’chakuti timayesetsa kuti kulambira kwathu kukhale koyera ndiponso kuti tisadetsedwe ndi chipembedzo chonyenga. Nthawi zonse timakumbukira mawu ouziridwa otichenjeza amene ali pa Yesaya 52:11 akuti: “Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka.” Masiku ano timakhala oyera mwauzimu mwa kupeweratu kukhudza chilichonse chimene Atate wathu wakumwamba amaona kuti n’chodetsa pa nkhani ya kupembedza. N’chifukwa chake timaonetsetsa kuti sitikuchita nawo zikondwerero za chipembedzo chonyenga ndiponso maholide zimene ndi zofala masiku ano. N’zoona kuti kukhalabe oyera n’kovuta. Koma anthu a Yehova, amayesetsa kukhalabe oyera chifukwa chakuti kuchita zimenezi kumawathandiza kukhalabe m’chikondi cha Mulungu.
21. Kodi tingatani kuti tikhalebe m’chikondi cha Mulungu?
21 Yehova amafuna kuti tikhale m’chikondi chake mpaka kalekale. Koma aliyense payekha afunika kuyesetsa mmene angathere kuti akhalebe m’chikondi cha Mulungu. Tingachite zimenezi mwa kutengera chitsanzo cha Yesu ndiponso kusonyeza kuti timakonda Yehova mwa kumvera malamulo Ake. Tikatero, palibe chilichonse chimene ‘chingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.’—Aroma 8:38, 39.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi chikumbumtima chathu chingatithandize bwanji kukhalabe m’chikondi cha Mulungu?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda anthu amene Yehova amawakonda?
• N’chifukwa chiyani kulemekeza ulamuliro kuli kofunika?
• Kodi n’chifukwa chiyani kukhala oyera n’kofunika kwa anthu a Mulungu?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 20]
BUKU LIMENE LIMALIMBIKITSA MAKHALIDWE ABWINO
Pamsonkhano wachigawo wa 2008, panatuluka buku la masamba 224 la mutu wakuti, “Keep Yourselves in God’s Love.” Kodi cholinga cha buku latsopanoli n’chiyani? Bukuli lakonzedwa kuti lithandize Akhristu kudziwa ndiponso kukonda mfundo za Yehova, ndipo limafotokoza kwambiri khalidwe limene Akhristu ayenera kukhala nalo. Kuphunzira mosamala buku limeneli kudzatithandiza kusakayikira ngakhale pang’ono kuti kutsatira mfundo za Yehova ndi njira yabwino kwambiri pa moyo wathu ndipo kungatithandize kudzapeza moyo wosatha.
Chofunika kwambiri n’chakuti bukuli lakonzedwa kuti litithandize kuzindikira kuti kumvera Yehova si kolemetsa, koma ndi njira imene timasonyezera kuti timakonda Yehova. Motero bukuli lingatichititse kudzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani ineyo ndimamvera Yehova?’
Nthawi zambiri anthu amene amasiya kukonda Yehova, vuto limakhala khalidwe lawo osati kusadziwa zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani inayake. Motero tifunika kukonda kwambiri malamulo ndi mfundo za Yehova zimene zimatitsogolera pa moyo wathu n’kumaziona kuti ndi zofunika kwambiri. Tikukhulupirira kuti buku latsopano limeneli lithandiza nkhosa za Yehova padziko lonse kukhala zolimba pochita zabwino, kusonyeza kuti Satana ndi wabodza ndipo koposa zonse kukhalabe m’chikondi cha Mulungu.—Yuda 21.
[Chithunzi patsamba 18]
“Ngati musunga malamulo anga, mudzakhalabe m’chikondi changa, mmenenso ine ndasungira malamulo a Atate ndi kukhalabe m’chikondi chake”