Buku Lothandiza pa Moyo Wamakono
Mabuku opereka uphungu ngotchuka kwambiri m’dziko lamakono. Koma amatha ntchito ndipo posapita nthaŵi amakonzedwanso kapenanso amaloŵedwa m’malo ndi ena. Bwanji nanga za Baibulo? Linatha kulembedwa pafupifupi zaka 2,000 zapitazo. Komabe, uthenga wake woyambirira sunasinthidwepo kapena kukonzedwanso. Kodi zingatheke kuti buku loterolo nkukhala ndi malangizo othandiza masiku ano?
ENA amati sizingatheke. “Kulibe munthu amene angalimbikitse kugwiritsira ntchito buku [lophunziramo] chemistry la m’chaka cha 1924 m’kalasi lamakono la chemistry,” analemba motero Dr. Eli S. Chesen, pofotokoza chifukwa chake anaganiza kuti Baibulo linatha ntchito.1 Lingaliro limeneli likuoneka lanzeru. Ndi iko komwe, munthu waphunzira zochuluka za thanzi la maganizo ndi za khalidwe la munthu kuchokera pamene Baibulo linalembedwa. Chotero zingatheke bwanji kuti buku lakale limenelo nkukhala lofunika pa moyo wamakono?
Mfundo Zosasintha ndi Nthaŵi
Pamene nzoona kuti nthaŵi zasintha, zofunika zazikulu za anthu zakhala chimodzimodzi. Anthu kuyamba ndi kale lonse m’mbiri amafuna kukondedwa. Amafuna kukhala achimwemwe ndi kukhala ndi moyo watanthauzo. Amafuna uphungu umene ungawathandize kulimbana ndi mavuto a zachuma, mmene angakhalire bwino m’maukwati awo, ndi mmene angaphunzitsire ana awo makhalidwe abwino ndi mwambo. Baibulo lili ndi uphungu umene umakwaniritsa zofunika zazikuluzo.—Mlaliki 3:12, 13; Aroma 12:10; Akolose 3:18-21; 1 Timoteo 6:6-10.
Uphungu wa Baibulo umasonyeza kuti ilo limamvetsetsa chibadwa cha munthu. Tiyeni tipende zitsanzo zina za mfundo zake zolunjika ndi zosasintha ndi nthaŵi zimene zili zothandiza pa moyo wamakono.
Malangizo Othandiza mu Ukwati
Banja, ikutero magazini yakuti UN Chronicle, “ndilo chigwirizano chakale kuposa zonse ndipo ndilo maziko enieni a chikhalidwe cha anthu; ndilo mlunzanitsi wofunika kwambiri pakati pa mibadwo.” Komabe, “mlunzanitsi wofunika kwambiri” ameneyu akuduka mofulumira kwambiri. “M’dziko lamakono,” ikutero Chronicle, “mabanja ambiri ali m’mavuto aakulu amene akusokoneza moyo wake kuti usamayende bwino, amenetu akuika pangozi kukhalapo kwake.”2 Kodi Baibulo limapereka uphungu wotani kuthandiza mabanja kupulumuka?
Choyamba, Baibulo limanena zochuluka mmene amuna ndi akazi awo ayenera kuonerana. Mwachitsanzo, limati kwa amuna: ‘Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha; pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga.’ (Aefeso 5:28, 29) Mkazi anauzidwa ‘kuopa mwamuna’ wake.—Aefeso 5:33.
Talingalirani mapindu akutsatira uphungu wa Baibulo umenewo. Mwamuna amene akonda mkazi wake ‘monga ngati thupi la iye yekha’ samada mkazi wake kapena kumchita nkhanza. Sammenya, ndipo samtukwana kapena kumsautsa mtima. M’malo mwake, amamŵerengera ndi kumlingalira muja amadzichitira yekha. (1 Petro 3:7) Chotero mkazi wake amamva kukhala wokondedwa ndi wotetezeka mu ukwati wake. Mwanjira imeneyo amaikira ana ake chitsanzo chabwino kusonyeza mmene ayenera kuchitira ndi akazi. Komanso, mkazi amene ‘amaopa’ mwamuna wake samamchotsera ulemu wake mwa kumsuliza nthaŵi zonse kapena kumnyoza. Chifukwa chakuti mkaziyo amapatsa mwamuna wake ulemu, iye amaona kuti mkazi wake amamkhulupirira, kumyanja, ndi kumŵerengera.
Kodi uphungu umenewo ngwothandiza m’dziko lamakono? Zimasangalatsa kudziŵa kuti aja amene ali akatswiri pa kufufuza mabanja lerolino anena zofanana ndi zimenezo. Woyang’anira programu yopatsa mabanja uphungu anati: “Mabanja abwino kwambiri amene ndikuwadziŵa ndi aja amene mayi ndi tate amakondana kwambiri. . . . Unansi wofunika ndi wolimba umenewu umapangitsa ana kumva kuti ali pamtendere.”3
Pazaka zambiri, uphungu wa Baibulo wakhala wodalirika kwambiri kuposa uphungu wa aphungu ambiri a mabanja amenenso zolinga zawo nzabwino. Ndi iko komwe, si kale kwambiri pamene akatswiri ambiri anali kulimbikitsa kuti chisudzulo ndiyo njira yamwamsanga ndi yosavuta yomasukira ku ukwati wamavuto. Lero, ambiri a iwo akulimbikitsa anthu kusunga maukwati awo ngati nkotheka. Koma kusintha kumeneku kwakhalapo pambuyo poti mabanja ambiri awonongeka.
Kusiyana ndi zimenezo, Baibulo limapereka uphungu wodalirika ndi wabwino pankhani ya ukwati. Limavomereza kuti nthaŵi zina zinthu zikafika poipa chisudzulo chimaloleka. (Mateyu 19:9) Komanso, limatsutsa kusudzulana pazifukwa zopanda kumutu. (Malaki 2:14-16) Limatsutsanso kusakhulupirika mu ukwati. (Ahebri 13:4) Limatero kuti ukwati nkudzipereka: ‘Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.’a—Genesis 2:24; Mateyu 19:5, 6.
Uphungu wa Baibulo pa ukwati ngwofunika lerolino monganso unalili pamene Baibulo linalembedwa. Pamene mwamuna ndi mkazi wake akondana ndi kulemekezana ndi kuona ukwati monga unansi wa iwo okha, ukwati ungapulumuke—limodzi ndi banja.
Malangizo Othandiza Makolo
Zaka makumi ambiri zapitazo, makolo ambiri—posonkhezeredwa ndi “malingaliro achimakono” a kaleredwe ka ana—anaganiza kuti “kulanga ana kunali koletsedwa.”8 Iwo anali kuopa kuti kuikira ana malire kungawasautse mtima ndi kuwakhumudwitsa. Aphungu okhala ndi zolinga zabwino pa kaleredwe ka ana anali kulimbikitsa kuti makolo sayenera kulanga ana awo kwambiri. Koma akatswiri ambiri amenewo tsopano akusinthanso maganizo awo ponena za nchito ya chilango, ndipo makolo osamala akufuna kuti nkhani imeneyi imveketsedwe bwino.
Komabe, pazaka zonsezo Baibulo lapereka uphungu wabwino ndiponso womveka wonena za kulera ana. Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, linati: “Atate inu, musamakwiyitsa ana anu, koma pitirizani kuwalera m’chilango ndi kuwongolera maganizo kwa Yehova.” (Aefeso 6:4, NW) Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “chilango” limatanthauza “maleredwe, kuphunzitsa, kulangiza.”9 Baibulo limatero kuti chilango chotero, kapena kulangiza, ndiwo umboni wa chikondi cha makolo. (Miyambo 13:24) Ana amakula ali ndi malangizo omveka a makhalidwe abwino ndipo amakhala akudziŵa chabwino ndi choipa. Chilango chimawasonyeza kuti makolo awo amasamala za iwo ndiponso za mtundu wa anthu omwe iwo akukhala.
Koma ulamuliro wa makolo—‘nthyole yolangira’—suyenera kukhala wankhanza.b (Miyambo 22:15; 29:15) Baibulo limachenjeza makolo kuti: “Musamawawongolera mopambanitsa ana anu, kuti mungawatayitse mtima.” (Akolose 3:21, Phillips) Limavomerezanso kuti nthaŵi zambiri kulanga mwana mwa kumkwapula sindiko njira yothandiza kwambiri yomphunzitsira. Miyambo 17:10 imati: “Chidzudzulo chiloŵa mkati mwa wozindikira, kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.” Ndiponso, Baibulo limalimbikitsa chilango choteteza. Pa Deuteronomo 11:19 makolo akulimbikitsidwa kugwiritsira ntchito mpata wa nthaŵi yocheza kukhomereza mwa ana awo makhalidwe abwino.—Onaninso Deuteronomo 6:6, 7.
Uphungu wosasintha wa m’Baibulo kwa makolo ngwomveka. Ana afunika kuwalanga nthaŵi zonse ndiponso mwachikondi. Zochitika zikusonyeza kuti uphungu umenewo umagwiradi ntchito.c
Kugonjetsa Zopinga Zomwe Zimagaŵa Anthu
Anthu lero ngogaŵikana chifukwa cha zopinga zonga kusankhana fuko, dziko, ndi mtundu. Zinthu zimenezo zonga makoma zasonkhezera anthu padziko lonse lapansi kuphana m’nkhondo popanda chifukwa. Malinga ndi zimene zachitika m’mbiri, palibe chiyembekezo chakuti amuna ndi akazi a mafuko ndi maiko osiyanasiyana adzaona kuti ali olingana ndi kuchitirana molingana. “Njira yothetsera vutolo,” akutero wandale wina wa mu Afirika, “ili m’mitima yathu.”11 Komatu kusintha mtima wa munthu si nkhani yapafupi ayi. Komabe, taonani mmene uthenga wa Baibulo umakopera mtima ndi kulimbikitsa mzimu woonana chimodzimodzi.
Chiphunzitso cha Baibulo chakuti Mulungu “[mwa munthu, NW] mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu” chimachotseratu ganizo lakuti fuko lina nlopambana. (Machitidwe 17:26) Chimasonyeza kuti kwenikweni pali fuko limodzi lokha—fuko la anthu. Baibulo limatilimbikitsanso ‘kukhala akutsanza a Mulungu,’ amene limati: “Alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Aefeso 5:1; Machitidwe 10:34, 35) Aja amene amalilemekeza kwambiri Baibulo, amenenso amayesetsa kutsatira ziphunzitso zake, chidziŵitso chimenechi chimawagwirizanitsa. Mphamvu yake imagwira ntchito mkatikati mwawo, mumtima wa munthu, kusungunula zopinga zoikidwamo ndi anthu zimene zimagaŵa anthu. Taonani chitsanzochi.
Pamene Hitler anali pankhondo mu Ulaya yense, panali gulu limodzi la Akristu—Mboni za Yehova—amene anakana zolimba kuthandizana nawo kupha anthu opanda mlandu. Iwo ‘sananyamule lupanga’ kumenyana ndi anthu anzawo. Sanachite zimenezo chifukwa chofuna kukondweretsa Mulungu. (Yesaya 2:3, 4; Mika 4:3, 5) Anakhulupiriradi zimene Baibulo limaphunzitsa—kuti kulibe mtundu kapena fuko loposa linzake. (Agalatiya 3:28) Chifukwa cha kukonda kwawo mtendere, Mboni za Yehova zinali pakati pa akaidi oyamba m’misasa yachibalo.—Aroma 12:18.
Koma si onse amene ankati akutsatira Baibulo omwe anachita zimenezo. Nkhondo Yadziko II itangotha, Martin Niemöller, mtsogoleri wa chipembedzo wachiprotestanti wa ku Germany, analemba kuti: “Yense amene afuna kupatsa Mulungu mlandu wa [nkhondo] sadziŵa Mawu a Mulungu, kapena safuna kuwadziŵa. . . . Matchalitchi achikristu, m’mbiri yonse, mobwerezabwereza akhala akudalitsa nkhondo, asilikali, ndi zida ndipo . . . apempherera mwanjira yosakhala yachikristu konse kuti adani awo akawonongeke kunkhondo. Wonsewu ndi mlandu wathu ndiponso mlandu wa makolo athu, koma si mlandu wa Mulungu ayi. Ndipo ife Akristu amakono timachita manyazi pamaso pa otchedwa ampatuko onga Ophunzira Baibulo Akhama [Mboni za Yehova], amene mazanamazana ndipo zikwizikwi anapita kumisasa yachibalo [ngakhale] kufa chifukwa anakana utumiki wa nkhondo nakana kuwombera anthu mfuti.”12
Mpaka lero, Mboni za Yehova zimadziŵika kwambiri chifukwa cha ubale wawo, umene umagwirizanitsa Aluya ndi Ayuda, Akroati ndi Asebu, Ahutu ndi Atutsi. Komabe, Mboni sizizengereza kutchula kuti umodzi umenewo watheka, osati chifukwa chakuti izo nzabwino kuposa ena, koma chifukwa chakuti mphamvu ya uthenga wa Baibulo imawasonkhezera.—1 Atesalonika 2:13.
Malangizo Othandiza pa Kukhala ndi Maganizo Abwino
Thanzi la munthu nthaŵi zambiri limakhudzidwa ndi mkhalidwe wa maganizo ake ndi mtima wake. Mwachitsanzo, asayansi pakufufuza kwawo apeza kuti mkwiyo umakhala ndi zotsatira zake zoipa. “Umboni wochuluka womwe ulipo ukusonyeza kuti anthu amene amakwiya msanga ali pangozi yaikulu yodwala nthenda ya mtima (ndi matenda enanso) chifukwa cha zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo kusoŵa mabwenzi, kusokonezeka kwa zinthu m’thupi atakwiya, ndi kuchita zinthu zambiri zangozi pa thanzi lawo,” akutero Dr. Redford Williams, Director of Behavioral Research pa Duke University Medical Center, ndi mkazi wake, Virginia Williams, m’buku lawo lakuti Anger Kills.13
Zaka zikwi zambiri asayansi asanafufuze zimenezo, Baibulo, ndi mawu apafupi koma omveka, linasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa mkhalidwe wa mtima wathu ndi thanzi lathu: “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi; koma nsanje ivunditsa mafupa.” (Miyambo 14:30; 17:22) Mwanzeru, Baibulo linalangiza kuti: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo” ndi kuti, “Usakangaze mumtima mwako kukwiya.”—Salmo 37:8; Mlaliki 7:9.
Baibulo lilinso ndi uphungu wanzeru mmene munthu angalamulirire mkwiyo. Mwachitsanzo, Miyambo 19:11 imati: “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.” Liwu lachihebri la “kulingalira” latengedwa ku verebu imene imafotokoza za “kudziŵa chifukwa” chake.14 Uphungu wanzeru ngwakuti: “Yambani mwaganiza musanachite kalikonse.” Kuyesetsa kumvetsa chifukwa chimene ena amalankhulira kapena kuchita mwanjira ina yake kungathandize munthu kukhala wololera kwambiri—ndipo wosakwiyakwiya.—Miyambo 14:29.
Uphungu wina wothandiza ukupezeka pa Akolose 3:13, umene umati: “Lolerana[ni] wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha.” Kukhumudwa pa tinthu tating’onong’ono ndimo mmene moyo wakhalira. Mawu akutiwo “loleranani” akusonyeza kulekerera zinthu zimene sitimakonda mwa ena. “Kukhululukira” kumatanthauza kuleka mkwiyo. Nthaŵi zina kumakhala kwanzeru kuleka zakukhosi m’malo mozisunga; kusunga mkwiyowo kumangowonjezera mtolo wathu.—Onani bokosi lakuti “Malangizo Othandiza pa Maunansi a Anthu.”
Lero, pali ambiri amene amapereka uphungu ndi malangizo. Koma Baibulo nlosiyana nawo kotheratu. Uphungu wake si nthanthi wamba ayi, ndipo nzeru yake simativulaza konse. M’malo mwake, nzeru yake ‘yakhala yodalirika kwambiri.’ (Salmo 93:5, NW) Ndiponso, uphungu wa Baibulo ngwosasintha. Ngakhale kuti linamalizidwa pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, mawu ake adakagwirabe ntchito. Ndipo amagwira ntchito ndi mphamvu imodzimodzi kaya khungu lathu likhale lamaonekedwe otani kapenanso kaya tikukhala m’dziko liti. Mawu a Baibulo alinso ndi mphamvu—mphamvu yosintha anthu kukhala abwino. (Ahebri 4:12) Chotero kuŵerenga bukulo ndi kugwiritsira ntchito mfundo zake kungawongolere moyo wanu kukhala wabwino.
[Mawu a M’munsi]
a Liwu lachihebri lakuti da·vaqʹ, lotembenuzidwa kuti “nadzadziphatika” panopo, “lili ndi tanthauzo la kummamatira wina wake mwachikondi ndi mokhulupirika.”4 M’Chigiriki, liwu lotembenuzidwa kuti “nadzaphatikizana” pa Mateyu 19:5 lili paubale ndi liwu lotanthauza “kumamatiza,” “kuphatika ndi sementi,” “kulumikizana zolimba.”5
b M’nthaŵi za m’Baibulo, liwulo “nthyole” (Chihebri, sheʹvet) linali kutanthauza “mtengo” kapena “ndodo,” ngati ija imene mbusa amagwiritsira ntchito.10 Pano, nthyole ya ulamuliro ikutanthauza kulangiza mwachikondi, osati nkhanza yokhaulitsa ayi.—Yerekezerani ndi Salmo 23:4.
c Onani mitu yakuti “Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake,” “Thandizani Wachinyamata Wanu Kukula Bwino,” “Kodi Muli ndi Wopanduka m’Nyumba?”, ndi wakuti “Tetezerani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga” m’buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Mawu Otsindika patsamba 24]
Baibulo limapereka uphungu wabwino ndiponso womveka pa moyo wa banja
[Bokosi patsamba 23]
Mikhalidwe ya Mabanja Abwino
Zaka zambiri zapitazo mphunzitsi wina amenenso ndi katswiri pa zabanja anayamba kufufuza kwambiri. Pakufufuzako anapempha akatswiri oposa 500 amene amapatsa mabanja uphungu kuti akambepo pa mikhalidwe imene anaona m’mabanja “abwino.” Zimene zinasangalatsa nzakuti mikhalidwe yambiri imene anaitchula ndi ija imene Baibulo linalimbikitsa kalekale.
Kulankhulana kwabwino kunali koyamba, kuphatikizapo njira zabwino zothetsera mikangano. Chizoloŵezi chopezeka m’mabanja onse abwino nchakuti “palibe amene amapita kukagona ali wokwiya ndi mnzake,” anatero wofufuzayo.6 Komabe, zaka zoposa 1,900 zapitazo, Baibulo linalangiza kuti: “Kwiyani, koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26) Nthaŵi za Baibulo tsiku linali kuyamba dzuŵa litaloŵa ndi kuthanso dzuŵa litaloŵa tsiku lotsatira. Chotero, kalekale, akatswiri amakono asanaphunzire za mabanja, Baibulo mwanzeru linalangiza kuti: Thetsani msanga mikangano—tsiku lisanathe ndipo lina lisanayambe.
Mabanja abwino “samayamba kukambitsirana nkhani zimene wina angakwiye nazo pamene akukonzeka kuchoka panyumba kapena kugona,” ndizo anapeza wofufuzayo. “Nthaŵi ndi nthaŵi ndinamva mawu akuti ‘panthaŵi yake.’”7 Mabanja amenewo mosadziŵa anali kubwereza mwambi wa m’Baibulo umene unalembedwa zaka zoposa 2,700 zapitazo: ‘Mawu oyenera a panthaŵi yake akunga zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.’ (Miyambo 15:23; 25:11) Fanizo limeneli lingakhale likunena za zokometsera zagolidi zonga zipatso zoikidwa m’nsengwa zasiliva zochemba—zimene zinali chuma chamtengo wapatali ndiponso zokongola m’nthaŵi za Baibulo. Limasonyeza kukongola kwake ndi phindu lake la mawu okambidwa panthaŵi yoyenera. Zinthu zitavuta, mawu oyenera okambidwa panthaŵi yake ngamtengo wapatali.—Miyambo 10:19.
[Bokosi patsamba 26]
Malangizo Othandiza pa Maunansi a Anthu
“Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe: nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.” (Salmo 4:4) Nthaŵi zambiri patakhala zoputa zazing’ono, mungachite mwanzeru kusalankhula, ndipo mudzapewa kukhumudwitsana.
“Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.” (Miyambo 12:18) Yambani mwaganiza musanalankhule. Mawu osasamala angavulaze ena ndi kuwononga ubwenzi.
“Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu oŵaŵitsa aputa msunamo.” (Miyambo 15:1) Pamafunika kudziletsa kuti munthu ayankhe mofatsa, koma njira imeneyi nthaŵi zambiri imachepetsa mavuto ndi kulimbikitsa maunansi amtemdere.
“Chiyambi cha ndewu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.” (Miyambo 17:14) Kuli kwanzeru kuchoka musanakwiye pamene zinthu zikuipa.
“Usafulumire kusonyeza mkwiyo; pakuti zitsiru ndizo zimasunga mkwiyo.” (Mlaliki 7:9, The New English Bible) Nthaŵi zambiri mkwiyo ndiwo umayamba munthu asanachite kanthu. Munthu wofulumira kukwiya ngwopusa, chifukwa zimenezo zingampangitse kulankhula kapena kuchita kanthu kena mwansontho.
[Chithunzi patsamba 25]
Mboni za Yehova zinali pakati pa akaidi oyamba m’misasa yachibalo