-
Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
-
-
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUSAMALA POLANKHULA?
4, 5. Kodi miyambi ina ya m’Baibulo imafotokoza kuti mawu ali ndi mphamvu yotani?
4 Chifukwa chimodzi chofunika kwambiri chomwe tiyenera kukhalira osamala polankhula n’chakuti mawu ali ndi mphamvu. Lemba la Miyambo 15:4 limati: “Lilime lodekha lili ngati mtengo wa moyo, koma lilime lachinyengo limapweteketsa mtima.”a Mawu odekha amalimbikitsa ena monga mmene madzi amapangitsira mtengo umene unafota kusangalala. Mosiyana ndi zimenezo, mawu oipa a lilime lachinyengo amakhumudwitsa ena. Zoonadi, zolankhula zathu zingavulaze kapena kuchiritsa ena.—Miyambo 18:21.
-
-
Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
-
-
a Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti ‘chinyengo’ pa Miyambo 15:4 angatanthauzenso ‘kukhota’ kapena ‘kupotoka.’
-