Lozetsani Mtima Wanu ku Kuzindikira
“Yehova apatsa nzeru; kudziŵa [“chidziwitso,” NW] ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.”—MIYAMBO 2:6.
1. Kodi tingalozetse motani mtima wathu ku kuzindikira?
YEHOVA ndiye Mlangizi wathu Wamkulu. (Yesaya 30:20, 21, NW) Koma kodi tiyenera kuchitanji kuti tipindule ndi ‘kudziŵadi Mulungu’ kovumbulidwa m’Mawu ake? China nchakuti tiyenera ‘kulozetsa mtima wathu ku kuzindikira’—kukhala ndi chikhumbo chaphamphu chakupeza mkhalidwe umenewu ndi kuusonyeza. Kuti tichite zimenezi, tiyenera kuyang’ana kwa Mulungu, pakuti mwamuna wanzeru anati: “Yehova apatsa nzeru; kudziŵa [“chidziŵitso”] ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.” (Miyambo 2:1-6) Kodi chidziŵitso, nzeru, ndi kuzindikira nchiyani?
2. (a) Kodi chidziŵitso nchiyani? (b) Kodi mungafotokoze kuti nzeru nchiyani? (c) Kodi kuzindikira nchiyani?
2 Chidziŵitso ndicho kudziŵa zinthu kupyolera mwa zochitika, kuona, kapena kuphunzira. Nzeru ndiyo kukhoza kugwiritsira ntchito chidziŵitso. (Mateyu 11:19) Mfumu Solomo anasonyeza nzeru pamene akazi aŵiri analimbirana mwana mmodzi ndipo anagwiritsira ntchito chidziŵitso chake cha chikondi chimene mayi amakhala nacho pa mwana wake kuthetsera mkanganowo. (1 Mafumu 3:16-28) Kuzindikira ndiko “luntha la kuweruza.” Ndiko “mphamvu kapena luso la maganizo limene iwo amasiyanitsira chinthu china ndi chinzake.” (Webster’s Universal Dictionary) Tikalozetsa mtima wathu ku kuzindikira, Yehova adzatipatsa kupyolera mwa Mwana wake. (2 Timoteo 2:1, 7) Koma kodi kuzindikira kumakhudza motani mbali za moyo zosiyanasiyana?
Kuzindikira ndi Kalankhulidwe Kathu
3. Kodi mungaifotokoze motani Miyambo 11:12, 13 ndi tanthauzo lake lakukhala ‘wosoŵa mtima’?
3 Kuzindikira kumatithandiza kudziŵa kuti pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:7) Mkhalidwe umenewu umachititsa kuti tizisamala zimene tinena. Miyambo 11:12, 13 imati: “Wopeputsa mnzake asoŵa nzeru [“mtima,” NW]; koma wozindikira amatonthola. Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi; koma wokhulupirika mtima abisa mawu.” Inde, mwamuna kapena mkazi wopeputsa munthu wina “asoŵa mtima.” Malinga ndi wolemba dikishonale Wilhelm Gesenius, munthu wotero “alibe luntha.” Saganiza bwino, ndipo ntchito ya liwu lakuti “mtima” imasonyeza kuti akusoŵa mikhalidwe yabwino ya munthu wamkati. Ngati munthu amene amati ndi Mkristu apitiriza ndi kukambakamba kwake mpaka kusinjirira ena kapena kulalata, akulu oikidwa ayenera kuchitapo kanthu kuti athetse mkhalidwe woipawu mumpingo.—Levitiko 19:16; Salmo 101:5; 1 Akorinto 5:11.
4. Kodi Akristu ozindikira ndi okhulupirika amatani nacho chinsinsi?
4 Mosiyana ndi aja ‘osoŵa mtima,’ anthu ‘ozindikira’ amatonthola pamene afunikira kutero. Samaulula chinsinsi. (Miyambo 20:19) Podziŵa kuti kulankhula kosadziletsa kungavulaze ena, anthu ozindikira ‘ngokhulupirika mtima.’ Ngokhulupirika kwa okhulupirira anzawo ndipo samaulula zinsinsi zimene zingawaike pangozi. Ngati Akristu ozindikira alandira chidziŵitso chachinsinsi cha mtundu uliwonse chokhudza mpingo, amachisunga okha kufikira gulu la Yehova litaona kuti kuli bwino kudziŵitsa ena mwa kuchifalitsa iwo okha.
Kuzindikira ndi Khalidwe Lathu
5. Kodi ‘zitsiru’ zimaona motani zoipa, ndipo chifukwa ninji?
5 Miyambi ya Baibulo imatithandiza kugwiritsira ntchito kuzindikira ndi kupeŵa khalidwe loipa. Mwachitsanzo, Miyambo 10:23 imati: “Maseŵero a chitsiru ndiwo kuchita zoipa; koma maseŵero a wozindikira ndiwo nzeru.” Anthu amene amayesa “zoipa” ngati “maseŵero” saona kuipa kwa njira yawo ndipo saganiza kuti onse adzadziŵerengera mlandu kwa Mulungu. (Aroma 14:12) Malingaliro a ‘zitsiru’ zimenezo amapotoka moti zimaganiza kuti Mulungu saona zoipa zawo. Mwa ntchito zawo, amakhala akunena kuti: “Kulibe Mulungu.” (Salmo 14:1-3; Yesaya 29:15, 16) Posatsogozedwa ndi mapulinsipulo aumulungu, alibe kuzindikira ndipo satha kuweruza zinthu bwino.—Miyambo 28:5.
6. Kodi nchifukwa ninji zoipa ndizo utsiru, ndipo tidzaziona motani ngati ndife ozindikira?
6 “Wozindikira” adziŵa kuti zoipa si “maseŵero” ayi. Adziŵa kuti zimamkwiyitsa Mulungu ndipo zingatiwonongere unansi wathu ndi iye. Khalidwe lotero ndi uchitsiru chifukwa limalanda anthu ulemu, kuwononga maukwati, kuvulaza zonse ziŵiri maganizo ndi thupi, ndipo limatayitsa mkhalidwe wauzimu. Chifukwa chake, tiyeni tilozetse mtima wathu ku kuzindikira ndi kupeŵa zoipa zamtundu uliwonse.—Miyambo 5:1-23.
Kuzindikira ndi Mzimu Wathu
7. Kodi mkwiyo umachita zotani m’thupi?
7 Kulozetsa mtima wathu ku kuzindikira kumatithandizanso kulamulira mzimu wathu. “Wosakwiya msanga apambana kumvetsa [“kuzindikira,” NW],” imatero Miyambo 14:29, “koma wansontho akuza utsiru.” Chifukwa china chimene munthu wozindikira amalimbikira kupeŵa mkwiyo wosalamulirika nchakuti umayambukira thupi lathu moipa. Ungakweze BP ndi kuyambitsa matenda a m’chifuŵa. Madokotala anena kuti mkwiyo ndi ukali ndiyo mikhalidwe ya mtima imene imakuza kapena kuchititsa matenda onga phumi, matenda a khungu, m’mimba, ndi zilonda za m’mimba.
8. Kodi kukhala wansontho kungachite chiyani, koma kodi kuzindikira kungatithandize motani pamenepa?
8 Sikuti tiyenera kugwiritsira ntchito kuzindikira ndi kukhala “wosakwiya msanga” chabe kuti tipeŵe kuwononga thanzi lathu ayi. Kukhala wansontho kungatichititse zinthu zopusa zimene tingachite nazo chisoni. Kuzindikira kumatipangitsa kuganiza zimene zingatsatire kalankhulidwe kosadziletsa kapena khalidwe lansontho, motero kumatiletsa ‘kukuza utsiru’ mwa kuchita chinthu chopanda nzeru. Makamaka, kuzindikira kumatithandiza kudziŵa kuti ukali umasokoneza kaganizidwe kathu, moti sititha kuganiza bwino. Zimenezi zingasakaze kukhoza kwathu kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kusunga mapulinsipulo olungama a Mulungu. Inde, kulola mkwiyo wosalamulirika kumawononga mwauzimu. Ndipotu “zopsa mtima” zili m’gulu la “ntchito za thupi” zonyansa zimene zingatiletse kuloŵa Ufumu wa Mulungu. (Agalatiya 5:19-21) Choncho, monga Akristu ozindikira, tikhale ‘otchera khutu, odekha polankhula, odekha pakupsa mtima.’—Yakobo 1:19.
9. Kodi kuzindikira ndi kukonda abale kungatithandize motani kuthetsa kusamvana?
9 Titakwiya, kuzindikira kungatiuze kukhala chete kuti tipeŵe mikangano. Miyambo 17:27 imati: “Wopanda chikamwakamwa apambana kudziŵa; ndipo wofatsa mtima ali wanzeru [“wozindikira,” NW].” Kuzindikira ndi kukonda abale kudzatithandiza kuona kuti kulamulira chikhumbo cha kubwetekuka zinthu zopweteka kuli kofunika. Ngati talalata kale chifukwa cha mkwiyo, chikondi ndi kudzichepetsa zidzatisonkhezera kupepesa ndi kuwongola zinthu. Koma bwanji ngati wina watiputa. Tikambe naye payekha mofatsa ndi modzichepetsa ndipo cholinga chachikulu chikhale kubwezeretsa mtendere.—Mateyu 5:23, 24; 18:15-17.
Kuzindikira ndi Banja Lathu
10. Kodi nzeru ndi kuzindikira zili ndi ntchito yanji pamoyo wa banja?
10 Apabanja afunika kusonyeza nzeru ndi kuzindikira, pakuti mikhalidwe imeneyi idzamanga nyumba. Miyambo 24:3, 4 imatero kuti: “Nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa. Kudziŵa kudzaza zipinda zake ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake.” Nzeru ndi kuzindikira zili monga njerwa zabwino zomangira moyo wa banja wachimwemwe. Kuzindikira kumathandiza makolo achikristu kusonkhezera ana awo kufotokoza zakukhosi kwawo ndi nkhaŵa zawo. Munthu wozindikira atha kulankhulana ndi mnzake wa muukwati, kumvetsera ndi kudziŵa zimene zili mumtima mwake ndi zolingalira zake.—Miyambo 20:5.
11. Kodi mkazi wokwatiwa wozindikira ‘angamange nyumba yake’ motani?
11 Nzeru ndi kuzindikira nzofunikadi pa moyo wa banja wachimwemwe. Mwachitsanzo, Miyambo 14:1 imati: “Mkazi yense wanzeru amanga banja lake; koma wopusa alipasula ndi manja ake.” Mkazi wokwatiwa wanzeru ndi wozindikira womvera mwamuna wake moyenera amagwiritsa ntchito kaamba ka ubwino wa banja lake, choncho amathandiza kumanga banja lake. Chimene ‘chimamanga banja lake’ nchakuti nthaŵi zonse amalankhula zabwino za mwamuna wake, motero amawonjeza ulemu umene ena amampatsa. Ndipo mkazi waluso ndi wozindikira, amenenso amaopa Yehova mwaulemu, amadzipezera thamo.—Miyambo 12:4; 31:28, 30.
Kuzindikira ndi Moyo Wathu
12. Kodi aja ‘osoŵa mtima’ amauona motani utsiru, ndipo chifukwa ninji?
12 Kuzindikira kumatithandiza kutsata njira yoyenera pazochita zathu zonse. Miyambo 15:21 imasonyeza zimenezi, yomwe imati: “Wosoŵa nzeru [“mtima,” NW] akondwera ndi utsiru; koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ake.” Kodi tingati mwambiwu ukunenanji? Njira yautsiru imakondweretsa amuna, akazi, ndi ana opusa. Iwo ‘asoŵa mtima,’ alibe cholinga chabwino, ndipo ngopandiratu nzeru kwakuti amakondwera ndi utsiru.
13. Kodi Solomo anazindikiranji ponena za kuseka ndi chiphwete?
13 Mfumu Solomo ya Israyeli yozindikira inadziŵa kuti chiphwete sichithandiza konse. Iyo inati: “Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe. Ndinati, Kuseka ndi misala; ndi chimwemwe kodi chichita chiyani?” (Mlaliki 2:1, 2) Monga mwamuna wozindikira, Solomo anapeza kuti chisangalalo ndi kuseka sizikhutiritsa mwa izo zokha, pakuti sizimadzetsa chimwemwe chenicheni chosatha. Kuseka kungatithandize kuiŵala mavuto athu kanthaŵi koma pambuyo pake angatulukirenso, aakulu kwambiri. Ndi chifukwa chabwino, Solomo anati kuseka ndi “misala.” Chifukwa? Chifukwa kuseka kosalingalira kumaphimba kuganiza bwino. Kungatichititse kuona zinthu zazikulu mopepuka. Sitinganene kuti chimwemwe chimene anadzetsa mawu ndi zochita za wanthabwala wa m’bwalo la mfumu chinatulutsa zabwino. Kuzindikira tanthauzo la zimene Solomo anapeza ponena za kuseka ndi chisangalalo kumatithandiza kupeŵa kukhala “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.”—2 Timoteo 3:1, 4.
14. Kodi munthu wozindikira “aongola mayendedwe ake” bwanji?
14 Kodi zili bwanji kuti munthu wozindikira “aongola mayendedwe ake”? Kuzindikira kwauzimu ndi kugwiritsira ntchito mapulinsipulo aumulungu kumatsogoza anthu panjira yolungama ndi yoongoka. Baibulo la Byington limati mosapita m’mbali: “Utsiru ukondweretsa munthu wopanda mutu, koma munthu waluntha adzayenda molunjika.” “Munthu wozindikira” amalambula njira yolunjika yoyendamo mapazi ake ndipo atha kusiyanitsa chabwino ndi choipa chifukwa chotsata Mawu a Mulungu m’moyo wake.—Ahebri 5:14; 12:12, 13.
Yang’anani kwa Yehova Nthaŵi Zonse Kaamba ka Kuzindikira
15. Kodi tikuphunziraponji pa Miyambo 2:6-9?
15 Kuti tiyende panjira yolungama ya moyo, ife tonse tifunika kuvomereza kuti ndife opanda ungwiro ndi kuyang’ana kwa Yehova kaamba ka kuzindikira kwauzimu. Miyambo 2:6-9 imati: “Yehova apatsa nzeru; kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake; Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni; ndiye chikopa cha oyenda molunjika; kuti achinjirize njira za chiweruzo, nadikire khwalala la opatulidwa ake. Pamenepo udzazindikira chilungamo ndi chiweruzo, zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.”—Yerekezerani ndi Yakobo 4:6.
16. Nchifukwa ninji kulibe nzeru, luntha kapena uphungu wotsutsana ndi Yehova?
16 Podziŵa kuti timadalira Yehova, tiyeni modzichepetsa tiyesetse kuzindikira chifuniro chake mwa kukumba mozama Mawu ake. Iye ali ndi nzeru zonse, ndipo uphungu wake umapindula nthaŵi zonse. (Yesaya 40:13; Aroma 11:34) Kunena zoona, uphungu uliwonse wotsutsana naye ngwachabe. Miyambo 21:30 imati: “Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.” (Yerekezerani ndi Miyambo 19:21.) Kuzindikira kwauzimu kokha, kopezeka mwa kuphunzira Mawu a Mulungu mothandizidwa ndi zofalitsa zoperekedwa mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndiko kudzatithandiza kulondola njira yoyenera m’moyo. (Mateyu 24:45-47) Chifukwa chake, tiyeni titsogoze moyo wathu mogwirizana ndi uphungu wa Yehova, podziŵa kuti ngakhale uphungu wina wosiyana uoneke wabwino motani, sungafanane ndi Mawu ake.
17. Kodi chingachitike nchiyani uphungu utaperekedwa wolakwika?
17 Akristu ozindikira amene amapereka uphungu adziŵa kuti uyenera kuzikidwa zolimba pa Mawu a Mulungu ndi kuti afunikira phunziro la Baibulo ndi kusinkhasinkha asanayankhe funso. (Miyambo 15:28) Ngati mafunso ayankhidwa molakwa pankhani zazikulu, pangakhale chivulazo chachikulu. Chifukwa chake, akulu achikristu afunika kuzindikira kwauzimu ndipo ayenera kupempherera chitsogozo cha Yehova pamene akufuna kuthandiza okhulupirira anzawo mwauzimu.
Mukhale ndi Kuzindikira Kwauzimu Kochuluka
18. Mumpingo mutabuka vuto, kodi kuzindikira kungatithandize bwanji kukhalabe okhazikika mwauzimu?
18 Kuti tikondweretse Yehova, tifunikira “chidziŵitso [“kuzindikira,”NW] m’zonse.” (2 Timoteo 2:7) Kuphunzira Baibulo mwakhama ndi kutsatira chitsogozo cha mzimu wa Mulungu ndi gulu lake kudzatithandiza kuzindikira zochita titakhala mumkhalidwe umene ungatiloŵetse panjira yolakwa. Mwachitsanzo, tinene kuti nkhani ina mumpingo sikusamalidwa mwanjira imene tikuganiza. Kuzindikira kwauzimu kudzatithandiza kuona kuti chimenecho si chifukwa chosiyira kuyanjana ndi anthu a Yehova ndi kuleka kutumikira Mulungu. Talingalirani za mwaŵi wathu wotumikira Yehova, za ufulu wauzimu umene tili nawo, za chimwemwe chimene timapeza mu utumiki wathu monga olengeza Ufumu. Kuzindikira kwauzimu kumatithandiza kukhala ndi kapenyedwe koyenera ndi kukumbukira kuti ndife odzipatulira kwa Mulungu ndi kuti tiyenera kusunga unansi wathu ndi iye, kaya ena achita zotani. Ngati palibe chimene tingachite mwateokrase kuti tisamalire vutolo, tifunikira kuyembekeza moleza mtima kuti Yehova aongole zinthu. M’malo moleka kapena kutaya mtima, ‘tiyembekeze Mulungu.’—Salmo 42:5, 11.
19. (a) Kodi mfundo yaikulu ya pemphero la Paulo m’malo mwa Afilipi inali yotani? (b) Kodi kuzindikira kungatithandize motani ngati sitikumvetsetsa kanthu kena?
19 Kuzindikira kwauzimu kumatithandiza kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu ndi anthu ake. Paulo anauza Akristu ku Filipi kuti: “Ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chiwonjezere, m’chidziŵitso [cholongosoka, NW], ndi kuzindikira konse; kuti mukayese inu zinthu zosiyana [“zofunika kwambiri,” NW]; kuti mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Kristu.” (Afilipi 1:9, 10) Kuti tilingalire bwino, tifunikira “chidziŵitso [cholongosoka], ndi kuzindikira konse.” Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “kuzindikira” panopa limatanthauza “kuganizira makhalidwe kosamala.” Titaphunzira kanthu kena, tiyenera kuganizira za kugwirizana kwake ndi Mulungu ndi Kristu ndi kusinkhasinkha za mmene kamaonetsera kwambiri umunthu wa Yehova ndi zogaŵira zake. Zimenezi zimakuza kuzindikira kwathu ndi chiyamikiro chathu cha zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu atichitira ife. Ngati sitikumvetsetsa kanthu kena, kuzindikira kudzatithandiza kuona kuti sitikutaya chikhulupiriro chathu mwa zinthu zonse zofunika zimene taphunzira ponena za Mulungu, Kristu, ndi chifuno chaumulungu.
20. Kodi ndi motani mmene tingakhalire ndi kuzindikira kwauzimu kochuluka?
20 Tidzakhala ndi kuzindikira kwauzimu kochuluka ngati nthaŵi zonse tigwirizanitsa malingaliro athu ndi zochita zathu ndi Mawu a Mulungu. (2 Akorinto 13:5) Kuchita zimenezi mwanjira yanzeru kudzatithandiza kukhala odzichepetsa, osati oumirira nganganga malingaliro athu ndiponso osuliza ena. Kuzindikira kudzatithandiza kupindula ndi chidzudzulo ndi kutsimikiza zinthu zofunika kwambiri. (Miyambo 3:7) Popeza tikufuna kukondweretsa Yehova, tiyesetse kudzala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Mawu ake. Chimenechi chidzatithandiza kusiyanitsa chabwino ndi choipa, kudziŵa chofunika koposa, ndi kuulimbikira mokhulupirika unansi wathu wamtengo wapatali ndi Yehova. Zonsezi zidzatheka tikalozetsa mtima wathu ku kuzindikira. Komabe, pakufunika chinthu china. Tiyenera kulola kuzindikira kutichinjiriza.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Nchifukwa ninji tiyenera kulozetsa mtima wathu ku kuzindikira?
◻ Kodi kuzindikira kungakhudze motani kalankhulidwe kathu ndi khalidwe lathu?
◻ Kodi kuzindikira kungaukhudze motani mzimu wathu?
◻ Nchifukwa ninji tiyenera kuyang’ana kwa Yehova nthaŵi zonse kaamba ka kuzindikira?
[Chithunzi patsamba 13]
Kuzindikira kumatithandiza kulamulira mzimu wathu
[Chithunzi patsamba 15]
Mfumu Solomo wozindikira anadziŵa kuti chiphwete sichikhutiritsa konse